Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 9

Samueli Adzoza Sauli

Panali munthu wina wa fuko la Benjamini, wotchuka, dzina lake Kisi, mwana wa Abieli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. Iyeyu anali ndi mwana dzina lake Sauli, mnyamata wa maonekedwe abwino. Pakati pa Aisraeli onse panalibe wofanana naye. Anali wamtali kotero kuti anthu onse ankamulekeza mʼmapewa.

Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.” Choncho iwo anadutsa dziko la mapiri a Efereimu ndi dera la Salisa, koma sanawapeze. Anadutsa ku Saalimu koma abuluwo sanawapeze. Kenaka anadutsa dziko la Benjamini, koma osawapezabe.

Atafika ku dera la Zufi, Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Tiye tibwerere, mwina abambo anga angasiye kudandaula za abulu ndipo adzayamba kudandaula za ife.”

Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.”

Sauli anafunsa mnyamata wake kuti, “Tikapita tikamupatsa chiyani munthuyo pakuti chakudya chimene chinali mʼmatumba mwathu chatha? Tilibe mphatso iliyonse yoti timutengere munthu wa Mulungu. Nanga tili ndi chiyani?”

Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.” (Kale mu Israeli ngati munthu afuna kukapempha nzeru kwa Mulungu ankanena kuti, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene lero akutchedwa mneneri, kale ankatchedwa mlosi).

10 Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo.

11 Akukwera phiri kupita ku mzindawo anakumana ndi atsikana akutuluka mu mzindamo kukatunga madzi, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?”

12 Iwo anayankha, “Inde alipo. Ali kutsogolo kwanuku, fulumirani tsopano, wangobwera kumene mu mzinda wathu uno lero, chifukwa lero anthu akupereka nsembe ku phiri. 13 Mukangolowa mu mzindawo mumupeza asanapite ku phiri kukadya. Anthu sangayambe kudya iye asanabwere chifukwa iyeyu ayenera kudalitsa nsembeyo. Kenaka anthu oyitanidwa adzayamba kudya. Pitani tsopano, chifukwa muyenera kumupeza nthawi ino.”

14 Choncho anapita ku mzinda kuja. Akulowa mu mzindamo, anaona Samueli akutuluka mu mzindamo akubwera kumene kunali iwo, koma amapita ku phiri, ku malo wopatulika.

15 Koma chadzulo lake Sauli asanafike, Yehova anali atamuwuza kale Samueli za zimenezi kuti, 16 “Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”

17 Samueli atamuona Sauli, Yehova anamuwuza kuti, “Munthu ndinakuwuza uja ndi uyu. Iyeyu adzalamulira anthu anga.”

18 Tsono Sauli anayandikira Samueli pa chipata ndipo anamufunsa, “Kodi mungandiwuze kumene kuli nyumba ya mlosi?”

19 Samueli anayankha, “Ine ndine mlosiyo. Tsogolani kupita ku phiri pakuti lero mudya ndi ine, ndipo mawa mmawa ndidzakuwuzani zonse zimene zili mu mtima mwanu. 20 Musadere nkhawa za abulu anu amene akhala akusowa masiku atatu apitawa, poti apezeka kale. Kodi Aisraeli onse akufunitsitsa ndani? Kodi si ndiwe ndi nyumba yonse ya abambo ako?”

21 Sauli anayankha, “Inetu ndine Mbenjamini, fuko lalingʼono la mafuko onse a Israeli, ndipo banja langa ndi lalingʼono pakati pa mabanja a fuko la Benjamini. Nanga nʼchifukwa chiyani mukunena zimenezi kwa ine?”

22 Ndipo Samueli anatenga Sauli ndi mnyamata wake uja ndi kulowa nawo mʼchipinda chachikulu ndipo anawakhazika kutsogolo kwa anthu oyitanidwa. Onse pamodzi analipo anthu makumi atatu. 23 Tsono Samueli anati kwa wophika, “Bwera nayo nyama imene ndinakupatsa, imene ndinakuwuza kuti uyisunge pambali.”

24 Kotero wophikayo anatenga mwendo wa nyama ndipo anawuyika patsogolo pa Sauli. Samueli anati “Nayi nyama imene ndinakusungira kuti pa nthawi yake udye pamodzi ndi anthu amene ndawayitana.” Ndipo Sauli anadya tsiku limenelo ndi Samueli.

25 Atatsika kuchoka ku phiri kuja, Samueli anamukonzera Sauli malo ogona pa denga la nyumba yake, ndipo Sauli anagona pamenepo. 26 Tsono mʼbandakucha Samueli anayitana Sauli pa dengapo nati, “Konzeka ndipo ine ndikuperekeza.” Choncho Sauli anadzuka ndipo onse awiri, Samueli ndi Sauli anakalowa mu msewu. 27 Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, “Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu.”

Aroma 7

Chitsanzo cha Banja pa Mphamvu za Malamulo

Kodi simukudziwa abale kuti Malamulo ali ndi ulamuliro pa munthu pokhapokha ngati ali ndi moyo? Ine ndikuyankhula kwa anthu amene akudziwa Malamulo. Mwachitsanzo, Malamulo amati mkazi wokwatiwa ndi womangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wakeyo nthawi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma ngati mwamuna wake amwalira, mkaziyo ndi womasulidwa ku lamulo la ukwati. Koma ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina pamene mwamuna wake ali moyo, amatchedwa wachigololo. Koma ngati mwamuna wakeyo amwalira, mkaziyo amasuka ku lamulo ndipo si wachigololo, ngakhale kuti wakwatiwa ndi mwamuna wina.

Chimodzimodzi inunso, abale anga, munafa ku Malamulo kudzera mʼthupi la Khristu, kuti mukwatiwe ndi wina, ndi Iye amene anauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu chipatso. Pakuti pamene tinkalamulidwa ndi khalidwe lathu lauchimo, zilakolako zauchimo zimene Malamulo anaziwutsa zinkagwira ntchito mʼmatupi mwathu kotero kuti zinabala imfa. Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa.

Kulimbana ndi Mphamvu za Tchimo

Nanga ife tinene chiyani? Kodi Malamulo ndi oyipa? Ayi. Nʼkosatheka! Kunena zoona, popanda Malamulo, ine sindikanazindikira tchimo. Pakuti sindikanadziwa kuti kusirira ndi tchimo ngati Malamulo sakananena kuti, “Usasirire.” Koma chifukwa cha Malamulo uchimo unapeza mwayi owutsa mʼkati mwanga khalidwe lililonse la kusirira. Pakuti pakanapanda Malamulo, uchimo ukanakhala wopanda mphamvu. Nthawi ina ndinali ndi moyo popanda Malamulo. Koma nditayamba kudziwa Malamulo, pomwepo uchimo unayamba kuphuka, 10 ndipo ine ndinafa. Ine ndinazindikira kuti Malamulo omwe ankayenera kubweretsa moyo anabweretsa imfa.

11 Pakuti uchimo unapeza mwayi chifukwa cha Malamulo ndipo kudzera mʼMalamulowo, unandinyenga ndi kundiyika mu imfa. 12 Choncho lamulo ndi loyera, lolungama ndi labwino. 13 Kodi chomwe ndi chabwino tsopano chinasanduka imfa kwa ine? Si choncho ayi! Koma kuti uchimo uzindikirike kuti ndi uchimo unabala imfa mwa ine kudzera mu chomwe chinali chabwino, kotero kuti kudzera mu lamulo uchimo ukhale oyipa kopitirira.

14 Ife tikudziwa kuti Malamulo ndi auzimu; koma ine ndine munthu wofowoka chabe, wogulitsidwa ngati kapolo ku uchimo. 15 Ine sindizindikira zimene ndimachita. Pakuti zimene ndimafuna kuchita sindizichita koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimazichita. 16 Ndipo ngati ndimachita zimene sindimafuna kuzichita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti lamulo ndi labwino. 17 Monga mmene zililimu, si inenso mwini amene ndimazichita zimenezi, koma tchimo limene lili mʼkati mwanga. 18 Ine ndikudziwa kuti mwa ine mulibe kanthu kabwino, ndiye kuti mʼthupi langa lauchimo. Pakuti ndimafuna kuchita zabwino, koma ndimalephera kuzichita. 19 Ine sindichita zabwino zimene ndimafuna koma ndimachita zonyansa zimene sindikuzifuna. 20 Tsopano ngati ine ndimachita zimene sindikuzifuna, si inenso amene ndimazichita, koma ndi tchimo limene lili mʼkati mwanga.

21 Tsono ndapeza kuti lamuloli likugwira ntchito. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, zoyipa zili nane pomwepo. 22 Mtima wanga umakondwera ndi lamulo la Mulungu. 23 Koma mʼkati mwanga ndimaona lamulo lina likugwira ntchito kulimbana ndi zomwe mtima wanga umavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa wamʼndende walamulo la uchimo lomwe likugwira ntchito mʼkati mwa ziwalo zanga. 24 Kalanga ine! Adzandipulumutsa ndani ku thupi la imfali? 25 Atamandike Mulungu, amene amandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu!

Kotero tsono, ineyo ndi mtima wanga ndimatumikira lamulo la Mulungu, koma ndi thupi langa ndimatumikira lamulo la uchimo.

Yeremiya 46

46 Yehova anamupatsa Yeremiya uthenga wonena za anthu a mitundu ina.

Uthenga Wonena za Igupto

Kunena za Igupto:

Yehova ananena za gulu lankhondo la Farao Neko mfumu ya ku Igupto limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni analigonjetsa ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda,

anati, “Konzani zishango zanu ndi malihawo,
    ndipo yambanipo kupita ku nkhondo!
Mangani akavalo,
    ndipo kwerani inu okwerapo!
Khalani pa mzere
    mutavala zipewa!
Nolani mikondo yanu,
    valani malaya anu ankhondo!
Yeremiya anati: Kodi ndikuona chiyani?
    Achita mantha
akubwerera,
    ankhondo awo agonjetsedwa.
Akuthawa mofulumirapo
    osayangʼananso mʼmbuyo,
    ndipo agwidwa ndi mantha ponseponse,”
            akutero Yehova.
Waliwiro sangathe kuthawa
    ngakhale wankhondo wamphamvu sangathe kupulumuka.
Akunka napunthwa ndi kugwa
    kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate.

“Kodi ndani amene akukwera ngati Nailo,
    ngati mtsinje wa madzi amkokomo?
Igupto akusefukira ngati Nailo,
    ngati mitsinje ya madzi amkokomo.
Iye akunena kuti, ‘Ndidzadzuka ndi kuphimba dziko lapansi;
    ndidzawononga mizinda ndi anthu ake.’
Tiyeni, inu akavalo!
    Thamangani inu magaleta!
Tulukani, inu ankhondo,
    ankhondo a ku Kusi ndi Puti amene mumanyamula zishango,
    ankhondo a ku Ludi amene mumaponya uta.
10 Koma tsikulo ndi la Ambuye Yehova Wamphamvuzonse;
    tsiku lolipsira, lolipsira adani ake.
Lupanga lake lidzawononga ndi kukhuta magazi,
    lidzaledzera ndi magazi.
Pakuti Yehova, Yehova Wamphamvuzonse, adzapereka adani ake ngati nsembe
    mʼdziko la kumpoto mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.

11 “Pita ku Giliyadi ukatenge mankhwala
    iwe namwali Igupto.
Wayesayesa mankhwala ambiri koma osachira;
    palibe mankhwala okuchiritsa.
12 Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako;
    kulira kwako kwadzaza dziko lapansi.
Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana,
    onse awiri agwa pansi limodzi.”

13 Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za kubwera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kudzathira nkhondo Igupto ndi uwu:

14 “Mulengeze ku Igupto. Mulengeze ku Migidoli.
    Mulengezenso ku Mefisi ndi ku Tapanesi.
Muwawuze anthu akumeneko kuti, ‘Imani pamalo panu ndi kukhala okonzeka kudziteteza,
    chifukwa lupanga lidzawononga zonse zimene muli nazo.’
15 Chifukwa chiyani mulungu wanu wamphamvu uja Apisi wathawa?
    Iye sakanatha kulimba chifukwa Yehova anamugwetsa.
16 Ankhondo anu apunthwa ndi kugwa.
    Aliyense akuwuza mnzake kuti,
‘Tiyeni tibwerere kwathu,
    ku dziko kumene tinabadwira,
    tithawe lupanga la adani athu.’
17 Kumeneku iwo adzafuwula kuti,
    ‘Farao, mfumu ya ku Igupto mupatseni dzina lakuti,
    Waphokoso, Wotaya mwayi wake.’

18 “Pali Ine wamoyo,” ikutero Mfumu,
    imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse,
“wina adzabwera amene ali ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena,
    ngati phiri la Karimeli loti njoo mʼmbali mwa nyanja.
19 Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo
    inu anthu a ku Igupto,
pakuti Mefisi adzasanduka chipululu
    ndipo adzakhala bwinja mopanda wokhalamo.

20 “Igupto ali ngati mwana wangʼombe wokongola,
    koma chimphanga chikubwera
    kuchokera kumpoto kudzalimbana naye.
21 Ngakhale ankhondo aganyu amene ali naye
    ali ngati ana angʼombe onenepa.
Nawonso abwerera mʼmbuyo, nathawa pamodzi.
    Palibe amene wachirimika.
Ndithu, tsiku la tsoka lawafikira;
    ndiyo nthawi yowalanga.
22 Aigupto akuthawa ndi liwu lawo lili ngati la njoka yothawa
    pamene adani abwera ndi zida zawo,
abwera ndi nkhwangwa
    ngati anthu odula mitengo.
23 Iwo adzadula nkhalango ya Igupto,”
            akutero Yehova,
    “ngakhale kuti ndi yowirira.
Anthuwo ndi ochuluka kupambana dzombe,
    moti sangatheke kuwerengeka.
24 Anthu a ku Igupto achita manyazi
    atengedwa ukapolo ndi anthu a kumpoto.”

25 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, “Ndili pafupi kulanga Amoni mulungu wa Tebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Igupto pamodzi ndi milungu yake yonse, mafumu ake ndi onse amene amamukhulupirira. 26 Ndidzawapereka kwa amene akufuna kuwapha, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi atsogoleri ake ankhondo. Komabe, mʼtsogolomo Igupto adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Yehova.

27 “Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha;
    usataye mtima, iwe Israeli.
Ndithu Ine ndidzakupulumutsa kuchokera ku mayiko akutali,
    ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera ku mayiko kumene anapita nazo ku ukapolo.
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala motakasuka ndi pa mtendere,
    ndipo palibenso wina amene adzamuopsa.
28 Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha,
    pakuti Ine ndili nawe,” akutero Yehova.
“Ndidzawonongeratu mitundu yonse ya anthu
    a ku mayiko kumene ndakupirikitsira,
    Koma iwe sindidzakuwononga kotheratu.
Ndidzakulanga iwe ndithu koma moyenerera;
    sindidzakulekerera osakulanga.”

Masalimo 22

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide.

22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya?
    Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe?
    Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha,
    usikunso, ndipo sindikhala chete.

Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu;
    ndinu matamando a Israeli.
Pa inu makolo athu anadalira;
    iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa.
    Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.

Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,
    wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
Onse amene amandiona amandiseka;
    amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
“Iyeyu amadalira Yehova,
    musiyeni Yehovayo amulanditse.
Musiyeni Yehova amupulumutse
    popeza amakondwera mwa Yehovayo.”

Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.
    Munachititsa kuti ndizikudalirani
    ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
10 Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;
    kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
11 Musakhale kutali ndi ine,
    pakuti mavuto ali pafupi
    ndipo palibe wina wondipulumutsa.

12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira;
    ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
13 Mikango yobangula pokadzula nyama,
    yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
14 Ine ndatayika pansi ngati madzi
    ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake.
Mtima wanga wasanduka phula;
    wasungunuka mʼkati mwanga.
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale,
    ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada;
    mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
16 Agalu andizungulira;
    gulu la anthu oyipa landizinga.
    Alasa manja ndi mapazi anga.
17 Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse;
    anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
18 Iwo agawana zovala zanga pakati pawo
    ndi kuchita maere pa zovala zangazo.

19 Koma Inu Yehova, musakhale kutali;
    Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.
20 Pulumutsani moyo wanga ku lupanga,
    moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.
21 Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango;
    pulumutseni ku nyanga za njati.

22 Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga;
    ndidzakutamandani mu msonkhano.
23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!
    Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!
    Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza
    kuvutika kwa wosautsidwayo;
Iye sanabise nkhope yake kwa iye.
    Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.

25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.
    Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta;
    iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.
    Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
27 Malekezero onse a dziko lapansi
    adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,
ndipo mabanja a mitundu ya anthu
    adzawerama pamaso pake,
28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova
    ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.

29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;
    onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;
    iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;
    mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake
    kwa anthu amene pano sanabadwe
    pakuti Iye wachita zimenezi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.