M’Cheyne Bible Reading Plan
Davide Achita Nkhondo ndi Aamoni
19 Patapita nthawi Nahasi mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 2 Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake.
Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni kudzamupepesa, 3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” 4 Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anawameta ndi kudula zovala zawo pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera ndipo anawabweza kwawo.
5 Munthu wina atafika ndi kufotokozera Davide za anthuwo, iye anatuma amithenga kukakumana nawo, chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”
6 Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, Hanuni ndi Aamoni anatumiza siliva wolemera makilogalamu 34,000 kuti akalipirire magaleta ndi okwerapo ake a ku Mesopotamiya; Aramu-Maaka ndi Zoba. 7 Iwo analipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi ankhondo ake. Amenewa anabwera ndi kudzamanga misasa yawo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni anabwera kuchokera ku mizinda yawo ndipo anapita kukachita nkhondo.
8 Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. 9 Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene mafumu amene anabwera nawo anali kwa wokha, ku malo wopanda mitengo.
10 Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake; iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. 11 Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. 12 Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse; koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. 13 Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.”
14 Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. 15 Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai mʼbale wake ndi kulowa mu mzinda. Motero Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.
16 Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, pamodzi ndi mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezeri, Sofaki akuwatsogolera.
17 Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani. Iyeyo anapita kukakumana nawo ndipo anakhala mʼmizere yankhondo moyangʼanana ndipo iwo anamenyana naye. 18 Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 7,000 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Iye anaphanso Sofaki, mtsogoleri wawo wankhondo.
19 Mafumu amene ali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anachita mtendere ndi Davide ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake.
Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.
Davide Alanda Raba
20 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Yowabu anatsogolera gulu la ankhondo. Iye anawononga Aamoni, kenaka anapita ku mzinda wa Raba ndipo anawuzungulira, koma Davide anatsala ku Yerusalemu. Yowabu anathira nkhondo mzinda wa Raba ndipo anawuwononga. 2 Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Ndipo Davide anavala chipewacho. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, 3 ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka Davide pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.
Davide Achita Nkhondo ndi Afilisti
4 Patapita nthawi, nkhondo inayambika pakati pa Aisraeli ndi Afilisti ku Gezeri. Nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Sipai, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai, ndipo Afilisti anagonja.
5 Pa nkhondo inanso ndi Afilisti, Elihanani mwana wa Yairi anapha Lahimi mʼbale wake wa Goliati Mgiti, amene mkondo wake unali ngati ndodo yowombera nsalu.
6 Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati, panali munthu wina wamtali kwambiri, wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. 7 Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha.
8 Anthu amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.
1 Ndine Petro, mtumwi wa Yesu Khristu.
Ndikulemba kalatayi kwa onse osankhidwa ndi Mulungu, alendo mʼdziko lapansi, obalalikira ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya ndi Bituniya. 2 Mulungu Atate anakusankhani, atakudziwani kuyambira pachiyambi, ndipo Mzimu Woyera wakuyeretsani kuti mumvere Yesu Khristu ndikutsukidwa ndi magazi ake.
Chisomo ndi mtendere zikhale ndi inu mochuluka.
Kuyamika Mulungu Chifukwa cha Chiyembekezo Chamoyo
3 Alemekezedwe Mulungu, Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu. Mwachifundo chake chachikulu anatibadwitsa kwatsopano, mʼchiyembekezo chamoyo pomuukitsa Yesu Khristu kwa akufa, 4 kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba. 5 Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza. 6 Zimenezi zikukondweretseni kwambiri, ngakhale tsopano, kwa kanthawi kochepa, mukumva zowawa mʼmayesero osiyanasiyana. 7 Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. 8 Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. 9 Motero mukulandira mphotho ya chikhulupiriro chanu, ndiyo chipulumutso cha moyo wanu.
10 Kunena za chipulumutso chimenechi, aneneri amene ananeneratu za chisomo chimene chimabwera kwa inu, anafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi, 11 kufuna kudziwa nthawi ndi momwe zidzachitikire zinthu zimene Mzimu wa Khristu amene ali mwa iwo ankanenera za kuvutika kwa Khristu, ndi ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake. 12 Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.
Khalani Oyera Mtima
13 Choncho konzani mtima wanu, khalani odziretsa; khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa chisomo chimene mudzapatsidwe pamene Yesu Khristu adzaonekera. 14 Monga ana omvera, musatsatenso zilakolako zoyipa zomwe munali nazo pamene munali osadziwa. 15 Koma monga amene anakuyitanani ndi woyera, inunso khalani oyera mtima mʼmakhalidwe anu wonse. 16 Pakuti, kwalembedwa kuti, “Khalani oyera mtima, chifukwa Ine ndine Woyera.”
17 Popeza mumapemphera kwa Atate amene amaweruza munthu aliyense mopanda tsankho molingana ndi zochita zake, pa nthawi imene muli alendo pa dziko lapansi khalani moopa Mulungu. 18 Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu. 19 Koma munawomboledwa ndi magazi a mtengowapatali a Khristu, Mwana Wankhosa wopanda banga kapena chilema. 20 Iye anasankhidwa lisanalengedwe dziko lapansi, koma waonetsedwa chifukwa cha inu pa nthawi ino yotsiriza. 21 Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa namupatsa ulemerero. Nʼchifukwa chake chikhulupiriro ndi chiyembekezo chanu chili mwa Mulungu.
22 Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima. 23 Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. 24 Pakuti,
“Anthu onse ali ngati udzu,
ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.
Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,
25 koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.”
Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.
Yona Apita ku Ninive
3 Ndipo Yehova anayankhula ndi Yona kachiwiri kuti, 2 “Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.”
3 Yona anamvera mawu a Yehova ndipo anapita ku Ninive. Tsono Ninive unali mzinda waukulu kwambiri; wofunika masiku atatu kuwudutsa. 4 Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.” 5 Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli.
6 Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi. 7 Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti,
“Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake:
“Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa. 8 Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa. 9 Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.”
10 Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.
Fanizo la Wofesa
8 Zitatha izi, Yesu anayendayenda kuchoka mzinda wina kupita wina ndiponso mudzi wina kupita wina, akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi awiri aja anali naye, 2 komanso akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi matenda: Mariya, wotchedwa Magadalena, amene mwa iye munatuluka ziwanda zisanu ndi ziwiri; 3 Yohana mkazi wa Kuza, woyangʼanira mʼnyumba ya Herode; Suzana; ndi ena ambiri analinso. Akazi awa ankawathandiza ndi chuma chawo.
4 Anthu ambiri ankasonkhana, ndipo pamene anthu ankabwera kwa Yesu kuchokera ku midzi, Iye anawawuza fanizo ili, 5 “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya. 6 Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi. 7 Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula. 8 Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.”
Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.”
9 Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo. 10 Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti,
“ngakhale akuona, asapenye;
ngakhale akumva, asazindikire.”
11 “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. 12 Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa. 13 Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa. 14 Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima. 15 Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.
Nyale ndi Choyikapo Chake
16 “Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala. 17 Pakuti palibe kanthu kobisika kamene sikadzawululika, ndipo palibe kanthu kophimbika kamene sikadzadziwika kapena kuonetsedwa poyera. 18 Choncho ganizirani mozama. Iye amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, iye amene alibe, ngakhale chimene akuganiza kuti ali nacho adzalandidwa.”
Amayi ndi Abale a Yesu
19 Tsopano amayi ndi abale a Yesu anabwera kudzamuona Iye, koma analephera kuti afike pafupi ndi Iye chifukwa cha gulu la anthu. 20 Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunja, akufuna kukuonani.”
21 Yesu anayankha kuti, “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.”
Yesu Aletsa Namondwe
22 Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka. 23 Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.
24 Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, “Ambuye, Ambuye, ife tikumira!”
Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. 25 Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Chikhulupiriro chanu chili kuti?”
Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye.”
Achiritsidwa Munthu Wogwidwa ndi Ziwanda
26 Iwo anawolokera ku chigawo cha Gerasa chimene chili tsidya lina la nyanja kuchokera ku Galileya. 27 Yesu ataponda pa mtunda, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda wochokera mu mzindawo. Kwa nthawi yayitali munthuyu sanavale zovala kapena kukhala mʼnyumba, koma amakhala ku manda. 28 Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, “Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!” 29 Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha.
30 Yesu anamufunsa kuti, “Dzina lako ndani?”
Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. 31 Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima.
32 Gulu lalikulu la nkhumba limadya pamenepo mʼmbali mwa phiri. Ziwandazo zinamupempha Yesu kuti azilole kuti zikalowe mu nkhumbazo ndipo Iye anazilola. 33 Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira.
34 Oweta nkhumbazo ataona zimene zinachitikazo, anathamanga ndi kukanena izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi. 35 Ndipo anthu anapita kukaona zimene zinachitika. Atafika kwa Yesu, anapeza munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja atakhala pa mapazi a Yesu, atavala ndipo ali ndi nzeru zake; ndipo iwo anachita mantha. 36 Amene anaona izi anawuza anthu mmene munthu wogwidwa ndi ziwandayo anachiritsidwira. 37 Kenaka anthu onse a ku chigawo cha Gerasa anamupempha Yesu kuti achoke kwa iwo, chifukwa anadzazidwa ndi mantha. Choncho Iye analowa mʼbwato nachoka.
38 Munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja, anapempha Yesu kuti apite nawo, koma Yesu anamubweza nati, 39 “Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye.
Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu
40 Yesu atabwerera, gulu lalikulu la anthu linamulandira, chifukwa onse ankamuyembekezera. 41 Nthawi yomweyo munthu wotchedwa Yairo, woweruza wa mu sunagoge, anabwera ndi kugwa pa mapazi a Yesu, namupempha Iye kuti apite ku nyumba kwake, 42 chifukwa mwana wake yekhayo wamkazi, kamtsikana ka zaka khumi ndi ziwiri, kanali pafupi kufa.
Pamene Yesu ankapita gulu la anthu linkamupanikiza. 43 Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa. 44 Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka.
45 Yesu anafunsa kuti, “Wandikhudza ndani?”
Onse atakana, Petro anati, “Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani.”
46 Koma Yesu anati, “Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine.”
47 Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. 48 Kenaka anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”
49 Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, “Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa.”
50 Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, “Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa.”
51 Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. 52 Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, “Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo.”
53 Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. 54 Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, “Mwana wanga, dzuka!” 55 Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya. 56 Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.