Beginning
146 Tamandani Yehova.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
2 Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse;
ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.
3 Musamadalire mafumu,
anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.
4 Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi;
zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.
5 Wodala ndi amene thandizo lake ndi
Mulungu wa Yakobo.
6 Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi,
nyanja ndi zonse zili mʼmenemo;
Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
7 Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa
ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Yehova amamasula amʼndende,
8 Yehova amatsekula maso anthu osaona,
Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi,
Yehova amakonda anthu olungama.
9 Yehova amasamalira alendo
ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye,
koma amasokoneza njira za anthu oyipa.
10 Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya,
Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse.
Tamandani Yehova.
147 Tamandani Yehova.
Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu,
nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!
2 Yehova akumanga Yerusalemu;
Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.
3 Akutsogolera anthu osweka mtima
ndi kumanga mabala awo.
4 Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi,
ndipo iliyonse amayitchula dzina.
5 Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri;
nzeru zake zilibe malire.
6 Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa,
koma amagwetsa pansi anthu oyipa.
7 Imbirani Yehova ndi mayamiko;
imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
8 Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo;
amapereka mvula ku dziko lapansi
ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.
9 Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe
ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.
10 Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo,
kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.
11 Yehova amakondwera ndi amene amamuopa,
amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.
12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu;
tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,
13 pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako
ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.
14 Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako
ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.
15 Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi;
mawu ake amayenda mwaliwiro.
16 Amagwetsa chisanu ngati ubweya
ndi kumwaza chipale ngati phulusa.
17 Amagwetsa matalala ngati miyala.
Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?
18 Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka;
amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.
19 Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo,
malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.
20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;
anthu enawo sadziwa malamulo ake.
Tamandani Yehova.
148 Tamandani Yehova.
Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
2 Mutamandeni, inu angelo ake onse,
mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
5 Zonse zitamande dzina la Yehova
pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
6 Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
analamula ndipo sizidzatha.
7 Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
8 inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
9 inu mapiri ndi zitunda zonse,
inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
inu nkhalamba ndi ana omwe.
13 Onsewo atamande dzina la Yehova
pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
matamando a anthu ake onse oyera mtima,
Aisraeli, anthu a pamtima pake.
Tamandani Yehova.
149 Tamandani Yehova.
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.
2 Israeli asangalale mwa mlengi wake;
anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.
3 Atamande dzina lake povina
ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.
4 Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake;
Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.
5 Oyera mtima asangalale mu ulemu wake
ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.
6 Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo,
ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,
7 kubwezera chilango anthu a mitundu ina,
ndi kulanga anthu a mitundu yonse,
8 kumanga mafumu awo ndi zingwe,
anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,
9 kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo
Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse.
Tamandani Yehova.
150 Tamandani Yehova.
Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika;
mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.
2 Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu;
mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
3 Mutamandeni poyimba malipenga,
mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.
4 Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina,
mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.
5 Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga,
mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.
6 Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.
Tamandani Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.