Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 23

Yosiya Akonzanso Pangano

23 Pamenepo mfumu inayitanitsa akuluakulu onse a ku Yuda ndi Yerusalemu. Mfumuyo inapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu ena onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inawerenga mawu onse a mʼBuku la Chipangano limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova, anthu onse akumva. Mfumu inayimirira pambali pa chipilala ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo, mawu ndi malangizo ake ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukwaniritsa mawu a mʼpanganoli, olembedwa mʼbukuli. Pamenepo anthu onse anadzipereka kutsatira panganoli.

Mfumu inalamula wansembe wamkulu Hilikiya, ansembe othandizana naye ndi alonda a pa khomo kuti achotse mʼNyumba ya Yehova ziwiya zonse zopembedzera Baala ndi Asera ndiponso mafano a zinthu zamlengalenga. Yosiya anazitentha kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Chigwa cha Kidroni ndipo phulusa lake anapita nalo ku Beteli. Iye anachotsa ansembe a mafano amene anayikidwa ndi mafumu a Yuda kuti azifukiza lubani ku malo opembedzera mafano a ku mizinda ya ku Yuda ndi kumalo ozungulira Yerusalemu, amene ankafukiza lubani kwa Baala, dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zonse zamlengalenga. Anachotsa fano la Asera mʼNyumba ya Yehova napita nalo kunja kwa Yerusalemu, ku Chigwa cha Kidroni, nalitentha kumeneko. Anapera fanolo ndi kukataya phulusa lake pa manda a anthu wamba. Iye anagwetsanso tinyumba ta ochita zachiwerewere, timene tinali mʼNyumba ya Yehova, kumene akazi ankalukirako mikanjo yovala popembedza Asera.

Yosiya anabweretsanso ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda, nawononga malo opembedzera mafano, kuyambira ku Geba mpaka ku Beeriseba, kumene ansembe ankafukizako lubani. Anagwetsa nyumba za milungu zimene zinali pa chipata cha Yoswa, bwanamkubwa wa mzindawo, kumanzere kwa chipata cha mzinda. Ngakhale kuti ansembe a ku malo opembedzera mafanowo sanawalole kuti atumikire pa guwa lansembe la Yehova mu Yerusalemu, koma ankadya buledi wopanda yisiti pamodzi ndi ansembe anzawo.

10 Mfumu Yosiya anawononganso Tofeti, amene anali ku Chigwa cha Hinomu, kuti wina aliyense asagwiritse ntchito malowo popereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto kwa Moleki. 11 Anachotsa pa chipata cholowera ku Nyumba ya Yehova akavalo amene mafumu a Yuda anawapereka ngati nsembe kwa dzuwa. Akavalo anali pafupi ndi bwalo la chipinda cha mkulu wina wotchedwa Natani-Meleki. Ndipo Yosiya anatentha magaleta opembedzera dzuwa.

12 Anagwetsa maguwa amene mafumu a Yuda anawamanga pa denga pafupi ndi chipinda chapamwamba cha Ahazi, ndiponso maguwa amene Manase anamanga mʼmabwalo awiri a Nyumba ya Yehova. Yosiya anawachotsa kumeneko nawaphwanya ndi kutaya zidutswa zake mʼChigwa cha Kidroni. 13 Mfumuyo inawononga malo opembedzera mafano amene ali kummawa kwa Yerusalemu cha kumpoto kwa Phiri la Chiwonongeko. Maguwawa Solomoni mfumu ya Israeli inamangira Asitoreti, fano lalikazi lonyansa la Asidoni, Kemosi, fano lonyansa la Amowabu, ndi Moleki, fano lonyansa la anthu a ku Amoni. 14 Yosiya anaphwanya miyala ya chipembedzo ndiponso anadula mitengo ya fano la Asera ndipo anakwirira malowo ndi mafupa a anthu.

15 Ngakhalenso guwa lansembe la ku Beteli, malo opembedzera mafano amene anapanga Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli, Yosiya anawononga guwalo ndi malo opembedzera mafanowo. Iye anatentha malo opembedzera mafanowo ndi kuwapera ndipo anatenthanso fano la Asera. 16 Kenaka Yosiya anayangʼanayangʼana ndipo ataona manda amene anali pomwepo, mʼmbali mwa phiri, analamula kuti afukule mandawo ndi kutulutsa mafupa kuti awatenthe paguwapo kuti alidetse, potsatira mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu analoseratu za zimenezi.

17 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi chizindikiro cha manda chimene ndikuwaonawo ndi chayani?”

Anthu a mu mzindamo anayankha kuti, “Ndi chizindikiro cha manda a munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda amene ananeneratu zimene inu mwalichita guwa lansembe la Beteli.”

18 Mfumuyo inati, “Alekeni manda amenewo, munthu asachotse mafupa ake.” Choncho anawasiya mafupa akewo pamodzi ndi mafupa a mneneri wa ku Samariya uja.

19 Monga momwe Yosiya anachitira ku Beteli, anachotsa ndi kuwononga nyumba za milungu zonse ndi malo opembedzera mafano amene mafumu anamanga mʼmizinda ya ku Samariya omwe anakwiyitsa Yehova. 20 Yosiya anapha ansembe onse amene ankatumikira ku malo opembedzera mafano, anawaphera pa maguwa awo ndi kutentha mafupa awo. Kenaka iye anapita ku Yerusalemu.

21 Mfumu inalamula anthu onse kuti, “Chitani Chikondwerero cha Paska kulemekeza Yehova Mulungu wanu, motsatira zomwe zalembedwa mʼBuku la Chipangano.” 22 Paska yotere inali isanachitikepo kuyambira nthawi ya oweruza amene anatsogolera Israeli, kapenanso nthawi yonse ya mafumu a Yuda sipanachitikenso Paska ngati imeneyo. 23 Koma mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, Paska imeneyi anachitira Yehova mu Yerusalemu.

24 Kuwonjezera apa, Yosiya anachotsa anthu a mawula, woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, milungu ya mʼnyumba, mafano ndiponso zinthu zonse zonyansa zopezeka mu Yuda ndi Yerusalemu. Iye anachita izi pokwaniritsa lamulo lolembedwa mʼbuku limene Hilikiya analipeza mʼNyumba ya Yehova. 25 Yosiyayo asanalowe ufumu, ngakhale atamwalira, panalibenso mfumu ina yofanana naye imene inatembenukira kwa Yehova monga anachitira, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse, motsatira Malamulo onse a Mose.

26 Komabe Yehova sanachotse mkwiyo wake woopsa, umene anali nawo pa Yuda chifukwa cha zonse zimene anachita Manase poputa mkwiyo wa Mulungu. 27 Choncho Yehova anati, “Ndidzawachotsanso anthu a ku Yuda pamaso panga monga ndinachotsera anthu a ku Israeli ndipo ndidzawukana mzinda wa Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha, pamodzi ndi Nyumba ino imene ndinati, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo.’ ”

28 Ntchito zina za Yosiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?

29 Yosiya akanali mfumu, Farao wotchedwa Neko, mfumu ya Igupto, anapita ku Mtsinje wa Yufurate kukathandiza mfumu ya ku Asiriya. Mfumu Yosiya anapita kukachita naye nkhondo, koma Neko anakumana naye ndi kumupha ku Megido. 30 Atumiki a Yosiyayo ananyamula mtembo wake mu galeta kuchokera ku Megido mpaka ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda akeake. Ndipo anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namudzoza, ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.

Yehowahazi Mfumu ya Yuda

31 Yehowahazi anakhala mfumu ali ndi 23 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Hamutali, mwana wa Yeremiya wa ku Libina. 32 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake. 33 Farao Neko anamuyika mʼndende ku Ribula mʼdziko la Hamati kuti asalamulirenso mu Yerusalemu. Farao analamula Yuda kuti azikhoma msonkho wa siliva wolemera makilogalamu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogalamu 34. 34 Farao Neko anayika Eliyakimu mwana wa Yosiya kuti akhale mfumu mʼmalo mwa abambo ake Yosiya, ndipo anasintha dzina lake kukhala Yehoyakimu. Koma iye anatenga Yehowahazi kupita naye ku Igupto ndipo anakafera kumeneko. 35 Yehoyakimu anapereka kwa Farao Neko siliva ndi golide amene anamufuna uja. Koma kuti iye apereke zimenezi, amankhometsa msonkho mʼdziko mwakemo ndipo amalandira siliva ndi golide kuchokera kwa anthu a mʼdzikomo molingana ndi chuma cha munthu aliyense.

Yehoyakimu Mfumu ya Yuda

36 Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Zebuda, mwana wa Pedaya wa ku Ruma. 37 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake.

Ahebri 5

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera. Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.

Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni. Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti,

“Iwe ndiwe Mwana wanga;
    Ine lero ndakhala Atate ako.”

Ndipo penanso anati,

“Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya,
    monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye. 10 Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.

Awachenjeza kuti Asataye Chikhulupiriro

11 Tili ndi zambiri zoti tinganene pa zimenezi, koma ndi zovuta kukufotokozerani chifukwa ndinu ochedwa kuphunzira. 12 Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba! 13 Aliyense amene amangodya mkaka okha, akanali mwana wakhanda, sakudziwa bwino chiphunzitso cha chilungamo. 14 Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.

Yoweli 2

Chilango cha Mulungu

Lizani lipenga mu Ziyoni.
    Chenjezani pa phiri langa loyera.
Onse okhala mʼdziko anjenjemere,
    pakuti tsiku la Yehova likubwera,
layandikira;
    tsiku la mdima ndi chisoni,
    tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.
Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri,
    gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera,
gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo
    ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
Patsogolo pawo moto ukupsereza,
    kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu.
Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni,
    kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu,
    kulibe kanthu kotsalapo.
Maonekedwe awo ali ngati akavalo;
    akuthamanga ngati akavalo ankhondo.
Akulumpha pamwamba pa mapiri
    ndi phokoso ngati la magaleta,
ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu,
    ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo.

Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima;
    nkhope iliyonse imagwa.
Amathamanga ngati ankhondo;
    amakwera makoma ngati asilikali.
Onse amayenda pa mizere,
    osaphonya njira yawo.
Iwo sakankhanakankhana,
    aliyense amayenda molunjika.
Amadutsa malo otchingidwa
    popanda kumwazikana.
Amakhamukira mu mzinda,
    amathamanga mʼmbali mwa khoma.
Amakwera nyumba ndi kulowamo;
    amalowera pa zenera ngati mbala.

10 Patsogolo pawo dziko limagwedezeka,
    thambo limanjenjemera,
dzuwa ndi mwezi zimachita mdima,
    ndipo nyenyezi zimaleka kuwala.
11 Yehova amabangula
    patsogolo pawo,
gulu lake lankhondo ndi losawerengeka,
    ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake.
Tsiku la Yehova ndi lalikulu;
    ndi loopsa.
    Ndani adzapirira pa tsikulo?

Ngʼambani Mtima Wanu

12 “Ngakhale tsopano,
    bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse
    posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.

13 Ngʼambani mtima wanu
    osati zovala zanu.
Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,
    pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka,
    ndipo amaleka kubweretsa mavuto.
14 Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni,
    nʼkutisiyira madalitso,
a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
    kwa Yehova Mulungu wanu.

15 Lizani lipenga mu Ziyoni,
    lengezani tsiku losala zakudya,
    itanitsani msonkhano wopatulika.
16 Sonkhanitsani anthu pamodzi,
    muwawuze kuti adziyeretse;
sonkhanitsani akuluakulu,
    sonkhanitsani ana,
    sonkhanitsani ndi oyamwa omwe.
Mkwati atuluke mʼchipinda chake,
    mkwatibwi atuluke mokhala mwake.
17 Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova,
    alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova.
Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu.
    Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka,
    kuti anthu a mitundu ina awalamulire.
Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti,
    ‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ”

Yankho la Yehova

18 Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lake
    ndi kuchitira chisoni anthu ake.

19 Yehova adzawayankha kuti,

“Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta
    ndipo mudzakhuta ndithu;
sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzo
    kwa anthu a mitundu ina.

20 “Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu,
    kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu,
gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa
    ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo.
Ndipo mitembo yawo idzawola,
    fungo lake lidzamveka.”

Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
21     Iwe dziko usachite mantha;
    sangalala ndipo kondwera.
Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.
22     Inu nyama zakuthengo, musachite mantha,
    pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira.
Mitengo ikubala zipatso zake;
    mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.
23 Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani,
    kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu,
pakuti wakupatsani
    mvula yoyambirira mwachilungamo chake.
Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka,
    mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.
24 Pa malo opunthira padzaza tirigu;
    mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta.

25 “Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe,
    dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono,
    dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka;
gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.
26 Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta,
    ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,
    amene wakuchitirani zodabwitsa;
ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.
27 Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli,
    kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
    ndi kuti palibenso wina;
ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.

Tsiku la Yehova

28 “Ndipo patapita nthawi,
    ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.
Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,
    nkhalamba zanu zidzalota maloto,
    anyamata anu adzaona masomphenya.
29 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi
    ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.
30 Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga
    ndi pa dziko lapansi,
    ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
31 Dzuwa lidzadetsedwa
    ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi
    lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye.
32 Ndipo aliyense amene adzayitana
    pa dzina la Ambuye adzapulumuka;
pakuti chipulumutso chidzakhala pa Phiri la Ziyoni
    ndi mu Yerusalemu,
    monga Yehova wanenera,
pakati pa otsala
    amene Yehova wawayitana.

Masalimo 142

Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero.

142 Ndikulirira Yehova mofuwula;
    ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo.
Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake;
    ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga,
    ndinu amene mudziwa njira yanga.
Mʼnjira imene ndimayendamo
    anthu anditchera msampha mobisa.
Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani;
    palibe amene akukhudzika nane.
Ndilibe pothawira;
    palibe amene amasamala za moyo wanga.

Ndilirira Inu Yehova;
    ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga,
    gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.”
Mverani kulira kwanga
    pakuti ndathedwa nzeru;
pulumutseni kwa amene akundithamangitsa
    pakuti ndi amphamvu kuposa ine.
Tulutseni mʼndende yanga
    kuti nditamande dzina lanu.

Ndipo anthu olungama adzandizungulira
    chifukwa cha zabwino zanu pa ine.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.