Beginning
BUKU LACHINAYI
Masalimo 90–106
Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.
90 Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo
pa mibado yonse.
2 Mapiri asanabadwe,
musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,
kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.
3 Inu mumabwezera anthu ku fumbi,
mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
4 Pakuti zaka 1,000 pamaso panu
zili ngati tsiku limene lapita
kapena ngati kamphindi ka usiku.
5 Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,
iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
6 ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,
pofika madzulo wauma ndi kufota.
7 Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu;
ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.
8 Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu,
machimo athu obisika poonekera pamaso panu.
9 Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu;
timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.
10 Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70,
kapena 80 ngati tili ndi mphamvu;
komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa,
zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.
11 Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu?
Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.
12 Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,
kuti tikhale ndi mtima wanzeru.
13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
Achitireni chifundo atumiki anu.
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,
kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,
kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,
kukongola kwanu kwa ana awo.
17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.
91 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba
adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
2 Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,
Mulungu wanga amene ndimadalira.”
3 Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje
ndi ku mliri woopsa;
4 Adzakuphimba ndi nthenga zake,
ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;
kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
5 Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku,
kapena muvi wowuluka masana,
6 kapena mliri umene umayenda mu mdima,
kapena zowononga za pa nthawi ya masana.
7 Anthu 1,000 atha kufa pambali pako,
anthu 10,000 kudzanja lako lamanja,
koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe.
8 Udzapenya ndi maso ako
ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.
9 Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo;
wavomera Yehova kukhala kothawira kwako.
10 Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera,
zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako.
11 Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe,
kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse;
12 ndipo adzakunyamula ndi manja awo,
kuti phazi lako lisagunde pa mwala.
13 Udzapondaponda mkango ndi njoka,
udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka.
14 “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa;
ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
15 Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;
ndidzakhala naye pa mavuto,
ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
16 Ndidzamupatsa moyo wautali
ndi kumupulumutsa.”
Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata.
92 Nʼkwabwino kutamanda Yehova
ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,
2 Kulengeza chikondi chanu mmawa,
ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,
3 kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi
ndi mayimbidwe abwino a zeze.
4 Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova;
Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.
5 Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova,
maganizo anu ndi ozamadi!
6 Munthu wopanda nzeru sadziwa,
zitsiru sizizindikira,
7 kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu
ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula,
adzawonongedwa kwamuyaya.
8 Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.
9 Zoonadi adani anu Yehova,
zoonadi adani anu adzawonongeka;
onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.
10 Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati;
mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.
11 Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane,
makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.
12 Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa,
adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
13 odzalidwa mʼnyumba ya Yehova,
adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.
14 Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo,
adzakhala anthete ndi obiriwira,
15 kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama;
Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”
93 Yehova akulamulira, wavala ulemerero;
Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,
dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
2 Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;
Inu ndinu wamuyaya.
3 Nyanja zakweza Inu Yehova,
nyanja zakweza mawu ake;
nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
4 Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,
ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,
Yehova mmwamba ndi wamphamvu.
5 Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;
chiyero chimakongoletsa nyumba yanu
mpaka muyaya.
94 Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango,
Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
2 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi;
bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
3 Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova,
mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?
4 Amakhuthula mawu onyada;
onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
5 Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova;
amapondereza cholowa chanu.
6 Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko;
amapha ana amasiye.
7 Iwo amati, “Yehova sakuona;
Mulungu wa Yakobo salabadirako.”
8 Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu;
zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
9 Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva?
Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
10 Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga?
Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
11 Yehova amadziwa maganizo a munthu;
Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.
12 Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza,
munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
13 mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto,
mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake;
Iye sadzasiya cholowa chake.
15 Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo,
ndipo onse olungama mtima adzachitsata.
16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa?
Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
17 Yehova akanapanda kundithandiza,
bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
18 Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,”
chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
19 Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,
chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.
20 Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu
umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
21 Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama
ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
22 Koma Yehova wakhala linga langa,
ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
23 Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo
ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo;
Yehova Mulungu wathu adzawawononga.
95 Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe,
tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu
2 Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko
ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.
3 Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,
mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.
4 Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi,
ndipo msonga za mapiri ndi zake.
5 Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye,
ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.
6 Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,
tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
7 pakuti Iye ndiye Mulungu wathu
ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,
ndi nkhosa za mʼdzanja lake.
Lero ngati inu mumva mawu ake,
8 musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba,
monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.
9 Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa,
ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.
10 Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo;
ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera
ndipo sanadziwe njira zanga.”
11 Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti,
“Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.