Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 11

Sauli Apulumutsa Mzinda wa Yabesi

11 Nahasi, Mwamoni anapita ndi kuzungulira mzinda wa Yabesi Giliyadi. Tsono anthu onse a ku Yabesi anapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe pangano, ndipo tidzakutumikirani.”

Koma Nahasi Mwamoni uja anayankha kuti, “Ndidzachita nanu pangano pokhapokha nditakolowola diso lakumanja la aliyense wa inu kuti ndichititse manyazi Aisraeli onse.”

Akuluakulu a mzinda wa Yabesi anati kwa iye, “Utipatse masiku asanu ndi awiri kuti titumize uthenga mu Israeli monse. Ngati sipapezeka wodzatipulumutsa, ndiye ife tidzadzipereka kwa iwe.”

Amithenga aja atafika kwawo kwa Sauli ku Gibeya ndi kufotokoza nkhaniyi kwa anthu onse, iwo analira motaya mtima. Pa nthawiyo nʼkuti Sauli akubwera kuchokera ku munda, ali pambuyo pa ngʼombe zake za ntchito ndipo anafunsa. “Nʼchiyani chawavuta anthuwa kuti azilira motere?” Ndipo anamufotokozera zomwe anthu a mu mzinda wa Yabesi ananena.

Sauli atamva mawu awo, Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwa mphamvu ndipo anakwiya kwambiri. Tsono anatenga ngʼombe ziwiri za ntchito, nazidula nthulinthuli. Ndipo anatumiza amithenga ndi nthulizo dziko lonse la Israeli ndi mawu akuti, “Umo ndi mmene adzachite ndi ngʼombe ya aliyense amene satsata Sauli ndi Samueli.” Ndipo anthu anachita mantha aakulu motero kuti onse ananyamuka ndi mtima umodzi. Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000.

Tsono Sauli anawuza amithenga ochokera ku Yabesi aja kuti, “Mukawawuze anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti mawa nthawi ya masana adzapulumutsidwa.” Pamene amithengawo anapita ndi kukafotokoza nkhani imeneyi kwa anthu a ku Yabesi, iwo anasangalala kwambiri. 10 Choncho anthu a ku Yabesi anawuza Nahasi kuti, “Mawa tidzadzipereka kwa inu ndipo inu mudzachite nafe chilichonse chokukomerani.”

11 Tsono mmawa mwake Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Mmamawa kusanache iwo analowa mʼmisasa ya Aamoni ndi kuwapha mpaka masana. Amene anapulumuka anabalalika, aliyense kwakekwake.

Sauli Avomerezedwa kukhala mfumu

12 Kenaka anthu anafunsa Samueli kuti, “Kodi ndani aja ankanena kuti, ‘Kodi Sauli nʼkutilamulira ife?’ Bwera nawoni kuno kuti tidzawaphe.”

13 Koma Sauli anati, “Palibe amene ati aphedwe lero, pakuti lero lino Yehova wagwira ntchito yopulumutsa Israeli.”

14 Ndipo Samueli anati kwa anthuwo, “Tiyeni tipite ku Giligala kuti tikatsimikizenso kuti Sauli ndi mfumu yathu.” 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo kumeneko Samueli anakalonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anthu anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova, ndipo Sauli ndi Aisraeli onse anachita chikondwerero chachikulu.

Aroma 9

Chisankho Chopambana cha Mulungu

Ine ndikunena zoona mwa Khristu. Sindikunama ndipo chikumbumtima changa kudzera mwa Mzimu Woyera chikundichitira umboni. Ndili ndi chisoni chachikulu ndipo ndikumva kupwetekeka kosalekeza mu mtima mwanga. Pakuti ndikanafuna ine mwini nditatembereredwa ndi kuchotsedwa mwa Khristu chifukwa cha abale anga, amene ndi a mtundu wanga, anthu Aisraeli. Iwo anasankhidwa kukhala ana. Mulungu anawapatsa ulemerero, anachita nawo mapangano, kuwapatsa Malamulo, Nyumba yopembedzeramo ndi malonjezano ake. Awo ndi makolo athu. Kuchokera kwa iwo mʼthupi ndi kumene kunachokera makolo a Khristu Yesu amene ndi Mulungu wolamulira zinthu zonse, alemekezeke mpaka muyaya! Ameni.

Sikuti mawu a Mulungu analephera. Pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli. Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. Koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. Kutanthauza kuti, si ana obadwa mʼthupi amene ndi ana a Mulungu koma ndi ana a lonjezano amene amatengedwa kukhala zidzukulu za Abrahamu. Pakuti Mulungu analonjeza ponena kuti, “Pa nthawi yake ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”

10 Ndipo si pokhapo ayi. Ana awiri a Rebeka aja abambo awo anali mmodzi, kholo lathu Isake. 11 Komabe, ana amapasawa asanabadwe kapena asanachite chilichonse chabwino kapena choyipa, nʼcholinga choti chifuniro cha Mulungu chosankhiratu munthu aliyense chipitirire, 12 osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifuniro cha Iye mwini, anawuza Rebeka kuti, “Wamkulu adzatumikira wamʼngʼono.” 13 Monga momwe kwalembedwa kuti, “Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.”

14 Nanga tsono tidzanena chiyani? Kodi Mulungu ndi osalungama? Ayi, ndi pangʼono pomwe! 15 Pakuti Mulungu anawuza Mose kuti,

“Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo,
    ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.”

16 Nʼchifukwa chake, izi sizitengera zokhumba za munthu kapena kuyesetsa koma chifundo cha Mulungu. 17 Malemba akuti Mulungu anamuwuza Farao kuti, “Ine ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga, kuti mwa iwe dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi.” 18 Choncho Mulungu amachitira chifundo munthu amene akufuna kumuchitira chifundo ndipo amawumitsa mtima munthu amene Iye akufuna kumuwumitsa mtima.

19 Tsono mmodzi wa inu nʼkundifunsa kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mulungu amatipeza olakwa? Nanga ndani amene amakana chifuniro chake?” 20 Koma ndiwe yani, munthu wamba, woti nʼkutsutsana ndi Mulungu? “Kodi chimene chinawumbidwa nʼkufunsa amene anachiwumba kuti, ‘Kodi unandiwumbiranji motere?’ ” 21 Kodi wowumba alibe ufulu wowumba kuchokera ku dothi lomwelo mbiya yamtengowapatali ndi ina yamtengo wotsika?

22 Koma Mulungu, anafuna kuonetsa mkwiyo wake ndi kuti mphamvu yake idziwike. Iye anapirira modekha mtima kwambiri zochita za anthu omwe anawakwiyirawo amene anayeneradi chiwonongeko. 23 Iye anachita izi kufuna kuonetsa kulemera kwa ulemerero wake ndi kuti udziwike kwa amene analandira chifundo chake. Iye anawakonzeratu kuti alandire ulemerero wake 24 ngakhale ifenso amene anatiyitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso kwa a mitundu ina. 25 Monga momwe Mulungu akunenera mʼbuku la Hoseya kuti,

“Amene sanali anthu anga ndidzawatcha ‘anthu anga;’
    ndipo Ine ndidzatcha ‘wokondedwa wanga’ amene sali wokondedwa wanga,”

26 ndipo,

“Pamalo omwewo pamene ananena kuti,
    ‘Sindinu anthu anga,’
pomweponso adzawatchula kuti, ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ ”

27 Yesaya anafuwula za Aisraeli kuti,

“Ngakhale chiwerengero cha Aisraeli chingakhale ngati mchenga wa ku nyanja,
    otsala okha ndiye adzapulumuke.
28 Pakuti Ambuye adzagamula milandu
    ya anthu pa dziko lapansi mofulumira ndi kumaliziratu.”

29 Monga momwe Yesaya ananena malo ena kuti,

“Ngati Yehova Wamphamvuzonse
    akanapanda kutisiyira zidzukulu,
ife tikanawonongeka
    ngati anthu a ku Sodomu, tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.”

Kusakhulupirira kwa Aisraeli

30 Kodi nanga tidzati chiyani? Tidzati a mitundu ina amene sanafune chilungamo analandira chilungamo chachikhulupiriro 31 koma Aisraeli, amene anafuna chilungamo cha lamulo sanachilandire. 32 Chifukwa chiyani? Chifukwa iwo sanachifune ndi chikhulupiriro koma ngati mwa ntchito. Iwo anapunthwa pa “Mwala wopunthwitsa.” 33 Monga momwe kwalembedwa kuti,

“Taonani, Ine ndikuyika mwala mu Ziyoni wopunthwitsa anthu,
    thanthwe limene limagwetsa anthu.
Koma amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”

Yeremiya 48

Uthenga Wonena za Mowabu

48 Ponena za Mowabu:

Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,

“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa.
    Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa;
    linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.
Palibenso amene akutamanda Mowabu;
    ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa:
    ‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’
Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete;
    ankhondo adzakupirikitsani.
Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu.
    Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’
Mowabu wawonongeka;
    ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.
Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti,
    akulira kwambiri pamene akupita.
Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumveka
    pa njira yotsikira ku Horonaimu.
Thawani! Dzipulumutseni;
    khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.
Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu,
    nanunso mudzatengedwa ukapolo,
ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo,
    pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.
Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse,
    ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke.
Chigwa chidzasanduka bwinja
    ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa
    monga Yehova wayankhulira.
Mtsineni khutu Mowabu
    chifukwa adzasakazika;
mizinda yake idzasanduka mabwinja,
    wopanda munthu wokhalamo.

10 “Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika!
    Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!

11 “Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake,
    ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,
osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina;
    iye sanatengedwepo ukapolo.
Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja
    ndipo fungo lake silinasinthe.
12 Nʼchifukwa chake masiku akubwera,”
    akutero Yehova,
“pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko
    ndipo adzamukhutula;
adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake
    pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.
13 Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi,
    monga momwe Aisraeli anachitira manyazi
    ndi Beteli amene ankamukhutulira.

14 “Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali.
    Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’
15 Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake;
    anyamata ake okongola apita kukaphedwa,”
    ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
16 Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi;
    masautso ake akubwera posachedwa.
17 Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira,
    inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake;
nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija,
    taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”

18 “Tsikani pa ulemerero wanu
    ndipo khalani pansi powuma,
    inu anthu okhala ku Diboni,
pakuti wowononga Mowabu
    wabwera kudzamenyana nanu,
    wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.
19 Inu amene mumakhala ku Aroeri,
    imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera.
Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka,
    afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’ ”
20 Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika.
    Lirani mwachisoni ndipo fuwulani!
Lengezani ku mtsinje wa Arinoni
    kuti Mowabu wawonongedwa.
21 Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri,
    ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,
22     Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,
23     Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,
24     Keriyoti ndi Bozira
    ndi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.
25 Mphamvu za Mowabu zawonongeka;
    mkono wake wathyoka,”
            akutero Yehova.

26 “Muledzeretseni Mowabu,
    chifukwa anadzikuza powukira Yehova.
Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake;
    mulekeni akhale chinthu chomachiseka.
27 Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka?
    Kodi Israeli anapezeka pakati pa akuba
kuti nthawi zonse poyankhula za iye,
    iwe uzimupukusira mutu momunyoza?
28 Inu amene mumakhala ku Mowabu,
    siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe.
Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake
    pa khomo la phanga.

29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu,
    kunyada kwake nʼkwakukulu.
Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula.
    Ali ndi mtima wodzikweza.
30 Ine ndikuzidziwa ntchito zake,
            akutero Yehova.
    Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.
31 Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu,
    ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu,
    ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.
32 Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri.
    Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa
imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja;
    zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri.
Wowononga wasakaza
    zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.
33 Chimwemwe ndi chisangalalo zatha
    ku minda ya zipatso ya ku Mowabu.
Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa;
    palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa.
Ngakhale kufuwula kulipo,
    koma sikufuwula kwa chimwemwe.

34 “A ku Hesiboni ndi Eleali akulira
    ndipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi,
kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya.
    Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
35 Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabu
    kupereka nsembe mʼmalo awo opembedzera
    ndi kufukiza lubani kwa milungu yawo,”
            akutero Yehova.
36 “Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro.
    Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro
    chifukwa chuma chimene anachipata chatha.
37 Aliyense wameta mutu wake
    ndi ndevu zake;
manja a munthu aliyense ndi ochekacheka,
    ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.
38 Pa madenga onse a ku Mowabu
    ndiponso mʼmisewu yake
anthu akungolira,
    pakuti ndaphwanya Mowabu
    ngati mtsuko wopanda ntchito,”
            akutero Yehova.
39 “Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira!
    Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi.
Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka,
    chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”

40 Yehova akuti,

“Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhanga
    chimene chatambalitsa mapiko ake.
41 Mizinda idzagwidwa
    ndipo malinga adzalandidwa.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu
    idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
42 Mowabu sudzakhala mtundu wa anthu
    chifukwa unadzikuza powukira Yehova.
43 Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikira
    inu anthu a ku Mowabu,”
            akutero Yehova.
44 “Aliyense wothawa zoopsa
    adzagwera mʼdzenje,
aliyense wotuluka mʼdzenje
    adzakodwa mu msampha.
Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu
    pa nthawi ya chilango chake,”
            akutero Yehova.

45 “Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni
    chifukwa chotopa.
Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,
    malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni.
Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,
    dziko la anthu onyada.
46 Tsoka kwa iwe Mowabu!
    Anthu opembedza Kemosi awonongeka.
Ana ako aamuna ndi aakazi
    atengedwa ukapolo.

47 “Komabe masiku akutsogolo
    ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,”
            akutero Yehova.

Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.

Masalimo 25

Salimo la Davide.

25 Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
    Ndimadalira Inu Mulungu wanga.
Musalole kuti ndichite manyazi
    kapena kuti adani anga andipambane.
Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye
    sadzachititsidwa manyazi
koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi
    ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.

Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,
    phunzitseni mayendedwe anu;
tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,
    pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,
    ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
    pakuti ndi zakalekale.
Musakumbukire machimo a ubwana wanga
    ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
    pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

Yehova ndi wabwino ndi wolungama;
    choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama
    ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika
    kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
11 Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova,
    khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
12 Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova?
    Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.
13 Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse,
    ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.
14 Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa;
    amawulula pangano lake kwa iwowo.
15 Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse,
    pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.

16 Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima,
    pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.
17 Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira;
    masuleni ku zowawa zanga.
18 Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga
    ndipo mufafanize machimo anga onse.
19 Onani mmene adani anga achulukira
    ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.
20 Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa;
    musalole kuti ndichite manyazi,
    pakuti ndimathawira kwa Inu.
21 Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze,
    chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.

22 Wombolani Israeli Inu Mulungu,
    ku mavuto ake onse!

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.