Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 66-69

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo.

66 Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
    Imbani ulemerero wa dzina lake;
    kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!
    Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri
    kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
Dziko lonse lapansi limaweramira inu;
    limayimba matamando kwa Inu;
    limayimba matamando pa dzina lanu.”
            Sela.

Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
    ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma,
    iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi.
    Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya,
    maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina.
    Anthu owukira asadzitukumule.

Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,
    mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
Iye watchinjiriza miyoyo yathu
    ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;
    munatiyenga ngati siliva.
11 Inu mwatilowetsa mʼndende
    ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;
    ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,
    koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.

13 Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza
    ndi kukwaniritsa malumbiro anga.
14 Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza
    ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.
15 Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu
    ndi chopereka cha nkhosa zazimuna;
    ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi.
            Sela

16 Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu.
    Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.
17 Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga,
    matamando ake anali pa lilime panga.
18 Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga
    Ambuye sakanamvera;
19 koma ndithu Mulungu wamvetsera
    ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.
20 Matamando akhale kwa Mulungu
    amene sanakane pemphero langa
    kapena kuletsa chikondi chake pa ine!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo.

67 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,
    achititse kuti nkhope yake itiwalire.
Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,
    chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,
    pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo
    ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

Nthaka yabereka zokolola zake;
    tidalitseni Mulungu wathu.
Mulungu atidalitse
    kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

68 Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;
    adani ake athawe pamaso pake.
Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.
    Monga phula limasungunukira pa moto,
    oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
Koma olungama asangalale
    ndi kukondwera pamaso pa Mulungu;
    iwo akondwere ndi kusangalala.

Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
    mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
    dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
    ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,
    amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;
    koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.

Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,
    pamene munayenda kudutsa chipululu,
dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,
    pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.
    Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;
    munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
10 Anthu anu anakhala mʼmenemo
    ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.

11 Ambuye analengeza mawu,
    ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;
12 “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro;
    mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.
13 Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto,
    mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva,
    nthenga zake ndi golide wonyezimira.”
14 Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko,
    zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.

15 Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero;
    mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.
16 Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri,
    pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira,
    kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
17 Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka,
    ndi miyandamiyanda;
    Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
18 Pamene Inu munakwera mmwamba,
    munatsogolera a mʼndende ambiri;
    munalandira mphatso kuchokera kwa anthu,
ngakhale kuchokera kwa owukira,
    kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.

19 Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu
    amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
20 Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;
    Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.

21 Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,
    zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
22 Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani;
    ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.
23 Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu,
    pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”

24 Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu;
    mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo;
    pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
26 Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu;
    tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera,
    pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda,
    ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.

28 Kungani mphamvu zanu Mulungu;
    tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
29 Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,
    mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,
    gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.
Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.
    Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
31 Nthumwi zidzachokera ku Igupto;
    Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.

32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi
    imbirani Ambuye matamando.
            Sela
33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba
    amene amabangula ndi mawu amphamvu.
34 Lengezani za mphamvu za Mulungu,
    amene ulemerero wake uli pa Israeli
    amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;
    Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.

Matamando akhale kwa Mulungu!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.”

69 Pulumutseni Inu Mulungu,
    pakuti madzi afika mʼkhosi
Ine ndikumira mʼthope lozama
    mʼmene mulibe popondapo.
Ndalowa mʼmadzi ozama;
    mafunde andimiza.
Ndafowoka ndikupempha chithandizo;
    kummero kwanga kwawuma gwaa,
mʼmaso mwanga mwada
    kuyembekezera Mulungu wanga.
Iwo amene amadana nane popanda chifukwa
    ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;
ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,
    iwo amene akufunafuna kundiwononga.
Ndikukakamizidwa kubwezera
    zomwe sindinabe.

Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,
    kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.

Iwo amene amadalira Inu
    asanyozedwe chifukwa cha ine,
    Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Iwo amene amafunafuna Inu
    asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine,
    Inu Mulungu wa Israeli.
Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu,
    ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.
Ndine mlendo kwa abale anga,
    munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;
pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa
    ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.
10 Pamene ndikulira ndi kusala kudya,
    ndiyenera kupirira kunyozedwa;
11 pomwe ndavala chiguduli,
    anthu amandiseweretsa.
12 Iwo amene amakhala pa chipata amandinena,
    ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.

13 Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye,
    pa nthawi yanu yondikomera mtima;
mwa chikondi chanu chachikulu
    Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.
14 Mundilanditse kuchoka mʼmatope,
    musalole kuti ndimire,
pulumutseni ine kwa iwo
    amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.
15 Musalole kuti chigumula chindimeze,
    kuya kusandimeze
    ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.
16 Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu;
    mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.
17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu,
    ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.
18 Bwerani pafupi ndi kundilanditsa;
    ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.

19 Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera,
    kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.
20 Mnyozo waswa mtima wanga
    ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse;
ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni,
    koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.
21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa
    ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.

22 Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha;
    chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.
23 Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso
    ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.
24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo;
    mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.
25 Malo awo akhale wopanda anthu
    pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.
26 Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza
    ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.
27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,
    musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.
28 Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo
    ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

29 Ndikumva zowawa ndi kuzunzika;
    lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.

30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,
    ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,
    kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.
32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,
    Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!
33 Yehova amamvera anthu osowa
    ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.

34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,
    nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,
35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni
    ndi kumanganso mizinda ya Yuda,
anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
36     ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,
    ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.