Beginning
14 “Munthu wobadwa mwa amayi
amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha.
2 Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota;
amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa.
3 Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa?
Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu?
4 Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa?
Palibe ndi mmodzi yemwe!
5 Masiku a munthu ndi odziwikiratu;
munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake
ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha.
6 Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule
kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu.
7 “Mtengo uli nacho chiyembekezo:
ngati wadulidwa, udzaphukiranso
ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.
8 Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka
ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi,
9 koma pamene chinyontho chafika udzaphukira
ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.
10 Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda,
amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko.
11 Monga madzi amaphwera mʼnyanja
kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma,
12 momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso;
mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka
kapena kudzutsidwa ku tulo tawo.
13 “Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda
ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita!
Achikhala munandiyikira nthawi,
kuti pambuyo pake mundikumbukirenso.
14 Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo?
Masiku anga onse a moyo wovutikawu
ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa.
15 Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani;
inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu.
16 Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe anga
koma simudzalondola tchimo langa.
17 Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba;
inu mudzaphimba tchimo langa.
18 “Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekasweka
ndipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake,
19 monganso madzi oyenda amaperesera miyala
ndipo madzi othamanga amakokololera nthaka,
momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu.
20 Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu;
Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali.
21 Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo;
akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo.
22 Iye amangomva zowawa za mʼthupi lake
ndipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.”
Mawu a Elifazi
15 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
2 “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere,
kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa?
3 Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake,
kapena kuyankhula mawu opanda phindu?
4 Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu
ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu.
5 Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo;
ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali.
6 Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga;
milomo yakoyo ikukutsutsa.
7 “Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa?
Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe?
8 Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu?
Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha?
9 Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa?
Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe?
10 Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu,
anthu amvulazakale kupambana abambo ako.
11 Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira,
mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe?
12 Chifukwa chiyani ukupsa mtima,
ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako,
13 moti ukupsera mtima Mulungu
ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako?
14 “Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima
kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima?
15 Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake,
ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake,
16 nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota,
amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi.
17 “Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera;
ndilole ndikuwuze zimene ndaziona,
18 zimene anandiphunzitsa anthu anzeru,
sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo.
19 (Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa
pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo).
20 Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake,
munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse.
21 Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake,
pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo.
22 Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa;
iyeyo ndi woyenera kuphedwa.
23 Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya;
amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi.
24 Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri;
zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo,
25 chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu
ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse.
26 Amapita mwa mwano kukalimbana naye
atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba.
27 “Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa
ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri,
28 munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka
ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu,
nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka.
29 Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa,
ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi.
30 Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo;
lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake,
ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa.
31 Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe,
pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu.
32 Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane,
ndipo nthambi zake sizidzaphukanso.
33 Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse,
adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake.
34 Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala
ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu.
35 Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa;
mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”
Mawu a Yobu
16 Pamenepo Yobu anayankha kuti,
2 “Ndinamvapo zambiri monga zimenezi;
nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.
3 Kodi mawu anu ochulukawo adzatha?
Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?
4 Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu,
inuyo mukanakhala monga ndilili inemu;
Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu
ndi kukupukusirani mutu wanga.
5 Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani;
chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.
6 “Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa;
ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.
7 Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu;
mwawononga banja langa lonse.
8 Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni;
kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.
9 Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane,
amachita kulumira mano;
mdani wanga amandituzulira maso.
10 Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza;
amandimenya pa tsaya mwachipongwe
ndipo amagwirizana polimbana nane.
11 Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa
ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.
12 Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya;
anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya.
Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;
13 anthu ake oponya mauta andizungulira.
Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga
ndipo akutayira pansi ndulu yanga.
14 Akundivulaza kawirikawiri,
akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.
15 “Ndasokerera chiguduli pa thupi langa
ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.
16 Maso anga afiira ndi kulira,
ndipo zikope zanga zatupa;
17 komatu manja anga sanachite zachiwawa
ndipo pemphero langa ndi lolungama.
18 “Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga;
kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!
19 Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba;
wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.
20 Wondipembedzera ndi bwenzi langa,
pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;
21 iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu
monga munthu amadandaulira bwenzi lake.
22 “Pakuti sipapita zaka zambiri
ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.