Beginning
Za Kulangidwa kwa Kusi
18 Tsoka kwa anthu a ku Kusi.
Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko a dzombe.
2 Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo,
mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi,
ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro,
kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala,
ndi woopedwa ndi anthu.
Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena.
Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”
3 Inu nonse anthu a pa dziko lonse,
inu amene mumakhala pa dziko lapansi,
pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri
yangʼanani,
ndipo pamene lipenga lilira
mumvere.
4 Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti,
“Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana,
monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha,
monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”
5 Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka
ndiponso mphesa zitayamba kupsa,
Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira,
ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.
6 Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama
ndiponso zirombo zakuthengo;
mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe,
ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.
7 Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse,
zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala,
kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe,
mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo,
anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.
Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.
Za Kulangidwa kwa Igupto
19 Uthenga onena za Igupto:
Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro,
ndipo akupita ku Igupto.
Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake,
ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha.
2 “Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha;
mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake,
mnansi ndi mnansi wake,
mzinda ndi mzinda unzake,
ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
3 Aigupto adzataya mtima
popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo;
adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa,
kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.
4 Ndidzawapereka Aigupto
kwa olamulira ankhanza,
ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,”
akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
5 Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa,
ndipo mʼmbali mwa mtsinje mudzangʼaluka ndi kuwuma.
6 Ngalande zake zidzanunkha;
ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma.
Bango ndi dulu zidzafota,
7 ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailo
ndi ku mathiriro a mtsinjewo.
Zonse zodzalidwa mʼmbali mwa Nailo
zidzawuma, zidzawuluzika ndipo sizidzaonekanso.
8 Asodzi adzabuwula ndi kudandaula,
onse amene amaponya mbedza mu Nailo;
onse amene amaponya makoka mʼmadzi
adzalira.
9 Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima,
anthu oluka nsalu zofewa zabafuta adzataya chiyembekezo.
10 Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi,
ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu.
11 Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru;
aphungu a nzeru a Farao amalangiza zopusa.
Kodi mungathe kunena bwanji kwa Farao kuti,
“Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru,
wophunzira wa mafumu akale?”
12 Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti?
Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsa
zimene Yehova Wamphamvuzonse
wakonza kuchitira dziko la Igupto.
13 Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru,
atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa;
atsogoleri a dziko la Igupto
asocheretsa anthu a dzikolo.
14 Yehova wasocheretsa
anthu a ku Igupto.
Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita,
ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake.
15 Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite,
mtsogoleri kapena wotsatira, nthambi ya kanjedza kapena bango.
16 Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga. 17 Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.
18 Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.
19 Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso. 20 Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa. 21 Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo. 22 Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.
23 Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi. 24 Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi. 25 Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”
Za Chilango cha Igupto ndi Kusi
20 Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda, 2 nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.
3 Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi, 4 momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto. 5 Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi. 6 Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”
Za Chilango cha Babuloni
21 Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja.
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja,
kuchokera ku chipululu,
dziko lochititsa mantha.
2 Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya:
Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga.
Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda!
Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.
3 Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha,
ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka;
ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva,
ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
4 Mtima wanga ukugunda,
ndipo ndikunjenjemera ndi mantha;
chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna
chasanduka chinthu choopsa kwa ine.
5 Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo,
akuyala mphasa,
akudya komanso kumwa!
Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo,
pakani mafuta zishango zanu!”
6 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi;
“Pita, kayike mlonda
kuti azinena zimene akuziona.
7 Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo
ndipo akuyenda awiriawiri,
okwera pa bulu
kapena okwera pa ngamira,
mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
8 Ndipo mlondayo anafuwula kuti,
“Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera;
Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.
9 Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta
ali ndi gulu la akavalo.
Mmodzi wa iwo akuti,
‘Babuloni wagwa, wagwa!
Mafano onse a milungu yake
agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”
10 Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu,
ine ndikukuwuzani zimene ndamva
ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,
Mulungu wa Israeli.
Za Chilango cha Edomu
11 Uthenga wonena za Duma:
Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti,
“Iwe mlonda, usikuwu utha liti?
Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
12 Mlonda akuyankha kuti,
“Kukucha, koma kudanso.
Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano;
ndipo ubwerenso udzafunse.”
Za Chilango cha Arabiya
13 Uthenga wonena za Arabiya:
Inu anthu amalonda a ku Dedani,
amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,
14 perekani madzi kwa anthu aludzu.
Inu anthu a ku Tema
perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.
15 Iwo akuthawa malupanga,
lupanga losololedwa,
akuthawa uta wokokakoka
ndiponso nkhondo yoopsa.
16 Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu. 17 Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.
Za Chilango cha Yerusalemu
22 Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya:
Kodi chachitika nʼchiyani,
kuti nonsenu mukwere pa madenga?
2 Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,
iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?
Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,
kapena kufera pa nkhondo.
3 Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi;
koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe.
Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo,
ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
4 Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;
ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.
Musayesere kunditonthoza
chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
5 Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione
mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo
mʼChigwa cha Masomphenya.
Malinga agumuka,
komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
6 Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta
ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.
Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
7 Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,
ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
8 zonse zoteteza Yuda zachotsedwa.
Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana
zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
9 inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide
anali ndi malo ambiri ogumuka;
munasunga madzi
mu chidziwe chakumunsi.
10 Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu
ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
11 Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime
chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,
koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,
kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
12 Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi;
kumeta mutu wanu mpala
ndi kuvala ziguduli.
13 Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;
munapha ngʼombe ndi nkhosa;
munadya nyama ndi kumwa vinyo.
Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa
pakuti mawa tifa!”
14 Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
15 Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,
amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16 Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo
kuti udzikumbire manda kuno,
kudzikumbira manda pa phiri
ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
17 “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba
ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
18 Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira
ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.
Kumeneko ndiko ukafere
ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.
Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
19 Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako
ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
20 “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. 21 Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. 22 Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. 23 Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. 24 Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
25 “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.