M’Cheyne Bible Reading Plan
16 Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu. 2 Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova. 3 Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.
4 Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli. 5 Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga, 6 ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.
Nyimbo Yotamanda ya Davide
7 Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:
8 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
9 Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;
nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.
10 Nyadirani dzina lake loyera;
ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova.
11 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
funafunani nkhope yake nthawi zonse.
12 Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita,
zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake,
13 inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake,
inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.
14 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi.
15 Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse,
mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda,
16 pangano limene anachita ndi Abrahamu,
lonjezo limene analumbira kwa Isake.
17 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo,
kwa Israeli monga pangano lamuyaya.
18 “Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani
monga cholowa chimene udzachilandira.”
19 Ali anthu owerengeka,
ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo,
20 iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,
ku ufumu wina kupita ku ufumu wina.
21 Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze;
chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu:
22 “Musakhudze odzozedwa anga;
musawachitire choyipa aneneri anga.”
23 Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi;
lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
24 Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse,
ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.
25 Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.
26 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake,
koma Yehova analenga kumwamba.
27 Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake;
mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye.
28 Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,
29 perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake.
Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake;
pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake.
30 Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi!
Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
31 Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere;
anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!”
32 Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo!
33 Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba,
idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova,
pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
34 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino;
chikondi chake chikhala mpaka muyaya.
35 Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,
mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina,
kuti tiyamike dzina lanu loyera,
kuti tikutamandeni.”
36 Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli,
kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.”
37 Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse. 38 Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata.
39 Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni 40 kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli. 41 Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.” 42 Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.
43 Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.
Za Lilime
3 Abale anga, ambiri musakhale aphunzitsi chifukwa mumadziwa kuti aphunzitsife tidzaweruzidwa mowuma kuposa anthu ena onse. 2 Tonsefe timapunthwa mʼnjira zambiri. Ngati wina salakwa poyankhula, ameneyo ndi munthu wangwiro, wodziwa kuyangʼanira bwino thupi lake lonse.
3 Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse. 4 Taonani sitima zapamadzi. Ngakhale ndi zazikulu kwambiri ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, zimawongoleredwa ndi tsigiro lalingʼono kulikonse kumene woyendetsayo akufuna kupita. 5 Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa. 6 Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena.
7 Mitundu yonse ya nyama, ya mbalame, ya zokwawa ndi ya zolengedwa za mʼnyanja, zikuwetedwa ndipo munthu wakhala akuziweta, 8 koma palibe munthu amene angaweta lilime. Lilime ndipo silitha kupuma, ndi lodzaza ndi ululu wakupha.
9 Ndi lilime lomwelo timatamanda Ambuye ndi Atate athu, komanso ndi lilime lomwelo timalalatira anthu, amene anapangidwa mʼchifanizo cha Mulungu. 10 Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi. 11 Kodi madzi abwino ndi a mchere angatuluke pa kasupe mmodzi? 12 Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu nʼkubala mphesa, kapena mtengo wampesa nʼkubala nkhuyu? Kasupe wa madzi a mchere sangatulutsenso madzi abwino.
Mitundu Iwiri ya Nzeru
13 Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake 14 Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi odzikonda, musadzitamandire kapena kukana choonadi. 15 “Nzeru” zotere sizochokera kumwamba koma ndi za mʼdziko lapansi, si zauzimu koma ndi za ziwanda. 16 Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.
17 Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima. 18 Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.
Masomphenya a Obadiya
1 Masomphenya a Obadiya.
Ambuye Yehova akunena kwa Edomu kuti,
Tamva uthenga wochokera kwa Yehova:
Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu kukanena kuti,
“Konzekani, tiyeni tikachite nkhondo ndi Edomu.”
2 “Taona, ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina;
udzanyozedwa kwambiri.
3 Kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,
iwe amene umakhala mʼmapanga a mʼmatanthwe
ndipo umamanga nyumba zako pa mapiri ataliatali,
iwe amene umanena mu mtima mwako kuti,
‘Ndani anganditsitse pansi?’
4 Koma ngakhale umawuluka ngati chiwombankhanga
ndi kumanga chisa chako pakati pa nyenyezi,
ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”
akutero Yehova.
5 “Anthu akuba akanabwera kwa iwe,
kapena anthu olanda zinthu akanafika usiku,
aa, tsoka lanji limene likukudikira iwe!
Kodi akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
Ngati anthu othyola mphesa akanafika,
kodi akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
6 Koma Esau adzalandidwa zinthu zonse,
chuma chake chobisika chidzabedwa!
7 Anthu onse ogwirizana nawo adzakupirikitsira kumalire;
abwenzi ako adzakunyenga ndi kukugonjetsa;
amene amadya chakudya chako adzakutchera msampha,
koma iwe sudzazindikira zimenezi.”
8 Yehova akunena kuti, “Tsiku limenelo,
kodi sindidzawononga anthu onse anzeru a ku Edomu,
anthu odziwa zinthu mʼmapiri a Esau?
9 Ankhondo ako, iwe Temani, adzachita mantha,
ndipo aliyense amene ali mʼphiri la Esau
adzaphedwa pa nkhondo.
10 Chifukwa cha nkhanza zimene unachitira mʼbale wako Yakobo,
udzakhala wamanyazi;
adzakuwononga mpaka muyaya.
11 Pamene adani
ankamulanda chuma chake
pamene alendo analowa pa zipata zake
ndi kuchita maere pa Yerusalemu,
pa tsikulo iwe unali ngati mmodzi wa iwo.
12 Iwe sunayenera kunyoza mʼbale wako
pa nthawi ya tsoka lake,
kapena kunyogodola Ayuda
chifukwa cha chiwonongeko chawo,
kapena kuwaseka pa nthawi ya
mavuto awo.
13 Iwe sunayenera kudutsa pa zipata za anthu anga
pa nthawi ya masautso awo,
kapena kuwanyogodola
pa tsiku la tsoka lawo,
kapena kulanda chuma chawo
pa nthawi ya masautso awo.
14 Sunayenera kudikirira pamphambano ya misewu
kuti uphe Ayuda othawa,
kapena kuwapereka kwa adani awo Ayuda opulumuka
pa nthawi ya mavuto awo.”
15 “Tsiku la Yehova layandikira
limene adzaweruza mitundu yonse ya anthu.
Adzakuchitira zomwe unawachitira ena;
zochita zako zidzakubwerera wekha.
16 Iwe unamwa pa phiri langa loyera,
koteronso mitundu ina yonse idzamwa kosalekeza;
iwo adzamwa ndi kudzandira
ndipo adzayiwalika pa mbiri ya dziko lapansi.
17 Koma pa Phiri la Ziyoni padzakhala chipulumutso;
phirilo lidzakhala lopatulika,
ndipo nyumba ya Yakobo
idzalandira cholowa chake.
18 Nyumba ya Yakobo idzasanduka moto
ndipo nyumba ya Yosefe idzasanduka lawi la moto;
nyumba ya Esau idzasanduka chiputu,
ndipo adzayitenthe pa moto ndi kuyipsereza.
Sipadzakhala anthu opulumuka
kuchokera mʼnyumba ya Esau.”
Yehova wayankhula.
19 Anthu ochokera ku Negevi adzakhala
ku mapiri a Esau,
ndipo anthu ochokera mʼmbali mwa mapiri
adzatenga dziko la Afilisti.
Adzakhala mʼminda ya Efereimu ndi Samariya,
ndipo Benjamini adzatenga Giliyadi.
20 Aisraeli amene ali ku ukapolo
adzalandira dziko la Kanaani mpaka ku Zarefati;
a ku Yerusalemu amene ali ku ukapolo ku Sefaradi
adzalandira mizinda ya ku Negevi.
21 Opulumukawo adzapita ku Phiri la Ziyoni
ndipo adzalamulira mapiri a Esau.
Koma ufumuwo udzakhala wa Yehova.
Yesu Ayitana Ophunzira Oyamba
5 Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu. 2 Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo. 3 Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.
4 Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.”
5 Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.”
6 Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. 7 Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira.
8 Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!” 9 Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, 10 chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo.
Kenaka Yesu anati kwa Simoni, “Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 11 Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.
Yesu Achiritsa Munthu Wakhate
12 Yesu ali ku mudzi wina, munthu amene anali ndi khate thupi lonse anabwera kwa Iye. Munthuyo ataona Yesu, anagwa chafufumimba ndipo anamupempha Iye kuti, “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
13 Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo. Iye anati, “Ine ndikufuna, yeretsedwa!” Ndipo nthawi yomweyo khate lake linachoka.
14 Kenaka Yesu anamulamula kuti, “Usawuze wina aliyense, koma pita, kadzionetse kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose anakulamulirani za kuyeretsedwa kwanu monga umboni kwa iwo.”
15 Koma mbiri yake inafalikirabe kwambiri kotero kuti magulu a anthu anabwera kudzamvetsera ndi kuti achiritsidwe ku matenda awo. 16 Koma Yesu nthawi zambiri ankachoka kupita ku malo a yekha kukapemphera.
Yesu Achiritsa Wofa Ziwalo
17 Tsiku lina pamene ankaphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, amene anachokera ku midzi yonse ya Galileya ndi ku Yudeya ndi Yerusalemu, anakhala pansi pomwepo. Ndipo mphamvu ya Ambuye inalipo yakuti Iye achiritse odwala. 18 Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu. 19 Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu.
20 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati, “Mnzanga, machimo ako akhululukidwa.”
21 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, “Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?”
22 Yesu anadziwa zomwe iwo amaganiza ndipo anafunsa kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi mʼmitima mwanu? 23 Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo yenda?’ ” 24 Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ ” 25 Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu. 26 Aliyense anadabwa ndi kuchita mantha ndipo anayamika Mulungu. Iwo anadabwa kwambiri ndipo anati, “Lero taona zinthu zosayiwalika.”
Kuyitanidwa kwa Levi
27 Zitatha izi, Yesu anachoka ndipo anaona wolandira msonkho dzina lake Levi atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anati kwa iye, “Nditsate Ine.” 28 Ndipo Levi anayimirira, nasiya zonse ndi kumutsata Iye.
29 Kenaka Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu ku nyumba yake ndipo gulu lalikulu la amisonkho ndi ena ankadya naye pamodzi. 30 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amene anali a gulu lawo anadandaula kwa ophunzira ake, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukudya ndi kumwa pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”
31 Yesu anawayankha kuti, “Amene sakudwala safuna singʼanga, koma odwala. 32 Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.”
Yesu Afunsidwa za Kusala Kudya
33 Iwo anati kwa Iye, “Ophunzira a Yohane amasala kudya ndi kupemphera kawirikawiri, monganso ophunzira a Afarisi, koma anu amangodya ndi kumwa.”
34 Yesu anawayankha kuti, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya pamene mkwati ali pakati pawo? 35 Koma nthawi ikubwera pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo. Masiku amenewo adzasala kudya.”
36 Iye anawawuza fanizo ili: “Palibe amene amangʼamba chigamba kuchokera pa chovala chatsopano ndi kuchisokerera pa chakale. Ngati atatero, ndiye kuti adzangʼamba chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chochokera pa chovala chatsopano chija sichidzagwirizana ndi chakale. 37 Ndipo palibe amene amakhuthulira vinyo watsopano mʼmatumba a vinyo akale. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa zikopazo, vinyo adzatayika ndipo zikopa za vinyozo zidzawonongeka. 38 Ayi, vinyo watsopano ayenera kuthiridwa mʼmatumba a vinyo azikopa zatsopano. 39 Ndipo palibe amene atamwa vinyo wakale amafuna watsopano, pakuti amati, ‘Wakale ndi okoma.’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.