Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 13-14

Abweretsanso Bokosi la Chipangano

13 Davide anakambirana ndi akuluakulu ake, atsogoleri a anthu 1,000 ndi atsogoleri a anthu 100. Ndipo anati kwa gulu lonse la Israeli, “Ngati kukukomerani komanso ngati chili chifuniro cha Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kulikonse kumene kuli abale athu ena onse ku dziko lonse la Israeli ndiponso kwa ansembe ndi Alevi amene ali nawo mʼmidzi yawo ndi madera odyetsera ziweto, kuti abwere adzakhale nafe. Tiyeni tibweretsenso Bokosi la Mulungu wathu kuno kwathu, pakuti nthawi ya Sauli sitinafunse za bokosili.” Gulu lonse linavomereza izi, pakuti anthu onse anaona kuti kunali kofunika kutero.

Kotero Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse, kuchokera ku mtsinje wa Sihori ku Igupto mpaka ku Lebo Hamati, kuti abweretse Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriati-Yearimu. Davide pamodzi ndi Aisraeli onse anapita ku Baalahi (Kiriati-Yearimu) ku Yuda kukatenga Bokosi la Yehova Mulungu, amene amakhala pakati pa akerubi. Limeneli ndiye Bokosi la Chipangano lomwe limadziwika ndi Dzina lake.

Iwo anachotsa Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu pa ngolo yatsopano. Uza ndi Ahiyo ndiwo ankayendetsa ngoloyo. Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Mulungu, poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.

Atafika pa malo opunthira tirigu ku Kidoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire bokosilo, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. 10 Yehova anapsera mtima Uza ndipo anamukantha chifukwa chogwira bokosilo. Choncho iyeyo anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.

11 Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.

12 Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Mulungu ndipo anafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu lingafike bwanji kwathu?” 13 Iye sanapitenso nalo Bokosi la Mulungu ku Mzinda wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. 14 Ndipo Bokosi la Mulungu linakhala mʼbanja la Obedi-Edomu mʼnyumba mwake kwa miyezi itatu ndipo Yehova anadalitsa nyumba yake ndi chilichonse chimene anali nacho.

Nyumba ya Davide ndi Banja Lake

14 Hiramu mfumu ya ku Turo inatumiza amithenga kwa Davide pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri a miyala ndi amisiri a matabwa kuti adzamumangire nyumba yaufumu. Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza kwambiri ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli.

Davide anakwatira akazi ena ambiri ku Yerusalemu ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri. Mayina a ana amene anaberekera ku Yerusalemu anali awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni, Ibihari, Elisua, Elipeleti, Noga, Nefegi, Yafiya, Elisama, Beeliada ndi Elifeleti.

Davide Agonjetsa Afilisti

Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya dziko lonse la Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anapita kukakumana nawo. Ndipo Afilisti anabwera ndi kulanda zinthu mʼChigwa cha Refaimu. 10 Davide anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?”

Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka mʼmanja mwako.”

11 Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Mulungu waphwanya adani anga ine ndikuona.” Motero anawatcha malowa Baala Perazimu. 12 Afilisti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide analamulira kuti itenthedwe ndi moto.

13 Nthawi inanso Afilisti anadzalanda katundu mu Chigwamo. 14 Choncho Davide anafunsa Mulungu ndipo Mulunguyo anayankha kuti, “Usapite molunjika, koma uzungulire kumbuyo kwawo. Ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku. 15 Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukapite kukamenyana nawo, chifukwa izi zikasonyeza kuti Mulungu ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.” 16 Kotero Davide anachita zimene Mulungu anamulamulira ndipo anakantha ankhondo a Afilisti njira yonse kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri.

17 Choncho mbiri ya Davide inafalikira dziko lonse, ndipo Yehova anachititsa kuti mayiko ena azimuopa.

Yakobo 1

Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu,

kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana.

Landirani moni.

Masautso ndi Mayesero

Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse. Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita.

Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. 10 Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. 11 Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.

12 Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

13 Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. 14 Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. 15 Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.

16 Musanyengedwe abale anga okondedwa. 17 Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. 18 Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.

Kumva ndi Kuchita

19 Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. 20 Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. 21 Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.

22 Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. 23 Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. 24 Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera. 25 Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.

26 Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe. 27 Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.

Amosi 8

Dengu la Zipatso Zakupsa

Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa. Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?”

Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.”

Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.

“Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!”

Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa
    ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu.

Mumanena kuti,

“Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti
    kuti tigulitse zinthu?
Ndipo tsiku la Sabata litha liti
    kuti tigulitse tirigu,
kuti tichepetse miyeso,
    kukweza mitengo
    kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,
tigule osauka ndi ndalama zasiliva
    ndi osowa powapatsa nsapato,
    tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”

Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita.

“Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi,
    ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni?
Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo;
    lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata
    ngati mtsinje wa ku Igupto.

“Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti,

“Ndidzadetsa dzuwa masana
    ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo.
10 Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni
    ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro.
Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu
    ndi kumeta mipala mitu yanu.
Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo,
    ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.

11 “Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti,
    “Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse;
osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi,
    koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
12 Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina.
    Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa,
kufunafuna mawu a Yehova,
    koma sadzawapeza.

13 “Tsiku limenelo

“anamwali okongola ndi anyamata amphamvu
    adzakomoka ndi ludzu.
14 Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya,
    kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’
    kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’
Iwowo adzagwa
    ndipo sadzadzukanso.”

Luka 3

Yohane Mʼbatizi Akonza Njira

Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene. Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu. Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti:

“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
konzani njira ya Ambuye,
    wongolani njira zake.
Chigwa chilichonse chidzadzazidwa
    ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa,
misewu yokhotakhota idzawongoledwa,
    ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.
Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”

Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera? Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana. Nkhwangwa ili kale pa muzu wamitengo, ndipo mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa pa moto.”

10 Gulu la anthuwo linafunsa kuti, “Nanga tsono tichite chiyani?”

11 Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”

12 Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?”

13 Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.” 14 Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”

15 Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu. 16 Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto. 17 Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.” 18 Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.

19 Koma pamene Yohane anadzudzula Herode wolamulirayo chifukwa chokwatira Herodia, mkazi wa mʼbale wake, ndi zoyipa zina zonse anazichita, 20 Herode anawonjezanso choyipa ichi pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.

Ubatizo wa Yesu

21 Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. 22 Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”

Makolo a Yesu

23 Ndipo Yesu anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ntchito yake. Monga mmene anthu ankaganizira, Iyeyo anali mwana wa Yosefe,

mwana wa Heli, 24 mwana wa Matate,

mwana wa Levi, mwana wa Meliki,

mwana wa Yaneyi, mwana wa Yosefe

25 mwana wa Matati, mwana wa Amosi,

mwana wa Naomi, mwana wa Esli,

mwana wa Nagai, 26 mwana wa Maati,

mwana wa Matatiyo, mwana wa Simeoni,

mwana wa Yosefe, mwana wa Yoda

27 mwana wa Yohanani, mwana wa Resa,

mwana wa Zerubabeli, mwana wa Salatieli,

mwana wa Neri, 28 mwana wa Meliki,

mwana wa Adi, mwana wa Kosamu,

mwana wa Elmadama, mwana wa Ere,

29 mwana wa Jose, mwana wa Eliezara,

mwana wa Yorimu, mwana wa Matati,

mwana wa Levi, 30 mwana wa Simeoni,

mwana wa Yuda, mwana wa Yosefe,

mwana wa Yonamu, mwana wa Eliakimu,

31 mwana wa Meleya, mwana wa Mena,

mwana wa Matata, mwana wa Natani,

mwana wa Davide, 32 mwana wa Yese,

mwana wa Obedi, mwana wa Bowazi,

mwana wa Salimoni, mwana wa Naasoni,

33 mwana wa Aminadabu, mwana wa Arni,

mwana wa Hezronu, mwana wa Perezi,

mwana wa Yuda, 34 mwana wa Yakobo,

mwana wa Isake, mwana wa Abrahamu,

mwana wa Tera, mwana wa Nakoro,

35 mwana wa Serugi, mwana wa Reu,

mwana wa Pelegi, mwana wa Eberi,

mwana wa Sela, 36 mwana wa Kainane,

mwana wa Arfaksadi, mwana wa Semu,

mwana wa Nowa, mwana wa Lameki,

37 mwana wa Metusela, mwana wa Enoki,

mwana wa Yaredi mwana wa Malaleeli,

mwana wa Kainane, 38 mwana wa Enosi,

mwana wa Seti,

mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.