Beginning
24 Usachitire nsanje anthu oyipa,
usalakalake kuti uzikhala nawo,
2 pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa,
ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.
3 Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru,
ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;
4 Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake
ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.
5 Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri,
ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu.
6 Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo.
Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo.
7 Nzeru ndi chinthu chapatali kwambiri kwa chitsiru;
chilibe choti chiyankhule pabwalo la milandu pa chipata.
8 Amene amakonzekera kuchita zoyipa
adzatchedwa mvundulamadzi.
9 Kukonzekera kuchita za uchitsiru ndi tchimo,
ndipo munthu wonyoza amanyansa anthu.
10 Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti
mphamvu yako ndi yochepadi!
11 Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe;
uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa.
12 Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,”
kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi?
Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi?
Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?
13 Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino;
uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.
14 Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako;
ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo,
ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.
15 Usachite zachifwamba nyumba ya munthu wolungama ngati munthu woyipa.
Usachite nayo nkhondo nyumba yake;
16 paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso.
Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.
17 Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako.
Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.
18 Kuopa kuti Yehova ataziona zimenezi nayipidwa nazo,
angaleke kukwiyira mdaniyo.
19 Usavutike mtima chifukwa cha anthu ochita zoyipa
kapena kuchitira nsanje anthu oyipa,
20 paja munthu woyipa alibe tsogolo.
Moyo wa anthu oyipa adzawuzimitsa ngati nyale.
21 Mwana wanga, uziopa Yehova ndi mfumu,
ndipo usamagwirizana ndi anthu owachitira mwano,
22 awiri amenewa amagwetsa tsoka mwadzidzidzi.
Ndani angadziwe mavuto amene angagwetse?
Malangizo Enanso a Anthu Anzeru
23 Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa:
Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
24 Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,”
anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
25 Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino
ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.
26 Woyankhula mawu owona
ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.
27 Ugwiriretu ntchito zako zonse,
makamaka za ku munda
ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.
28 Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa,
kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
29 Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine;
ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”
30 Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi
ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
31 Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga,
mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa,
ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
32 Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga
ndipo ndinatolapo phunziro ili:
33 Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,”
kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
34 umphawi udzafika pa iwe ngati mbala
ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.
Miyambo Ina ya Solomoni
25 Iyi ndi miyambo inanso ya Solomoni, imene anthu a Hezekiya mfumu ya ku Yuda analemba.
2 Ulemerero wa Mulungu uli pa kubisa zinthu;
ulemerero wa mafumu uli pa kufufuza zinthuzo.
3 Monga momwe kwatalikira kumwamba ndi momwe kulili kuzama kwa dziko lapansi,
ndi momwemonso alili maganizo a mfumu kusadziwika kwake.
4 Chotsa zoyipa mʼsiliva
ndipo wosula adzapanga naye ziwiya.
5 Chotsa munthu woyipa pamaso pa mfumu;
ndipo ufumu wake udzakhazikika mu chilungamo.
6 Usamadzikuze ukakhala pamaso pa mfumu,
ndipo usamakhale pamalo pa anthu apamwamba;
7 paja ndi bwino kuti mfumu ichite kukuwuza kuti, “Bwera pamwamba pano,”
kulekana ndi kuti ikuchititse manyazi chifukwa cha wina wokuposa.
Chimene wachiona ndi maso ako,
8 usafulumire kupita nacho ku bwalo la milandu
nanga udzachita chiyani pa mapeto pake
ngati mnansi wako adzakuchititsa manyazi?
9 Kamba mlandu ndi mnansi wako,
koma osawulula chinsinsi cha munthu wina
10 kuopa kuti wina akamva mawu ako adzakuchititsa manyazi
ndipo mbiri yako yoyipa sidzatha.
11 Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera
ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.
12 Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide
kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.
13 Wamthenga wodalirika ali ngati madzi ozizira pa nthawi yokolola
kwa anthu amene amutuma;
iye amaziziritsa mtima bwana wake.
14 Munthu wonyadira mphatso imene sayipereka
ali ngati mitambo ndi mphepo yopanda mvula.
15 Kupirira ndiye kumagonjetsa mfumu,
ndipo kufewa mʼkamwa kutha kumafatsitsa munthu wowuma mtima.
16 Ngati upeza uchi, ingodya okukwanira,
kuopa ungakoledwe nawo ndi kuyamba kusanza.
17 Uzipita kamodzikamodzi ku nyumba ya mnzako
ukawirikiza kupita, udzadana naye.
18 Munthu wochitira mnzake umboni wonama,
ali ngati chibonga kapena lupanga kapena muvi wakuthwa.
19 Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto,
kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.
20 Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni
kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira
kapena kuthira mchere pa chilonda.
21 Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye;
ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe.
22 Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake,
ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.
23 Monga momwe mphepo yampoto imabweretsera mvula,
chonchonso mjedu umadzetsa mkwiyo.
24 Nʼkwabwino kukhala pa ngodya ya denga
kuposa kukhala mʼnyumba ndi mkazi wolongolola.
25 Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali
ali ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.
26 Munthu wolungama amene amagonjera munthu woyipa
ali ngati kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oyipa.
27 Sibwino kudya uchi wambiri,
sibwinonso kudzifunira wekha ulemu.
28 Munthu amene samatha kudziretsa
ali ngati mzinda umene adani awuthyola ndi kuwusiya wopanda malinga.
26 Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola,
ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru.
2 Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira,
ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.
3 Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu,
choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru.
4 Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake,
kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho.
5 Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake,
kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru.
6 Kutuma chitsiru kuti akapereke uthenga
kuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto.
7 Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu
ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
8 Kupereka ulemu kwa chitsiru
zili ngati kukulunga mwala mʼlegeni.
9 Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwa
ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
10 Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda,
ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase.
11 Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wake
chili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake.
12 Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezo
kuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru.
13 Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango,
mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!”
14 Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake,
momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake.
15 Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale;
zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake.
16 Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzeru
kuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera.
17 Munthu wongolowera mikangano imene si yake
ali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera.
18 Monga munthu wamisala amene
akuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa,
19 ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake,
amene amati, “Ndimangoseka chabe!”
20 Pakasowa nkhuni, moto umazima;
chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha.
21 Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto,
ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano.
22 Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma;
chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu.
23 Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothi
ndi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa.
24 Munthu wachidani amayankhula zabwino
pamene mu mtima mwake muli chinyengo.
25 Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire,
pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa.
26 Ngakhale amabisa chidani mochenjera,
koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu.
27 Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha;
ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini.
28 Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka,
ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.