Beginning
17 “Mtima wanga wasweka,
masiku anga atha,
manda akundidikira.
2 Ndithudi, anthu ondiseka andizungulira;
maso anga akupenyetsetsa mdani wanga.
3 “Inu Mulungu, patseni chikole chimene mukufuna.
Ndani wina amene adzandiperekera ine chikole?
4 Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu;
choncho simudzawalola kuti apambane.
5 Ngati munthu apereka mnzake chifukwa cha chuma,
ana ake sadzaona mwayi.
6 “Mulungu wandisandutsa chisudzo chochiseka aliyense,
munthu amene anthu amalavulira malovu nkhope yake.
7 Mʼmaso mwanga mwada ndi chisoni;
ndawonda ndi mutu womwe.
8 Anthu olungama akudabwa nazo zimenezi;
anthu osachimwa akupsera mtima anthu osapembedza Mulungu.
9 Komabe anthu olungama adzasunga njira zawo,
ndipo anthu a makhalidwe abwino mphamvu zawo zidzanka zikuchuluka.
10 “Tsono bwerani nonsenu, bwerezaninso mawu anuwo,
sindidzapezapo munthu wanzeru pakati panupo.
11 Masiku anga atha, zimene ndinakonza zalephereka,
pamodzinso ndi zokhumba za mtima wanga.
12 Anthu awa amasandutsa usiku kukhala usana,
nthawi ya usiku iwo amati ‘kwatsala pangʼono kucha.’
13 Ngati nyumba imene ndikuyiyembekezera ndi manda,
ngati ndiyala bedi langa mu mdima,
14 ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’
ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’
15 tsono chiyembekezo changa chili kuti?
Ndani angaone populumukira panga?
16 Ndithu sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse,
polowa mʼmanda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.”
Mawu a Bilidadi
18 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,
2 “Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi?
Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula.
3 Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe
ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako?
4 Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako,
kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo?
Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?
5 “Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa;
malawi a moto wake sakuwalanso.
6 Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima;
nyale ya pambali pake yazima.
7 Mayendedwe ake amgugu azilala;
fundo zake zomwe zamugwetsa.
8 Mapazi ake amulowetsa mu ukonde
ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.
9 Msampha wamkola mwendo;
khwekhwe lamugwiritsitsa.
10 Amutchera msampha pansi mobisika;
atchera diwa pa njira yake.
11 Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse,
zikutsatira mayendedwe ake onse.
12 Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala,
tsoka likumudikira.
13 Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse;
miyendo yake, manja ake, zonse zawola.
14 Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira,
ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse.
15 Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo;
awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda.
16 Mizu yake ikuwuma pansi
ndipo nthambi zake zikufota
17 Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi;
sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko.
18 Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima,
ndipo amupirikitsa pa dziko lonse.
19 Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake,
kulibe wotsala kumene iye ankakhala.
20 Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake;
anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu.
21 Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa;
amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.”
Mawu a Yobu
19 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Kodi mudzakhala mukundizunza mpaka liti,
ndi kundilasa ndi mawu anuwo?
3 Inuyo mwandinyoza kwambiri;
mwanditsutsa mopanda manyazi.
4 Ngati ndi zoona kuti ine ndasochera,
cholakwachotu nʼchanga.
5 Ngati ndithudi mukudziyika nokha pamwamba panga,
ndi kugwiritsa ntchito kunyozedwa kwanga polimbana nane,
6 pamenepa dziwani kuti Mulungu wandilakwira
ndipo wandizinga ukonde wake.
7 “Ngakhale ndifuwule kuti, ‘Akundizunza!’ Palibe wondiyankha;
ngakhale ndipemphe thandizo, palibe wondichitira zolungama.
8 Mulungu wanditsekera njira yanga kotero sindingathe kudutsa;
waphimba njira zanga ndi mdima.
9 Iye wandilanda ulemu wanga
ndipo wandivula chipewa chaufumu pamutu panga.
10 Wandiphwanyaphwanya mbali zonse ndipo ndatheratu;
Iye wazula chiyembekezo changa ngati mtengo.
11 Wandikwiyira ndipo
akundiyesa mmodzi mwa adani ake.
12 Ankhondo ake akubwera kwa ine mwamphamvu,
akonzekera zodzalimbana nane
ndipo azungulira nyumba yanga.
13 “Mulungu wandisiyanitsa ndi abale anga;
wasandutsa odziwana nane kukhala achilendo kwa ine.
14 Abale anga andithawa;
abwenzi anga andiyiwala.
15 Anthu odzacheza ku nyumba kwanga ndiponso antchito anga aakazi andisandutsa mlendo;
ndasanduka mlendo mʼmaso mwawo.
16 Ndikayitana wa ntchito wanga, iye sandiyankha,
ngakhale ndikapempha ndi pakamwa panga sandichitira kanthu.
17 Mpweya wanga umamunyansa mkazi wanga;
ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi.
18 Inde, ngakhale ana amandinyoza;
akandiona amandinyodola.
19 Anzanga onse apamtima amanyansidwa nane;
iwo amene ndinkawakonda andiwukira.
20 Ndangotsala khungu ndi mafupa okhaokha;
ndapulumuka lokumbakumba.
21 “Mvereni chisoni, inu abwenzi anga, mvereni chisoni,
pakuti dzanja la Mulungu landikantha.
22 Chifukwa chiyani mukundilondola ngati Mulungu?
Kodi simunatope nalo thupi langa?
23 “Aa, achikhala mawu anga analembedwa,
achikhala analembedwa mʼbuku,
24 akanalembedwa pa mwala ndi chitsulo,
akanalembedwa pa thanthwe kuti sangathe kufufutidwa!
25 Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo,
ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
26 Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka,
mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu.
27 Ine ndemwe ndidzamuona Iye
ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi.
Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi!
28 “Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji,
popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’
29 Inu muyenera kuopa lupanga;
pakuti mkwiyo wake umalangadi ndi lupanga;
zikadzatero muzadziwa kuti chiweruzo chilipo ndithu.”
Mawu a Zofari
20 Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti
2 “Kuvutika kwa mʼmaganizo kwanga kwandifulumiza kuti ndiyankhe
chifukwa ndasautsidwa kwambiri.
3 Ndikumva kudzudzula kondinyoza,
ndipo kumvetsetsa kwanga kwa zinthu kwandifulumiza kuti ndiyankhe.
4 “Ndithudi iwe ukudziwa momwe zinthu zakhala zikuchitikira kuyambira kale,
kuchoka nthawi imene munthu analengedwa pa dziko lapansi,
5 kuti chisangalalo cha woyipa nʼchosachedwa kutha,
chimwemwe cha wosapembedza Mulungu nʼchakanthawi kochepa.
6 Ngakhale atamayenda mapewa ake ali mmwamba
ndipo mutu wake uli nengʼaa,
7 iye adzatheratu monga momwe imatayikira ndowe yake yomwe;
iwo amene ankamuona adzati, ‘Kodi uje uja ali kuti?’
8 Adzazimirira ngati maloto ndipo sadzapezekanso,
adzachotsedwa ngati masomphenya a usiku.
9 Diso limene linamuona silidzamuonanso;
sadzapezekanso pamalo pake.
10 Ana ake adzabwezera zonse
zimene iyeyo analanda anthu osauka;
11 Mphamvu zaunyamata zimene zili mʼthupi mwake
zidzagona naye limodzi mʼfumbi.
12 “Ngakhale zoyipa zili zozuna mʼkamwa mwake
ndipo amazibisa kunsi kwa lilime lake,
13 ngakhale salola kuzilavula,
ndipo amazisunga mʼkamwa mwake,
14 koma chakudya chake chidzawawasa mʼmimba mwake;
chidzasanduka ngati ndulu ya njoka mʼkati mwa iyeyo.
15 Adzachisanza chuma chimene anachimeza;
Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo.
16 Iye adzayamwa ndulu ya njoka ndipo
ululu wa mphiri udzamupha.
17 Sadzasangalala ndi timitsinje,
mitsinje yoyenda uchi ndi mafuta.
18 Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya;
sadzasangalala ndi phindu la malonda ake.
19 Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo;
iyeyo analanda nyumba zimene sanamange.
20 “Chifukwa choti umbombo wake sutha,
sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho.
21 Palibe chatsala kuti iye adye;
chuma chake sichidzachedwa kutha.
22 Ngakhale ndi munthu wachuma, mavuto adzamugwera;
mavuto aakulu adzamugwera.
23 Akadya nʼkukhuta,
Mulungu adzamugwetsera ukali wamoto
ngati mvula yosalekeza.
24 Ngakhale athawe mkondo wachitsulo,
muvi wamkuwa wosongoka udzamulasa.
25 Muviwo adzawutulutsira ku msana,
songa yake yowala kuchoka mʼmphafa mwake.
Adzagwidwa ndi mantha aakulu;
26 mdima wandiweyani ukudikira chuma chake.
Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza
ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake.
27 Zamumlengalenga zidzawulula kulakwa kwake;
dziko lapansi lidzamuwukira.
28 Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake,
katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu.
29 Izi ndi zimene Mulungu amasungira anthu oyipa,
mphotho imene Mulungu amayikira iwowo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.