Beginning
Nzeru Iposa Zonse
4 Ananu, mverani malangizo a abambo anu;
tcherani khutu kuti mupeze nzeru zodziwira zinthu.
2 Zimene ndikukuphunzitsani ndi zabwino.
Choncho musasiye malangizo anga.
3 Paja ndinalinso mwana mʼnyumba mwa abambo anga;
mwana mmodzi yekha wapamtima pa amayi anga.
4 Ndipo abambo anandiphunzitsa ndi mawu akuti,
“Ugwiritse mawu anga pa mtima pako,
usunge malamulo anga kuti ukhale ndi moyo.
5 Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu;
usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo.
6 Usasiye nzeru ndipo idzakusunga.
Uziyikonda ndipo idzakuteteza.
7 Fundo yayikulu pa za nzeru ndi iyi: upeze nzeru.
Kaya pali china chilichonse chimene ungapeze, koma upeze nzeru yomvetsa bwino zinthu.
8 Uyilemekeze nzeruyo ndipo idzakukweza;
ikumbatire nzeruyo ndipo idzakupatsa ulemu.
9 Idzayika sangamutu yokongola yamaluwa pamutu pako;
idzakupatsa chipewa chaufumu chaulemu.”
10 Mwana wanga, umvere ndi kuvomereza zimene ndikunena,
ndipo zaka za moyo wako zidzakhala zochuluka.
11 Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru.
Ndakutsogolera mʼnjira zolungama.
12 Pamene ukuyenda, mapazi ako sadzawombana;
ukamadzathamanga, sudzapunthwa.
13 Ugwiritse zimene ndikukuphunzitsazi osazitaya ayi.
Uwasamale bwino pakuti moyo wako wagona pamenepa.
14 Usayende mʼnjira za anthu oyipa
kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.
15 Pewa njira zawo, usayende mʼmenemo;
uzilambalala nʼkumangopita.
16 Pakuti iwo sagona mpaka atachita zoyipa;
tulo salipeza mpaka atapunthwitsa munthu wina.
17 Paja chakudya chawo ndicho kuchita zoyipa basi
ndipo chakumwa chawo ndi chiwawa.
18 Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha
kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.
19 Koma njira ya anthu oyipa ili ngati mdima wandiweyani;
iwo sadziwa chomwe chimawapunthwitsa.
20 Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena;
tchera khutu ku mawu anga.
21 Usayiwale malangizo angawa,
koma uwasunge mu mtima mwako.
22 Pakuti amapatsa moyo kwa aliyense amene awapeza
ndipo amachiritsa thupi lake lonse.
23 Ndipotu mtima wako uziwuyangʼanira bwino ndithu
pakuti ndiwo magwero a moyo.
24 Usiyiretu kuyankhula zokhotakhota;
ndipo ulekeretu kuyankhula zinthu zonyansa.
25 Maso ako ayangʼane patsogolo;
uziyangʼana kutsogolo molunjika.
26 Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako
ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa.
27 Usapatukire kumanja kapena kumanzere;
usapite kumene kuli zoyipa.
Chenjezo kwa Mkazi Wachigololo
5 Mwana wanga, mvetsera bwino za nzeru zimene ndikukuwuzazi,
tchera khutu ku mawu odziwitsa bwino zinthu ndikukupatsa,
2 kuti uthe kuchita zinthu mochenjera ndi mwanzeru
ndiponso kuti utetezedwe ku mayankhulidwe a mkazi wachilendo.
3 Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi.
Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta,
4 koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu;
ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
5 Mapazi ake amatsikira ku imfa;
akamayenda ndiye kuti akupita ku manda.
6 Iye saganizirapo za njira ya moyo;
njira zake ndi zokhotakhota koma iye sadziwa izi.
7 Tsopano ana inu, mundimvere;
musawasiye mawu anga.
8 Uziyenda kutali ndi mkazi wotereyo,
usayandikire khomo la nyumba yake,
9 kuopa kuti ungadzalanditse ulemerero wako kwa anthu ena;
ndi zaka zako kwa anthu ankhanza,
10 kapenanso alendo angadyerere chuma chako
ndi phindu la ntchito yako kulemeretsa anthu ena.
11 Potsiriza pa moyo wako udzabuwula,
thupi lako lonse litatheratu.
12 Ndipo udzati, “Mayo ine, ndinkadana ndi kusunga mwambo!
Mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!
13 Sindinamvere aphunzitsi anga
kapena alangizi anga.
14 Ine ndatsala pangʼono kuti ndiwonongeke
pakati pa msonkhano wonse.”
15 Imwa madzi a mʼchitsime chakochako,
madzi abwino ochokera mʼchitsime chako.
16 Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu?
Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda?
17 Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha,
osati uyigawireko alendo.
18 Yehova adalitse kasupe wako,
ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako.
19 Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino.
Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse,
ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse.
20 Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo?
Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?
21 Pakuti mayendedwe onse a munthu Yehova amawaona,
ndipo Iye amapenyetsetsa njira zake zonse.
22 Ntchito zoyipa za munthu woyipa zimamukola yekha;
zingwe za tchimo lake zimamumanga yekha.
23 Iye adzafa chifukwa chosowa mwambo,
adzasocheretsedwa chifukwa cha uchitsiru wake waukulu.
Za Moyo wa Uchitsiru
6 Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole,
ngati walonjeza kumulipirira mlendo,
2 ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena,
wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako.
3 Tsono popeza iwe mwana wanga
wadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse:
pita msanga ukamupemphe mnansi wako;
kuti akumasule!
4 Usagone tulo,
usawodzere.
5 Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje,
ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka.
6 Pita kwa nyerere, mlesi iwe;
kaonetsetse njira zake kuti uphunzirepo kanthu!
7 Zilibe mfumu,
zilibe woyangʼanira kapena wolamulira,
8 komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe
ndipo zimatuta chakudyacho nthawi yokolola.
9 Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe?
Kodi tulo tako tidzatha liti?
10 Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono
ndingopinda manjawa pangʼono kuti ndipumule,
11 umphawi udzakugwira ngati mbala
ndipo usiwa udzafika ngati munthu wachifwamba.
12 Munthu wachabechabe, munthu woyipa,
amangoyendayenda ndi kumayankhula zoyipa,
13 amatsinzinira maso ake,
namakwakwaza mapazi ake
ndi kulozaloza ndi zala zake,
14 amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo
ndipo nthawi zonse amangokhalira kuyambitsa mikangano pakati pa anthu.
15 Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa;
adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa.
16 Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo,
zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa:
17 maso onyada,
pakamwa pabodza,
manja akupha munthu wosalakwa,
18 mtima wokonzekera kuchita zoyipa,
mapazi othamangira msanga ku zoyipa,
19 mboni yonama yoyankhula mabodza
komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.
Chenjezo pa za Chigololo
20 Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;
ndipo usataye zimene anakuphunzitsa amayi ako.
21 Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse,
uzimangirire mʼkhosi mwako.
22 Ukamayenda, zidzakulozera njira;
ukugona, zidzakulondera;
ukudzuka, zidzakuyankhula.
23 Paja malamulo awa ali ngati nyale,
malangizowa ali ngati kuwunika,
ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo
moyo weniweni,
24 kukupulumutsa kwa mkazi wadama,
zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere.
25 Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake,
asakukope ndi zikope zake,
26 paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi
ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse.
27 Kodi munthu angathe kutenga moto
zovala zake osapsa?
28 Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto
mapazi ake osapserera?
29 Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina.
Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa.
30 Paja anthu sayinyoza mbala ikaba
chifukwa chakuti ili ndi njala.
31 Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri,
ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake.
32 Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru.
Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.
33 Adzalandira mabala ndi mʼnyozo,
ndipo manyazi ake sadzamuchokera.
34 Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa,
ndipo sadzachita chifundo pobwezera.
35 Iye savomera dipo lililonse;
sangapepeseke ngakhale umupatse mphatso zochuluka motani.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.