Beginning
Miyambo ya Solomoni
10 Miyambo ya Solomoni:
Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,
koma mwana wopusa amamvetsa amayi ake chisoni.
2 Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa,
koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
3 Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala;
koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa.
4 Wochita zinthu mwaulesi amasauka,
koma wogwira ntchito mwakhama amalemera.
5 Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru,
koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.
6 Madalitso amakhala pa mutu wa munthu wolungama,
koma pakamwa pa munthu woyipa pamaphimba chiwawa.
7 Munthu wolungama anzake adzamukumbukira ngati mdalitso,
koma dzina la munthu woyipa lidzayiwalika.
8 Munthu wa mtima wanzeru amasamala malamulo,
koma chitsiru chomangolongolola chidzawonongeka.
9 Munthu woyenda mwangwiro amayenda mosatekeseka;
koma amene amayenda njira yokhotakhota adzadziwika.
10 Aliyense wotsinzinira maso mwachinyengo amabweretsa mavuto,
koma wodzudzula chitsiru molimba mtima amabweretsa mtendere.
11 Pakamwa pa munthu wolungama ndi kasupe wamoyo,
koma pakamwa pa munthu woyipa pamabisa chiwawa.
12 Udani umawutsa mikangano,
koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.
13 Nzeru imapezeka pa milomo ya munthu wozindikira zinthu,
koma pa msana pa munthu wopanda nzeru sipachoka chikwapu.
14 Anzeru amasunga chidziwitso
koma pakamwa pa chitsiru pamatulutsa zowononga.
15 Chuma cha munthu wolemera
ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.
16 Moyo ndiye malipiro a munthu wolungama,
koma phindu la anthu oyipa ndi uchimo ndi imfa.
17 Wosamalira malangizo amayenda mʼnjira ya moyo,
koma wonyoza chidzudzulo amasochera.
18 Amene amabisa chidani chake ndi munthu wonama,
ndipo amene amafalitsa miseche ndi chitsiru.
19 Mawu akachuluka zolakwa sizisowa,
koma amene amasunga pakamwa pake ndi wanzeru.
20 Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri,
koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu.
21 Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri;
koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru.
22 Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma,
ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.
23 Kwa chitsiru kuchita zinthu zoyipa ndiye chinthu chomusangalatsa,
koma kwa munthu womvetsa bwino zinthu nzeru ndiyo imamusangalatsa.
24 Chimene munthu woyipa amachiopa chidzamuchitikira;
chimene munthu wolungama amachilakalaka adzachipeza.
25 Pamene namondwe wawomba, anthu oyipa amachotsedwa,
koma anthu olungama amakhazikika mpaka muyaya.
26 Momwe amakhalira vinyo wosasa mʼkamwa ndi momwe umakhalira utsi mʼmaso,
ndi momwenso amakhalira munthu waulesi kwa amene amutuma.
27 Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo;
koma zaka za anthu oyipa zidzafupikitsidwa.
28 Chiyembekezo cha olungama chimapatsa chimwemwe,
koma chiyembekezo cha anthu ochimwa chidzafera mʼmazira.
29 Njira za Yehova ndi linga loteteza anthu ochita zabwino,
koma wochita zoyipa adzawonongeka.
30 Munthu wolungama sadzachotsedwa, pamalo pake
koma oyipa sadzakhazikika pa dziko.
31 Pakamwa pa munthu wolungama pamatulutsa za nzeru,
koma lilime lokhota lidzadulidwa.
32 Milomo ya anthu olungama imadziwa zoyenera kuyankhula,
koma pakamwa pa anthu ochimwa pamatulutsa zokhota zokhazokha.
11 Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa,
koma amakondwera ndi muyeso woyenera.
2 Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi,
koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.
3 Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera,
koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.
4 Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu,
koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.
5 Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo,
koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.
6 Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa,
koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.
7 Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso.
Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.
8 Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,
koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.
9 Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake,
koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.
10 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera,
ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.
11 Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima,
koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.
12 Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru,
koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.
13 Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi;
koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.
14 Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa;
koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.
15 Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto,
koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere.
16 Mkazi wodekha amalandira ulemu,
koma amuna ankhanza amangopata chuma.
17 Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino
koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.
18 Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu,
koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.
19 Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo,
koma wothamangira zoyipa adzafa.
20 Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota
koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.
21 Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa,
koma anthu olungama adzapulumuka.
22 Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba,
ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa.
23 Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha,
koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu.
24 Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe;
wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe.
25 Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera;
iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.
26 Anthu amatemberera womana anzake chakudya,
koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho.
27 Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo,
koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.
28 Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota,
koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.
29 Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto,
ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.
30 Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo,
ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.
31 Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi,
kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!
12 Munthu amene amakonda mwambo amakonda kudziwa zinthu,
koma amene amadana ndi chidzudzulo ndi wopusa.
2 Munthu wabwino amapeza kuyanja pamaso pa Yehova,
koma Yehova amatsutsa munthu wochita chinyengo.
3 Munthu sangakhazikike bwino pochita zoyipa,
koma maziko a anthu olungama sadzatekeseka.
4 Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake,
koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
5 Maganizo a anthu olungama ndi owongoka,
koma malangizo a anthu oyipa ndi achinyengo.
6 Mawu a anthu oyipa ndi ophetsa,
koma mawu a anthu olungama amapulumutsa.
7 Anthu oyipa amagonjetsedwa ndipo amayiwalika,
koma nyumba ya anthu olungama idzakhalabe.
8 Munthu amatamandidwa malinga ndi nzeru zake,
koma anthu amitima yokhota amanyozedwa.
9 Nʼkwabwino kukhala munthu wonyozeka koma wodzigwirira ntchito nʼkukhala ndi zonse zofunika,
kuposa kukhala wodzikuza koma ulibe ndi chakudya chomwe.
10 Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake,
koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.
11 Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka,
koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.
12 Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa,
koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.
13 Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa;
koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.
14 Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake
ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.
15 Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino,
koma munthu wanzeru amamvera malangizo.
16 Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo,
koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.
17 Woyankhula zoona amapereka umboni woona,
koma mboni yabodza imafotokoza zonama.
18 Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga,
koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.
19 Mawu woona amakhala mpaka muyaya
koma mawu abodza sakhalitsa.
20 Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo;
koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.
21 Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama,
koma munthu woyipa mavuto samuthera.
22 Pakamwa pa bodza pamamunyansa Yehova,
koma amakondwera ndi anthu oyankhula zoona.
23 Munthu wochenjera amabisa nzeru zake,
koma munthu wopusa amaonetsa uchitsiru wake poyera.
24 Ogwira ntchito mwakhama adzalamulira,
koma aulesi adzakhala ngati kapolo.
25 Nkhawa imakhala ngati katundu wolemera mu mtima mwa munthu,
koma mawu abwino amamusangalatsa.
26 Munthu wolungama amatsogolera mnansi wake,
koma ntchito za anthu oyipa zimawasocheretsa.
27 Munthu waulesi sapeza chimene akufuna,
koma munthu wakhama amapeza chuma chamtengo wapatali.
28 Mʼnjira yachilungamo muli moyo;
koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.