Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 16

Ahazi Mfumu ya Yuda

16 Mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Ahazi anakhala mfumu ali ndi zaka makumi awiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zabwino pamaso pa Yehova Mulungu wake monga momwe Davide kholo lake ankachitira. Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Israeli mpaka kupereka mwana wake wamwamuna pa moto ngati nsembe yopsereza, potsatira zonyansa za anthu a mitundu imene Yehova anayipirikitsa mʼdzikomo Aisraeli asanafike. Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzera mafano, pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.

Ndipo Rezini mfumu ya Aramu ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli anapita kukachita naye nkhondo ku Yerusalemu ndipo anazinga Ahazi, koma sanathe kumugonjetsa. Nthawi imeneyo Rezini mfumu ya Aramu anatenganso Elati ndi kumubwezera kwa Aaramu, nathamangitsa anthu a ku Yuda mu Elatimo. Aedomu anapita kukakhala ku Elati ndipo akukhalako mpaka lero lino.

Ahazi anatuma amithenga kwa Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya kuti, “Ine ndine mtumiki wanu ndipo ndili pansi panu. Bwerani mudzandipulumutse mʼdzanja la mfumu ya Aramu ndiponso mʼdzanja la mfumu ya Israeli amene akundithira nkhondo.” Ndipo Ahazi anatenga siliva ndi golide amene anamupeza mʼNyumba ya Yehova ndi mosungira chuma cha nyumba ya mfumu ndi kutumiza ngati mphatso kwa mfumu ya ku Asiriya. Mfumu ya ku Asiriya inamvera pokathira nkhondo mzinda wa Damasiko ndi kuwulanda. Anthu a mu mzindamo anawatumiza ku Kiri ndipo anapha Rezini.

10 Kenaka mfumu Ahazi inapita ku Damasiko kukakumana ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya. Iye anaona guwa lansembe ku Damasiko kuja ndipo anatumiza chitsanzo chake kwa wansembe Uriya, osasiyapo nʼkanthu komwe kuti athe kulimanga. 11 Choncho wansembe Uriya anamanga guwa lansembe molingana ndi chitsanzo chimene anamutumizira Mfumu Ahazi kuchokera ku Damasiko ndipo anatsiriza kumanga guwalo Ahazi asabwere kuchokera ku Damasiko kuja. 12 Mfumu itabwera kuchokera ku Damasiko kuja ndi kuona guwalo, inasendera pafupi ndi kupereka nsembe paguwapo. 13 Mfumu inapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya chakudya. Inapereka nsembe yachakumwa ndi kuwaza magazi a nsembe yake yachiyanjano paguwapo. 14 Guwa lamkuwa limene linali pamaso pa Yehova analichotsa kutsogolo kwa nyumbayo, kulichotsa pakati pa guwa latsopano ndi Nyumba ya Yehova ndi kukaliyika cha kumpoto kwa guwa latsopanolo.

15 Pamenepo Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uriya kuti, “Pa guwa lalikulu latsopano uziperekapo nsembe yopsereza ya mmawa ndi nsembe ya chakudya ya madzulo, nsembe yopsereza ya mfumu ndi nsembe yake ya chakudya ndiponso nsembe za anthu onse a mʼdziko, za chakudya ndi chakumwa. Pa guwali uziwazapo magazi a nsembe zonse zopsereza ndi nsembe zina zonse. Koma ine ndizigwiritsa ntchito guwa lansembe lamkuwa pofuna kufunsira nzeru.” 16 Ndipo wansembe Uriya anachita monga analamulira Mfumu Ahazi.

17 Mfumu Ahazi anachotsa maferemu a maphaka nachotsapo mabeseni. Iye anatsitsa mbiya yayikulu imene inali pamwamba pa ngʼombe zamkuwa ndipo anayika pansi pa chiwundo cha miyala. 18 Iye anachotsa kadenga ka pa Sabata kamene kanamangidwa mʼkati mwa Nyumba ya Yehova ndiponso anatseka chipata cholowera mfumu cha kunja kwa nyumba ya Yehova pofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya.

19 Ntchito zina za Ahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 20 Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Tito 2

Malangizo Osiyanasiyana

Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.

Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.

Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa. Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako. Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.

Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo 10 kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu.

11 Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. 12 Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, 13 pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu, 14 amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.

15 Tsono zimenezi ndi zinthu zomwe uyenera kuphunzitsa. Uziwalimbikitsa anthu ndi kuwatsutsa komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ayi.

Hoseya 9

Chilango cha Israeli

Iwe Israeli, usakondwere;
    monga imachitira mitundu ina.
Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako;
    umakonda malipiro a chiwerewere
    pa malo aliwonse opunthira tirigu.
Malo opunthira tirigu ndi malo opsinyira mphesa sadzadyetsa anthu;
    adzasowa vinyo watsopano.
Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova.
    Efereimu adzabwerera ku Igupto
    ndipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.
Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova,
    kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo.
Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa;
    onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa.
Chakudya ichi chidzakhala chodya okha,
    sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.

Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika;
    pa masiku a zikondwerero za Yehova?
Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko,
    Igupto adzawasonkhanitsa,
    ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda.
Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva,
    ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
Masiku achilango akubwera,
    masiku obwezera ali pafupi.
    Israeli adziwe zimenezi.
Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri
    ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri.
Mneneri amamuyesa chitsiru,
    munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
Mneneri pamodzi ndi Mulungu wanga
    ndiwo alonda a Efereimu,
koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse,
    ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
Iwo azama mu zachinyengo
    monga masiku a Gibeya.
Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo
    ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.

10 “Pamene ndinamupeza Israeli
    zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu.
Nditaona makolo anu,
    zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa.
Koma atafika ku Baala Peori,
    anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi
    ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho.
11 Ulemerero wa Efereimu udzawuluka ngati mbalame.
    Sipadzakhalanso kubereka ana, kuyembekezera kapena kutenga pathupi.
12 Ngakhale atalera ana
    ndidzachititsa kuti mwana aliyense amwalire.
Tsoka kwa anthuwo
    pamene Ine ndidzawafulatira!
13 Ndaona Efereimu ngati Turo,
    atadzalidwa pa nthaka ya chonde.
Koma Efereimu adzatsogolera
    ana ake kuti akaphedwe.”

14 Inu Yehova, muwapatse.
    Kodi mudzawapatsa chiyani?
Apatseni mimba yomangopita padera
    ndi mawere owuma.

15 “Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala,
    Ine ndinawada kumeneko.
Chifukwa cha machitidwe awo auchimo,
    ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga.
Sindidzawakondanso;
    atsogoleri awo onse ndi owukira.
16 Efereimu wathedwa,
    mizu yake yauma
    sakubalanso zipatso.
Ngakhale atabereka ana,
    Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”

17 Mulungu wanga adzawakana
    chifukwa sanamumvere Iye;
    adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.

Masalimo 126-128

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

126 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,
    tinali ngati amene akulota.
Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;
    malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.
Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,
    “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
Yehova watichitira zinthu zazikulu,
    ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,
    monga mitsinje ya ku Negevi.
Iwo amene amafesa akulira,
    adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.
Iye amene amayendayenda nalira,
    atanyamula mbewu yokafesa,
adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,
    atanyamula mitolo yake.

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Solomoni.

127 Yehova akapanda kumanga nyumba,
    omanga nyumbayo agwira ntchito pachabe.
Yehova akapanda kulondera mzinda,
    mlonda akanangolondera pachabe.
Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa
    ndi kusagona msanga madzulo,
kuvutikira chakudya choti mudye,
    pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova,
    ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.
Ana a pa unyamata ali ngati mivi mʼmanja
    mwa munthu wankhondo.
Wodala munthu
    amene motengera mivi mwake mwadzaza.
Iwo sadzachititsidwa manyazi
    pamene alimbana ndi adani awo pa zipata.

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

128 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,
    amene amayenda mʼnjira zake.
Udzadya chipatso cha ntchito yako;
    madalitso ndi chuma zidzakhala zako.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka
    mʼkati mwa nyumba yako;
ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi
    kuzungulira tebulo lako.
Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa
    amene amaopa Yehova.

Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni
    masiku onse a moyo wako;
uwone zokoma za Yerusalemu,
    ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako.

Mtendere ukhale ndi Israeli.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.