Beginning
24 “Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze?
Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa?
2 Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo;
amadyetsa ziweto zimene aba.
3 Amalanda abulu a ana amasiye
ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole.
4 Amachotsa mʼmisewu anthu osauka,
ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko.
5 Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu,
amayendayenda kufuna chakudya;
dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo.
6 Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake,
ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa.
7 Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala;
pa nthawi yozizira amasowa chofunda.
8 Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri
ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo.
9 Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere;
ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole.
10 Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala;
amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala.
11 Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa;
amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu.
12 Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda,
anthu ovulala akulirira chithandizo.
Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense.
13 “Pali ena amene amakana kuwala,
amene safuna kuyenda mʼkuwalako
kapena kukhala mʼnjira zake.
14 Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka
ndipo amakapha osauka ndi amphawi;
nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.
15 Munthu wachigololo amadikira chisisira;
iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’
ndipo amaphimba nkhope yake.
16 Mbala zimathyola nyumba usiku,
koma masana zimadzitsekera;
izo zimathawa kuwala.
17 Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera.
Iwo amachita ubale ndi zoopsa za mdima.
18 “Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi;
minda yawo ndi yotembereredwa pa dzikolo
kotero kuti palibe amene amapita ku minda ya mpesa.
19 Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana
ndi momwemonso mmene manda amachotsera omwe achimwa.
20 Mayi wowabereka amawayiwala,
mphutsi zimasangalala powadya;
anthu oyipa sakumbukiridwanso
koma amathyoka ngati mtengo.
21 Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana,
ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye.
22 Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake;
ngakhale munthuyo atakhazikika, alibe chiyembekezo cha moyo wake.
23 Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka,
koma amakhala akupenyetsetsa njira zawo.
24 Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso;
amatsitsidwa ndipo amachotsedwa monga ena onse;
amadulidwa ngati ngala za tirigu.
25 “Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza
ndi kusandutsa mawu anga kukhala wopanda pake?”
Mawu a Bilidadi
25 Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
2 “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu,
Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.
3 Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka?
Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?
4 Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu?
Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?
5 Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni,
ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,
6 nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi,
mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”
Mawu a Yobu
26 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu!
Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka!
3 Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru!
Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!
4 Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa?
Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako?
5 “Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi,
ndi zonse zokhala mʼmadzimo.
6 Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu;
chiwonongeko ndi chosaphimbidwa.
7 Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho;
Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe.
8 Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake,
koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
9 Iye amaphimba mwezi wowala,
amawuphimba ndi mitambo yake.
10 Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta,
kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima.
11 Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera,
ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
12 Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja;
ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe.
13 Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga,
dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija.
14 Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake;
tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona!
Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”
27 Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:
2 “Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama,
Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga,
3 nthawi zonse pamene ndili ndi moyo,
mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga,
4 pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa,
lilime langa silidzayankhula zachinyengo.
5 Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona;
mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga.
6 Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere;
chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga.
7 “Mdani wanga akhale ngati woyipa,
wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama!
8 Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa,
pamene Mulungu achotsa moyo wake?
9 Kodi Mulungu amamva kulira kwake
pamene zovuta zamugwera?
10 Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse?
Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse?
11 “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo
sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse.
12 Inu mwadzionera nokha zonsezi.
Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake?
13 “Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa,
cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse.
14 Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo
zidzukulu zake zidzasowa zakudya.
15 Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri,
ndipo akazi awo amasiye sadzawalira.
16 Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi,
ndi kukundika zovala ngati mchenga,
17 zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale,
ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo.
18 Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche,
ili ngati msasa umene mlonda amamanga.
19 Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko;
akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita.
20 Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula;
mphepo yamkuntho imamunyamula usiku.
21 Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo
imamuchotsa pamalo pake.
22 Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni,
pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro.
23 Mphepoyo imamuwomba ndithu
ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.”
28 Pali mgodi wa siliva
ndiponso malo oyengerapo golide.
2 Chitsulo amachikumba pansi,
ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa.
3 Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale,
amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo,
kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani.
4 Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu,
kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko;
iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku.
5 Nthaka, imene imatulutsa zakudya,
kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto;
6 miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake,
ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide.
7 Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi,
palibe kamtema amene anayiona.
8 Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo,
ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo.
9 Munthu amaphwanya matanthwe olimba,
ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde.
10 Amabowola njira mʼmatanthwewo;
ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo.
11 Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso,
motero amatulutsira poyera zinthu zobisika.
12 “Koma nzeru zingapezeke kuti?
Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
13 Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo;
nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo.
14 Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’
Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’
15 Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri,
mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri.
16 Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri,
kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro.
17 Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi,
sungayigule ndi zokometsera zagolide.
18 Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe;
mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi.
19 Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi;
nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri.
20 “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti?
Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
21 Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse,
ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga.
22 Chiwonongeko ndi imfa zikuti,
‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’
23 Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko,
ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala,
24 pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi
ndipo amaona zonse za kunsi kwa thambo.
25 Iye atapatsa mphepo mphamvu zake,
nayeza kuzama kwa nyanja,
26 atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa
ndi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu,
27 pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake;
nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe.
28 Ndipo Iye anati kwa munthu,
‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo
ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.