Beginning
96 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano;
Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.
2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake;
lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
3 Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko,
ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.
4 Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.
5 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano,
koma Yehova analenga mayiko akumwamba.
6 Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake,
mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.
7 Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
8 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake;
bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.
9 Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake;
njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.
10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.”
Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe;
Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.
11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere;
nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
12 minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo.
Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;
13 idzayimba pamaso pa Yehova,
pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi;
adzaweruza dziko lonse mwachilungamo
ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.
97 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;
magombe akutali akondwere.
2 Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;
chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
3 Moto umapita patsogolo pake
ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
4 Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;
dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
5 Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,
pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
6 Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,
ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.
7 Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,
iwo amene amanyadira mafano;
mulambireni, inu milungu yonse!
8 Ziyoni akumva ndipo akukondwera,
midzi ya Yuda ikusangalala
chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
9 Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;
ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.
10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama,
ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama
ndipo tamandani dzina lake loyera.
Salimo.
98 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;
dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera
zamuchitira chipulumutso.
2 Yehova waonetsa chipulumutso chake
ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.
3 Iye wakumbukira chikondi chake
ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;
malekezero onse a dziko lapansi aona
chipulumutso cha Mulungu wathu.
4 Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,
muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.
5 Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,
ndi zeze ndi mawu a kuyimba,
6 ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna
fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.
7 Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.
8 Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,
mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;
9 izo ziyimbe pamaso pa Yehova,
pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,
ndi mitundu ya anthu mosakondera.
99 Yehova akulamulira,
mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
dziko lapansi ligwedezeke.
2 Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
3 Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
Iye ndi woyera.
4 Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
5 Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mulambireni pa mapazi ake;
Iye ndi woyera.
6 Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
ndipo Iyeyo anawayankha.
7 Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.
8 Inu Yehova Mulungu wathu,
munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
9 Kwezani Yehova Mulungu wathu
ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.
Salimo. Nyimbo yothokoza.
100 Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
2 Mulambireni Yehova mosangalala;
bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
3 Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.
Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;
ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.
4 Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
5 Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;
kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.
Salimo la Davide.
101 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;
kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
2 Ndidzatsata njira yolungama;
nanga mudzabwera liti kwa ine?
Ndidzayenda mʼnyumba mwanga
ndi mtima wosalakwa.
3 Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa
pamaso panga.
Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;
iwo sadzadziphatika kwa ine.
4 Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;
ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.
5 Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri
ameneyo ndidzamuletsa;
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,
ameneyo sindidzamulekerera.
6 Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,
kuti akhale pamodzi ndi ine;
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa
adzanditumikira.
7 Aliyense wochita chinyengo
sadzakhala mʼnyumba mwanga.
Aliyense woyankhula mwachinyengo
sadzayima pamaso panga.
8 Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu
onse oyipa mʼdziko;
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa
mu mzinda wa Yehova.
Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko.
102 Yehova imvani pemphero langa;
kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
2 Musandibisire nkhope yanu
pamene ndili pa msautso.
Munditcherere khutu;
pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.
3 Pakuti masiku anga akupita ngati utsi;
mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
4 Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu;
ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
5 Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula
ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
6 Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu,
monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
7 Ndimagona osapeza tulo; ndakhala
ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
8 Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe;
iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
9 Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa
ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
10 chifukwa cha ukali wanu waukulu,
popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
11 Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo;
Ine ndikufota ngati udzu.
12 Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya;
kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
13 Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni
pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo;
nthawi yoyikika yafika.
14 Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu;
fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova,
mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
16 Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni
ndi kuonekera mu ulemerero wake.
17 Iye adzayankha pemphero la anthu otayika;
sadzanyoza kupempha kwawo.
18 Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo,
kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:
19 “Yehova anayangʼana pansi kuchokera ku malo ake opatulika mmwamba,
kuchokera kumwamba anayangʼana dziko lapansi,
20 kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende,
kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.”
21 Kotero dzina la Yehova lidzalengezedwa mu Ziyoni
ndi matamando ake mu Yerusalemu,
22 pamene mitundu ya anthu ndi maufumu
adzasonkhana kuti alambire Yehova.
23 Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga;
Iyeyo anafupikitsa masiku anga.
24 Choncho Ine ndinati:
“Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga;
zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.
25 Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi
ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu.
26 Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo;
zidzatha ngati chovala.
Mudzazisintha ngati chovala
ndipo zidzatayidwa.
27 Koma Inu simusintha,
ndipo zaka zanu sizidzatha.
28 Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu;
zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.