Beginning
Mathero a Zinthu Zonse ndi Wofanana
9 Ndinalingalira zonse ndanenazi ndipo ndinapeza kuti anthu olungama ndi anthu anzeru ali mʼmanja mwa Mulungu pamodzi ndi zimene amachita, koma palibe amene amadziwa zimene zikumudikira mʼtsogolo mwake, kaya chikondi kapena chidani. 2 Onsewa mathero awo ndi amodzi, anthu olungama ndi anthu oyipa, abwino ndi oyipa, oyera ndi odetsedwa, amene amapereka nsembe ndi amene sapereka nsembe.
Zomwe zimachitikira munthu wabwino,
zimachitikiranso munthu wochimwa,
zomwe zimachitikira amene amalumbira,
zimachitikiranso amene amaopa kulumbira.
3 Choyipa chimene chili mʼzonse zochitika pansi ndi ichi: Mathero a zonse ndi amodzi. Ndithu, mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoyipa, ndipo mʼmitima mwawo muli zamisala pamene ali ndi moyo, potsiriza pake iwo amakakhala pamodzi ndi anthu akufa. 4 Aliyense amene ali ndi moyo amakhala ndi chiyembekezo, pajatu galu wamoyo aposa mkango wakufa!
5 Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa,
koma akufa sadziwa kanthu;
alibe mphotho ina yowonjezera,
ndipo palibe amene amawakumbukira.
6 Chikondi chawo, chidani chawo
ndiponso nsanje yawo, zonse zinatha kalekale;
sadzakhalanso ndi gawo
pa zonse zochitika pansi pano.
7 Pita, kadye chakudya chako mokondwera ndi kumwa vinyo wako ndi mtima wosangalala, pakuti tsopano Mulungu akukondwera ndi zochita zako. 8 Uzivala zovala zoyera nthawi zonse, uzidzola mafuta mʼmutu mwako nthawi zonse. 9 Uzikondwerera moyo pamodzi ndi mkazi wako amene umamukonda, masiku onse a moyo uno wopanda phindu, amene Mulungu wakupatsa pansi pano. Pakuti mkaziyo ndiye gawo la moyo wako pa ntchito yako yolemetsa pansi pano. 10 Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku manda kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.
11 Ine ndinaonanso chinthu china pansi pano:
opambana pa kuthamanga si aliwiro,
kapena opambana pa nkhondo si amphamvu,
ndiponso okhala ndi chakudya si anzeru,
kapena okhala ndi chuma si odziwa zambiri,
kapena okomeredwa mtima si ophunzira;
koma mwayi umangowagwera onsewa pa nthawi yake.
12 Kungoti palibe munthu amene amadziwa kuti nthawi yake idzafika liti:
monga momwe nsomba zimagwidwira mu ukonde,
kapena mmene mbalame zimakodwera mu msampha,
chimodzimodzinso anthu amakodwa mu msampha pa nthawi yoyipa,
pamene tsoka limawagwera mosayembekezera.
Nzeru Iposa Uchitsiru
13 Ine ndinaonanso pansi pano chitsanzo ichi cha nzeru chimene chinandikhudza kwambiri: 14 Panali mzinda waungʼono umene unali ndi anthu owerengeka. Ndipo mfumu yamphamvu inabwera kudzawuthira nkhondo, inawuzungulira ndi kumanga mitumbira yankhondo. 15 Tsono mu mzindamo munali munthu wosauka koma wanzeru, ndipo anapulumutsa mzindawo ndi nzeru zakezo. Koma palibe amene anakumbukira munthu wosaukayo. 16 Choncho ine ndinati, “Nzeru ndi yopambana mphamvu.” Koma nzeru ya munthu wosauka imanyozedwa, ndipo palibe amene amalabadirako za mawu ake.
17 Mawu oyankhula mofatsa a munthu wanzeru, anthu amawasamalira kwambiri
kupambana kufuwula kwa mfumu ya zitsiru.
18 Nzeru ndi yabwino kupambana zida zankhondo,
koma wochimwa mmodzi amawononga zinthu zambiri zabwino.
10 Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira,
choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.
2 Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino,
koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa.
3 Chitsiru ngakhale chikamayenda mu msewu,
zochita zake ndi zopanda nzeru
ndipo chimaonetsa aliyense kuti icho ndi chitsirudi.
4 Ngati wolamulira akukwiyira,
usachoke pa ntchito yako;
kufatsa kumakonza zolakwa zazikulu.
5 Pali choyipa chimene ndinachiona pansi pano,
kulakwitsa kumene kumachokera kwa wolamulira:
6 Zitsiru amazipatsa ntchito zambiri zapamwamba,
pamene anthu olemera amawapatsa ntchito zotsika.
7 Ndaona akapolo atakwera pa akavalo,
pamene akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.
8 Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha;
amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.
9 Amene amaphwanya miyala adzapwetekedwa ndi miyalayo;
amene amawaza nkhuni adzapwetekedwa nazo.
10 Ngati nkhwangwa ili yobuntha
yosanoledwa,
pamafunika mphamvu zambiri potema,
koma luso limabweretsa chipambano.
11 Nʼkopanda phindu kudziwa kuseweretsa njoka
ngati njokayo yakuluma kale.
12 Mawu a pakamwa pa munthu wanzeru ndi okondweretsa,
koma chitsiru chidzawonongedwa ndi milomo yake yomwe.
13 Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa;
potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala
14 ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu.
Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo,
ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?
15 Chitsiru chimatopa msanga ndi ntchito yochepa;
ndipo sichikhala ndi mphamvu zobwererera ku mudzi.
16 Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana,
ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.
17 Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka
ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake,
kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.
18 Ngati munthu ndi waulesi, denga lake limaloshoka;
ngati manja ake ndi alobodo nyumba yake imadontha.
19 Phwando ndi lokondweretsa anthu,
ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo,
koma ndalama ndi yankho la chilichonse.
20 Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako,
kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako,
pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako
nʼkukafotokoza zomwe wanena.
Kuponya Chakudya pa Madzi
11 Ponya chakudya chako pa madzi,
udzachipezanso patapita masiku ambiri.
2 Ndalama zako uzisungitse kwa anthu asanu ndi awiri, inde kwa anthu asanu ndi atatu,
pakuti sudziwa ndi tsoka lanji limene likubwera pa dziko.
3 Ngati mitambo yadzaza ndi madzi,
imagwetsa mvula pa dziko lapansi.
Mtengo ukagwera cha kummwera kapena cha kumpoto,
ndiye kuti udzagonera kumene wagwerako.
4 Amene amayangʼana mphepo sadzadzala;
amene amayangʼana mitambo sadzakolola.
5 Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo,
kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi,
momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu,
Mlengi wa zinthu zonse.
6 Dzala mbewu zako mmawa
ndipo madzulo usamangoti manja lobodo,
pakuti sudziwa chimene chidzapindula,
mwina ichi kapena icho,
kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.
Kumbukira Mlengi Wako
7 Kuwala nʼkwabwino,
ndipo maso amasangalala kuona dzuwa.
8 Munthu akakhala wa zaka zambiri,
mulekeni akondwerere zaka zonsezo,
koma iye azikumbukira masiku a mdima,
pakuti adzakhala ochuluka.
Chilichonse chimene chikubwera ndi chopanda phindu.
9 Kondwera mnyamata iwe, pamene ukanali wamngʼono,
ndipo mtima wako usangalale pa nthawi ya unyamata wako.
Tsatira zimene mtima wako ukufuna,
ndiponso zimene maso ako akuona,
koma dziwa kuti pa zinthu zonsezo
Mulungu adzakuweruza.
10 Choncho uchotse zokusautsa mu mtima mwako,
upewe zokupweteka mʼthupi mwako,
pakuti unyamata ndi ubwana ndi zopandapake.
12 Uzikumbukira mlengi wako
masiku a unyamata wako,
masiku oyipa asanafike,
nthawi isanafike pamene udzanena kuti,
“Izi sizikundikondweretsa.”
2 Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala,
mwezi ndi nyenyezi zidzada.
Mitambo idzabweranso mvula itagwa.
3 Nthawi imene manja ako adzanjenjemera,
miyendo yako idzafowoka,
pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka,
ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.
4 Makutu ako adzatsekeka,
ndipo sudzamva phokoso lakunja;
sudzamvanso kusinja kwa pa mtondo
kapena kulira kwa mbalame mmawa.
5 Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera,
amaopa kuyenda mʼmisewu;
Mutu umatuwa kuti mbuu,
amayenda modzikoka ngati ziwala
ndipo chilakolako chimatheratu.
Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyaya
ndipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.
6 Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke,
kapena mbale yagolide isanasweke;
mtsuko usanasweke ku kasupe,
kapena mkombero usanathyoke ku chitsime.
7 Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera,
mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.
8 “Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki.
“Zonse ndi zopandapake!”
Mawu Otsiriza
9 Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri. 10 Mlaliki anafufuzafufuza kuti apeze mawu oyenera, ndipo zimene analemba zinali zolondola ndiponso zoona.
11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga, zokamba zawo zimene anasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomera, yoperekedwa ndi mʼbusa mmodzi. 12 Samalira mwana wanga, za kuwonjezera chilichonse pa zimenezi.
Kulemba mabuku ambiri sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.
13 Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa:
uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake,
pakuti umenewu ndiwo udindo
wa anthu onse.
14 Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse,
kuphatikizanso zinthu zonse zobisika,
kaya zabwino kapena zoyipa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.