M’Cheyne Bible Reading Plan
Fuko la Isakara
7 Ana a Isakara anali awa:
Tola, Puwa, Yasubu ndi Simironi ndipo onse analipo anayi.
2 Ana a Tola ndi awa:
Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600.
3 Mwana wa Uzi anali
Izirahiya.
Ana a Izirahiya anali:
Mikayeli, Obadiya, Yoweli ndi Isiya. Onse asanu anali atsogoleri a mabanja. 4 Monga mwa chiwerengero cha mabanja awo, panali anthu 36,000 odziwa kumenya nkhondo, pakuti iwo anali ndi akazi ndi ana ambiri.
5 Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo.
Fuko la Benjamini
6 Ana atatu a Benjamini anali awa:
Bela, Bekeri ndi Yediaeli.
7 Ana a Bela anali awa:
Eziboni, Uzi, Uzieli, Yerimoti ndi Iri. Iwowa anali atsogoleri a mabanja awo ndipo onse pamodzi analipo asanu. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali anthu 22,034 odziwa kumenya nkhondo.
8 Ana a Bekeri anali awa:
Zemira, Yowasi, Eliezara, Eliyoenai, Omiri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri. 9 Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali atsogoleri a mabanja ndi anthu 20,200 odziwa kumenya nkhondo.
10 Mwana wa Yediaeli anali
Bilihani.
Ana a Bilihani anali awa:
Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara. 11 Ana onsewa a Yediaeli anali atsogoleri a mabanja. Analipo anthu 17,200 amene anali okonzeka kupita ku nkhondo.
12 Asupi ndi Ahupi anali zidzukulu za Iri, ndipo Ahusimu anali zidzukulu za Aheri.
Fuko la Nafutali
13 Ana a Nafutali anali awa:
Yahazieli, Guni, Yezeri ndi Salumu, zidzukulu za Biliha.
Fuko la Manase
14 Ana a Manase anali awa:
Asirieli ndi mwana amene anabereka kwa mzikazi wake wa ku Aramu. Mzikazi yemweyo anaberekanso Makiri abambo ake a Giliyadi. 15 Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka.
Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha.
16 Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Perezi. Mʼbale wake anamutcha Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rakemu.
17 Mwana wa Ulamu anali
Bedani.
Awa anali ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase. 18 Mlongo wake Hamoleketi anabereka Isihodi, Abiezeri ndi Mahila.
19 Ana a Semida anali:
Ahiyani, Sekemu, Likihi ndi Aniyamu.
Fuko la Efereimu
20 Ana a Efereimu anali awa:
Sutela, Beredi,
Tahati, Eliada,
Tahati, 21 Zabadi,
Sutela.
Ezeri ndi Eladi anaphedwa ndi anthu a ku Gati, pamene anabwera kudzalanda zoweta zawo. 22 Efereimu, abambo awo, anawalira masiku ambiri, ndipo abale ake anabwera kudzamutonthoza. 23 Kenaka anagona ndi mkazi wake, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Beriya, chifukwa tsoka linagwera banja lake. 24 Mwana wake wamkazi anali Seera, amene anamanga mzinda wa Beti-Horoni Wakumunsi, Wakumtunda kudzanso Uzeni-Seera.
25 Mwana wina wa Efereimu anali Refa amene zidzukulu zake zinali Resefu,
Tela, Tahani,
26 Ladani, Amihudi,
Elisama, 27 Nuni
ndi Yoswa.
28 Malo amene ankakhala anali Beteli ndi midzi yozungulira, cha kummawa kunali Naarani, Gezeri ndi midzi yake ya kumadzulo ndi Sekemu ndi midzi yake mpaka ku Aya ndi midzi yake. 29 Mʼmbali mwa malire a Manase munali Beti-Seani, Taanaki, Megido ndi Dori, pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Yosefe mwana wa Israeli zimakhala mʼmizinda imeneyi.
Fuko la Aseri
30 Ana a Aseri anali awa:
Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya. Mlongo wawo anali Sera.
31 Ana a Beriya anali awa:
Heberi ndi Malikieli amene anabereka Birizaiti.
32 Heberi anabereka Yafuleti, Someri, Hotamu ndi Suwa, mlongo wawo.
33 Ana a Yafuleti anali awa:
Pasaki, Bimuhali ndi Asivati.
Awa anali ana a Yafuleti.
34 Ana a Someri anali awa:
Ahi, Rohiga, Yehuba ndi Aramu.
35 Ana a mʼbale wake Helemu anali awa:
Zofa, Imuna, Selesi ndi Amali.
36 Ana a Zofa anali awa:
Suwa, Harineferi, Suwali, Beri, Imula, 37 Bezeri, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Bera.
38 Ana a Yeteri anali awa:
Yefune, Pisipa ndi Ara.
39 Ana a Ula anali awa:
Ara, Hanieli ndi Riziya.
40 Onsewa anali zidzukulu za Aseri, atsogoleri a mabanja, anthu omveka, ankhondo olimba mtima, ndi akuluakulu pakati pa atsogoleri anzawo. Chiwerengero cha anthu odziwa kumenya nkhondo chomwe chinalembedwa chinali 26,000.
Adzukulu a Benjamini ndi Sauli
8 Benjamini anabereka Bela mwana wake woyamba,
wachiwiri Asibeli, wachitatu Ahara,
2 wachinayi Noha ndipo wachisanu Rafa.
3 Ana a Bela anali awa:
Adari, Gera, Abihudi, 4 Abisuwa, Naamani, Ahowa, 5 Gera, Sefufani ndi Hiramu.
6 Zidzukulu za Ehudi, zimene zinali atsogoleri a mabanja a amene amakhala ku Geba ndipo zinasamutsidwa kupita ku Manahati zinali izi:
7 Naamani, Ahiya ndi Gera, amene anawasamutsa ndipo anabereka Uza ndi Ahihudi.
8 Saharaimu anabereka ana ku Mowabu atalekana ndi akazi ake, Husimu ndi Baara. 9 Mwa mkazi wake Hodesi anabereka Yobabu, Zibiya, Mesa, Malikamu, 10 Yeusi, Sakiya ndi Mirima. Awa ndiye ana ake, atsogoleri a mabanja awo. 11 Mwa mkazi wake Husimu anabereka Abitubi ndi Elipaala.
12 Ana a Elipaala anali awa:
Eberi, Misamu, Semedi (amene anamanga mizinda ya Ono ndi Lodi ndi midzi yake yozungulira) 13 ndiponso Beriya ndi Sema, amene anali atsogoleri a mabanja a amene ankakhala ku Ayaloni ndipo anathamangitsa nzika za ku Gati.
14 Ahiyo, Sasaki, Yeremoti, 15 Zebadiya, Aradi, Ederi, 16 Mikayeli, Isipa ndi Yoha anali ana a Beriya.
17 Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Heberi, 18 Isimerai, Iziliya ndi Yobabu anali ana a Elipaala.
19 Yakimu, Zikiri, Zabidi, 20 Elienai, Ziletai, Elieli, 21 Adaya, Beraya ndi Simirati anali ana a Simei.
22 Isipani, Eberi, Elieli, 23 Abidoni, Zikiri, Hanani, 24 Hananiya, Elamu, Anitotiya, 25 Ifideya ndi Penueli anali ana a Sasaki.
26 Samuserai, Sehariya, Ataliya, 27 Yaaresiya, Eliya ndi Zikiri anali ana a Yerohamu.
28 Onsewa anali atsogoleri a mabanja, anthu otchuka potsata mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu.
29 Yeiyeli amene amabereka Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni.
Dzina la mkazi wake linali Maaka, 30 ndipo mwana wake woyamba anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu, 31 Gedori, Ahiyo, Zekeri 32 ndi Mikiloti, amene anabereka Simea. Iwowa ankakhalanso ku Yerusalemu ndi abale awo.
33 Neri anabereka Kisi. Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala.
34 Mwana wa Yonatani anali
Meri-Baala, amene anabereka Mika.
35 Ana a Mika anali awa:
Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi.
36 Ahazi anabereka Yehoyada, Yehoyada anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimuri anabereka Moza. 37 Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Rafa, Eleasa ndi Azeli.
38 Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi, ndipo mayina awo anali awa:
Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Onsewa anali ana a Azeli.
39 Ana a Eseki mʼbale wake anali awa:
Mwana wake woyamba Ulamu, wachiwiri Yeusi ndipo wachitatu Elifeleti. 40 Ana a Ulamu anali asilikali olimba mtima amene amadziwa kugwiritsa ntchito uta. Iwo anali ndi ana ndi adzukulu ambiri ndipo onse analipo 150.
Onsewa anali adzukulu a Benjamini.
Za Chikhulupiriro cha anthu Akale
11 Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu. 2 Ndi chikhulupiriro chimenechi makolo athu akale anayamikidwa.
3 Ndi chikhulupiriro timazindikira kuti dziko lapansi ndi la mmwamba zinapangidwa ndi Mawu a Mulungu, ndikuti zinthu zoonekazi zinachokera ku zinthu zosaoneka. 4 Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa imene Kaini anapereka. Ndi chikhulupiriro anatchedwa munthu wolungama Mulungu atayamikira zopereka zake. Ngakhale iye anafa, akuyankhulabe chifukwa cha chikhulupiriro chakecho.
5 Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa wamoyo, motero iye sanalawe imfa; sanapezeke chifukwa Mulungu anamutenga. Pakuti asanatengedwe anayamikiridwa kuti ankakondweretsa Mulungu. 6 Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.
7 Ndi chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anachita mantha napanga chombo kuti apulumutsire banja lake. Ndi chikhulupiriro chake anatsutsa dziko lapansi ndipo analandira chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.
8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita. 9 Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso. 10 Pakuti amadikira mudzi wokhala ndi maziko, umene mmisiri ndi womanga wake ndi Mulungu.
11 Ndi chikhulupiriro Sara analandira mphamvu zokhala ndi pakati ngakhale kuti zaka zake zobala mwana zinali zitapita kale, popeza anamutenga amene analonjeza kukhala wokhulupirika. 12 Nʼchifukwa chake mwa munthu mmodzi, amene anali ngati wakufa, munatuluka mibado yochuluka ngati nyenyezi ndi yosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
13 Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi. 14 Anthu amene amanena zinthu zotere amaonekeratu kuti akufuna dziko lawo lenileni. 15 Akanakhala kuti akuganizira za dziko limene analisiya akanapeza mpata obwerera kwawo. 16 Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.
17 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, Mulungu atamuyesa, anapereka Isake ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu anamulonjeza, anakhala wokonzeka kupereka nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. 18 Za mwana ameneyu Mulungu anamuwuza iye kuti, “Zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.” 19 Abrahamu amazindikira kuti Mulungu angathe kuukitsa akufa, ndipo tingathe kunena mofanizira kuti iye analandiranso Isake ngati wouka kwa akufa.
20 Ndi chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau pa zatsogolo lawo.
21 Ndi chikhulupiriro, pamene Yakobo ankamwalira anadalitsa ana awiri a Yosefe, ndipo anapembedza Mulungu atatsamira ndodo yake.
22 Ndi chikhulupiriro Yosefe ali pafupi kumwalira anayankhula za kutuluka kwa Aisraeli mu Igupto ndipo anawawuza zoti adzachite ndi mafupa ake.
23 Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.
24 Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao. 25 Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. 26 Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo. 27 Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo. 28 Ndi chikhulupiriro anachita Paska ndi kuwaza magazi, kuti mngelo wowononga ana oyamba kubadwa asaphe ana oyamba kubadwa a Aisraeli.
29 Ndi chikhulupiriro Aisraeli anawoloka Nyanja Yofiira ngati pa mtunda powuma, koma Aigupto atayesa kutero anamizidwa.
30 Ndi chikhulupiriro mpanda wa Yeriko unagwa, Aisraeli atawuzungulira kasanu ndi kawiri.
31 Ndi chikhulupiriro Rahabe, mkazi wadama sanaphedwe pamodzi ndi osamvera aja chifukwa analandira bwino ozonda aja ku nyumba kwake.
32 Kodi ndinenenso chiyani? Nthawi yandichepera yoti ndinene za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, Samueli ndi aneneri, 33 amene ndi chikhulupiriro anagonjetsa mafumu, anakhazikitsa chilungamo ndi kulandira zimene zinalonjezedwa. Anatseka pakamwa pa mikango, 34 anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo. 35 Amayi ena analandira anthu awo amene anafa, ataukitsidwanso. Enanso anazunzidwa ndipo anakana kumasulidwa, kuti adzaukenso ndi moyo wabwino. 36 Ena anawaseka ndi kuwakwapula, pamenenso ena anamangidwa ndi kupita ku ndende. 37 Anagendedwa miyala; anachekedwa pakati; ena anaphedwa ndi lupanga. Iwo anayendayenda atavala zikopa zankhosa ndi zikopa zambuzi, umphawi okhaokha, ozunzidwa ndi kuvutitsidwa. 38 Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje.
39 Onsewa anayamikidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, komabe palibe wa iwo amene analandira zimene analonjezedwa. 40 Mulungu anatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife.
Mawu Odandawulira Aisraeli
5 Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo:
2 “Namwali Israeli wagwa,
moti sadzadzukanso,
wasiyidwa mʼdziko lake lomwe,
popanda woti ndi kumudzutsa.”
3 Ambuye Yehova akuti,
“Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu
udzatsala ndi anthu 100 okha;
mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu
udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”
4 Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi:
“Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo;
5 musafunefune Beteli,
musapite ku Giligala,
musapite ku Beeriseba.
Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,
ndipo Beteli adzawonongekeratu.”
6 Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo,
mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto;
motowo udzawononga,
ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.
7 Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa
ndi kunyoza chilungamo.
8 (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana,
amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa
ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku,
amene amayitana madzi a mʼnyanja
ndi kuwathira pa dziko lapansi,
Yehova ndiye dzina lake.
9 Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu
ndi kuwononga mizinda yotetezedwa),
10 inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu
ndi kunyoza amene amanena zoona.
11 Mumapondereza munthu wosauka
ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu.
Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema,
inuyo simudzakhalamo.
Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa,
inu simudzamwa vinyo wake.
12 Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu
ndi kukula kwa machimo anu.
Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu
ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.
13 Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu,
popeza ndi nthawi yoyipa.
14 Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa,
kuti mukhale ndi moyo.
Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu,
monga mmene mumanenera kuti ali nanu.
15 Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino;
mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu.
Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo
anthu otsala a mʼbanja la Yosefe.
16 Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena:
“Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula,
ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse.
Adzayitana alimi kuti adzalire,
ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.
17 Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha,
pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,”
akutero Yehova.
Tsiku la Yehova
18 Tsoka kwa inu amene mumalakalaka
tsiku la Yehova!
Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova?
Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala.
19 Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango
amakumana ndi chimbalangondo,
ngati pamene munthu walowa mʼnyumba,
natsamira dzanja lake pa khoma
ndipo njoka nʼkuluma.
20 Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala,
mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse?
21 “Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza;
sindikondwera nayo misonkhano yanu.
22 Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya,
Ine sindidzazilandira.
Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano,
Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe.
23 Musandisokose nazo nyimbo zanu!
Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu.
24 Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi,
chilungamo ngati mtsinje wosaphwa!
25 “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja
munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli?
26 Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu,
ndi nyenyezi ija Kaiwani,
mulungu wanu,
mafano amene munadzipangira.
27 Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,”
akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse.
Mawu Oyamba
1 Ambiri anayesa kufotokoza nkhani ya zimene zinakwaniritsidwa pakati pathu, 2 monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu. 3 Popeza inenso ndafufuza mosamalitsa chilichonse kuyambira pachiyambi, zandikomera kukulemberani mwatsatanetsatane inu wolemekezeka Tiofilo, 4 kuti mudziwe bwinobwino zoona za zinthu zimene mwaphunzitsidwa.
Aneneratu za Kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi
5 Mʼmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe dzina lake Zakariya wa gulu la ansembe la Abiya; mkazi wake Elizabeti analinso wa fuko la Aaroni. 6 Onse awiri anali olungama pamaso pa Mulungu, ndipo amasunga malamulo ndi malangizo onse a Ambuye osalakwa konse. 7 Koma analibe ana chifukwa Elizabeti anali wosabereka; ndipo onse anali okalamba.
8 Nthawi yogwira ntchito yotumikira ansembe a gulu la Zekariya, Zekariya ankatumikira ngati wansembe pamaso pa Mulungu, 9 Zakariyayo anasankhidwa mwa maere, monga mwa mwambo wa unsembe, kupita mʼNyumba ya Ambuye kukafukiza lubani. 10 Ndipo nthawi yofukiza lubani itafika, gulu lonse lopembedza linkapemphera kunja.
11 Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira. 12 Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha. 13 Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane. 14 Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake, 15 chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa. 16 Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. 17 Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.”
18 Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.”
19 Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu. 20 Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”
21 Pa nthawiyi, anthu ankadikira Zakariya ndipo anadabwa chifukwa anatenga nthawi yayitali ali mʼNyumba ya Mulungu. 22 Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula.
23 Nthawi yake yotumikira itatha, anabwerera kwawo. 24 Zitatha izi, mkazi wake Elizabeti anakhala ndi pakati ndipo anadzibisa kwa miyezi isanu. 25 Iye anati, “Ambuye wandichitira izi, kuti mʼmasiku ano wandionetsera kukoma mtima kwake ndi kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.”
Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu
26 Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, 27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. 28 Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”
29 Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. 30 Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. 31 Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. 32 Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, 33 ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”
34 Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?”
35 Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. 37 Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”
38 Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.