Beginning
Mawu Oyamba: Cholinga ndi Mutu
1 Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:
2 Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo;
kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
3 kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru,
akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
4 Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera,
achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
5 Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake,
ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
6 kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo,
mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.
7 Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.
Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.
Malangizo kuti Asunge Nzeru
Malangizo kwa Achinyamata
8 Mwana wanga, mvera malangizo a abambo ako
ndipo usakane mawu okuwongolera a amayi ako.
9 Ali ngati sangamutu yokongola ya maluwa pamutu pako
ndiponso ali ngati mkanda mʼkhosi mwako.
10 Mwana wanga, ngati anthu oyipa afuna kukukopa
usamawamvere.
11 Akadzati, “Tiye kuno;
tikabisale kuti tiphe anthu,
tikabisalire anthu osalakwa;
12 tiwameze amoyo ngati manda,
ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje.
13 Motero tidzapeza zinthu zosiyanasiyana zamtengowapatali
ndi kudzaza nyumba zathu ndi zolanda;
14 Bwera, chita nafe maere,
ndipo tidzagawana chuma chathu tonse.”
15 Mwana wanga, usayende nawo pamodzi,
usatsagane nawo mʼnjira zawozo.
16 Iwowatu amangofuna zoyipa zokhazokha,
amathamangira kukhetsa magazi.
17 Nʼkopanda phindu kutchera msampha
mbalame zikuona!
18 Koma anthu amenewa amangobisalira miyoyo yawo yomwe;
amangodzitchera okha msampha!
19 Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza;
chumacho chimapha mwiniwake.
Chenjezo Pomwe Tikana Nzeru
20 Nzeru ikufuwula mu msewu,
ikuyankhula mokweza mawu mʼmisika;
21 ikufuwula pa mphambano ya misewu,
ikuyankhula pa zipata za mzinda kuti,
22 “Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti?
Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti?
Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?
23 Tamverani mawu anga a chidzudzulo.
Ine ndikukuwuzani maganizo anga
ndi kukudziwitsani mawu anga.
24 Popeza ndinakuyitanani koma inu munakana kumvera.
Ndinayesa kukuthandizani koma panalibe amene anasamala.
25 Uphungu wanga munawunyoza.
Kudzudzula kwanga simunakusamale.
26 Ndiye inenso ndidzakusekani mukadzakhala mʼmavuto;
ndidzakunyogodolani chikadzakugwerani chimene mumachiopacho.
27 Chiwonongeko chikadzakugwerani ngati namondwe,
tsoka likadzakufikirani ngati kamvuluvulu,
mavuto ndi masautso akadzakugwerani.
28 “Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha;
mudzandifunafuna, koma simudzandipeza.
29 Popeza iwo anadana ndi chidziwitso
ndipo sanasankhe kuopa Yehova,
30 popeza iwo sanasamale malangizo anga
ndipo ananyoza chidzudzulo changa.
31 Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo
ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.
32 Pakuti anthu osachangamuka amaphedwa chifukwa cha kusochera kwawo,
ndipo zitsiru zimadziwononga zokha chifukwa cha mphwayi zawo.
33 Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa bata;
adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”
Ubwino Wanzeru
2 Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga
ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,
2 ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru
ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;
3 ngati upempha kuti uzindikire zinthu
inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,
4 ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva
ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,
5 ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova;
ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.
6 Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru,
ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
7 Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo.
Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
8 pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama.
Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.
9 Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo,
kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.
10 Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako,
kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.
11 Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga;
kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.
12 Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa,
kwa anthu amabodza,
13 amene amasiya njira zolungama
namayenda mʼnjira zamdima,
14 amene amakondwera pochita zoyipa
namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.
15 Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota,
ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.
16 Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo;
kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,
17 amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake
ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.
18 Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa;
njira zake zimamufikitsa ku manda.
19 Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera
kapena kupezanso njira zamoyo.
20 Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino,
uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.
21 Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko
ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;
22 Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo,
ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.
Phindu Lina la Nzeru
3 Mwana wanga, usayiwale malangizo anga,
mtima wako usunge malamulo anga.
2 Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka
ndipo udzakhala pa mtendere.
3 Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere.
Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda
ndi kuwalemba pa mtima pako.
4 Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino
pamaso pa Mulungu ndi anthu.
5 Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse
ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
6 Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo,
ndipo Iye adzawongola njira zako.
7 Usamadzione ngati wa nzeru.
Uziopa Yehova ndi kupewa zoyipa.
8 Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino
ndi mafupa ako adzakhala olimba.
9 Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse;
zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova.
10 Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri,
ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.
11 Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova,
ndipo usayipidwe ndi chidzudzulo chake.
12 Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda,
monga abambo achitira mwana amene amakondwera naye.
13 Wodala munthu amene wapeza nzeru,
munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu,
14 pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva,
phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide.
15 Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali;
ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.
16 Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali;
mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemu.
17 Njira zake ndi njira zosangalatsa,
ndipo mu njira zake zonse muli mtendere.
18 Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa;
wodala munthu amene amayigwiritsa kwambiri.
19 Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru.
Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba.
20 Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka
ndiponso mitambo inagwetsa mvula.
21 Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino.
Zimenezi zisakuchokere.
22 Zimenezi zidzakupatsa moyo,
moyo wake wosangalatsa ndi wabwino ngati mkanda wa mʼkhosi.
23 Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu,
ndipo phazi lako silidzapunthwa;
24 pamene ugona pansi, sudzachita mantha;
ukadzagona pansi tulo tako tidzakhala tokoma.
25 Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi
kapena chiwonongeko chimene chidzagwera anthu oyipa,
26 pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima
ndipo adzasunga phazi lako kuti lisakodwe mu msampha.
27 Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino,
pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi.
28 Usanene kwa mnansi wako kuti,
“Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa”
pamene uli nazo tsopano.
29 Usamukonzere chiwembu mnansi wako,
amene anakhala nawe pafupi mokudalira.
30 Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa
pamene iye sanakuchitire zoyipa.
31 Usachite naye nsanje munthu wachiwawa
kapena kutsanzira khalidwe lake lililonse.
32 Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa
koma amayanjana nawo anthu olungama.
33 Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa,
koma amadalitsa nyumba ya anthu olungama.
34 Anthu onyoza, Iye amawanyoza,
koma amakomera mtima anthu odzichepetsa.
35 Anthu anzeru adzalandira ulemu,
koma zitsiru adzazichititsa manyazi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.