Beginning
13 Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake,
koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.
2 Munthu amapeza zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake,
koma anthu osakhulupirika amalakalaka zachiwawa basi.
3 Iye amene amagwira pakamwa pake amateteza moyo wake,
koma amene amayankhula zopanda pake adzawonongeka.
4 Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu,
koma munthu wakhama adzalemera.
5 Munthu wolungama amadana ndi zabodza,
koma zochita za munthu woyipa zimanyansa ndiponso zimachititsa manyazi.
6 Chilungamo chimateteza munthu wangwiro,
koma tchimo limagwetsa munthu wochimwa.
7 Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse;
munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri.
8 Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake,
koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.
9 Nyale ya munthu wolungama ndi yokondweretsa,
koma nyale ya munthu woyipa imazimitsidwa.
10 Chipongwe chosamalabadirako za anthu ena chimadzetsa mikangano,
koma womva malangizo a anzawo ndiwo ali ndi nzeru.
11 Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono
koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.
12 Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima,
koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.
13 Amene amanyoza malangizo adzawonongeka,
koma amene amasamala lamulo amalandira mphotho.
14 Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo;
amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.
15 Munthu wa nzeru zabwino amapeza kuyanja pakati pa anthu,
koma munthu wosakhulupirika adzawonongeka.
16 Munthu wochenjera amachita zinthu mwanzeru,
koma chitsiru chimaonetsa poyera uchitsiru wake.
17 Wamthenga woyipa amagwetsa anthu mʼmavuto,
koma nthumwi yodalirika imabweretsa mtendere.
18 Wokana mwambo adzasauka ndi kunyozedwa,
koma wosamala chidzudzulo adzalemekezedwa.
19 Chinthu chochilakalaka chikachitika chimasangalatsa mtima,
koma zitsiru zimadana ndi kuleka zoyipa.
20 Woyenda ndi anthu anzeru nayenso adzakhala wanzeru;
koma woyenda ndi zitsiru adzapwetekeka.
21 Choyipa chitsata mwini,
koma wochita zolungama adzalandira mphotho yabwino.
22 Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa,
koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.
23 Tsala la munthu wosauka limalola chakudya chambiri,
koma anthu opanda chilungamo amachilanda.
24 Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda,
koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.
25 Munthu wolungama amakhala ndi zakudya zoti adye nʼkukhuta,
koma mʼmimba mwa munthu woyipa mumakhala pululu ndi njala.
14 Mkazi wanzeru amamanga banja lake,
koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.
2 Amene amayenda molungama amaopa Yehova,
koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova.
3 Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana,
koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza.
4 Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya,
koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso.
5 Mboni yokhulupirika sinama,
koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.
6 Wonyoza anzake amafunafuna nzeru koma osayipeza,
koma munthu womvetsa bwino amadziwa zinthu msanga.
7 Khala kutali ndi munthu wopusa
chifukwa sudzapeza mawu a nzeru.
8 Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake.
Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe.
9 Zitsiru zimanyoza za kulapa machimo, awo,
koma kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.
10 Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake,
ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake.
11 Nyumba ya munthu woyipa idzapasuka,
koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.
12 Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu,
koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa.
13 Ngakhale poseka mtima utha kumva kuwawa,
ndipo mathero achimwemwe akhoza kukhala chisoni.
14 Munthu wosakhulupirika adzalandira zogwirizana ndi ntchito yake,
koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito yake.
15 Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse,
koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake.
16 Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa,
koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala.
17 Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru,
ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo.
18 Anthu opusa amalandira uchitsiru,
koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu.
19 Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino,
ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama.
20 Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda,
koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri.
21 Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa
koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.
22 Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera?
Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika.
23 Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu,
koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.
24 Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe,
koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru.
25 Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo,
koma mboni yabodza imaphetsa.
26 Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira
ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.
27 Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo,
kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.
28 Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu,
koma popanda anthu kalonga amawonongeka.
29 Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri,
koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake.
30 Mtima wodekha umapatsa thupi moyo,
koma nsanje imawoletsa mafupa.
31 Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake,
koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.
32 Anthu oyipa adzakanthidwa chifukwa cha ntchito zawo zomwe,
koma olungama adzatetezedwa mwa imfa yawo.
33 Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu,
koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru.
34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,
koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.
35 Mfumu imasangalatsidwa ndi wantchito wanzeru,
koma imachitira ukali wantchito wochititsa manyazi.
15 Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo,
koma mawu ozaza amautsa ukali.
2 Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru,
koma pakamwa pa zitsiru pamatulutsa za uchitsiru.
3 Maso a Yehova ali ponseponse,
amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.
4 Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo,
koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.
5 Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake,
koma wochenjera amasamala chidzudzulo.
6 Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri,
zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.
7 Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru;
koma mitima ya zitsiru sitero.
8 Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova,
koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.
9 Ntchito za anthu oyipa zimamunyansa Yehova
koma amakonda amene amafunafuna chilungamo.
10 Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa.
Odana ndi chidzudzulo adzafa.
11 Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova,
nanji mitima ya anthu!
12 Wonyoza sakonda kudzudzulidwa;
iye sapita kwa anthu anzeru.
13 Mtima wokondwa umachititsa nkhope kukhala yachimwemwe,
koma mtima wosweka umawawitsa moyo.
14 Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna nzeru,
koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.
15 Munthu woponderezedwa masiku ake onse amakhala oyipa,
koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthawi zonse.
16 Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova,
kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.
17 Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi,
kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.
18 Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano,
koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.
19 Njira ya munthu waulesi ndi yowirira ndi mtengo waminga,
koma njira ya munthu wolungama ili ngati msewu waukulu.
20 Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,
koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.
21 Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru,
koma munthu womvetsa zinthu amayenda mowongoka.
22 Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka,
koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.
23 Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera,
ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.
24 Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo
kuti apewe malo okhala anthu akufa.
25 Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada
koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.
26 Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova,
koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.
27 Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake,
koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.
28 Munthu wolungama amaganizira za mmene ayankhire,
koma pakamwa pa munthu woyipa pamatulutsa mawu oyipa.
29 Yehova amakhala kutali ndi anthu oyipa,
koma amamva pemphero la anthu olungama.
30 Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima
ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.
31 Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo
adzakhala pakati pa anthu anzeru.
32 Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha,
koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.
33 Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru,
ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.