M’Cheyne Bible Reading Plan
Apirikitsa Mitundu Ina ya Anthu
7 Pamene Yehova Mulungu wanu wakufikitsani mʼdziko limene mukukalowa ndi kulilanda ndi kuthamangitsa pamaso panu mitundu ya anthu iyi: Ahiti, Agirigasi, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi; yomwe ndi mitundu isanu ndi iwiri yayikulu ndi yamphamvu kuposa inu; 2 Yehova Mulungu wanu akadzawapereka mʼmanja mwanu, ndipo inu mukadzawagonjetsa, mudzawawononge kwathunthu. Musadzachite mgwirizano ndi anthuwo ndiponso musadzawachitire chifundo. 3 Musadzakwatirane nawo. Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna kapena kutenga ana anu aamuna ndi kuwapereka kwa ana awo aakazi. 4 Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu. 5 Koma mukachite izi: Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, mukadule mitengo yawo ya Asera, ndi kutentha mafano awo pa moto. 6 Pakuti inu ndinu anthu opatulika kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani pakati pa anthu onse pa dziko lapansi kuti mukhale ake, chuma chake cha mtengo wapatali.
7 Yehova sanakukondeni chifukwa choti munali ochuluka kuposa ena pakuti inuyo ndiye munali ochepetsetsa mwa anthu onse. 8 Koma chifukwa chakuti Yehova anakukondani nasunga lumbiro lake limene analumbira kwa makolo anu. Ndi chifukwa chake anakutulutsani ndi mphamvu yake yopanda malire ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo, kuchoka mʼmanja mwa Farao mfumu ya ku Igupto. 9 Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake. 10 Koma
iwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo;
sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye.
11 Choncho muziyesetsa kusunga malamulo, malangizo ndi maphunziro amene ndikukulamulani lero lino kuti muchite.
12 Mukamvera malamulo amenewa, ndi kusamala kuwatsata, ndiye kuti Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano lake la chikondi chosasinthika ndi inu, monga analumbira kwa makolo anu. 13 Iye adzakukondani nakudalitsani ndi kukuchulukitsani. Adzadalitsa chipatso cha mʼmimba mwanu, zokolola za mʼdziko mwanu, tirigu wanu, vinyo wanu ndi mafuta anu, ana angʼombe zanu ndi ana ankhosa zanu mʼdziko limene analumbirira kwa makolo anu kuti akupatseni inu. 14 Inu mudzadalitsika kuposa mtundu wina uliwonse wa anthu ndipo palibe mwamuna kapena mkazi aliyense pakati panu amene adzakhale wosabereka. Ziweto zanu nazonso, sipadzapezeka zosabereka. 15 Yehova adzakupewetsani ku matenda aliwonse. Sadzakugwetserani matenda owopsa aja munawadziwa ku Igupto, koma adzawagwetsera pa odana nanu. 16 Muwononge anthu onse amene Yehova Mulungu wanu awapereka kwa inu. Musawamvere chisoni ndipo musatumikire milungu yawo pakuti umenewo udzakhala msampha kwa inu.
17 Mukhoza kunena kuti, “Anthu awa ndi amphamvu kuposa ifeyo. Nanga tingawapirikitse bwanji?” 18 Koma musachite nawo mantha, kumbukirani bwino zimene Yehova Mulungu wanu anachita ndi Farao pamodzi ndi Igupto yense. 19 Munadzionera nokha ndi maso anu mayesero aakulu, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, mphamvu yake yopanda malire imene Yehova Mulungu wanu anakutulutsirani. Yehova Mulungu adzachita zimenezo ndi anthu onse amene muwaopa tsopano. 20 Kuwonjezera apo, Yehova Mulungu wanu adzatumiza mavu pakati pawo mpaka atamaliza onse amene adzakubisalirani. 21 Musaopsedwe nawo pakuti Yehova Mulungu wanu, amene ali pakati panu, ndi Mulungu wamkulu ndi woopsa. 22 Yehova Mulungu wanu adzapirikitsa anthu a mitundu yonse pamaso panu, pangʼonopangʼono. Sadzakulolani kuti muwathe nthawi imodzi, kuti nyama zakuthengo zingadzaswane mokuzungulirani. 23 Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu, adzawasokoneza kufikira atawonongedwa. 24 Iye adzapereka mafumu awo mʼdzanja lanu, ndipo adzafafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Palibe amene adzalimbana nanu, inu mudzawawononga. 25 Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo. 26 Musabweretse chinthu chonyansa mʼnyumba mwanu kuopa kuwonongedwa ngati chonyasacho. Muziyipidwa ndi kunyansidwa nacho kwambiri pakuti chidzawonongedwanso.
BUKU LACHINAYI
Masalimo 90–106
Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.
90 Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo
pa mibado yonse.
2 Mapiri asanabadwe,
musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,
kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.
3 Inu mumabwezera anthu ku fumbi,
mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
4 Pakuti zaka 1,000 pamaso panu
zili ngati tsiku limene lapita
kapena ngati kamphindi ka usiku.
5 Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,
iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
6 ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,
pofika madzulo wauma ndi kufota.
7 Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu;
ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.
8 Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu,
machimo athu obisika poonekera pamaso panu.
9 Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu;
timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.
10 Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70,
kapena 80 ngati tili ndi mphamvu;
komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa,
zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.
11 Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu?
Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.
12 Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,
kuti tikhale ndi mtima wanzeru.
13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
Achitireni chifundo atumiki anu.
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,
kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,
kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,
kukongola kwanu kwa ana awo.
17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.
Chimwemwe cha Opulumutsidwa
35 Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala;
dziko lowuma lidzakondwa
ndi kuchita maluwa. 2 Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka
lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe.
Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni,
maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni.
Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova,
ukulu wa Mulungu wathu.
3 Limbitsani manja ofowoka,
limbitsani mawondo agwedegwede;
4 nenani kwa a mitima yamantha kuti;
“Limbani mtima, musachite mantha;
Mulungu wanu akubwera,
akubwera kudzalipsira;
ndi kudzabwezera chilango adani anu;
akubwera kudzakupulumutsani.”
5 Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso
ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
6 Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala,
ndipo osayankhula adzayimba mokondwera.
Akasupe adzatumphuka mʼchipululu
ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
7 mchenga wotentha udzasanduka dziwe,
nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe.
Pamene panali mbuto ya ankhandwe
padzamera udzu ndi bango.
8 Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu;
ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika.
Anthu odetsedwa
sadzayendamo mʼmenemo;
zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
9 Kumeneko sikudzakhala mkango,
ngakhale nyama yolusa sidzafikako;
sidzapezeka konse kumeneko.
Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
10 Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera.
Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba;
kumeneko adzakondwa mpaka muyaya.
Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe,
ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Buku la Mwana Wankhosa
5 Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri. 2 Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?” 3 Koma panalibe ndi mmodzi yemwe kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena kunsi kwa dziko lapansi woti afutukule bukulo kapena kuona zamʼkati mwake. 4 Ndinalira kwambiri chifukwa panalibe amene anapezeka woyenera kufutukula bukuli kapena kuona zamʼkati mwake. 5 Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”
6 Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi. 7 Iye anabwera natenga buku lija limene linali mʼdzanja lamanja la wokhala pa mpando waufumuyo. 8 Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima. 9 Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti,
“Inu ndinu woyenera kulandira bukuli
ndi kumatula zomatira zake,
chifukwa munaphedwa,
ndipo magazi anu munagulira Mulungu
anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.
10 Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu,
ndipo adzalamulira dziko lapansi.”
11 Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja. 12 Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti,
“Mwana Wankhosa amene anaphedwayu
ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu,
ulemerero ndi mayamiko.”
13 Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti,
“Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa,
kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu
mpaka muyaya!”
14 Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.