M’Cheyne Bible Reading Plan
Ndondomeko ya Kamangidwe ka Nyumba ya Mulungu
28 Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima.
2 Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.” 3 Koma Mulungu anati kwa ine, “Usandimangire nyumba chifukwa ndiwe munthu wankhondo ndipo wakhala ukukhetsa magazi.”
4 “Komabe Yehova Mulungu wa Israeli anasankha ine pakati pa onse a banja langa kukhala mfumu ya Israeli kwamuyaya. Iye anasankha Yuda kukhala mtsogoleri, ndipo pa banja la Yuda anasankha banja langa. Pakati pa ana aamuna a abambo anga, kunamukomera Iye kundikhazika mfumu ya Aisraeli onse. 5 Pa ana anga ambiri onse amene Yehova wandipatsa, Iye wasankha mwana wanga Solomoni kuti akhale pa mpando waufumu wa ufumu wa Yehova kuti alamulire Israeli.” 6 Yehova anati kwa ine, “Solomoni mwana wako ndiye amene adzamanga nyumba yanga ndi mabwalo anga, pakuti Ine ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. 7 Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya ngati iye saleka kutsatira malamulo ndi malangizo anga, monga momwe zikuchitikira leromu.”
8 “Tsono lero ine ndikulamula inu pamaso pa Aisraeli onse ndi pa msonkhano wa Yehova, ndipo Mulungu wathu akumva: Mutsatire mosamala malamulo a Yehova Mulungu wathu, kuti dziko labwinoli likhale lanu ndi kuti mudzalipereke kwa zidzukulu zanu kukhala cholowa chawo kwamuyaya.”
9 “Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya. 10 Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.”
11 Kotero Davide anapatsa Solomoni mwana wake mapulani a khonde la Nyumba ya Mulungu, nyumba zake, mosungiramo katundu, zipinda zake zamʼmwamba, zipinda zamʼkati ndi malo a nsembe zopepesera machimo. 12 Iye anapatsa Solomoni mapulani a zonse zimene ankaziganizira za bwalo la Nyumba ya Yehova ndi zipinda zonse zozungulira, zipinda zosungiramo chuma cha Nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Yehova. 13 Davide anamulangiza za magulu a ansembe ndi Alevi ndi ntchito yonse yotumikira mʼNyumba ya Yehova, komanso za zinthu zonse zogwirira ntchito potumikira. 14 Iye anakonzeratu za kulemera kwa golide wopangira zida zonse zagolide zogwirira ntchito zosiyanasiyana, ndiponso kulemera kwa siliva wopangira zida zonse zasiliva zogwirira ntchito zosiyanasiyana: 15 kulemera kwa golide wopangira choyikapo nyale chagolide ndi nyale zake; ndiponso kulemera kwa siliva wa choyikapo nyale chilichonse ndi nyale zake, molingana ndi kagwiritsidwe ka choyikapo nyale chilichonse; 16 kulemera kwa golide wa tebulo iliyonse yoyikapo buledi wopatulika; kulemera kwa siliva wopangira matebulo asiliva; 17 muyeso wa golide woyengeka bwino wopangira mafoloko, mbale ndi zotungira; muyeso wa golide wa beseni lililonse la siliva; 18 ndiponso muyeso wa golide wabwino wopangira guwa la zofukiza. Davide anamupatsanso ndondomeko ya mapangidwe a galeta, akerubi agolide atatambasula mapiko awo kuphimba Bokosi la Chipangano la Yehova.
19 Davide anati, “Zonsezi ndalemba kuchokera kwa Yehova, ndipo Iye wachita kuti ndimvetsetse zonse za mapulaniwa.”
20 Davide anatinso kwa mwana wake Solomoni, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndipo uchite ntchitoyi. Usachite mantha kapena kutaya mtima pakuti Yehova Mulungu wanga ali nawe. Iye sadzakukhumudwitsa kapena kukusiya mpaka ntchito yonse ya Nyumba ya Mulungu itatha. 21 Magulu a ansembe ndi Alevi ndi okonzeka kugwira ntchito ya Nyumba ya Mulungu, ndipo munthu waluso aliyense wodzipereka adzakuthandiza pa ntchito yonse. Akuluakulu ndi anthu onse adzamvera chilichonse chomwe udzalamula.”
Aphunzitsi Onyenga
2 Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. 2 Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi. 3 Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira.
4 Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. 5 Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo. 6 Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu. 7 Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa. 8 (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva). 9 Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. 10 Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro.
Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba. 11 Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye. 12 Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa.
13 Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo. 14 Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa! 15 Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama. 16 Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo.
17 Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani. 18 Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa. 19 Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira. 20 Ngati anapulumuka ku zodetsa za dziko lapansi podziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, pambuyo pake nagwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zomwezo, potsiriza adzakhala oyipa kuposa mmene analili poyamba. 21 Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa. 22 Kwa iwo miyambi iyi ndi yoona, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndipo, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhunizikanso mʼmatope.”
Wolamulira Wochokera ku Betelehemu
5 Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo,
pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe.
Adzakantha ndi ndodo pa chibwano
cha wolamulira wa Israeli.
2 “Koma iwe Betelehemu Efurata,
ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda,
mwa iwe mudzatuluka
munthu amene adzalamulira Israeli,
amene chiyambi chake nʼchakalekale,
nʼchamasiku amakedzana.”
3 Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwa
mpaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire.
Ndipo abale ake onse otsalira adzabwerera
kudzakhala pamodzi ndi Aisraeli.
4 Iye adzalimbika, ndipo adzaweta nkhosa zake
mwa mphamvu ya Yehova,
mu ulemerero wa dzina la Yehova Mulungu wake.
Ndipo iwo adzakhala mu mtendere,
pakuti ukulu wake udzakhala ponseponse pa dziko lapansi.
5 Ndipo Iye adzakhala mtendere wawo.
Chipulumutso ndi Chiwonongeko
Asiriya akadzalowa mʼdziko lathu
ndi kuyamba kuthira nkhondo malo athu otetezedwa,
tidzawadzutsira abusa asanu ndi awiri,
ngakhalenso atsogoleri asanu ndi atatu.
6 Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga,
dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo.
Adzatipulumutsa kwa Asiriya
akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu
kudzatithira nkhondo.
7 Otsalira a Yakobo adzakhala
pakati pa mitundu yambiri ya anthu
ngati mame ochokera kwa Yehova,
ngati mvumbi pa udzu,
omwe sulamulidwa ndi munthu
kapena kudikira lamulo la anthu.
8 Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu,
mʼgulu la anthu a mitundu yambiri,
ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango.
Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa,
amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula,
ndipo palibe angathe kuzilanditsa.
9 Mudzagonjetsa adani anu,
ndipo adani anu onse adzawonongeka.
10 Yehova akuti,
“Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onse
ndi kuphwasula magaleta anu.
11 Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanu
ndi kugwetsa malinga anu onse.
12 Ndidzawononga ufiti wanu
ndipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula.
13 Ndidzawononga mafano anu osema
pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu;
simudzagwadiranso zinthu zopanga
ndi manja anu.
14 Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu,
ndipo ndidzawononga mizinda yanu.
15 Ndidzayilanga mwaukali ndi mokwiya
mitundu imene sinandimvere Ine.”
Yesu Mʼnyumba ya Mfarisi
14 Pa tsiku lina la Sabata, Yesu atapita kukadya ku nyumba ya Mfarisi wodziwika, Afarisi anamulonda mosamalitsa. 2 Poteropo, patsogolo pake panali munthu amene anadwala matenda otupa mimba ndi miyendo. 3 Yesu anafunsa Afarisi ndi akatswiri amalamulo kuti, “Kodi ndi zololedwa kuchiritsa pa tsiku la Sabata kapena ayi?” 4 Koma iwo sanayankhe. Tsono atamutenga munthuyo, Iye anamuchiritsa ndipo anamuwuza kuti azipita.
5 Kenaka Iye anawafunsa kuti, “Kodi ngati mmodzi mwa inu ali ndi mwana wamwamuna kapena ngʼombe imene yagwera mʼchitsime tsiku la Sabata, kodi simungamuvuwulemo tsiku lomwelo?” 6 Ndipo iwo analibe choyankha.
Kudzichepetsa ndi Kulandira Ulemu
7 Iye ataona momwe alendo amasankhira malo aulemu pa tebulo, Iye anawawuza fanizo ili: 8 “Pamene wina wakuyitanani ku phwando la ukwati, musakhale pa malo aulemu ayi, chifukwa mwina anayitananso munthu wina wolemekezeka kuposa inu. 9 Ngati zitatero, ndiye kuti munthu uja amene anakuyitani inu nonse awiri adzakuwuzani kuti, ‘Mupatseni munthu uyu malo anu.’ Pamenepo inu mudzachita manyazi, pokakhala malo wotsika. 10 Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse. 11 Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”
12 Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako. 13 Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. 14 Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”
Fanizo la Phwando Lalikulu
15 Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”
16 Yesu anayankha kuti, “Munthu wina ankakonza phwando lalikulu ndipo anayitana alendo ambiri. 17 Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’
18 “Koma onse anayamba kupereka zifukwa mofanana. Woyamba anati, ‘Ine ndangogula kumene munda, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawuone. Pepani mundikhululukire.’
19 “Wina anati, ‘Ndangogula kumene ngʼombe khumi zokoka ngolo ndipo kupita kukaziyesa. Pepani mundikhululukire.’
20 “Wina anatinso, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sinditha kubwera.’
21 “Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’
22 “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’
23 “Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze. 24 Ine ndikukuwuzani inu kuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anayitanidwa adzalawa phwandolo.’ ”
Dipo la Kutsatira Yesu
25 Gulu lalikulu la anthu linkayenda naye Yesu ndipo atatembenukira kwa iwo anati, 26 “Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. 27 Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.
28 “Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire? 29 Pakuti ngati ayika maziko ndi kulephera kutsiriza, aliyense amene adzayiona adzamuseka, 30 nanena kuti, ‘Munthu uyu anayamba kumanga koma sanathe kutsiriza.’
31 “Kapena mfumu imene ikupita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, kodi siyamba yakhala pansi ndi kulingalira ngati ingathe ndi anthu 10,000 kulimbana ndi amene akubwera ndi 20,000? 32 Ngati singathe, idzatuma nthumwi pomwe winayo ali kutali ndi kukapempha mgwirizano wamtendere. 33 Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.
34 “Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani? 35 Suyeneranso ngakhale mʼnthaka kapena kudzala la manyowa; umatayidwa kunja.
“Amene ali ndi makutu akumva, amve.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.