Beginning
115 Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi
koma ulemerero ukhale pa dzina lanu,
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
2 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,
“Mulungu wawo ali kuti?”
3 Mulungu wathu ali kumwamba;
Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
4 Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
5 Pakamwa ali napo koma sayankhula,
maso ali nawo koma sapenya;
6 makutu ali nawo koma samva,
mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
7 manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;
mapazi ali nawo koma sayenda;
kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
8 Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,
chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
9 Inu Aisraeli, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
10 Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;
Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
11 Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
12 Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:
adzadalitsa nyumba ya Israeli,
adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
13 adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;
aangʼono ndi aakulu omwe.
14 Yehova akuwonjezereni madalitso;
inuyo pamodzi ndi ana anu.
15 Mudalitsidwe ndi Yehova,
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Kumwamba ndi kwa Yehova,
koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
17 Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,
amene amatsikira kuli chete;
18 ndi ife amene timatamanda Yehova,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Tamandani Yehova.
116 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;
Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
2 Pakuti ananditchera khutu,
ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.
3 Zingwe za imfa zinandizinga,
zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera;
ndinapeza mavuto ndi chisoni.
4 Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova:
“Inu Yehova, pulumutseni!”
5 Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama
Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.
6 Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima;
pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.
7 Pumula iwe moyo wanga,
pakuti Yehova wakuchitira zokoma.
8 Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,
maso anga ku misozi,
mapazi anga kuti angapunthwe,
9 kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova
mʼdziko la anthu amoyo.
10 Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati,
“Ndasautsidwa kwambiri.”
11 Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati,
“Anthu onse ndi abodza.”
12 Ndingamubwezere chiyani Yehova,
chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso
ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
pamaso pa anthu ake onse.
15 Imfa ya anthu oyera mtima
ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:
ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
Inu mwamasula maunyolo anga.
17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu
ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
pamaso pa anthu ake onse,
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,
mʼkati mwako iwe Yerusalemu.
Tamandani Yehova.
117 Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse;
mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu.
2 Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu,
ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha.
Tamandani Yehova.
118 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.
2 Israeli anene kuti:
“Chikondi chake ndi chosatha.”
3 Banja la Aaroni linene kuti,
“Chikondi chake ndi chosatha.”
4 Iwo amene amaopa Yehova anene kuti:
“Chikondi chake ndi chosatha.”
5 Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova,
ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.
6 Yehova ali nane; sindidzachita mantha.
Munthu angandichite chiyani?
7 Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa.
Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.
8 Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
kusiyana ndi kudalira munthu.
9 Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
kusiyana ndi kudalira mafumu.
10 Anthu a mitundu yonse anandizinga,
koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
11 Anandizinga mbali zonse,
koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
12 Anandizinga ngati njuchi,
koma anatha msanga ngati moto wapaminga;
mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
13 Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa,
koma Yehova anandithandiza.
14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.
15 Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano
ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti:
“Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
16 Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba
Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”
17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo
ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
18 Yehova wandilanga koopsa,
koma sanandipereke ku imfa.
19 Tsekulireni zipata zachilungamo,
kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova
chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
mwakhala chipulumutso changa.
22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
wasanduka wapangodya;
23 Yehova ndiye wachita zimenezi
ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.
25 Inu Yehova, tipulumutseni;
Yehova, tipambanitseni.
26 Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova.
Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
27 Yehova ndi Mulungu,
ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife.
Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu,
mpaka ku nyanga za guwa.
28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;
Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.
29 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.