M’Cheyne Bible Reading Plan
Samsoni Abwezera Afilisti
15 Patapita nthawi, mu nyengo yodula tirigu, Samsoni anatenga kamwana kambuzi ndipo anapita kukacheza kwa mkazi wake. Iye anati, “Ndikufuna kukalowa ku chipinda cha mkazi wanga.” Koma abambo a mkaziyo anamuletsa kutero.
2 Abambo a mkaziyo anati, “Ine ndimaganiza kuti umamuda kwambiri nʼchifukwa chake ndinamupereka kwa mnzako. Kodi mngʼono wake uja sindiye wokongola kupambana iye? Ingotengani ameneyo mʼmalo mwake.”
3 Samsoni anawawuza kuti, “Pano sindikhala wochimwa ndikawachita choyipa chachikulu Afilistiwa.” 4 Choncho Samsoni anapita nakagwira nkhandwe 300 nazimangirira michira ziwiriziwiri ndipo pa fundo iliyonse ya michirayo anamangirira nsakali. 5 Anayatsa nsakalizo kenaka ndi kuzitayira nkhandwe zija mʼminda ya tirigu ya Afilisti, ndipo zinatentha milu ya tirigu, ndi wosadula yemwe pamodzi ndi mitengo ya mpesa ndi ya olivi.
6 Tsono Afilisti anayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita izi?” Ena anati, “Ndi Samsoni mkamwini wa munthu wa ku Timna uja chifukwa Mtimunayo anatenga mkazi wake ndi kumupereka kwa mnzake.”
Choncho Afilisti anapita kukatentha mtsikanayo pamodzi ndi abambo ake. 7 Samsoni anawawuza kuti, “Ngati mumachita zangati zimenezi, ndiye ine sindileka mpaka nditakulipsirani.” 8 Choncho Samsoni anamenyana nawo koopsa ndipo anapha ambiri a iwo. Kenaka anakalowa mʼphanga la Etamu, nakhala momwemo.
9 Pambuyo pake Afilisti anakamanga misasa ya nkhondo mʼdziko la Yuda, ndi kuthira nkhondo mʼdera la Lehi. 10 Anthu a fuko la Yuda anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzamenyana nafe?”
Iwo anayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samsoni ndi kuti timuchite zofanana ndi zimene anatichita.”
11 Ndipo anthu 3,000 a ku Yuda anapita ku phanga la Etamu, ndi kukamufunsa Samsoni kuti, “Kodi iwe sudziwa kuti ife amatilamulira ndi Afilisti? Tsono ndi chiyani chimene watichitachi?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndinachita zomwe iwo anandichita.”
12 Iwo anati kwa iye, “Ife tabwera kuti tikumange ndi kukupereka kwa Afilisti.”
Ndipo Samsoni anati, “Lonjezani mwa lumbiro kuti simundipha ndinu.”
13 Iwo anamuyankha kuti, “Ayi, ife sitikupha. Koma tingokumanga ndi kukupereka mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano namutulutsa mʼphanga muja. 14 Samsoni anafika ku Lehi, ndipo Afilisti anamuchingamira akufuwula. Nthawi yomweyo Mzimu wa Yehova unatsika pa iye mwamphamvu ndipo zingwe zimene anamumanga nazo zinasanduka ngati thonje lopsa mʼmoto, zinachita ngati zasungunuka nʼkuchoka mʼmanja mwake. 15 Anapeza chibwano cha bulu amene anali atangofa kumene. Anachitola ndi kuphera nacho anthu 1,000.
16 Ndipo Samsoni anati,
“Ndi chibwano cha bulu,
milu ndi milu ya anthu.
Ndi chibwano cha bulu,
ndapha anthu 1,000.”
17 Atatsiriza kuyankhula, anataya chibwanocho, ndipo malowo anawatcha Ramati-Lehi.
18 Pambuyo pake anamva ludzu kwambiri ndipo anayitana Yehova mopempha kuti, “Inu mwapatsa mtumiki wanu chipulumutso chachikulu chotere. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osachita mdulidwewa?” 19 Pamenepo Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi, ndipo madzi anatuluka mʼdzenjemo. Samsoni anamwa madziwo, ndipo mphamvu zake zinabwerera nakhalanso monga analili. Choncho chitsimecho chinatchedwa Eni-Hakore, ndipo chilipobe ku Lehiko mpaka lero.
20 Samsoni anatsogolera Israeli pa nthawi ya Afilisti kwa zaka makumi awiri.
Paulo ku Efeso
19 Apolo ali ku Korinto, Paulo anadutsa mʼmayiko a ku mtunda ndipo anafika ku Efeso. Kumeneko anapeza ophunzira ena. 2 Iye anawafunsa kuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira?”
Iwo anayankha kuti, “Ayi, ife sitinamvepo kuti kuli Mzimu Woyera.”
3 Tsono Paulo anawafunsa kuti, “Nanga munabatizidwa ndi ubatizo wotani?”
Iwo anati, “Ubatizo wa Yohane.”
4 Paulo anati, “Ubatizo wa Yohane unali wa kutembenuka mtima. Iye anawuza anthu kuti akhulupirire amene amabwera, ameneyo ndiye Yesu.” 5 Atamva zimenezi, anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 6 Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera. 7 Anthu onsewo analipo khumi ndi awiri.
8 Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu. 9 Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano. 10 Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, kotero kuti Ayuda onse ndi Agriki amene amakhala ku Asiya anamva Mawu a Ambuye.
11 Mulungu anachita zodabwitsa zapadera kudzera mwa Paulo. 12 Kotero kuti mipango yopukutira thukuta ndi yovala pogwira ntchito, zomwe zinakhudza thupi la Paulo amapita nazo kwa odwala ndipo amachiritsidwa ndiponso mizimu yoyipa mwa iwo imatuluka.
Za Ana a Skeva
13 Ayuda ena amene ankayendayenda kutulutsa mizimu yoyipa anayesa kugwiritsa ntchito dzina la Ambuye Yesu pa amene anali ndi ziwanda. Iwo popemphera amati, “Ine ndikulamulira utuluke, mʼdzina la Yesu amene Paulo amamulalikira.” 14 Amene ankachita zimenezi anali ana asanu ndi awiri a Skeva, mkulu wa ansembe wa Chiyuda. 15 Tsiku lina mzimu woyipa unawayankha kuti, “Yesu ndimamudziwa ndiponso Paulo ndimamudziwa, nanga inu ndinu ndani?” 16 Pamenepo munthu amene anali ndi mzimu woyipa anawalumphira nawagwira onse. Iye anawamenya kwambiri, kotero kuti anathawa mʼnyumbamo ali maliseche, akutuluka magazi.
17 Ayuda ndi Agriki okhala ku Efeso atamva zimenezi, anachita mantha, ndipo anthu anachitira ulemu dzina la Ambuye Yesu koposa. 18 Ambiri a iwo amene tsopano anakhulupirira anafika ndi kuvomereza poyera ntchito zawo zoyipa. 19 Ambiri amene amachita za matsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi nawatentha pamaso pa anthu onse. Atawonkhetsa mtengo wa mabukuwo, unakwanira ndalama zasiliva 50,000. 20 Kotero Mawu a Ambuye anapitirira kufalikira ndipo anagwira ntchito mwamphamvu.
21 Zonsezi zitachitika Paulo anatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Makedoniya ndi ku Akaya. Iye anati, “Kuchokera kumeneko, ndiyenera kukafikanso ku Roma.” 22 Iye anatuma anthu awiri amene amamuthandiza, Timoteyo ndi Erasto ku Makedoniya, pamene iye anakhalabe ku Asiya kwa kanthawi.
Chipolowe ku Efeso
23 Pa nthawi yomweyo panachitika chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye. 24 Mmisiri wantchito zasiliva, dzina lake Demetriyo, amene amapanga mafano asiliva a Atemi ankabweretsa phindu lalikulu kwa amisiri a kumeneko. 25 Iye anasonkhanitsa pamodzi amisiriwo, pamodzinso ndi anthu ena ogwira ntchito yomweyo ndipo anati, “Anthu inu, mukudziwa kuti ife timapeza chuma chathu kuchokera pa ntchito imeneyi. 26 Ndipo inu mukuona ndi kumva kuti munthu uyu Paulo wakopa ndi kusokoneza anthu ambiri a ku Efeso ndiponso pafupifupi dziko lonse la Asiya. Iye akunena kuti milungu yopangidwa ndi anthu si milungu ayi. 27 Choopsa ndi chakuti sikungowonongeka kwa ntchito yathu yokha ayi, komanso kuti nyumba ya mulungu wamkulu wamkazi Atemi idzanyozedwa ndipo mulungu wamkazi weniweniyo amene amapembedzedwa ku Asiya konse ndi dziko lapansi, ukulu wake udzawonongekanso.”
28 Atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anayamba kufuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi.” 29 Nthawi yomweyo mu mzinda wonse munabuka chipolowe. Anthu anagwira Gayo ndi Aristariko, anzake a Paulo a ku Makedoniya, ndipo anathamangira nawo ku bwalo la masewero. 30 Paulo anafuna kulowa pakati pa gulu la anthu, koma ophunzira anamuletsa. 31 Ngakhale olamulira ena aderalo, amene anali abwenzi a Paulo, anatumiza uthenga kumuletsa kuti asayesere kulowa mʼbwalomo.
32 Munali chisokonezo mʼbwalomo pakuti ena amafuwula zina, enanso zina. Anthu ambiri sanadziwe ngakhale chomwe anasonkhanira. 33 Ayuda anamukankhira Alekisandro kutsogolo, ndipo ena anafuwula kumulangiza iye. Iye anatambasula dzanja kuti anthu akhale chete kuti afotokozere anthu nkhaniyo. 34 Koma pamene anthuwo anazindikira kuti ndi Myuda, onse pamodzi kwa maora awiri anafuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi wa ku Efeso!”
35 Mlembi wa mzindawo anakhazikitsa bata gulu la anthuwo ndipo anati, “Anthu a ku Efeso, kodi ndani pa dziko lonse lapansi amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso umayangʼanira nyumba ya mulungu wamkulu Atemi ndi fanizo lake, limene linagwa kuchokera kumwamba? 36 Chifukwa chake popeza zinthu izi palibe amene angazikane, inu mukuyenera kukhala chete osachita kanthu kalikonse mofulumira. 37 Inu mwabweretsa anthu awa pano, ngakhale kuti iwo sanabe mʼnyumba zathu zamapemphero kapena kunenera chipongwe mulungu wathu wamkazi. 38 Ngati tsono Demetriyo ndi amisiri anzake ali ndi nkhani ndi munthu wina aliyense, mabwalo a milandu alipo, oweruza aliponso. Akhoza kukapereka nkhaniyo kwa oweruza milanduwo. 39 Ngati mukufuna kubweretsa kanthu kali konse, ziyenera kukatsimikizidwa ndi bwalo lovomerezeka. 40 Monga mmene zililimu, ife titha kuzengedwa mlandu woyambitsa chipolowe chifukwa cha zimene zachitika lerozi. Motero ife sitingathe kufotokoza za chipolowechi popeza palibe nkhani yake.” 41 Iye atatha kunena zimenezi anawuza gulu la anthulo kuti libalalike.
Hananiya Atsutsana ndi Yeremiya
28 Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinayi, poyambirira pa ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, amene amachokera ku Gibiyoni, anandiwuza ine mʼNyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti, 2 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni. 3 Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni. 4 Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ”
5 Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anasonkhana mʼNyumba ya Yehova. 6 Anati, “Ameni! Yehova achitedi zomwezo! Yehova akwaniritse mawu amene waloserawo. Iye abweretsenso pa malo pano ziwiya za mʼNyumba ya Yehova ndi akapolo onse kuchokera ku Babuloni. 7 Komabe, tamvera zimene nditi ndikuwuze iweyo pamodzi ndi anthu onse: 8 Kunali aneneri kalelo, ine ndi iwe tisanabadwe. Iwowa analosera za nkhondo, mavuto ndi mliri kuti zidzagwera mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu. 9 Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”
10 Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola, 11 ndipo anawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Umu ndi mmene ndidzathyolere goli la Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonse pasanathe zaka ziwiri.’ ” Zitatero, mneneri Yeremiya anachoka.
12 Patapita nthawi pangʼono, mneneri Hananiya atathyola goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anawuza Yeremiya kuti, 13 “Pita, kawuze mneneri Hananiya kuti, ‘Yehova akuti: Iwe wathyola goli lamtengo, mʼmalo mwake Ine ndidzayika goli lachitsulo. 14 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo iwo adzamutumikiradi. Ndipo ndamupatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”
15 Ndipo mneneri Yeremiya anawuza mneneri Hananiya kuti, “Tamvera, Hananiya! Iweyo Yehova sanakutume, koma iwe wanyenga anthuwa kuti akhulupirire zabodza. 16 Nʼchifukwa chake Yehova akuti, ‘Ndatsala pangʼono kukuchotsa pa dziko lapansi. Iwe ufa chaka chino chisanathe, chifukwa wakhala ukulalikira zowukira Yehova.’ ”
17 Mʼmwezi wachisanu ndi chiwiri wa chaka chomwecho, mneneri Hananiya anamwaliradi.
Yesu Adzozedwa ku Betaniya
14 Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha. 2 Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”
3 Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.
4 Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? 5 Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.
6 Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 7 Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 8 Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 9 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”
10 Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu. 11 Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.
Mgonero wa Ambuye
12 Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”
13 Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye. 14 Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’ 15 Iye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.”
16 Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.
17 Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo. 18 Pamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.”
19 Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”
20 Iye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine. 21 Mwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
22 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”
23 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.
24 Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri. 25 Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”
26 Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.
Yesu Aneneratu zakuti Petro Adzamukana
27 Yesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa:
“ ‘Kantha Mʼbusa,
ndipo nkhosa zidzabalalika.’
28 Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”
29 Petro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.”
30 Yesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.”
31 Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.
Mu Getsemani
32 Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.” 33 Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima. 34 Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.”
35 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire. 36 Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”
37 Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi? 38 Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”
39 Kenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi. 40 Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.
41 Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. 42 Nyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!”
Amugwira Yesu
43 Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.
44 Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.” 45 Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona. 46 Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga. 47 Kenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake.
48 Yesu anati, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira, kuti mubwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? 49 Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.” 50 Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.
51 Mnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira, 52 anathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo.
Yesu ku Bwalo la Milandu
53 Anamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi. 54 Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.
55 Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse. 56 Ambiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane.
57 Kenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti, 58 “Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ” 59 Ngakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane.
60 Kenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?” 61 Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe.
Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?”
62 Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”
63 Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso? 64 Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?”
Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa. 65 Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.
Petro Akana Yesu
66 Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera. 67 Ataona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa.
Iye anati, “Iwenso unali pamodzi ndi Mnazareti, Yesu.”
68 Koma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata.
69 Pamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.” 70 Anakananso kachiwiri.
Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.”
71 Iye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.”
72 Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.