Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 21

Manase Mfumu ya Yuda

21 Manase anakhala mfumu ali ndi zaka khumi ndi ziwiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 55. Amayi ake anali Hefiziba. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira mchitidwe wonyansa wa mitundu imene Yehova anayipirikitsa pofika Aisraeli. Iyetu anamanganso malo opembedzera mafano amene Hezekiya abambo ake anawawononga. Anamangira Baala maguwa a nsembe ndi mtengo wa fano la Asera monga anachitira Ahabu mfumu ya Israeli ndipo ankapembedza zolengedwa zonse zamlengalenga. Anamanga maguwa ansembewa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Mu Yerusalemu ndidzayikamo Dzina langa.” Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova, Manase anamangamo maguwa opembedzerapo zinthu zamlengalenga. Iye anapsereza mwana wake pa moto ngati nsembe, ankachita za matsenga, ankawombeza mawula, ankapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndiponso ankapembedza mizimu. Iyeyo anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova ndipo anakwiyitsa Yehovayo.

Iye anatenga fano losema la Asera limene analipanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Yehova, Nyumba imene Yehova ananena kwa Davide ndi mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba iyi ndi mu Yerusalemu ndiwo malo amene ndasankha pakati pa mafuko onse a Aisraeli kuyikamo Dzina langa kwamuyaya. Sindidzalola kuti Aisraeli achotsedwe mʼdziko lawo limene ndinapatsa makolo awo ngati iwowo adzasamala kuchita zinthu zonse zimene ndinawalamula ndi kusunga malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anawapatsa.” Koma anthu sanamvere. Manase anawasocheretsa, kotero kuti anachita zoyipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Yehova anawawononga pamene Aisraeli ankafika.

10 Yehova anayankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri kuti, 11 “Manase mfumu ya Yuda wachita machimo onyansawa ndipo wachita zoyipa kupambana Aamori amene analipo kale iye asanabadwe ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda ndi mafano ake. 12 Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru. 13 Ndidzalanga Yerusalemu ndi Yuda pogwiritsa ntchito muyeso umene ndinalangira Samariya ndi Ahabu pamodzi ndi nyumba yake. Ndidzayeretsa Yerusalemu monga mmene munthu amachitira popukuta mbale ndipo atayipukuta amayivundikira pansi. 14 Ndidzawataya anthu otsala amene ndi cholowa changa ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Adzachotsedwa ndipo adaniwo adzawalanda zinthu zonse 15 chifukwa anachita zoyipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuchokera tsiku limene makolo awo anatuluka mu Igupto mpaka lero lino.’ ”

16 Kuwonjezera apo, Manase anakhetsa kwambiri magazi a anthu osalakwa mpaka magaziwo kuyenderera mu Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina, kuphatikiza pa kuchimwitsa Yuda, kotero kuti anthu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.

17 Ntchito zina za Manase ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 18 Manase anagona ndi makolo ake ndipo anayikidwa mʼmanda mʼmunda wa Uza, ku nyumba yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Amoni Mfumu ya Yuda

19 Amoni anakhala mfumu ali ndi zaka 22 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka ziwiri. Amayi ake anali Mesulemeti mwana wa Haruzi, wochokera ku Yotiba. 20 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Manase abambo ake. 21 Anatsatira makhalidwe onse a abambo ake. Ankapembedza mafano amene abambo akewo ankawapembedza ndipo ankawagwadira. 22 Iyeyo anasiya Yehova Mulungu wa makolo ake ndipo sanayende mʼnjira ya Yehova.

23 Nduna za Amoni zinamuchita chiwembu ndipo zinamupha mʼnyumba yake. 24 Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anachitira chiwembu Mfumu Amoni, nayika Yosiya mwana wake kukhala mfumu mʼmalo mwake.

25 Ntchito zina za Amoni ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 26 Iye anayikidwa mʼmanda ake mʼmunda wa Uza. Ndipo Yosiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Ahebri 3

Yesu ndi Wamkulu Kuposa Mose

Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza. Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu. Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo. Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu. Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo. Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.

Chenjezo pa Kusakhulupirira

Tsono monga Mzimu Woyera akuti,

“Lero mukamva mawu ake,
    musawumitse mitima yanu
ngati munachitira pamene munawukira,
    pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.
Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa,
    ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita.
10 Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo,
    ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera,
    ndipo iwo sadziwa njira zanga.’
11 Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti,
    ‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ”

12 Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo. 13 Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo. 14 Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi. 15 Monga kunanenedwa kuti,

“Lero ngati mumva mawu ake,
    musawumitse mitima yanu
    ngati momwe munachitira pamene munawukira.”

16 Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto? 17 Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja? 18 Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja. 19 Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.

Hoseya 14

Kulapa Kubweretsa Madalitso

14 Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.
    Machimo anu ndi amene akugwetsani!
Bweretsani zopempha zanu
    ndipo bwererani kwa Yehova.
Munene kwa Iye kuti,
    “Tikhululukireni machimo athu onse
ndi kutilandira mokoma mtima,
    kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
Asiriya sangatipulumutse;
    ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,
sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’
    kwa zimene manja athu omwe anazipanga,
    pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”

Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo
    ndipo ndidzawakonda mwaufulu
    pakuti ndaleka kuwakwiyira.
Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli
    Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.
Adzazika mizu yake pansi
    ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
    mphukira zake zidzakula.
Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,
    kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.
    Iye adzakula bwino ngati tirigu.
Adzachita maluwa ngati mphesa
    ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.
Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?
    Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.
Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;
    zipatso zako zimachokera kwa Ine.”

Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.
    Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.
Njira za Yehova ndi zolungama;
    anthu olungama amayenda mʼmenemo,
    koma anthu owukira amapunthwamo.

Masalimo 139

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

139 Inu Yehova, mwandisanthula
    ndipo mukundidziwa.
Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;
    mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga;
    mumadziwa njira zanga zonse.
Mawu asanatuluke pa lilime langa
    mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.

Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe;
    mwasanjika dzanja lanu pa ine.
Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga,
    ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.

Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu?
    Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu?
Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko;
    ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko.
Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa,
    ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja,
10 kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,
    dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.

11 Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu
    ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”
12 komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu;
    usiku udzawala ngati masana,
    pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu.

13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
    munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
    ntchito zanu ndi zodabwitsa,
    zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
    pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
    Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
    asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
    ndi zosawerengeka ndithu!
18 Ndikanaziwerenga,
    zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
    pamene ndadzuka, ndili nanube.

19 Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu!
    Chokereni inu anthu owononga anzanu!
20 Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa;
    adani anu amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.
21 Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova?
    Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani?
22 Ndimadana nawo kwathunthu;
    ndi adani anga.

23 Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga;
    Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
24 Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine,
    ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.