Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 86-89

Pemphero la Davide.

86 Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe,
    pakuti ndine wosauka ndi wosowa.
Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu.
    Inu ndinu Mulungu wanga;
    pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu.
Inu ndinu Mulungu wanga.
Mundichitire chifundo, Inu Ambuye,
    pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.
Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye,
    pakuti ndimadalira Inu.

Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino,
    wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.
Yehova imvani pemphero langa;
    mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.
Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu,
    pakuti Inu mudzandiyankha.

Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye;
    palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.
Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga
    idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye;
    iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.
10 Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa;
    Inu nokha ndiye Mulungu.

11 Ndiphunzitseni njira yanu Yehova,
    ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu;
patseni mtima wosagawikana
    kuti ndilemekeze dzina lanu.
12 Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;
    ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.
13 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine;
    mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.

14 Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo;
    anthu ankhanza akufuna kundipha,
    amene salabadira za Inu.
15 Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,
    wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo;
    perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu
    ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17 Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu
    kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi,
    pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.

Salimo la Ana a Kora.

87 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;
    Yehova amakonda zipata za Ziyoni
    kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.
Za ulemerero wako zimakambidwa,
    Iwe mzinda wa Mulungu:
            Sela
“Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni
    pakati pa iwo amene amandidziwa.
Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,
    ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”

Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,
    “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,
    ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”
Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:
    “Uyu anabadwira mʼZiyoni.”
            Sela
Oyimba ndi ovina omwe adzati,
    “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”

Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara.

88 Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa,
    usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.
Pemphero langa lifike pamaso panu;
    tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.

Pakuti ndili ndi mavuto ambiri
    ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda.
Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje;
    ndine munthu wopanda mphamvu.
Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa,
    monga ophedwa amene agona mʼmanda,
amene Inu simuwakumbukiranso,
    amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.

Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni,
    mʼmalo akuya a mdima waukulu.
Ukali wanu ukundipsinja kwambiri,
    mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse.
            Sela
Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enieni
    ndipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo.
Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;
    maso anga ada ndi chisoni.

Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse;
    ndimakweza manja anga kwa Inu.
10 Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa?
    Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu?
            Sela
11 Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda,
    za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?
12 Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima,
    kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?

13 Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo;
    mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.
14 Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikana
    ndi kundibisira nkhope yanu?

15 Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa;
    ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.
16 Ukali wanu wandimiza;
    zoopsa zanu zandiwononga.
17 Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula;
    zandimiza kwathunthu.
18 Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga;
    mdima ndiye bwenzi langa lenileni.

Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara.

89 Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya;
    ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya,
    kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.

Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga,
    ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya.
    Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ”
            Sela.

Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova,
    kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.
Pakuti ndani mu mlengalenga angalingane ndi Yehova?
    Ndani wofanana ndi Yehova pakati pa zolengedwa zakumwamba?
Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri;
    Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.
Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu?
    Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.

Mumalamula nyanja ya mafunde awukali;
    pamene mafunde ake awundana Inu mumawakhalitsa bata.
10 Munaphwanya Rahabe monga munthu wophedwa;
    ndi dzanja lanu lamphamvu munabalalitsa adani anu.
11 Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu;
    munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.
12 Munalenga Kumpoto ndi Kummwera;
    Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.
13 Mkono wanu ndi wamphamvu;
    dzanja lanu ndi lamphamvu, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.

14 Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu;
    chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.
15 Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu,
    amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova.
16 Amakondwera mʼdzina lanu tsiku lonse lathunthu;
    amasangalala koposa mʼchilungamo chanu.
17 Pakuti Inu ndiye ulemerero wawo ndi mphamvu yawo
    ndipo mwa kukoma mtima kwanu Inu mumakweza nyanga yathu.
18 Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova,
    Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.

19 Kale munayankhula mʼmasomphenya,
    kwa anthu anu okhulupirika munati,
“Ndapatsa mphamvu wankhondo;
    ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
    ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
    zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
    anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
    ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
    ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
    dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
    Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’
27 Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa;
    wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.
28 Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya,
    ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.
29 Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya,
    mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.

30 “Ngati ana ake adzataya lamulo langa
    ndi kusatsatira malangizo anga,
31 ngati adzaswa malamulo anga
    ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,
32 Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo,
    mphulupulu zawo powakwapula.
33 Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye,
    kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.
34 Sindidzaswa pangano langa
    kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.
35 Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga
    ndipo sindidzanama kwa Davide,
36 kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya
    ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;
37 udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi,
    mboni yokhulupirika mʼmitambo.
            Sela

38 “Koma tsopano Inu mwamukana, mwamutaya,
    mwamukwiyira kwambiri wodzozedwa wanu.
39 Mwakana pangano ndi mtumiki wanu
    ndipo mwadetsa mʼfumbi chipewa chake chaufumu.
40 Inu mwagumula makoma ake onse
    ndipo mwasandutsa bwinja malinga ake.
41 Onse amene amadutsa amalanda zinthu zake;
    iye wakhala chotonzedwa cha anansi ake.
42 Mwakweza dzanja lamanja la adani ake;
    mwachititsa kuti adani ake akondwere.
43 Mwabunthitsa lupanga lake,
    simunamuthandize pa nkhondo.
44 Inu mwathetsa kukongola kwa ulemerero wake
    ndipo mwagwetsa pansi mpando wake waufumu.
45 Mwachepetsa masiku a unyamata wake;
    mwamuphimba ndi chofunda chochititsa manyazi.
            Sela

46 “Mpaka liti Yehova? Kodi mudzadzibisa mpaka kalekale?
    Mpaka liti ukali wanu udzayaka ngati moto?
47 Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa
    pakuti munalenga kwachabe anthu onse!
48 Kodi ndi munthu uti angakhale ndi moyo ndi kusaona imfa?
    Kapena kudzipulumutsa yekha ku mphamvu ya manda?
            Sela
49 Inu Ambuye kodi chili kuti chikondi chanu chachikulu choyamba chija,
    chimene mwa kukhulupirika kwanu munalumbira kwa Davide?
50 Kumbukirani, Ambuye momwe mtumiki wanu wanyozedwera,
    momwe ndakhalira ndi kusunga mu mtima mwanga mawu a pangano a anthu a mitundu yonse,
51 mawu achipongwe amene adani anu akhala akunyoza, Inu Yehova,
    ndi mawu amene akhala akunyoza mayendedwe onse a wodzozedwa wanu.

52 “Matamando akhale kwa Yehova mpaka muyaya!”
Ameni ndi Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.