Beginning
Salimo la Davide.
103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;
ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
3 Amene amakhululuka machimo ako onse
ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
4 amene awombola moyo wako ku dzenje
ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
5 amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,
kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
6 Yehova amachita chilungamo
ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.
7 Iye anadziwitsa Mose njira zake,
ntchito zake kwa Aisraeli.
8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
9 Iye sadzatsutsa nthawi zonse,
kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
10 satichitira molingana ndi machimo athu,
kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,
koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,
koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
14 pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira,
amakumbukira kuti ndife fumbi.
15 Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu,
amaphuka ngati duwa la mʼmunda;
16 koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso
ndipo malo ake sakumbukirikanso.
17 Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya
chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,
ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
18 iwo amene amasunga pangano lake
ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
19 Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba
ndipo ufumu wake umalamulira onse.
20 Tamandani Yehova, inu angelo ake,
amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula,
amene mumamvera mawu ake.
21 Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba,
inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
kulikonse mu ulamuliro wake.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
mwavala ulemerero ndi ufumu.
2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
watambasula miyamba ngati tenti
3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
malawi amoto kukhala atumiki ake.
5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
silingasunthike.
6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
8 Inu munamiza mapiri,
iwo anatsikira ku zigwa
kumalo kumene munawakonzera.
9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
iwo sadzamizanso dziko lapansi.
10 Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa;
madziwo amayenda pakati pa mapiri.
11 Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo;
abulu akuthengo amapha ludzu lawo.
12 Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi;
zimayimba pakati pa thambo.
13 Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba;
dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake.
14 Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye,
ndi zomera, kuti munthu azilima
kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:
15 vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,
mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala,
ndi buledi amene amapereka mphamvu.
16 Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino,
mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala.
17 Mbalame zimamanga zisa zawo;
kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.
18 Mapiri ataliatali ndi a mbalale;
mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira.
19 Mwezi umasiyanitsa nyengo
ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.
20 Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku,
ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka.
21 Mikango imabangula kufuna nyama,
ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu.
22 Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala;
imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo.
23 Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake,
kukagwira ntchito yake mpaka madzulo.
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
Munazipanga zonse mwanzeru,
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,
yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,
zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,
ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.
27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inu
kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.
28 Mukazipatsa,
zimachisonkhanitsa pamodzi;
mukatsekula dzanja lanu,
izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.
29 Mukabisa nkhope yanu,
izo zimachita mantha aakulu;
mukachotsa mpweya wawo,
zimafa ndi kubwerera ku fumbi.
30 Mukatumiza mzimu wanu,
izo zimalengedwa
ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.
31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;
Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;
32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,
amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.
33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;
ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.
34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,
pamene ndikusangalala mwa Yehova.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
ndipo anthu oyipa asapezekenso.
Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.
Tamandani Yehova.
105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
2 Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
3 Munyadire dzina lake loyera;
mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
4 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
funafunani nkhope yake nthawi yonse.
5 Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
6 inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
inu ana a Yakobo, osankhika ake.
7 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.
8 Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,
mawu amene analamula kwa mibado yonse,
9 pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,
lumbiro limene analumbira kwa Isake.
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,
kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani
ngati gawo la cholowa chako.”
12 Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero,
ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,
13 ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina,
kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.
14 Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza;
anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:
15 “Musakhudze odzozedwa anga;
musachitire choyipa aneneri anga.”
16 Iye anabweretsa njala pa dziko
ndipo anawononga chakudya chonse;
17 Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo,
Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.
18 Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza,
khosi lake analiyika mʼzitsulo,
19 mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa,
mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.
20 Mfumu inatuma munthu kukamumasula,
wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.
21 Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake,
wolamulira zonse zimene iye anali nazo,
22 kulangiza ana a mfumu monga ankafunira
ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.
23 Tsono Israeli analowa mu Igupto;
Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.
24 Yehova anachulukitsa anthu ake;
ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;
25 amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake,
kukonzera chiwembu atumiki ake.
26 Yehova anatuma Mose mtumiki wake,
ndi Aaroni amene Iye anamusankha.
27 Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo,
zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.
28 Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima.
Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.
29 Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi,
kuchititsa kuti nsomba zawo zife.
30 Dziko lawo linadzaza ndi achule
amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.
31 Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka
ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.
32 Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala,
ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;
33 Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu,
nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.
34 Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera,
ziwala zosawerengeka;
35 zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo,
zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.
36 Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo,
zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.
37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.
42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
ndi kutsatira malamulo ake.
Tamandani Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.