M’Cheyne Bible Reading Plan
Davide Awerenga Ankhondo Ake
21 Satana anafuna kuvutitsa Aisraeli choncho anawutsa mtima wa Davide kuti awerenge Aisraeli. 2 Choncho Davide anati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, “Pitani mukawerenge Aisraeli kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani. Ndipo mudzandiwuze kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”
3 Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?”
4 Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu, kotero Yowabu anapita mu Israeli monse ndipo kenaka anabwera ku Yerusalemu. 5 Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda.
6 Koma Yowabu sanaphatikizepo fuko la Levi ndi fuko la Benjamini pa chiwerengerochi, pakuti lamulo la mfumu linamuyipira. 7 Lamulo limeneli silinakomerenso Mulungu. Kotero Iye analanga Israeli.
8 Choncho Davide anati kwa Mulungu, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”
9 Yehova anati kwa Gadi, mlosi wa Davide, 10 “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ”
11 Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa Iye, “Yehova akuti, ‘Musankhepo chimene mungakonde kuti chichitike: 12 mʼdziko mukhale njala zaka zitatu, mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu, akukukanthani ndi lupanga la Yehova, kapena mʼdziko mukhale mliri kwa masiku atatu, mngelo wa Yehova akuwononga Israeli yense.’ Ndipo tsono ganizirani bwino chomwe ndikamuyankhe amene wandituma.”
13 Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ine andilange ndi Yehova, pakuti chifundo chake ndi chachikulu kwambiri; koma ndisalangidwe ndi anthu.”
14 Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000. 15 Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.
16 Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba.
17 Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.”
18 Pamenepo mngelo wa Yehova analamula Gadi kuti awuze Davide kuti akamange guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. 19 Ndipo Davide anapita pomvera mawu amene Gadi ananena mʼdzina la Yehova.
20 Pamene Arauna ankapuntha tirigu, anatembenuka ndipo anaona mngelo ndipo ana ake anayi aamuna amene anali naye anabisala. 21 Davide anayandikira, ndipo Arauna atayangʼana ndi kumuona, anachoka popunthira tirigupo ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi pamaso pa Davide.
22 Davide anati kwa Arauna, “Undipatse malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe, kuti mliri uli pa anthuwa usiye. Undigulitse ine pa mtengo woyenera ndithu.”
23 Arauna anati kwa Davide, “Tengani! Mbuye wanga mfumu achite chomukomera. Taonani ine ndidzapereka ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, zopunthira tirigu zidzakhala nkhuni ndipo tiriguyu adzakhala chopereka chachakudya. Ndidzapereka zonsezi.”
24 Koma mfumu Davide inayankha Arauna kuti, “Ayi, ine ndikuti ndipereka mtengo wathunthu. Sindingatenge chinthu chako ndi kuchipereka kwa Yehova, kapena kupereka nsembe imene sindinayigule.”
25 Choncho Davide analipira Arauna masekeli agolide 600 chifukwa cha malowo. 26 Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Iye anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anayankha potumiza moto pa guwa lansembe zopsereza kuchokera kumwamba.
27 Tsono Yehova anayankhula kwa mngelo, ndipo analowetsa lupanga lake mʼchimake. 28 Pa nthawi imeneyo, Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi, anapereka nsembe pamenepo. 29 Tenti ya Yehova imene Mose anapanga mʼchipululu, ndi guwa lansembe zopsereza pa nthawi imeneyi zinali pa phiri ku Gibiyoni. 30 Koma Davide sanathe kupita kumeneko kuti akapemphere pamaso pa Yehova, chifukwa amaopa lupanga la mngelo wa Yehova.
2 Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse. 2 Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu, 3 pakuti tsopano mwalawadi kuti Ambuye ndi wabwino.
Mwala wa Moyo ndi Anthu Osankhidwa
4 Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali, 5 inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu. 6 Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti,
“Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni,
wosankhika ndi wamtengowapatali.
Amene akhulupirira Iye
sadzachititsidwa manyazi.”
7 Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira,
“Mwala umene amisiri anawukana
wasanduka mwala wa maziko,
8 ndi
“Mwala wopunthwitsa anthu
ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.”
Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.
9 Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa. 10 Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
11 Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu. 12 Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.
Kugonjera Olamulira
13 Gonjerani maulamuliro onse chifukwa cha Ambuye. Kaya ndi mfumu, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro waukulu, 14 kaya ndi mabwanamkubwa, pakuti watumidwa ndi mfumu kuti alange onse amene amachita zoyipa ndi kuyamikira onse amene amachita zabwino. 15 Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa. 16 Mukhale monga mfulu, koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo ngati chophimbira zoyipa; mukhale monga atumiki a Mulungu. 17 Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu.
Akapolo
18 Inu akapolo, gonjerani ambuye anu ndi kuwachitira ulemu, osati kwa iwo okha amene ndi abwino ndi omvetsa zinthu, komanso kwa amene ndi ankhanza. 19 Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo. 20 Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu. 21 Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.
22 “Iye sanachite tchimo
kapena kunena bodza.”
23 Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama. 24 Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa. 25 Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.
Mkwiyo wa Yona ndi Chifundo cha Yehova
4 Koma Yona anakhumudwa kwambiri ndipo anakwiya. 2 Iye anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kodi izi si zimene ndinanena ndikanali kwathu? Nʼchifukwa chaketu ine ndinafulumira kuthawa kupita ku Tarisisi. Ine ndinadziwa kuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chopanda malire, Mulungu amene mumaleka kubweretsa tsoka. 3 Ndipo tsopano, Inu Yehova, ingondiphani basi, pakuti ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”
4 Koma Yehova anayankha kuti, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye?”
5 Yona anatuluka mu mzindamo nakakhala pansi cha kummawa kwa mzindawo. Kumeneko anadzimangira chithando nakhala mʼmenemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitikire mzindawo. 6 Tsono Yehova Mulungu anameretsa msatsi ndi kuyikulitsa kuti ipereke mthunzi kwa Yona kuchotsa mavuto ake; ndipo Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha msatsiyo. 7 Koma tsiku linalo mmawa, Mulungu anabweretsa mbozi imene inadya msatsiyo ndipo inafota. 8 Dzuwa litatuluka, Yehova anabweretsa mphepo yotentha yochokera kummawa, ndipo dzuwa linatentha pamutu pa Yona kotero analenguka nalo. Iye anangofuna atafa, ndipo anati, “Ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.”
9 Koma Mulungu anati kwa Yona, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye chifukwa cha msatsi?”
Iye anayankha kuti, “Inde nʼkoyenera. Kukwiya kwanga nʼkofuna kufa nako.”
10 Koma Yehova anati, “Iwe ukumvera chisoni msatsiwo, ngakhale kuti sunawugwirire ntchito kapena kuwukulitsa. Inamera pa usiku umodzi ndipo inafanso pa usiku umodzi. 11 Koma mu Ninive muli anthu opitirira 120,000 amene sadziwa kusiyanitsa kuti chabwino nʼchiti ndipo choyipa nʼchiti, mulinso ziweto zochuluka. Kodi sindiyenera kumvera chisoni mzinda waukulu ngati uwu?”
Yesu Atuma Ophunzira ake Khumi ndi Awiri
9 Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. 2 Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala. 3 Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera. 4 Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo. 5 Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.” 6 Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse.
7 Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa, 8 ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso. 9 Koma Herode anati, “Ine ndinamudula mutu Yohane. Nanga uyu ndani amene ndikumva zinthu zotere za Iye?” Ndipo iye anayesetsa kuti amuone Iye.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
10 Atumwi atabwerera, anamuwuza Yesu zimene anachita. Kenaka Iye anawatenga napita kwa okha ku mudzi wa Betisaida. 11 Koma gulu la anthu linadziwa ndipo anamutsatira. Iye anawalandira ndi kuyankhula nawo za ufumu wa Mulungu, ndi kuchiritsa amene amafuna machiritso.
12 Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, “Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo.”
13 Iye anayankha kuti, “Apatseni chakudya kuti adye.”
Iwo anayankha kuti, “Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa.” 14 (Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000).
Koma Iye anati kwa ophunzira ake, “Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu.” 15 Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi. 16 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu. 17 Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala.
Petro Avomereza Khristu
18 Nthawi ina pamene Yesu amapemphera malo a yekha ali ndi ophunzira ake, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?”
19 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati mmodzi wa aneneri akalekale waukanso.”
20 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu mumati Ine ndine yani?”
Petro anayankha kuti, “Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Mulungu.”
Yesu Aneneratu za Imfa yake
21 Yesu anawachenjeza kwambiri kuti asawuze wina aliyense za izi. 22 Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”
23 Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine. 24 Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa. 25 Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini? 26 Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera. 27 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu.”
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
28 Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera. 29 Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri. 30 Anthu awiri, Mose ndi Eliya, 31 anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu. 32 Petro ndi anzake anali ndi tulo tambiri, koma atadzuka, iwo anaona ulemerero wake ndi anthu awiri atayima pamodzi ndi Iye. 33 Pamene anthuwo ankamusiya Yesu, Petro anati kwa Iye, “Ambuye, ndi chabwino kwa ife kuti tikhale pano. Tiloleni kuti timange misasa itatu, umodzi wanu, umodzi wa Mose ndi umodzi wa Eliya.” (Iye sanadziwe chimene amayankhula).
34 Pamene Iye ankayankhula, mtambo unaonekera ndi kuwaphimba iwo, ndipo anachita mantha pamene mtambowo unawakuta. 35 Mawu anachokera mu mtambomo nati, “Uyu ndi Mwana wanga amene ndamusankha; mumvereni Iye.” 36 Atamveka mawuwa, anaona kuti Yesu anali yekha. Ophunzirawo anazisunga izi mwa iwo okha ndipo sanawuze wina aliyense pa nthawiyi za zomwe iwo anaziona.
Kuchiritsidwa kwa Mwana Wogwidwa ndi Chiwanda
37 Mmawa mwake, akutsika ku phiri, anthu ambiri anakumana naye. 38 Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, “Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu. 39 Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga. 40 Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera.”
41 Yesu anayankha kuti, “Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno.”
42 Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake. 43 Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu.
Yesu Abwereza Kunena za Imfa yake
Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake, 44 “Tamvetsetsani zimene ndikufuna kukuwuzani: Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.” 45 Koma iwo sanazindikire zimene amatanthauza. Izi zinawadabwitsa kotero sanathe kuzimvetsa ndipo anaopa kumufunsa.
Wamkulu Ndani?
46 Mkangano unayambika pakati pa ophunzira wa kuti wamkulu koposa akanakhala ndani mwa iwo. 47 Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake. 48 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”
49 Yohane anati, “Ambuye, ife tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo tinayesa kumuletsa, chifukwa iyeyo si mmodzi wa ife.”
50 Yesu anati, “Wosamuletsa, pakuti amene satsutsana nanu ali mbali yanu.”
A Samariya Akana Yesu
51 Nthawi itayandikira yoti Iye atengedwe kupita kumwamba, Yesu anatsimikiza zopita ku Yerusalemu, 52 ndipo anatuma nthumwi kuti zitsogole. Iwo anapita mʼmudzi wa Asamariya kuti akonzekere kumulandira, 53 koma anthu kumeneko sanamulandire chifukwa Iye ankapita ku Yerusalemu. 54 Ophunzira awa, Yohane ndi Yakobo ataona zimenezi, anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukufuna ife tiyitane moto kuchokera kumwamba kuti uwawononge?” 55 Koma Yesu anatembenuka ndi kuwadzudzula, 56 ndipo iwo anapita ku mudzi wina.
Kutsatira Yesu
57 Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, “Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita.”
58 Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake.”
59 Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.”
Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.”
60 Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”
61 Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.”
62 Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.