Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 15

Azariya Mfumu ya Yuda

15 Mʼchaka cha 27 cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 16 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu. Iyeyo anachita zabwino pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake. Komabe malo opembedzerako mafano sanawachotse ndipo anthu anapitirizabe kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.

Ndipo Yehova analanga mfumu ndi nthenda ya khate mpaka tsiku limene inamwalira. Tsono mfumuyo inkakhala mʼnyumba yakeyake yapadera. Mwana wake Yotamu ndiye amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu ndiponso ndiye amene ankalamulira anthu mʼdzikomo.

Ntchito zina za Azariya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Azariya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Zekariya Mfumu ya Israeli

Mʼchaka cha 38 cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira makolo ake. Iye sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.

10 Salumu mwana wa Yabesi anachitira chiwembu Zekariya. Anamukantha anthu akuona, namupha, ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake. 11 Ntchito zina za Zekariya, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli. 12 Awa ndiwo mawu a Yehova amene anayankhula kwa Yehu kuti, “Ana ako adzalamulira Israeli mpaka mʼbado wachinayi.”

Salumu Mfumu ya Israeli

13 Salumu mwana wa Yabesi anakhala mfumu mʼchaka cha 39 cha ulamuliro wa Uziya mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Samariya mwezi umodzi. 14 Ndipo Menahemu mwana wa Gadi anachoka ku Tiriza napita ku Samariya nakantha Salumu mwana wa Yabesi ku Samariya, namupha ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwake.

15 Ntchito zina za Salumu ndiponso za chiwembu chimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.

16 Nthawi imeneyo Menahemu, kuchokera ku Tiriza, anakathira nkhondo mzinda wa Tipisa ndi anthu onse amene anali mʼmenemo ndi dera lonse lozungulira chifukwa iwo anakana kutsekula zipata zawo. Iye anatenga katundu yense mu mzinda wa Tipisa ndi kutumbula akazi onse oyembekezera.

Menahemu Mfumu ya Israeli

17 Mʼchaka cha 39 cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira mu Samariya zaka khumi. 18 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Nthawi yonse ya ulamuliro wake sanasiye machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.

19 Tsono Puli mfumu ya ku Asiriya inadzathira nkhondo dzikolo ndipo Menahemu anapatsa Puliyo makilogalamu 34,000 a siliva kuti amuthandize ndi kulimbikitsa ufumu wake. 20 Menahemu anapeza ndalamazo kudzera mu msonkho umene ankakhometsa Aisraeli. Munthu aliyense wachuma ankapereka masekeli a siliva makumi asanu kwa mfumu ya ku Asiriya. Choncho mfumu ya ku Asiriya inabwerera ndipo sinakhalenso mʼdzikomo.

21 Ntchito zina za Menahemu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 22 Menahemu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Pekahiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Pekahiya Mfumu ya Israeli

23 Mʼchaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka ziwiri. 24 Pekahiya anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Iye sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, omwe anachimwitsa nawo Israeli. 25 Ndipo Peka mwana wa Remaliya, mtsogoleri wake wa ankhondo, anamuchita chiwembu. Iye pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi anapha Pekahiya pamodzi ndi Arigobu ndi Ariyeli mʼchipinda choteteza nyumba ya mfumu mu Samariya. Kotero Peka anapha Pekahiya ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.

26 Ntchito zina za Pekahiya ndi zonse zimene anachita zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.

Peka Mfumu ya Israeli

27 Mʼchaka cha 52 cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira zaka makumi awiri. 28 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.

29 Nthawi ya Peka mfumu ya Israeli, Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kudzalanda Iyoni, Abeli-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi ndi Hazori. Mfumu ya ku Asiriya inatenga Giliyadi ndi Galileya, kuphatikizanso madera onse a Nafutali ndipo anatumiza Aisraeli ku Asiriya. 30 Kenaka Hoseya mwana wa Ela anachitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya. Anamukantha ndi kumupha ndipo anakhala mfumu mʼmalo mwake mʼchaka makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.

31 Ntchito zina za Peka ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?

Yotamu Mfumu ya Yuda

32 Mʼchaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. 33 Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Amayi ake anali Yerusa mwana wa Zadoki. 34 Iye anachita zabwino pamaso pa Yehova monga anachitira Uziya abambo ake. 35 Komabe malo opembedzera mafano sanawachotse ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.

36 Ntchito zina za Yotamu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 37 (Nthawi imeneyo, Yehova anayamba kumatuma Rezini mfumu ya Aaramu ndi Peka mwana wa Remaliya kudzamenyana ndi Yuda). 38 Yotamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Ahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Tito 1

Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe. Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu.

Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse:

Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.

Ntchito ya Tito ku Krete

Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira. Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera. Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo. Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo. Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.

Kudzudzula Olephera Kuchita Bwino

10 Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. 11 Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo. 12 Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.” 13 Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona, 14 kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi. 15 Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa. 16 Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.

Hoseya 8

Israeli Akolola Kamvuluvulu

“Ika lipenga pakamwa pako.
    Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova
chifukwa anthu aphwanya pangano langa
    ndiponso agalukira lamulo langa.
Israeli akulirira kwa Ine kuti,
    ‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’
Koma Israeli wakana zabwino;
    mdani adzamuthamangitsa.
Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga.
    Amasankha akalonga popanda chilolezo changa.
Amadzipangira mafano
    asiliva ndi agolide
    koma adzawonongeka nawo.
Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe!
    Mkwiyo wanga wayakira anthuwo.
Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
    Mafanowa ndi ochokera ku Israeli!
Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso;
    si Mulungu amene anamupanga.
Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa,
    mwana wangʼombe wa ku Samariya.

“Aisraeli amadzala mphepo
    ndipo amakolola kamvuluvulu.
Tirigu alibe ngala;
    sadzabala chakudya.
Akanabala chakudya
    alendo akanadya chakudyacho.
Israeli wamezedwa,
    tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina
    ngati chinthu cha chabechabe.
Pakuti iwo anapita ku Asiriya
    ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha.
    Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.
10 Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu,
    Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.
Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa
    ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.

11 “Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo,
    maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.
12 Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga,
    koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.
13 Amapereka nsembe za nyama kwa Ine
    ndipo iwo amadya nyamayo,
    koma Yehova sakondwera nazo.
Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo
    ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo:
    iwowo adzabwerera ku Igupto.
14 Israeli wayiwala Mlengi wake
    ndipo wamanga nyumba zaufumu;
    Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga.
Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo,
    moto umene udzatenthe malinga awo.”

Masalimo 123-125

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

123 Ndikweza maso anga kwa Inu,
    kwa Inu amene mumakhala kumwamba.
Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo,
    monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake,
choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu,
    mpaka atichitire chifundo.

Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo,
    pakuti tapirira chitonzo chachikulu.
Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza,
    chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

124 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    anene tsono Israeli,
akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
    potiwukira anthuwo,
iwo atatipsera mtima,
    akanatimeza amoyo;
chigumula chikanatimiza,
    mtsinje ukanatikokolola,
madzi a mkokomo
    akanatikokolola.

Atamandike Yehova,
    amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame
    yokodwa mu msampha wa mlenje;
msampha wathyoka,
    ndipo ife tapulumuka.
Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

125 Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni,
    limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Monga mapiri azungulira Yerusalemu,
    momwemonso Yehova azungulira anthu ake
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala
    pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama,
kuti anthu olungamawo
    angachite nawonso zoyipa.

Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino,
    amene ndi olungama mtima
Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota,
    Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa.

Mtendere ukhale pa Israeli.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.