Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 25

25 Choncho mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse la ankhondo, nadzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga misasa kunja kwa mzindawo ndipo anamanga mitumbira ya nkhondo kuzungulira mzindawo. Mzindawo anawuzinga mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha Mfumu Zedekiya. Pa tsiku lachisanu ndi chinayi pa mwezi wachinayi, njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti anthu analibe chakudya. Pamenepo khoma la mzindawo linabowoledwa ndipo gulu lonse la ankhondo linathawa usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Iwo anathawira cha ku Araba, koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika. Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula, kumene anagamula mlandu wa Zedekiyayo. Iwo anapha ana a Zedekiya iyeyo akuona. Kenaka anakolowola maso a Zedekiya namumanga ndi unyolo wamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.

Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, mʼchaka cha 19 cha Nebukadinezara, mfumu ya Babuloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, nduna ya mfumu ya Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. Iye anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu pamodzi ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse yofunika. 10 Gulu lonse la ankhondo la ku Babuloni limene linali ndi mkulu wa asilikali oteteza mfumu ija, linagumula malinga ozungulira Yerusalemu. 11 Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 12 Koma mkulu wa asilikaliyo anasiya anthu ena osauka kwambiri mʼdzikomo kuti azisamalira minda ya mpesa ndi minda ina.

13 Ababuloni anaphwanya zipilala zamkuwa, maphaka ndiponso mbiya ya mkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo anatenga mkuwawo napita nawo ku Babuloni. 14 Iwo anatenganso miphika, mafosholo, mbaniro za nyale, mbale ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼNyumbayo. 15 Mkulu wa asilikali uja anatenganso zofukizira lubani ndi mbale zowazira magazi. Zonsezi zinali zopangidwa ndi golide wabwino kwambiri kapena siliva.

16 Mkuwa wochokera ku zipilala ziwiri zija, mbiya ija ndi maphaka aja, zimene Solomoni anapanga mʼNyumba ya Yehova, kuchuluka kwake kunali kosawerengeka. 17 Chipilala chilichonse chinali chotalika mamita asanu ndi atatu. Mutu wa mkuwa umene unali pamwamba pa chipilalacho unali mita imodzi ndi theka ndipo unakongoletsedwa ndi ukonde wa makangadza a mkuwa amene anazungulira mutuwo. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi chinacho, ndipo chinali ndi ukonde.

18 Mkulu wa asilikali uja anagwira ukapolo mkulu wa ansembe Seraya, Zefaniya wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apakhomo. 19 Mwa anthu amene anali mu mzindamo, anatenga mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso alangizi asanu a mfumu. Anatenganso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankalemba anthu ntchito ya usilikali mʼdzikomo pamodzi ndi anthu ake 60 amene anali mu mzindamo. 20 Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anawatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya Babuloni ku Ribula. 21 Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloni inalamula kuti awakwapule ndi kuwapha.

Choncho Ayuda anatengedwa ukapolo kuwachotsa mʼdziko lawo.

22 Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala woyangʼanira anthu amene anatsala ku Yuda. 23 Atsogoleri onse ankhondo ndi anthu awo atamva kuti mfumu ya Babuloni yasankha Gedaliya kukhala bwanamkubwa, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. Atsogoleriwo mayina awo anali awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yaazaniya mwana wa Maakati, pamodzi ndi anthu awo. 24 Gedaliya analumbira powatsimikizira iwo ndi anthu awo. Iye anati, “Musachite mantha ndi atsogoleri Ababuloniwa. Khalani mʼdziko muno ndipo tumikirani mfumu ya Babuloni. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino.”

25 Koma pa mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa banja laufumu, anabwera ndi anthu khumi ndipo anapha Gedaliya pamodzi ndi Ayuda ndi anthu a ku Babuloni amene anali naye limodzi ku Mizipa. 26 Chifukwa cha zimenezi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo anathawira ku Igupto chifukwa choopa Ababuloni.

Kumasulidwa kwa Yehoyakini

27 Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda, chaka chimene Evili-Merodaki anakhala mfumu ya Babuloni, anamasula Yehoyakini mʼndende pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27. 28 Anamukomera mtima namukweza kupambana mafumu ena onse amene anali naye ku Babuloni. 29 Choncho Yoyakini anavula zovala zake za ku ndende, ndipo ankadya ndi mfumu masiku onse a moyo wake. 30 Mfumu inkamupatsa Yehoyakini chakudya tsiku lililonse pa moyo wake wonse.

Ahebri 7

Za Melikizedeki Mkulu wa Ansembe

Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.” Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.

Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha. Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu. Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu. Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo. Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo. Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu, 10 chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.

Yesu Wofanana ndi Melikizedeki

11 Kukanatheka kukhala wangwiro mwa unsembe wa Levi, pakuti Malamulo anapatsidwa kwa anthu mwa unsembe wa Levi, nʼchifukwa chiyani panafunikanso wansembe wina kuti abwere, wofanana ndi Melikizedeki, osati Aaroni? 12 Pakuti pamene unsembe usintha, malamulonso amayenera kusintha. 13 Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe. 14 Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la Yuda. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe. 15 Ndipo zimene tanenazi zimamveka bwino ngati tiona kuti pafika wansembe wina wofanana ndi Melikizedeki. 16 Yesu sanakhale wansembe chifukwa cha malamulo monga mwa mabadwidwe ake koma mwamphamvu ya moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu anamuchitira umboni kuti,

“Iwe ndi wansembe wamuyaya,
    monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.”

18 Choncho lamulo loyamba lachotsedwa chifukwa linali lofowoka ndi lopanda phindu. 19 Tsono Malamulo sangathe kusandutsa chilichonse kukhala changwiro, koma mʼmalo mwake mwalowa chiyembekezo chabwino, chimenechi timayandikira nacho kwa Mulungu.

20 Izi sizinachitiketu wopanda lumbiro. Ena ankakhala ansembe popanda lumbiro. 21 Koma Yesu ankakhala wansembe ndi lumbiro pamene Mulungu anati,

“Ambuye analumbira
    ndipo sangasinthe maganizo ake,
‘Iwe ndi wansembe wamuyaya.’ ”

22 Chifukwa cha lumbiroli, Yesu wakhala Nkhoswe ya Pangano lopambana.

23 Tsono ansembe akale aja analipo ambiri, popeza imfa imawalepheretsa kupitiriza ntchitoyi. 24 Koma Yesu popeza ndi wamuyaya, unsembe wake ndi wosatha. 25 Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.

26 Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku. 27 Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha. 28 Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya.

Amosi 1

Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli.

Amosi anati:

“Yehova akubangula mu Ziyoni
    ndipo akumveka ngati bingu mu Yerusalemu;
msipu wa abusa ukulira,
    ndipo pamwamba pa Karimeli pakuwuma.”

Chiweruzo pa Anthu Oyandikana ndi Israeli

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anapuntha Giliyadi
    ndi zopunthira za mano achitsulo,
Ine ndidzatumiza moto pa nyumba ya Hazaeli
    umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.
Ndidzathyola chipata cha Damasiko;
    ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni,
ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni.
    Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,”
            akutero Yehova.

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthu
    ndi kuwugulitsa ku Edomu,
ndidzatumiza moto pa makoma a Gaza
    umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodi
    komanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni.
Ndidzalanga Ekroni,
    mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,”
            akutero Ambuye Yehova.

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu,
    osasunga pangano laubale lija,
10 Ine ndidzatumiza moto pa makoma a Turo
    umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.”

11 Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga,
    popanda nʼchifundo chomwe.
Popeza mkwiyo wake unakulabe
    ndipo ukali wake sunatonthozeke,
12 Ine ndidzatumiza moto pa Temani
    umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Bozira.”

13 Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi
    nʼcholinga choti akuze malire awo,
14 Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Raba
    umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.
Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo,
    kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu.
15 Mfumu yawo idzatengedwa kupita ku ukapolo,
    iyo pamodzi ndi akuluakulu ake,”
            akutero Yehova.

Masalimo 144

Salimo la Davide.

144 Atamandike Yehova Thanthwe langa,
    amene amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
    zala zanga kumenya nkhondo.
Iye ndiye Mulungu wanga wachikondi ndi malo anga otetezedwa,
    linga langa ndi mpulumutsi wanga,
chishango changa mmene ine ndimathawiramo,
    amene amagonjetsa mitundu ya anthu pansi panga.

Inu Yehova, munthu nʼchiyani kuti mumamusamalira,
    mwana wa munthu kuti muzimuganizira?
Munthu ali ngati mpweya;
    masiku ake ali ngati mthunzi wosakhalitsa.

Ngʼambani mayiko akumwamba, Inu Yehova, ndipo tsikani pansi;
    khudzani mapiri kuti atulutse utsi.
Tumizani zingʼaningʼani ndi kubalalitsa adani;
    ponyani mivi yanu ndi kuwathamangitsa.
Tambasulani dzanja lanu kuchokera kumwamba;
    landitseni ndi kundipulumutsa,
ku madzi amphamvu,
    mʼmanja mwa anthu achilendo,
amene pakamwa pawo ndi podzala ndi mabodza,
    amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

Ndidzakuyimbirani nyimbo yatsopano Inu Mulungu;
    ndidzakuyimbirani nyimbo pa zeze wa nsambo khumi,
10 kwa Iye amene amapambanitsa mafumu,
    amene amapulumutsa Davide mtumiki wake ku lupanga loopsa.

11 Landitseni ndi kundipulumutsa,
    mʼmanja mwa anthu achilendo,
amene pakamwa pawo ndi podzaza ndi mabodza,
    amene dzanja lawo lamanja ndi lachinyengo.

12 Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo
    adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino,
ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala
    zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
13 Nkhokwe zathu zidzakhala zodzaza
    ndi zokolola za mtundu uliwonse.
Nkhosa zathu zidzaswana miyandamiyanda
    pa mabusa athu.
14     Ngʼombe zathu zidzanyamula katundu wolemera.
Sipadzakhala mingʼalu pa makoma,
    sipadzakhalanso kupita ku ukapolo,
    mʼmisewu mwathu simudzakhala kulira chifukwa cha mavuto.

15 Odala anthu amene adzalandira madalitso awa;
    odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.