Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 11-12

Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli

11 Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife abale anu. Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”

Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli.

Davide Agonjetsa Yerusalemu

Davide ndi Aisraeli onse anapita ku Yerusalemu (ku Yebusi). Ayebusi amene ankakhala kumeneko anamuwuza Davide kuti, “Simulowa muno.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.

Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali.

Tsono Davide anakhazikika mu lingamo, ndipo mzindawu anawutcha Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira, kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Ndipo Yowabu anakonzanso mbali ina ya mzindawu. Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Asilikali Otchuka a Davide

10 Awa ndiye anali atsogoleri amphamvu a Davide. Iwo pamodzi ndi Aisraeli onse, anathandiza kulimbikitsa ufumu wake kuti ukwanire madera onse, monga momwe Yehova analonjezera. 11 Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide:

Yasobeamu Mhakimoni anali mkulu wa atsogoleri. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300 nthawi imodzi.

12 Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi, mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu. 13 Iye anali ndi Davide ku Pasi-Damimu pamene Afilisti anasonkhana kudzachita nkhondo. Ankhondo anathawa Afilistiwo pamalo pamene panali munda wodzaza ndi barele. 14 Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa.

15 Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu. 16 Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. 17 Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!” 18 Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. 19 Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe.

Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.

20 Abisai mʼbale wa Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300. Choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja. 21 Iye analandira ulemu woposa atatuwo. Kotero anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti iyeyo sanali mʼgulu la anthu atatu aja.

22 Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango. 23 Ndipo iye anakanthanso Mwigupto amene anali wotalika mamita awiri ndi theka. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo wofanana ndi ndodo yowombera nsalu mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe. 24 Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja. 25 Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza.

26 Ankhondo amphamvuwa anali:

Asaheli mʼbale wa Yowabu,

Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

27 Samoti Mharori,

Helezi Mpeloni.

28 Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa,

Abiezeri wa ku Anatoti,

29 Sibekai Mhusati,

Ilai Mwahohi,

30 Maharai Mnetofa,

Heledi mwana wa Baana Mnetofa,

31 Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini,

Benaya Mpiratoni,

32 Hurai wa ku zigwa za Gaasi,

Abieli Mwaribati,

33 Azimaveti Mbaharumi,

Eliyahiba Msaaliboni,

34 ana a Hasemu Mgizoni,

Yonatani mwana wa Sage Mharari,

35 Ahiamu mwana wa Sakari Mharari,

Elifali mwana wa Uri,

36 Heferi Mmekerati,

Ahiya Mpeloni,

37 Heziro wa ku Karimeli

Naara mwana wa Ezibai,

38 Yoweli mʼbale wa Natani,

Mibihari mwana wa Hagiri,

39 Zeleki Mwamoni,

Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya.

40 Ira Mwitiri,

Garebu Mwitiri,

41 Uriya Mhiti,

Zabadi mwana wa Ahilai,

42 Adina mwana wa Siza Mrubeni, amene anali mtsogoleri wa Arubeni ndi anthu makumi atatu pamodzi naye,

43 Hanani mwana wa Maaka,

Yehosafati Mmitini,

44 Uziya Mwasiterati,

Sama ndi Yeiyeli ana a Hotamu Mwaroeri,

45 Yediaeli mwana wa Simiri,

ndi Yoha Mtizi mʼbale wake,

46 Elieli Mhavati,

Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu,

Itima Mmowabu,

47 Elieli, Obedi ndi Yaasieli Mmeobai.

Ankhondo Amene Anali ndi Davide, Sauli Asanafe

12 Nawa anthu amene anabwera kwa Davide ali ku Zikilagi pamene iye anathamangitsidwa ndi Sauli mwana wa Kisi (iwowo anali mʼgulu la asilikali amene ankamuthandiza pa nkhondo. Iwo anali ndi mauta ndipo amadziwa kuponya mivi komanso miyala, ndipo amatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwo anali abale ake a Sauli ochokera ku fuko la Benjamini.

Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri ndi Yowasi ana a Semaya wa ku Gibeya; Yezieli ndi Peleti ana a Azimaveti; Beraka, Yehu wa ku Anatoti, ndi Isimaiya wa ku Gibiyoni, munthu wamphamvu mʼgulu la anthu makumi atatu aja, yemwenso anali mtsogoleri wawo; Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gederi, Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya ndi Sefatiya Mharufi; Elikana, Isiya, Azareli, Yowezeri ndi Yasobeamu a ku banja la Kora; ndi Yowela ndi Zebadiya ana a Yerohamu wa ku Gedori.

Asilikali ena a fuko la Gadi anathawira kwa Davide ku linga lake ku chipululu. Iwo anali asilikali olimba mtima, okonzekera nkhondo ndipo amadziwa kugwiritsa ntchito chishango ndi mkondo. Iwowo anali woopsa ngati mikango ndipo anali aliwiro ngati ngoma zamʼmapiri.

Mtsogoleri wawo anali Ezeri,

wotsatana naye anali Obadiya, wachitatu anali Eliabu,

10 wachinayi anali Misimana, Yeremiya anali wachisanu,

11 wachisanu ndi chimodzi anali Atai, Elieli anali wachisanu ndi chiwiri,

12 wachisanu ndi chitatu anali Yohanani, Elizabadi anali wachisanu ndi chinayi,

13 wakhumi anali Yeremiya ndipo Makibanai anali wa 11.

14 Anthu a fuko la Gadi amenewa anali atsogoleri; angʼonoangʼono amalamulira anthu 100 pamene akuluakulu amalamulira anthu 1,000. 15 Awa ndi amene anawoloka Yorodani mwezi woyamba pamene mtsinje unali utasefukira mbali zonse, ndipo anathamangitsa aliyense amene amakhala mʼchigwa, mbali ya kumadzulo ndi kummawa.

16 Anthu ena a fuko la Benjamini ndi ena ochokera ku Yuda anabweranso kwa Davide pamene anali ku linga lake. 17 Davide anapita kukakumana nawo ndipo anati, “Ngati mwabwera kwa ine mwamtendere, kuti mundithandize, ndakonzeka kugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, ngakhale kuti sindinalakwe, Mulungu wa makolo anthu aone izi ndipo akuweruzeni.”

18 Kenaka Mzimu anabwera pa Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja ndipo anati:

“Inu Davide, ife ndife anu!
    Tili nanu limodzi, inu mwana wa Yese!
Kupambana, Kupambana kwa inu,
    ndiponso kupambana kukhale kwa iwo amene akukuthandizani
        pakuti Mulungu wanu adzakuthandizani.”

Kotero Davide anawalandira ndipo anawayika kukhala atsogoleri a magulu ake a ankhondo.

19 Anthu ena a fuko la Manase anathawira kwa Davide pamene anapita ndi Afilisti kukamenyana ndi Sauli. (Iye ndi anthu ake sanathandize Afilisti chifukwa, atsogoleri awo atakambirana, anamubweza Davide. Iwo anati, “Ife tidzawonongedwa ngati uyu adzabwerera kwa mbuye wake Sauli).” 20 Davide atapita ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase amene anathawira kwa iye anali awa: Adina, Yozabadi, Yediaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai; atsogoleri a magulu a anthu 1,000 a ku Manase. 21 Iwowa anathandiza Davide kulimbana ndi magulu achifwamba, pakuti onsewa anali asilikali olimba mtima ndipo anali atsogoleri mʼgulu lake la ankhondo. 22 Tsiku ndi tsiku anthu amabwera kudzathandiza Davide, mpaka anakhala ndi gulu lalikulu la ankhondo, ngati gulu la ankhondo a Mulungu.

Enanso Abwera kwa Davide ku Hebroni

23 Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene anabwera kwa Davide ku Hebroni kudzapereka ufumu wa Sauli kwa iye, monga momwe ananenera Yehova:

24 Anthu a fuko la Yuda onyamula chishango ndi mkondo analipo 6,800;

25 Anthu a fuko la Simeoni, asilikali okonzekera nkhondo analipo 7,100;

26 Anthu a fuko la Levi analipo 4,600, 27 mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aaroni anabweranso ndi anthu 3,700, 28 ndi Zadoki, mnyamata wankhondo wolimba mtima, anabwera ndi akuluakulu 22 ochokera mʼbanja lake;

29 Anthu a fuko la Benjamini, abale ake a Sauli analipo 3,000 ndipo ambiri anali ndi Sauli ku nyumba yake pa nthawiyi;

30 Anthu a fuko la Efereimu, asilikali olimba mtima, otchuka pa mabanja awo analipo 20,800;

31 Anthu a fuko latheka la Manase amene anawayitana kuti adzakhazikitse nawo ufumu wa Davide analipo 18,000;

32 Anthu a fuko la Isakara amene ankazindikira nthawi ndipo amadziwa zimene Israeli ankayenera kuchita, analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi abale awo onse amene amawatsogolera.

33 Anthu a fuko la Zebuloni, analipo 5,000. Iwowa anali asilikali odziwa bwino nkhondo, okhala ndi zida za mtundu uliwonse, okonzekera kudzathandiza Davide ndi mtima umodzi.

34 Anthu a fuko la Nafutali, analipo atsogoleri 1,000 pamodzi ndi anthu 37,000 onyamula zishango ndi mikondo;

35 Anthu a fuko la Dani, okonzekera nkhondo analipo 28,600.

36 Anthu a fuko la Aseri, asilikali odziwa bwino nkhondo, okonzekeradi nkhondo analipo 40,000;

37 Ndipo kuchokera kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase, amene anali ndi zida za mtundu uliwonse analipo 120,000.

38 Onsewa anali anthu odziwa kumenya nkhondo amene anadzipereka ku magulu awo. Iwo anabwera ku Hebroni ali otsimikiza kudzamuyika Davide kukhala mfumu ya Aisraeli. Aisraeli ena onse anali ndi mtima umodzinso womuyika Davide kukhala mfumu. 39 Anthuwa anakhala ndi Davide masiku atatu akudya ndi kumwa pakuti mabanja awo anawapatsa zakudya. 40 Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli.

Ahebri 13

Mawu Achilimbikitso Otsiriza

13 Pitirizani kukondana monga abale. Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa. Muzikumbukira amene ali mʼndende ngati kuti inunso ndi omangidwa, ndiponso amene akusautsidwa ngati inunso mukuvutika.

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga. Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati,

“Sadzakusiyani,
    kapena kukutayani konse.”

Kotero ife tikunena molimba mtima kuti,

“Ambuye ndiye mthandizi wanga;
    sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?”

Muzikumbukira atsogoleri anu, amene amakulalikirani Mawu a Mulungu. Ganizirani zamoyo wawo ndipo tsatirani chikhulupiriro chawo. Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse.

Musasocheretsedwe ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo. Nʼkwabwino kuti mitima yathu ilimbikitsidwe ndi chisomo osati ndi chakudya, chimene sichipindulitsa iwo amene amachidya. 10 Ife tili ndi guwa lansembe, ndipo ansembe otumikira mʼtenti cha Ayuda, saloledwa kudya zochokera pamenepo.

11 Mkulu wa ansembe amatenga magazi kukapereka nsembe chifukwa cha machimo, koma nyamayo imawotchedwa kunja kwa msasa. 12 Nʼchifukwa chakenso Yesu anafera kunja kwa mzinda kuti ayeretse anthu ake kudzera mʼmagazi ake. 13 Tiyeni tsono, tipite kwa iye kunja kwa msasa, titasenza chitonzo chake. 14 Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera.

15 Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake. 16 Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere. 17 Muzimvera atsogoleri anu ndi kugonjera ulamuliro wawo, iwo amakuyangʼanirani monga anthu amene adzayenera kufotokoza za ntchito yawo pamaso pa Mulungu. Muziwamvera kuti agwire ntchito yawo ndi chimwemwe osati molemedwa pakuti izi sizingakupindulireni.

18 Mutipempherere ifenso. Pakuti tikutsimikiza kuti tili ndi chikumbumtima changwiro ndipo timafuna kuchita zinthu zonse mwaulemu. 19 Ine ndikukupemphani kuti mundipempherere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga.

20 Mulungu wamtendere, amene kudzera mʼmagazi a pangano lamuyaya anaukitsa Ambuye athu Yesu kwa akufa, amene ndi Mʼbusa wamkulu, 21 akupatseni chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake ndipo Mulungu achite mwa ife, chimene chingamukomere kudzera mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ku nthawi zanthawi, Ameni.

22 Ndikukupemphani abale kuti mulandire mawu anga achilimbikitso, pakuti ndakulemberani mwachidule.

23 Ine ndikufuna kuti inu mudziwe kuti mʼbale wathu Timoteyo wamasulidwa. Ngati iye angafike msanga ndibwera naye kudzakuonani.

24 Mupereke moni kwa atsogoleri anu onse ndiponso kwa anthu onse a Mulungu. Abale ochokera ku Italiya akupereka moni.

25 Chisomo chikhale ndi inu nonse.

Amosi 7

Dzombe, Moto ndi Chingwe Chowongolera Khoma

Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”

Kotero Yehova anakhululuka.

Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.”

Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko. Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”

Kotero Yehova anakhululuka.

Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.”

Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma. Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?”

Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.”

Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso.

“Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa
    ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja;
    ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.”

Amosi ndi Amaziya

10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo. 11 Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi:

“ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga,
    ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo,
    kutali ndi dziko lake.’ ”

12 Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa. 13 Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.”

14 Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’ 16 Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti,

“ ‘Usanenere zotsutsa Israeli,
    ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”

17 “Tsono zimene akunena Yehova ndi izi:

“ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu,
    ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga.
Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa,
    ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu.
Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,
    kutali ndi dziko lake.’ ”

Luka 2

Kubadwa kwa Yesu

Mʼmasiku amenewo Kaisara Augusto anapereka lamulo kuti kalembera achitike mʼdziko lonse la Aroma. (Uyu ndi kalembera woyamba amene anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya). Ndipo aliyense anapita ku mzinda wa kwawo kukalembetsa.

Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide. Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera. Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo.

Abusa ndi Angelo

Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku. Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha. 10 Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse. 11 Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye. 12 Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.”

13 Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati,

14 “Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba,
    ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.”

15 Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”

16 Ndipo iwo anafulumira nyamuka nakapeza Mariya ndi Yosefe ndi mwana wakhanda, amene anagona modyera ngʼombe. 17 Pamene anamuona Iye, iwo anafotokoza zomwe anawuzidwa za mwanayo, 18 ndipo onse amene anamva zimene abusawa ananena anadabwa. 19 Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira. 20 Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja.

Yesu Aperekedwa mʼNyumba ya Mulungu

21 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe.

22 Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. 23 (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”), 24 ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.”

25 Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. 26 Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye. 27 Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo, 28 Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati:

29 “Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza,
    tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere.
30 Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu,
31     chimene Inu munakonza pamaso pa anthu onse,
32 kuwala kowunikira anthu a mitundu ina
    ndi kwa ulemerero kwa anthu anu Aisraeli.”

33 Abambo ndi amayi a Mwanayo anadabwa chifukwa cha zimene zinanenedwa za Iye. 34 Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: “Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho, 35 kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso.”

36 Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa, 37 ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera. 38 Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.

39 Yosefe ndi Mariya atachita zonse zimene zinkafunikira ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mudzi wa Nazareti. 40 Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Yesu mʼNyumba ya Mulungu

41 Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. 42 Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. 43 Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi. 44 Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo. 45 Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna. 46 Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47 Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. 48 Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, “Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe.”

49 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?” 50 Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.

51 Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.

52 Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.