Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 22

Buku la Malamulo Lipezeka

22 Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 31. Amayi ake anali Yedida mwana wa Adaiya wochokera ku Bozikati. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.

Mʼchaka cha 18 cha ufumu wake, Mfumu Yosiya anatuma mlembi wa nyumba ya mfumu, Safani, mwana wa Azariya, mwana wa Mesulamu, ku Nyumba ya Yehova. Iye anati, “Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu. Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova. Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.”

Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga. Ndipo Safani mlembi uja, anapita nakafotokozera mfumu kuti, “Atumiki anu apereka ndalama zija zinali mʼNyumba ya Yehova kwa anthu amene akugwira ntchito ndi kuyangʼanira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova.” 10 Kenaka Safani mlembiyo, anafotokozera mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku.” Ndipo Safani analiwerenga pamaso pa mfumu.

11 Mfumu itamva mawu a mʼBuku la Malamulo, inangʼamba zovala zake. 12 Iyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Akibo mwana wa Mikaya, Safani mlembi uja ndi Asaiya mtumiki wa mfumu, kuti, 13 “Pitani mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa anthu onse a mʼdziko la Yuda, za zomwe zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu kwambiri pa ife ndipo watiyakira chifukwa makolo athu sanamvere mawu a buku ili. Iwo sanachite molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼmenemu zokhudza ife.”

14 Choncho Hilikiya wansembe, Ahikamu, Akibo, Safani ndi Asaiya anapita kukayankhula ndi Hulida, mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala zaufumu. Mneneri wamkaziyu ankakhala mu Yerusalemu, ku chigawo chachiwiri cha mzindawo.

15 Ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Kamuwuzeni munthu amene wakutumani kwa ine kuti, 16 ‘Ichi ndi chimene Yehova akunena: Taonani, ndidzabweretsa mavuto pa malo ano ndi pa anthu ake, molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga. 17 Chifukwa anthuwo andisiya Ine ndi kumafukiza lubani kwa milungu ina nandikwiyitsa ndi mafano onse amene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzayaka pa malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’ 18 Koma mfumu ya Yuda imene inakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova kayiwuzeni kuti, ‘Ichi ndi chimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena molingana ndi mawu amene unamva: 19 Chifukwa unasweka mtima ndi kudzichepetsa wekha pamaso pa Yehova, pamene unamva zomwe zinayankhulidwa zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti adzakhala otembereredwa nasanduka bwinja, ndiponso chifukwa unangʼamba zovala ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, akutero Yehova. 20 Choncho taona, Ine ndidzakutenga kupita kwa makolo ako ndipo udzayikidwa mʼmanda mwako mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene ndidzabweretse pamalo pano.’ ”

Ndipo anthu aja anabwerera nakafotokoza mawu amenewa kwa mfumu.

Ahebri 4

Mpumulo wa Anthu a Mulungu

Popeza lonjezo lakuti tidzalowe mu mpumulo umene anatilonjeza lilipobe, tiyeni tisamale kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wodzalephera kulowamo. Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira. Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti,

“Ndili wokwiya ndinalumbira kuti,
    ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’ ”

Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi. Pena pake wayankhula za tsiku lachisanu ndi chiwiri mʼmawu awa: “Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, Mulungu anapumula ku ntchito zake zonse.” Pa ndime inonso akunena za zomwezo pamene akuti, “Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.”

Popeza kwatsalabe kuti ena adzalowe mu mpumulowo, koma aja anayamba kumva Uthenga Wabwino sanalowe chifukwa cha kusamvera kwawo. Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti,

“Lero mukamva mawu ake,
    musawumitse mitima yanu.”

Ngati Yoswa akanalowetsa anthu mu mpumulo, Mulungu sakananena pambuyo pake za tsiku lina. Kotero tsono kwatsala mpumulo wa Sabata kwa anthu a Mulungu; 10 Pakuti aliyense amene analowa mu mpumulo wa Mulungu anapuma pa ntchito zake, monga momwe Mulungu anachitira. 11 Tiyeni tsono tiyesetse kulowa mu mpumulo, kuti pasapezeke wina aliyense wolephera potsatira chitsanzo chawo cha kusamvera.

12 Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima. 13 Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.

Yesu Mkulu wa Ansembe Wopambana

14 Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. 15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe. 16 Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.

Yoweli 1

Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.

Kubwera kwa Dzombe

Inu akuluakulu, imvani izi;
    mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko.
Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu,
    kapena mʼnthawi ya makolo anu?
Muwafotokozere ana anu,
    ndipo ana anuwo afotokozere ana awo,
    ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.
Chimene dzombe losamera mapiko lasiya
    dzombe lowuluka ladya;
chimene dzombe lowuluka lasiya
    dzombe lalingʼono ladya;
chimene dzombe lalingʼono lasiya
    chilimamine wadya.

Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire!
    Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo;
lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano,
    pakuti wachotsedwa pakamwa panu.
Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa,
    wamphamvu ndi wosawerengeka;
uli ndi mano a mkango,
    zibwano za mkango waukazi.
Wawononga mphesa zanga
    ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu.
Wakungunula makungwa ake
    ndi kuwataya,
    kusiya nthambi zake zili mbee.

Lirani ngati namwali wovala chiguduli,
    chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.
Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
    sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova.
Ansembe akulira,
    amene amatumikira pamaso pa Yehova.
10 Minda yaguga,
    nthaka yauma;
tirigu wawonongeka,
    vinyo watsopano watha,
    mitengo ya mafuta yauma.
11 Khalani ndi nkhawa, inu alimi,
    lirani mofuwula inu alimi a mphesa;
imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele,
    pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.
12 Mpesa wauma
    ndipo mtengo wamkuyu wafota;
makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi,
    mitengo yonse ya mʼmunda yauma.
Ndithudi chimwemwe cha anthu
    chatheratu.

Mulungu Ayitana Anthu kuti Atembenuke

13 Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani;
    lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe.
Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse,
    inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga;
pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
    sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.
14 Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya,
    itanani msonkhano wopatulika.
Sonkhanitsani akuluakulu
    ndi anthu onse okhala mʼdziko
ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu
    ndipo alirire Yehova.

15 Kalanga ine tsikulo!
    Pakuti tsiku la Yehova layandikira;
    lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.

16 Kodi chakudya chathu sichachotsedwa
    ife tikuona?
Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu
    simulibe chimwemwe ndi chisangalalo?
17 Mbewu zikunyala
    poti pansi ndi powuma.
Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka;
    nkhokwe zapasuka
    popeza tirigu wauma.
18 Taonani mmene zikulirira ziweto;
    ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku
chifukwa zilibe msipu;
    ngakhalenso nkhosa zikusauka.

19 Kwa Inu Yehova ndilirira,
    pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo,
    malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.
20 Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu;
    timitsinje tonse taphwa
    ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.

Masalimo 140-141

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

140 Landitseni Yehova kwa anthu oyipa;
    tetezeni kwa anthu ankhanza,
amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa
    ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.
Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka;
    pa milomo yawo pali ululu wa mamba.
            Sela

Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa;
    tchinjirizeni kwa anthu ankhanza
    amene amakonza zokola mapazi anga.
Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika;
    iwo atchera zingwe za maukonde awo
    ndipo anditchera misampha pa njira yanga.
            Sela

Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
    Imvani kupempha kwanga Yehova.
Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu,
    mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.
Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova;
    musalole kuti zokonza zawo zitheke,
    mwina iwo adzayamba kunyada.
            Sela

Mitu ya amene andizungulira
    iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.
10 Makala amoto agwere pa iwo;
    aponyedwe pa moto,
    mʼmaenje amatope, asatulukemonso.
11 Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko;
    choyipa chilondole anthu ankhanza.

12 Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka,
    ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.
13 Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu,
    ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.

Salimo la Davide.

141 Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine.
    Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.
Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani;
    kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.

Yehova ikani mlonda pakamwa panga;
    londerani khomo la pa milomo yanga.
Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa;
    kuchita ntchito zonyansa
pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa;
    musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.

Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo;
    andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga.
    Mutu wanga sudzakana zimenezi.

Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.
    Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri,
    ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.
Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza,
    ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.”

Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse;
    ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.
Mundipulumutse ku misampha imene anditchera,
    ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.
10 Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo,
    mpaka ine nditadutsa mwamtendere.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.