Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 20

Kudwala kwa Hezekiya

20 Masiku amenewo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti: Konza nyumba yako chifukwa umwalira ndipo suchira.”

Hezekiya anatembenuka nayangʼana ku khoma ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri.

Yesaya asanatuluke mʼbwalo lapakati, Yehova anayankhula kuti, “Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova. Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”

Pamenepo Yesaya anati, “Konzani phala lankhuyu.” Iwo anakonza phalalo nalipaka pa chithupsacho ndipo Hezekiya anachira.

Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?”

Yesaya anayankha kuti, “Chizindikiro cha Yehova chosonyeza kuti Iye adzachita chimene walonjeza ndi ichi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?”

10 Hezekiya anati, “Nʼchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, kulekana nʼkuti chithunzithunzicho chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi.”

11 Pamenepo mneneri Yesaya anapemphera kwa Yehova ndipo Yehova anachititsa kuti chithunzithunzi chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi anamanga.

Akazembe Ochokera ku Babuloni

12 Pa nthawi imeneyo Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babuloni anatumiza amithenga kwa Hezekiya kukapereka makalata ndi mphatso, chifukwa nʼkuti atamva za kudwala kwa Hezekiyayo. 13 Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse.

14 Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?”

Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”

15 Mneneriyo anafunsa kuti, “Kodi anaona chiyani mʼnyumba yanu yaufumu?”

Hezekiya anayankha kuti, “Anaona china chilichonse mʼnyumba yanga yaufumu ndipo palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindinawaonetse mʼnyumba zanga zosungiramo chuma.”

16 Pamenepo Yesaya anawuza Hezekiya kuti, “Imvani zimene Yehova akunena: 17 Taonani, masiku akubwera ndithu pamene zonse za mʼnyumba yanu yaufumu, zonse zimene makolo anu anazisunga mpaka lero, zidzatengedwa kupita ku Babuloni. Palibe chimene chidzatsale, akutero Yehova. 18 Ndipo ena mwa ana anu omwe, amene mudzabereke adzatengedwa ndipo adzawasandutsa anthu ofulidwa mʼnyumba yaufumu ya mfumu ya Babuloni.”

19 Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhulawa ndi abwino. Pakuti iye ankaganiza kuti, ‘Kodi pa nthawi yanga sipadzakhala mtendere ndi bata?’ ”

20 Ntchito zina za Hezekiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 21 Hezekiya anamwalira nagona pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Ahebri 2

Kusamalira Chipulumutso

Nʼchifukwa chake, ife tiyenera kusamalira kwambiri zimene tinamva, kuopa kuti pangʼono ndi pangʼono tingazitaye. Popeza uthenga umene unayankhulidwa kudzera mwa angelo unali okhazikika ndithu, choncho aliyense amene ananyozera ndi kusamvera analandira chilango choyenera. Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira. Mulungu anachitiranso umboni pochita zizindikiro, zinthu zodabwitsa ndi zamphamvu zamitundumitundu ndi powapatsa mphatso za Mzimu Woyera monga mwachifuniro chake.

Yesu Wofanana ndi Abale ake

Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena. Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti,

“Kodi munthu ndani kuti muzimukumbukira,
    kapena mwana wa munthu kuti muzimusamalira?
Munamuchepetsa pangʼono kusiyana ndi angelo;
    munamupatsa ulemerero ndi ulemu.
    Munamupatsa ulamuliro pa zinthu zonse.”

Poyika zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, Mulungu sanasiye kanthu kamene sikali mu ulamuliro wake. Koma nthawi ino sitikuona zinthu pansi pa ulamuliro wake. Koma tikuona Yesu, amene kwa kanthawi kochepa anamuchepetsa pangʼono kwa angelo, koma tsopano wavala ulemerero ndi ulemu chifukwa anamva zowawa za imfa, kuti mwachisomo cha Mulungu, Iye afere anthu onse.

10 Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo. 11 Popeza iye amene ayeretsa ndi oyeresedwa onse ndi abanja limodzi. Nʼchifukwa chake Yesu sachita manyazi kuwatcha iwo abale ake. 12 Iye akuti,

“Ine ndidzawuza abale anga za dzina lanu.
    Ndidzakuyimbirani nyimbo zamatamando pamaso pa mpingo.”

13 Ndiponso,

“Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.”

Ndiponso Iye akuti,

“Ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Mulungu wandipatsa.”

14 Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi mnofu ndi magazi, Yesu nayenso anakhala munthu ngati iwowo kuti kudzera mu imfa yake awononge Satana amene ali ndi mphamvu yodzetsa imfa. 15 Pakuti ndi njira yokhayi imene Iye angamasule amene pa moyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa. 16 Pakuti tikudziwanso kuti sathandiza angelo, koma zidzukulu za Abrahamu. 17 Chifukwa cha zimenezi, Iye anayenera kukhala wofanana ndi abale ake pa zonse, kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika potumikira Mulungu, kuti potero achotse machimo a anthu. 18 Popeza Iye mwini anamva zowawa pamene anayesedwa, Iyeyo angathe kuthandiza amene akuyesedwanso.

Hoseya 13

Mkwiyo wa Yehova pa Israeli

13 Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera;
    anali wolemekezeka mu Israeli.
    Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.
Tsopano akunka nachimwirachimwirabe;
    akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo,
zifanizo zopangidwa mwaluso,
    zonsezo zopangidwa ndi amisiri.
Amanena za anthu awa kuti,
    “Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe
    ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa,
    ngati mame amene amakamuka msanga,
    ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu,
    ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.

Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
    amene ndinakutulutsani mu Igupto.
Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha,
    palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
Ndinakusamalira mʼchipululu,
    mʼdziko lotentha kwambiri.
Pamene ndinawadyetsa, iwo anakhuta;
    iwo atakhuta anayamba kunyada;
    ndipo anandiyiwala Ine.
Motero ndidzawalumphira ngati mkango,
    ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.
Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake,
    ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola.
Ndidzawapwepweta ngati mkango;
    chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.

“Iwe Israeli, wawonongedwa,
    chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.
10 Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse?
    Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti,
amene iwe unanena za iwo kuti,
    ‘Patseni mfumu ndi akalonga?’
11 Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima,
    ndipo ndinayichotsa mwaukali.
12 Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa,
    machimo ake alembedwa mʼbuku.
13 Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera,
    koma iye ndi mwana wopanda nzeru,
pamene nthawi yake yobadwa yafika
    iyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.

14 “Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda;
    ndidzawawombola ku imfa.
Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti?
    Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti?

“Sindidzachitanso chifundo,
15     ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake,
mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera,
    ikuwomba kuchokera ku chipululu.
Kasupe wake adzaphwa
    ndipo chitsime chake chidzawuma.
Chuma chake chonse chamtengowapatali
    chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
16 Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo,
    chifukwa anawukira Mulungu wawo.
Adzaphedwa ndi lupanga;
    ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi,
    akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”

Masalimo 137-138

137 Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira
    pamene tinakumbukira Ziyoni.
Kumeneko, pa mitengo ya misondozi
    tinapachika apangwe athu,
pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.
    Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;
    iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”

Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova
    mʼdziko lachilendo?
Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,
    dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.
Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga
    ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,
ngati sindiyesa iwe
    chimwemwe changa chachikulu.

Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita
    pa tsiku limene Yerusalemu anagonja.
Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi
    mpaka pa maziko ake!”

Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,
    wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera
    pa zimene watichitira.
Amene adzagwira makanda ako
    ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.

Salimo la Davide.

138 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
    ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
    ndipo ndidzayamika dzina lanu
    chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
    kupambana zinthu zonse.
Pamene ndinayitana, munandiyankha;
    munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.

Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
    pamene amva mawu a pakamwa panu.
Iwo ayimbe za njira za Yehova,
    pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
    koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
    mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
    mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
    chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
    musasiye ntchito ya manja anu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.