Beginning
19 Ndi wabwino munthu wosauka amene amayenda mu ungwiro,
aposa munthu wopusa woyankhula zokhota.
2 Si bwino kuti munthu akhale wopanda nzeru;
ndipo munthu woyenda mofulumira amaphonya njira.
3 Uchitsiru wa munthu umamubweretsera zovuta,
mtima wake umakwiyira Yehova.
4 Chuma chimachulukitsa abwenzi;
koma munthu wosauka bwenzi lake limamuthawa.
5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa;
ndipo iye amene amanena mabodza sadzapulumuka.
6 Anthu ambiri amafuna munthu wopatsa kuti awakomere mtima,
ndipo munthu amene amapereka mphatso ndi bwenzi la munthu aliyense.
7 Ngati munthu wosauka abale ake omwe amadana naye,
nanji abwenzi ake tsono!
Iwo adzamuthawa kupita kutali.
Amayesa kuwatsatira mowapembedza koma iwo samapezeka konse.
8 Iye amene amapeza nzeru ndiye kuti amakonda moyo wake.
Wosamalitsa kukhala wanzeru, zinthu zimamuyendera bwino.
9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,
ndipo iye amene amanena mabodza adzawonongeka.
10 Nʼkosayenera kuti chitsiru chizikhala ndi moyo wamanyado,
nanjinso kuti kapolo azilamulira akalonga!
11 Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga;
ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.
12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango,
koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pa udzu.
13 Mwana wopusa ndiye tsoka la abambo ake
ndipo mkazi wolongolola ndi wotopetsa ngati mvula yamvumbi.
14 Nyumba ndi chuma ndiye cholowa chochokera kwa makolo;
koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Yehova.
15 Ulesi umagonetsa tulo tofa nato
ndipo munthu wosatakataka amakhala ndi njala.
16 Amene amamvera malangizo amasunga moyo wake,
koma amene sasamala malamulo a Yehova adzafa.
17 Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova,
ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.
18 Langa mwana wako, chiyembekezo chikanalipo;
ngati sutero udzawononga moyo wake.
19 Munthu waukali woopsa ayenera kulandira chilango;
pakuti akamulekelera ndiye zidzayipa kuposa kale.
20 Mvera uphungu ndipo landira malangizo;
pa mapeto pake udzakhala wanzeru.
21 Munthu amakonzekera zambiri mu mtima mwake,
koma cholinga cha Yehova ndiye chidzachitike.
22 Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha;
nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.
23 Kuopa Yehova kumabweretsa moyo;
wotereyo amakhala mu mtendere; ndiye kuti choyipa sichidzamugwera.
24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale;
koma sangathe kufikitsa dzanja lakelo pakamwa pake.
25 Menya munthu wonyoza, ndipo anthu opanda nzeru adzachenjererapo;
dzudzula munthu wozindikira zinthu, ndipo iye adzapezapo chidziwitso.
26 Mwana wochita ndewu ndi abambo ake ndi kuthamangitsa amayi ake,
ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.
27 Mwana wanga, ukaleka kumvera malangizo,
udzapatukana ndi mawu opatsa nzeru.
28 Mboni yopanda pake imanyoza cholungama,
ndipo pakamwa pa anthu oyipa pamameza zoyipa.
29 Chilango chakonzedwa kale kuti chigwere anthu oyipa,
ndipo mkwapulo wakonzedwa kale kuti ukwapule misana ya anthu opusa.
20 Vinyo amachititsa munthu kukhala wonyoza ndipo chakumwa choledzeretsa chimachititsa munthu kukhala wolongolola;
aliyense wosochera nazo zimenezi alibe nzeru.
2 Ukali wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango;
amene amawuputa mkwiyowo amataya moyo wake.
3 Nʼchaulemu kwa munthu kupewa mikangano,
koma chitsiru chilichonse chimafulumira kulongolola.
4 Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera;
kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.
5 Zolinga za mtima wa munthu zili ngati madzi akuya,
munthu womvetsa zinthu ndiye yekha angawatunge.
6 Anthu ambiri amayankhula za kukhulupirika kwawo,
koma munthu wokhulupirika angamupeze ndani?
7 Munthu wolungama amakhala ndi makhalidwe abwino;
odala ndi ana ake amene amatsanzira moyo wake.
8 Mfumu ikhala pa mpando wake wa chiweruzo,
imapeta ndi maso ake anthu onse oyipa.
9 Ndani amene anganene kuti, “Ndawuyeretsa mtima wanga;
ndilibe tchimo lililonse?”
10 Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo
zonsezi Yehova zimamunyansa.
11 Ngakhale mwana amadziwika ndi zochita zake,
ngati zochita zake zili zoyera ndi zoyenera.
12 Makutu amene amamva ndi maso amene amaona,
zonsezi anazilenga ndi Yehova.
13 Usakonde tulo ungasauke;
khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
14 Munthu wogula chinthu amati, “Sichabwino, sichabwino.”
Koma akagula nʼkuchokapo amayamba kudzitama.
15 Pali golide ndi miyala yamtengowapatali,
koma milomo yoyankhula zanzeru ndi yamtengowapatali koposa zonsezi.
16 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;
kuti chikhale chikole chako chifukwa waperekera chikole munthu wachilendo.
17 Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu,
koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.
18 Zokonzekera zimapindula utafunsira uphungu;
ndipo usanamenye nkhondo yamba wapempha malangizo oyenera.
19 Amene amanka nanena miseche amawulula zachinsinsi.
Choncho usamagwirizane naye munthu woyankhula zopusayo.
20 Ngati munthu atemberera abambo ake kapena amayi ake,
moyo wake udzazimitsidwa ngati nyale mu mdima wandiweyani.
21 Cholowa chochipeza mofulumira poyamba,
sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.
22 Usanene kuti, “Ine ndidzabwezera choyipa chimenechi!”
Dikira Yehova, ndipo Iye adzakupulumutsa.
23 Miyeso yosintha imamunyansa Yehova;
ndipo masikelo onyenga si abwino.
24 Mayendedwe a munthu amawalamulira ndi Yehova,
tsono munthu angadziwe bwanji njira yake?
25 Ndi msampha kwa munthu kuyankhula mofulumira kuti “Chinthu ichi nʼchopatulika kwa Yehova,”
popeza mwina atha kusintha maganizo utalumbira kale.
26 Mfumu ya nzeru imapeta kwathunthu
anthu oyipa.
27 Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Yehova;
imafufuza ziwalo zake zonse zamʼkati.
28 Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu;
chilungamo chimalimbikitsa mpando wake waufumu.
29 Ulemerero wa achinyamata uli mu mphamvu zawo,
imvi ndi ulemerero wa anthu okalamba.
30 Mikwingwirima yopweteka ndiyo imachotsa zoyipa,
ndipo mikwapulo ndiyo imachotsa zamʼkatikati mwa munthu.
21 Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wamadzi mʼdzanja la Yehova;
Iye amautsongolera pa chilichonse chimene akufuna.
2 Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo,
koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.
3 Za chilungamo ndi zolondola
ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe.
4 Maso odzikuza ndi mtima wonyada,
zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.
5 Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake;
koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka.
6 Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa
ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.
7 Chiwawa cha anthu oyipa chidzawawononga,
pakuti iwo amakana kuchita zolungama.
8 Njira ya munthu wolakwa ndi yokhotakhota,
koma makhalidwe a munthu wosalakwa ndi olungama.
9 Nʼkwabwino kukhala wekha pa ngodya ya denga la nyumba,
kuposa kukhala mʼnyumba pamodzi ndi mkazi wolongolola.
10 Munthu woyipa amalakalaka zoyipa;
sachitira chifundo mnansi wake wovutika.
11 Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru;
koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.
12 Zolingalira za munthu woyipa nʼzosabisika pamaso pa Yehova,
ndipo Iye adzawononga woyipayo.
13 Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira,
nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.
14 Mphatso yoperekedwa mseri imathetsa mkwiyo,
ndipo chiphuphu choperekedwa mobisa chimathetsa mphamvu ya ukali woopsa.
15 Chilungamo chikachitika anthu olungama amasangalala,
koma anthu oyipa amaopsedwa nazo.
16 Munthu amene amachoka pa njira ya anthu anzeru
adzapezeka mʼgulu la anthu akufa.
17 Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi,
ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18 Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama
ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima.
19 Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu
kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga.
20 Munthu wanzeru samwaza chuma chake,
koma wopusa amachiwononga.
21 Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika,
amapeza moyo ndi ulemerero.
22 Munthu wanzeru amagonjetsa mzinda wa anthu amphamvu
ndi kugwetsa linga limene iwo amalidalira.
23 Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake
sapeza mavuto.
24 Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,”
iye amachita zinthu modzitama kwambiri.
25 Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha
chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito.
26 Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri,
koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.
27 Nsembe ya anthu oyipa imamunyansa Yehova,
nanji akayipereka ndi cholinga choyipa!
28 Mboni yonama idzawonongeka,
koma mawu a munthu wakumva adzakhala nthawi zonse.
29 Munthu woyipa amafuna kudzionetsa ngati wolimba mtima,
koma munthu wowongoka amaganizira njira zake.
30 Palibe nzeru, palibe kumvetsa bwino, palibenso uphungu,
zimene zingapambane Yehova.
31 Kavalo amamukonzera tsiku la nkhondo,
koma ndi Yehova amene amapambanitsa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.