Beginning
1 Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
Anthu Owukira
2 Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi!
Pakuti Yehova wanena kuti,
“Ndinabala ana ndi kuwalera,
koma anawo andiwukira Ine.
3 Ngʼombe imadziwa mwini wake,
bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake,
koma Israeli sadziwa,
anthu anga samvetsa konse.”
4 Haa, mtundu wochimwa,
anthu olemedwa ndi machimo,
obadwa kwa anthu ochita zoyipa,
ana odzipereka ku zoyipa!
Iwo asiya Yehova;
anyoza Woyerayo wa Israeli
ndipo afulatira Iyeyo.
5 Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe?
Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira?
Mutu wanu wonse uli ndi mabala,
mtima wanu wonse wafowokeratu.
6 Kuchokera ku phazi mpaka ku mutu
palibe pabwino,
paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda,
mabala ali magazi chuchuchu,
mabala ake ngosatsuka, ngosamanga
ndiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.
7 Dziko lanu lasanduka bwinja,
mizinda yanu yatenthedwa ndi moto;
minda yanu ikukololedwa ndi alendo
inu muli pomwepo,
dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
8 Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha
ngati nsanja mʼmunda wampesa,
ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka,
ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
9 Yehova Wamphamvuzonse akanapanda
kutisiyira opulumuka,
tikanawonongeka ngati Sodomu,
tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.
10 Imvani mawu a Yehova,
inu olamulira Sodomu;
mverani lamulo la Mulungu wathu,
inu anthu a ku Gomora!
11 Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani
nsembe zanu zochuluka?”
“Zandikola nsembe zanu zopsereza
za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa;
sindikusangalatsidwanso
ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
12 Ndani anakulamulirani kuti
mubwere nazo pamaso panga?
Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
13 Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo!
Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine.
Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa,
kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
14 Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika
ndimadana nazo.
Zasanduka katundu wondilemera;
ndatopa kuzinyamula.
15 Mukamatambasula manja anu popemphera,
Ine sindidzakuyangʼanani;
ngakhale muchulukitse mapemphero anu,
sindidzakumverani.
Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
16 sambani, dziyeretseni.
Chotsani pamaso panu
ntchito zanu zoyipa!
Lekani kuchita zoyipa,
17 phunzirani kuchita zabwino!
Funafunani chilungamo,
thandizani oponderezedwa.
Tetezani ana amasiye,
muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
18 Yehova akuti,
“Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu.
Ngakhale machimo anu ali ofiira,
adzayera ngati thonje.
Ngakhale ali ofiira ngati kapezi,
adzayera ngati ubweya wankhosa.
19 Ngati muli okonzeka kundimvera
mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
20 koma mukakana ndi kuwukira
mudzaphedwa ndi lupanga.”
Pakuti Yehova wayankhula.
21 Taonani momwe mzinda wokhulupirika
wasandukira wadama!
Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama;
mu mzindamo munali chilungamo,
koma tsopano muli anthu opha anzawo!
22 Siliva wako wasanduka wachabechabe,
vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.
23 Atsogoleri ako ndi owukira,
anthu ogwirizana ndi mbala;
onse amakonda ziphuphu
ndipo amathamangira mphatso.
Iwo sateteza ana amasiye;
ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.
24 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu,
Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti,
“Haa, odana nane ndidzawatha,
ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
25 Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe;
ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa,
monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
26 Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana,
aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja.
Kenaka iweyo udzatchedwa
mzinda wolungama,
mzinda wokhulupirika.”
27 Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama,
anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.
28 Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi,
ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.
29 “Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu
imene inkakusangalatsani;
mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda
imene munayipatula.
30 Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota,
mudzakhala ngati munda wopanda madzi.
31 Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma,
ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali;
motero zonse zidzayakira limodzi,
popanda woti azimitse motowo.”
Phiri la Yehova
2 Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:
2 Mʼmasiku otsiriza,
phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa
kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse,
lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,
ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.
3 Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti,
“Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,
ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.
Iye adzatiphunzitsa njira zake,
ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,
mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
4 Iye adzaweruza pakati pa mayiko,
ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri.
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu
ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,
kapena kuphunziranso za nkhondo.
5 Inu nyumba ya Yakobo, bwerani,
tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.
Tsiku la Yehova
6 Inu Yehova mwawakana anthu anu,
nyumba ya Yakobo.
Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa;
amawombeza mawula ngati Afilisti,
ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
7 Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide;
ndipo chuma chawo ndi chosatha.
Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo;
ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.
8 Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano;
iwo amapembedza ntchito ya manja awo,
amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.
9 Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa
ndi kutsitsidwa.
Inu Yehova musawakhululukire.
10 Lowani mʼmatanthwe,
bisalani mʼmaenje,
kuthawa kuopsa kwa Yehova
ndi ulemerero wa ufumu wake!
11 Kudzikuza kwa anthu kudzatha,
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa;
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.
12 Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku
limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama,
ndipo adzagonjetsa
onse amphamvu,
13 tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali,
ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,
14 tsiku la mapiri onse ataliatali
ndiponso la zitunda zonse zazitali,
15 tsiku la nsanja zonse zazitali
ndiponso malinga onse olimba,
16 tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi
ndiponso la mabwato onse okongola.
17 Kudzikuza kwa munthu kudzatha
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa,
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,
18 ndipo mafano onse adzatheratu.
19 Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe
ndi mʼmaenje a nthaka,
kuthawa mkwiyo wa Yehova,
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
20 Tsiku limenelo anthu adzatayira
mfuko ndi mileme
mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide,
amene anawapanga kuti aziwapembedza.
21 Adzathawira mʼmapanga a matanthwe
ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka
kuthawa mkwiyo wa Yehova
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
22 Lekani kudalira munthu,
amene moyo wake sukhalira kutha.
Iye angathandize bwanji wina aliyense?
Chiweruzo pa Yerusalemu ndi Yuda
3 Taonani tsopano, Ambuye
Yehova Wamphamvuzonse,
ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda
zinthu pamodzi ndi thandizo;
adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
2 anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,
oweruza ndi aneneri,
anthu olosera ndi akuluakulu,
3 atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,
aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
4 Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo;
ana akhanda ndiwo adzawalamulire.
5 Anthu adzazunzana,
munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake.
Anthu wamba adzanyoza
akuluakulu.
6 Munthu adzagwira mʼbale wake
mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati,
“Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu;
lamulira malo opasuka ano!”
7 Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti,
“Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake.
Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga;
musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
8 Yerusalemu akudzandira,
Yuda akugwa;
zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova,
sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
9 Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa;
amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu;
salibisa tchimo lawolo.
Tsoka kwa iwo
odziputira okha mavuto.
10 Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino,
pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.
11 Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo!
Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
12 Achinyamata akupondereza anthu anga,
ndipo amene akuwalamulira ndi akazi.
Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani;
akukuchotsani pa njira yanu.
13 Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu;
wakonzeka kuti aweruze anthu ake.
14 Yehova akuwazenga milandu
akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:
“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;
nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
15 Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga,
nʼkudyera masuku pamutu amphawi?”
Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
16 Yehova akunena kuti,
“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,
akuyenda atakweza makosi awo,
akukopa amuna ndi maso awo
akuyenda monyangʼama
akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
17 Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;
Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
18 Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi, 19 ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope, 20 maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa, 21 mphete ndi zipini, 22 zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama, 23 magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
24 Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,
mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;
mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;
mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;
mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
25 Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,
asilikali ako adzafera ku nkhondo.
26 Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;
Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.
4 Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri
adzagwira mwamuna mmodzi,
nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu,
ndi kuvala zovala zathu;
inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu.
Tichotseni manyazi aumbeta!”
Nthambi ya Yehova
2 Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli. 3 Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu. 4 Ambuye adzasambitsa akazi a Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zawo. Adzatsuka magazi amene anakhetsedwa mu Yerusalemu ndi mzimu wachiweruzo ndiponso mzimu wamoto. 5 Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova. 6 Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothawiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi owusiramo mvula.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.