Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 24-25

Magulu a Ansembe

24 Magulu a ana a Aaroni anali awa:

Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe. Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira. Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara. Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.

Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.

Maere woyamba anagwera Yehoyaribu,

achiwiri anagwera Yedaya,

achitatu anagwera Harimu,

achinayi anagwera Seorimu,

achisanu anagwera Malikiya,

achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,

10 achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi,

achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,

11 achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa,

a khumi anagwera Sekaniya,

12 a 11 anagwera Eliyasibu,

a 12 anagwera Yakimu,

13 a 13 anagwera Hupa,

a 14 anagwera Yesebeabu,

14 a 15 anagwera Biliga,

a 16 anagwera Imeri,

15 a 17 anagwera Heziri,

a 18 anagwera Hapizezi,

16 a 19 anagwera Petahiya,

a 20 anagwera Ezekieli,

17 a 21 anagwera Yakini,

a 22 anagwera Gamuli,

18 a 23 anagwera Delaya,

ndipo a 24 anagwera Maaziya.

19 Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.

Alevi Ena Onse

20 Za zidzukulu zina zonse za Levi:

Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli;

kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.

21 Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake:

Mtsogoleri anali Isiya.

22 Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti;

kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.

23 Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.

24 Mwana wa Uzieli: Mika;

kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.

25 Mʼbale wa Mika: Isiya;

kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.

26 Ana a Merari: Mahili ndi Musi.

Mwana wa Yaaziya: Beno.

27 Ana a Merari:

Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.

28 Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.

29 Kuchokera kwa Kisi:

Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.

30 Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti.

Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo. 31 Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.

Anthu Oyimba Nyimbo

25 Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi:

Kuchokera kwa ana a Asafu:

Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu.

Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake:

Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova.

Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake:

Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti. Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.

Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu. Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288. Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo.

Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe,
ana ndi abale ake.12
Maere achiwiri anagwera Gedaliya,
ndi abale ake ndi ana ake.12
10 Maere achitatu anagwera Zakuri,
ana ake ndi abale ake.12
11 Maere achinayi anagwera Iziri,
ana ake ndi abale ake.12
12 Maere achisanu anagwera Netaniya,
ana ake ndi abale ake.12
13 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya,
ana ake ndi abale ake.12
14 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela,
ana ake ndi abale ake.12
15 Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya,
ana ake ndi abale ake.12
16 Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya,
ana ake ndi abale ake.12
17 Maere a khumi anagwera Simei,
ana ake ndi abale ake.12
18 Maere a 11 anagwera Azareli,
ana ake ndi abale ake.12
19 Maere a 12 anagwera Hasabiya,
ana ake ndi abale ake.12
20 Maere a 13 anagwera Subaeli,
ana ake ndi abale ake.12
21 Maere a 14 anagwera Matitiya,
ana ake ndi abale ake.12
22 Maere a 15 anagwera Yeremoti,
ana ake ndi abale ake.12
23 Maere a 16 anagwera Hananiya,
ana ake ndi abale ake.12
24 Maere a 17 anagwera Yosibakasa,
ana ake ndi abale ake.12
25 Maere a 18 anagwera Hanani,
ana ake ndi abale ake.12
26 Maere a 19 anagwera Maloti,
ana ake ndi abale ake.12
27 Maere a 20 anagwera Eliyata,
ana ake ndi abale ake.12
28 Maere a 21 anagwera Hotiri,
ana ake ndi abale ake.12
29 Maere a 22 anagwera Gidaliti,
ana ake ndi abale ake.12
30 Maere a 23 anagwera Mahazioti,
ana ake ndi abale ake.12
31 Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri,
ana ake ndi abale ake12.
1 Petro 5

Akulu Ampingo ndi Anyamata mu Mpingo

Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo. Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,

“Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,
    koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”

Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.

10 Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba. 11 Kwa Iye kukhale mphamvu mpaka muyaya, Ameni.

Mawu Otsiriza

12 Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu. 13 Imani mwamphamvu mʼchisomochi. Mlongo wanu amene ali ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi nanu akupereka moni, nayenso Marko, mwana wanga, akupereka moni. 14 Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.

Mika 3

Atsogoleri ndi Aneneri Adzudzulidwa

Ndipo ine ndinati,

“Tamverani, inu atsogoleri a Yakobo,
    inu olamulira nyumba ya Israeli.
Kodi sindinu oyenera kudziwa kuweruza molungama,
    inu amene mumadana ndi zabwino ndi kukonda zoyipa;
inu amene mumasenda khungu la anthu anga,
    ndipo mumakungunula mnofu pa mafupa awo;
inu amene mumadya anthu anga,
    mumasenda khungu lawo
    ndi kuphwanya mafupa awo;
inu amene mumawadula nthulinthuli
    ngati nyama yokaphika?”

Pamenepo adzalira kwa Yehova,
    koma Iye sadzawayankha.
Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake
    chifukwa cha zoyipa zimene anazichita.

Yehova akuti,

“Aneneri amene
    amasocheretsa anthu anga,
ngati munthu wina awapatsa chakudya
    amamufunira ‘mtendere;’
ngati munthu wina sawapatsa zakudya
    amamulosera zoyipa.
Nʼchifukwa chake kudzakuderani,
    simudzaonanso masomphenya,
mdima udzakugwerani ndipo simudzawombezanso.
    Dzuwa lidzawalowera aneneriwo, ndipo mdima udzawagwera.
Alosi adzachita manyazi
    ndipo owombeza mawula adzanyazitsidwa.
Onse adzaphimba nkhope zawo
    chifukwa Mulungu sakuwayankha.”

Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu,
    ndi Mzimu wa Yehova,
    ndi kulungama, ndi kulimba mtima,
kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo,
    kwa Israeli za tchimo lake.
Imvani izi, inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo,
    inu olamulira nyumba ya Israeli,
inu amene mumadana ndi kuweruza kolungama;
    ndipo mumakhotetsa zinthu zonse zolondola;
10 inu amene mukumanga Ziyoni pokhetsa magazi,
    ndi Yerusalemu ndi kuyipa kwanu.
11 Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze,
    ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire,
    ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama.
Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti,
    “Kodi Yehova sali pakati pathu?
    Palibe tsoka limene lidzatigwere.”
12 Choncho chifukwa cha inu,
    Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
    ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.

Luka 12

Chenjezo ndi Chilimbikitso

12 Nthawi yomweyo, anthu miyandamiyanda atasonkhana, ndi kumapondanapondana, Yesu anayamba kuyankhula poyamba kwa ophunzira ake, nati, “Chenjereni ndi yisiti wa Afarisi, amene ndi chinyengo. Palibe chinthu chophimbika chimene sichidzawululika, kapena chobisika chimene sichidzadziwika. Chimene mwanena mu mdima chidzamveka dzuwa likuwala, ndipo zimene mwanongʼona mʼkhutu mʼchipinda chamʼkati, zidzayankhulidwa pa denga la nyumba.

“Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu. Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye. Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu. Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.

“Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu. Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu. 10 Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa.

11 “Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule, 12 pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.”

Fanizo la Munthu Wachuma Wopusa

13 Munthu wina mʼgulu la anthu anati kwa Iye, “Aphunzitsi, muwuzeni mʼbale wanga andigawireko chuma chamasiye.”

14 Yesu anayankha kuti, “Munthu iwe, ndani anandiyika Ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma pakati panu?” 15 Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”

16 Ndipo Iye anawawuza fanizo ili, “Munda wa munthu wina wachuma unabereka kwambiri. 17 Iye anaganiza kuti, ‘Ndichite chiyani? Ndilibe malo osungiramo mbewu zanga.’

18 “Ndipo Iye anati, ichi ndi chimene ndidzachite: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga zonse ndi kumanga zokulirapo, ndipo ndidzasungira mʼmenemo mbewu ndi katundu. 19 Ndipo ndidzawuza moyo wanga kuti, ‘Uli nazo zinthu zabwino zambiri zimene zikhalepo zaka zambiri, usapupulume; idya, imwa ndi kukondwera.’ ”

20 “Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’

21 “Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu.”

Musadere Nkhawa

22 Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala. 23 Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. 24 Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame. 25 Ndi ndani wa inu akhoza kuwonjeza ora pa moyo wake chifukwa cha kudandaula? 26 Popeza simungathe kuchita kanthu kakangʼono aka, nʼchifukwa chiyani mumadandaula ndi zinazi?

27 “Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa. 28 Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa! 29 Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. 30 Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. 31 Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.

Chuma cha Kumwamba

32 “Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu. 33 Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. 34 Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”

Kukhala a Atcheru

35 “Khalani okonzekeratu ndipo nyale zanu ziziyaka, 36 ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko. 37 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira. 38 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo adzawapeze ali okonzeka, ngakhale iye atabwera pa ora lachiwiri kapena lachitatu usiku. 39 Koma zindikirani izi: Ngati mwini nyumba akanadziwa ora limene mbala ibwera, sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe. 40 Inunso muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa ora limene simukumuyembekezera Iye.”

Wantchito Wokhulupirika ndi Wosakhulupirika

41 Petro anafunsa kuti, “Kodi mukunena fanizoli kwa ife, kapena kwa aliyense?”

42 Ambuye anayankha kuti, “Kodi tsono woyangʼanira wokhulupirika ndi wanzeru ndani? Kodi ndi amene mbuye wake wamuyika kukhala oyangʼanira antchito ake kuti aziwapatsa ndalama yachakudya pa nthawi yake yoyenera? 43 Zidzamukhalira bwino wantchito amene mbuye wake adzamupeza akuchita zimene pamene iye abwera. 44 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti adzamuyika kukhala woyangʼanira katundu wake yense. 45 Koma tiyerekeze kuti wantchitoyo aziganiza mu mtima mwake kuti, ‘Bwana wanga akuchedwa kwambiri kubwera,’ ndipo kenaka ndi kuyamba kumenya antchito aamuna ndi aakazi ndi kudya, kumwa ndi kuledzera. 46 Mbuye wake adzabwera tsiku limene iye sakumuyembekezera ndi ora limene iye sakudziwa. Iye adzamulanga ndi kumusiya kumalo kumene kuli osakhulupirira.

47 “Wantchito amene amadziwa chifuniro cha mbuye wake koma wosakonzeka kapena wosachita chimene mbuye wake akufuna adzakwapulidwa zikwapu zambiri. 48 Koma wantchito amene sadziwa koma nʼkuchita zinthu zoyenera chilango, adzakwapulidwa zikwapu zochepa. Aliyense amene anapatsidwa zambiri, adzayenera kubwezanso zambiri; ndipo amene anamusungitsa zambiri, adzamulamula kuti abweze zambirinso.”

Za Kugawikana

49 “Ine ndabwera kudzayatsa moto pa dziko lapansi, ndipo ndikanakonda ukanayaka kale. 50 Koma Ine ndiyenera kubatizidwa, ndipo ndikusautsika mu mtima mpaka utachitika! 51 Kodi mukuganiza kuti Ine ndinabwera kudzabweretsa mtendere pa dziko lapansi? Ayi, Ine ndikukuwuzani kuti, ndinabweretsa kugawikana. 52 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu. 53 Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”

Kumasulira Nthawi

54 Iye anati kwa gulu la anthu, “Pamene mukuona mtambo ukukwera kummawa, nthawi yomweyo inu mumati, ‘kugwa mvula,’ ndipo imagwadi. 55 Ndipo pamene mphepo yakummwera ikuwomba, inu mumati ‘kutentha’ ndipo kumaterodi. 56 Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?

57 “Bwanji simukuzindikira nokha zoyenera kuchita? 58 Pamene mukupita kwa woweruza ndi amene munalakwirana naye, yesetsani kwambiri kuti muyanjane naye mʼnjiramo, chifukwa mukapanda kutero akhoza kukutengerani ku bwalo la milandu ndipo woweruzayo adzakuperekani kwa woyangʼanira ndende, ndipo woyangʼanira ndendeyo adzakuponyani mʼndende. 59 Ine ndikuwuzani kuti, simudzatulukamo mpaka mutalipira ndalama zonse.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.