M’Cheyne Bible Reading Plan
Kupulumutsidwa kwa Yerusalemu
19 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. 2 Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 3 Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera. 4 Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ”
5 Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, 6 Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. 7 Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
8 Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
9 Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11 Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka? 12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa? 13 Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”
Pemphero la Hezekiya
14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 16 Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.
17 “Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. 18 Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu. 19 Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”
Yankho la Mulungu Kudzera mwa Yesaya
20 Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ” 21 Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa:
“Namwali wa Ziyoni
akukunyoza ndi kukuseka iwe.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu
akupukusa mutu wake kumbuyo kwako.
22 Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani?
Kodi ndani amene wamufuwulira mawu ako
ndi kumuyangʼana monyada?
Wachitiratu izi Woyera wa Israeli!
23 Kudzera mwa amithenga ako
wonyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta ochuluka
ndinakwera mapiri ataliatali,
pa msonga za mapiri a Lebanoni.
Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri,
mitengo yake ya payini yabwino kwambiri.
Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni,
mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.
24 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
ndipo ndinamwa madzi a kumeneko.
Ndi mapazi anga
ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’ ”
25 “ ‘Kodi sunamvepo?
Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale.
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
tsopano ndachita kuti zichitikedi,
iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa
kukhala milu ya miyala.
26 Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu,
athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi.
Ali ngati mbewu za mʼmunda,
ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu womera pa denga,
umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ”
27 “ ‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako,
kutuluka kwako ndi kulowa kwako,
ndi mkwiyo wako pa Ine.
28 Chifukwa chakuti wandikwiyira
ndipo ndamva za mwano wako,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa
njira yomwe unadzera pobwera.’
29 “Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi:
“Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa,
ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera.
Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola,
mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.
30 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsale
adzazika mizu ndi kubereka zipatso.
31 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.”
“Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.
32 “Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi:
“ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
kapena kuponyamo muvi.
Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake
kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.
33 Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera;
sadzalowa mu mzinda umenewu,
akutero Yehova.
34 Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa,
chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
35 Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda! 36 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko.
37 Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
Khristu Mwana wa Mulungu Aposa Angelo
1 Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. 2 Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. 3 Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero. 4 Mwanayu ndi wamkulu koposa angelo, monga momwe dzina limene analandira limaposa dzina la angelo.
5 Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati,
“Iwe ndiwe mwana wanga;
Ine lero ndakhala Atate ako.”
Kapena kunenanso kuti,
“Ine ndidzakhala abambo ake;
iye adzakhala mwana wanga.”
6 Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati,
“Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”
7 Iye ponena za angelo akuti,
“Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo,
amasandutsa atumiki ake malawi amoto.”
8 Koma za Mwana wake akuti,
“Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya,
ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.
9 Mwakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
Nʼchifukwa chake, Mulungu wanu wakukwezani kuposa anzanu
pokudzozani mafuta osonyeza chimwemwe.”
10 Mulungu akutinso,
“Ambuye, pachiyambi Inu munayika maziko a dziko lapansi;
ndipo zakumwambako ndi ntchito za manja anu.
11 Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu wachikhalire.
Izo zidzatha ngati zovala.
12 Mudzazipindapinda ngati chofunda;
ndipo zidzasinthidwa ngati chovala.
Koma Inu simudzasintha,
ndipo zaka zanu sizidzatha.”
13 Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti,
“Khala kudzanja langa lamanja
mpaka nditapanga adani ako
kukhale chopondapo mapazi ako.”
14 Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?
12 Efereimu amadya mpweya;
tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa
ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa.
Amachita mgwirizano ndi Asiriya
ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.
2 Yehova akuyimba mlandu Yuda;
Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake,
adzamulanga molingana ndi ntchito zake.
3 Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake;
iye atakula analimbana ndi Mulungu.
4 Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana;
analira napempha kuti amukomere mtima.
Mulungu anakumana naye ku Beteli
ndipo anayankhula naye kumeneko,
5 Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,
Yehova ndiye dzina lake lotchuka!
6 Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu;
pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama,
ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.
7 Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo;
iyeyo amakonda kubera anthu.
8 Efereimu amadzitama ponena kuti,
“Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri.
Palibe amene angandiloze chala
chifukwa cha kulemera kwanga.”
9 “Ine ndine Yehova Mulungu wako
amene ndinakutulutsa mu Igupto.
Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti,
monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.
10 Ndinayankhula ndi aneneri,
ndinawaonetsa masomphenya ambiri,
ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”
11 Kodi Giliyadi ndi woyipa?
Anthu ake ndi achabechabe!
Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala?
Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala
mʼmunda molimidwa.
12 Yakobo anathawira ku dziko la Aramu,
Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi,
ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.
13 Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto;
kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.
14 Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri.
Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa.
Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.
135 Tamandani Yehova.
Tamandani dzina la Yehova;
mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
2 amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova,
mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.
3 Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino;
imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
4 Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake,
Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.
5 Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu,
kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
6 Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,
kumwamba ndi dziko lapansi,
ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
7 Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi,
amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula
ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.
8 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
9 Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto,
kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
10 Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu
ndi kupha mafumu amphamvu:
11 Sihoni mfumu ya Aamori,
Ogi mfumu ya Basani,
ndi maufumu onse a ku Kanaani;
12 ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa,
cholowa cha anthu ake Aisraeli.
13 Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya,
mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
14 Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa,
ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.
15 Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
16 Pakamwa ali napo koma sayankhula
maso ali nawo, koma sapenya;
17 makutu ali nawo, koma sakumva
ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
18 Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo,
chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.
19 Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova;
inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova;
Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
21 Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni,
amene amakhala mu Yerusalemu.
Tamandani Yehova.
136 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino.
Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
2 Yamikani Mulungu wa milungu.
Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
3 Yamikani Ambuye wa ambuye,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
4 Iye yekhayo amene amachita zodabwitsa zazikulu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
5 Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
6 Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
7 Amene anapanga miyuni ikuluikulu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
8 Dzuwa lilamulire usana,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
9 Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
10 Amene anakantha ana woyamba kubadwa a Igupto,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
11 Natulutsa Israeli pakati pawo,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
12 Ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
13 Amene anagawa Nyanja Yofiira pakati,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
14 Nadutsitsa Israeli pakati pa nyanjayo,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
15 Koma anakokolola Farao ndi ankhondo ake mʼNyanja Yofiira,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
16 Amene anatsogolera anthu ake mʼchipululu
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
17 Amene anakantha mafumu akuluakulu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
18 Napha mafumu amphamvu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
19 Siloni mfumu ya Aamori,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
20 Ogi mfumu ya Basani,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
21 Napereka dziko lawo ngati cholowa,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
22 Cholowa cha mtumiki wake Israeli;
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
23 Amene anatikumbukira ife anthu opeputsidwa,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
24 Amene anatimasula kwa adani athu,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
25 Amene amapereka chakudya kwa cholengedwa chilichonse,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
26 Yamikani Mulungu wakumwamba,
pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.