M’Cheyne Bible Reading Plan
Rute ndi Bowazi ku Malo Wopunthira Tirigu ndi Barele
3 Tsiku lina Naomi anafunsa mpongozi wake Rute kuti, “Mwana wanga, kodi si kwabwino kuti ndikupezere kokhala kuti zinthu zizikuyendera bwino? 2 Bowazi amene adzakazi ake wakhala nawo nthawi yonseyi, si wachibale wathu kodi? Usiku uno akhala akupeta barele ku malo opunthira. 3 Samba ndi kudzola mafuta onunkhira, ndipo uvale zovala zako zabwino kwambiri. Kenaka upite ku malo opunthirako tirigu ndi barele koma munthuyo asakakuzindikire kufikira atamaliza kudya ndi kumwa. 4 Akamakagona, iwe ukaonetsetse malo amene wagonawo. Kenaka upite ndi kuvundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona. Iyeyo akakuwuza zoti uchite.”
5 Rute anayankha kuti, “Ndichita zonse zimene mwanena.”
6 Choncho Rute anapita ku malo opunthirawo ndipo anachita monga momwe apongozi ake anamuwuza.
7 Atamaliza kudya ndi kumwa, Bowazi anakhala wosangalala, ndipo anakagona pa mbali pa mulu wa barele. Tsono Rute anapita mwa kachetechete, navundukula chofunda ku mapazi ake ndi kugona.
8 Tsono pakati pa usiku Bowazi anadzidzimuka, natembenuka, ndipo anangoona mkazi akugona ku mapazi ake.
9 Iye anafunsa kuti, “Ndiwe yani?” Ndipo anayankha kuti, “Ndine mdzakazi wanu Rute. Popeza ndinu wachibale amene muyenera kundiwombola, ndiye mundilowe chokolo.”
10 Ndipo Bowazi anati, “Mwana wanga, Yehova akudalitse popeza kukoma mtima kumene wasonyeza panoku kwaposa koyamba kaja. Iwe sunathamangire anyamata olemera kapena osauka. 11 Ndipo tsopano mwana wanga usaope. Ine ndidzakuchitira chilichonse udzapemphe popeza anzanga onse amʼmudzi muno akudziwa kuti ndiwe mkazi wa khalidwe labwino. 12 Ngakhale kuti ndinedi wachibale woyenera kukusamala, koma alipo wachibale weniweni kuposa ine. 13 Gona konkuno usiku uno mpaka mmawa. Tsono ngati iyeyu adzakulowa chokolo, chabwino alowe. Koma ngati safuna kutero, ine ndikulumbira pamaso pa Yehova Wamoyo kuti ndidzakulowa chokolo. Ugone kuno mpaka mmawa.”
14 Choncho Rute anagona ku mapazi ake mpaka mmawa, koma anadzuka mmamawa kusanayere chifukwa Bowazi anati, “Aliyense asadziwe kuti kopondera barele kunabwera mkazi.”
15 Bowazi anati kwa Rute, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho ndipo uchiyale pansi.” Ndipo atayala, Bowazi anathira makilogalamu makumi awiri a barele ndi kumusenzetsa Rute. Rute anapita nakalowa mu mzinda.
16 Rute atafika kwa apongozi ake anamufunsa kuti, “Zinayenda bwanji mwana wanga?” Kenaka iye anafotokoza zonse zimene Bowazi anamuchitira.
17 Ndipo anati, “Munthuyo anandipatsa makilogalamu makumi awiri awa a barele, nandiwuza kuti usapite kwa apongozi ako wopanda kanthu.”
18 Kenaka Naomi anati, “Mwana wanga, dikira mpaka titaona mmene zinthu zikhalire chifukwa munthuyu salekera pomwepo, mpaka zinthuzi zitakonzeka lero.”
Bowazi Akwatira Rute
4 Nthawi yomweyo Bowazi anapita ku chipata cha mzinda ndi kukhala pansi kumeneko pabwalo losonkhanira. Tsono anangoona wachibale woyenera kulowa chokolo uja akufika. Ndipo Bowazi anati, “Patukirani kuno, bwenzi langa. Mubwere mudzakhale apa.” Choncho anapatuka nakakhala pansi.
2 Bowazi anayitananso akuluakulu khumi a mu mzindamo nati, “Dzakhaleni pansi apa,” ndipo anadzakhala pansi.
3 Kenaka anamuwuza oyenera kulowa chokolo uja kuti, “Naomi amene wabwera kuchoka ku Mowabu akugulitsa malo amene anali a malemu Elimeleki, mʼbale wathu uja. 4 Choncho ndinaganiza zokuwuza zimenezi kuti ugule mundawu pamaso pa anthu amene ali panowa, ndi pamaso pa akuluakulu mwa abale athu. Ngati ukufuna kuwuwombola, uwombole. Koma ngati sukufuna, undiwuze kuti ndidziwe, pakuti palibe wina angawuwombole koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Iye anati, “Ine ndidzawuwombola.”
5 Tsono Bowazi anati, “Tsiku limene ukagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mkazi wamasiye uja, kuti dzina la malemu lisungike pa cholowa chake.”
6 Pamenepo wachibaleyo anati, “Sindingathe kuwuwombola mundawu kuti ukhale wanga, kuopa kuti kutaya cholowa changa. Mugule ndinu. Ine sindingathe.”
7 (Kale mu Israeli zinkatere ngati munthu afuna kuwombola kanthu kapena kusinthana kanthu ndi mnzake kuti chikhale chakechake. Iye ankavula nsapato imodzi namupatsa mnzakeyo. Imeneyo ndiyo inali njira yochitira umboni mu Israeli).
8 Choncho wachibale uja atawuza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawu.” Iye anavula nsapato yake namupatsa Bowazi.
9 Ndipo Bowazi anawuza akuluakuluwo ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zinali za malemu Elimeleki, zonse zimene zinali za malemu Kiliyoni ndiponso za malemu Maloni. 10 Ndatenganso Rute Mmowabu uja mkazi wa malemu Maloni, kuti akhale mkazi wanga, kuti dzina la malemu Maloni lisungike pa cholowa chake, ndipo lisafafanizike pakati pa abale ake ngakhalenso mʼmudzi mwake. Nonsenu ndinu mboni lero lino.”
11 Ndipo akuluakulu aja ndi anthu onse amene anali pa chipata anati, “Ife ndife mboni, ndipo Yehova amusandutsa mkazi amene akudzalowa mʼnyumba yakoyu kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, amene anamanga banja la Israeli. Ukhale munthu wosasowa kanthu mu Efurata ndi munthu wotchuka mu Betelehemu. 12 Ana amene Yehova adzakupatsa mwa mkaziyu adzamange banja lako kukhala la Perezi, amene Tamara anamubalira Yuda.”
Makolo a Davide
13 Choncho Bowazi anakwatira Rute. Yehova anamudalitsa nakhala ndi pakati, ndipo anabereka mwana wamwamuna.
14 Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. “Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli. 15 Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.”
16 Kenaka Naomi anatenga mwanayo namufukata ndipo anakhala mlezi.
17 Amayi achinansi ake anati, “Naomi ali ndi mwana wamwamuna.” Ndipo anamutcha dzina lake Obedi. Iye anali abambo a Yese abambo ake a Davide.
18 Izi tsono ndizo zidzukulu za Perezi:
Perezi anali abambo a Hezironi.
19 Hezironi anali abambo a Ramu,
Ramu anali abambo a Aminadabu,
20 Aminadabu abambo a Naasoni,
Naasoni anali abambo a Salimoni,
21 Salimoni abambo a Bowazi,
Bowazi abambo a Obedi.
22 Obedi anali abambo a Yese,
ndipo Yese anali abambo a Davide.
Paulo pa Chilumba cha Melita
28 Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita. 2 Anthu a pa chilumbacho anatichitira zokoma zimene sizichitika kawirikawiri. Iwo anakoleza moto natilandira tonse chifukwa kumagwa mvula ndipo kumazizira. 3 Paulo anatola mtolo wankhuni, pamene amayika pa moto, munatulukamo njoka chifukwa cha kutentha, ndipo inamuluma pa dzanja. 4 Anthu a pa chilumbacho ataona njokayo ili lende pa dzanja lake, iwo anawuzana kuti, “Munthu uyu akuyenera kukhala munthu wopha anthu; pakuti ngakhale wapulumuka pa nyanja, chilungamo sichinamulore kuti akhale ndi moyo.” 5 Koma Paulo anayikutumulira pa moto njokayo, ndipo sanamve kupweteka. 6 Anthu anayembekezera kuti thupi lake litupa kapena agwa ndi kufa mwadzidzidzi, koma anadikira nthawi yayitali. Ataona kuti palibe kanthu kachilendo kanamuchitikira anasintha maganizo awo nanena kuti iye ndi mulungu.
7 Pafupi ndi malowa panali munda wa Popliyo, mkulu wa boma la pa chilumbacho. Iye anatilandira natisamala bwino masiku atatu. 8 Abambo ake anali gone, chifukwa amadwala malungo ndi kamwazi. Paulo analowa mʼchipinda chake kukawaona, ndipo atapemphera, anasanjika manja ake pa iwo nawachiritsa. 9 Zitachitika zimenezi, anthu onse odwala a pa chilumbacho anabwera ndipo anachiritsidwa. 10 Anthuwo anatilemekeza ife mʼnjira zambiri ndipo pamene tinakonzeka kuti tiyambe ulendo, anatipatsa zonse zomwe tinazisowa.
Paulo Afika ku Roma
11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pa sitima ina imene inakhala pa chilumbacho chifukwa cha kuzizira. Inali sitima ya ku Alekisandriya imene inali ndi chizindikiro cha milungu ya mapasa yotchedwa Kastro ndi Polikisi. 12 Tinakafika ku Surakusa ndipo kumeneko tinakhalako masiku atatu. 13 Kuchokera kumeneko tinayenda ndi kukafika ku Regio. Mmawa mwake mphepo yochokera kummwera inawomba, ndipo tsiku linalo tinakafika ku Potiyolo. 14 Kumeneko tinapezako abale amene anatiyitana kuti tikhale nawo sabata limodzi. Ndipo kenaka tinapita ku Roma. 15 Abale kumeneko atamva kuti tikubwera, anabwera kudzakumana nafe mpaka ku bwalo la Apiyo ndiponso ku nyumba za alendo zitatu. Atawaona anthu amenewa Paulo anayamika Mulungu ndipo analimbikitsidwa. 16 Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kukhala pa yekha ndi msilikali womulondera.
Paulo Alalikira kwa Ayuda ku Roma
17 Patapita masiku atatu, Paulo anasonkhanitsa pamodzi atsogoleri a Ayuda. Atasonkhana, Paulo anawawuza kuti, “Abale anga, ngakhale kuti ine sindinachite kanthu kalikonse kulakwira mtundu wathu kapena miyambo ya makolo athu, koma anandigwira mu Yerusalemu ndi kundipereka mʼmanja mwa Aroma. 18 Iwo anandifufuza ndipo anafuna kundimasula chifukwa sanandipeze wopalamula mlandu woyenera kuphedwa. 19 Koma Ayuda atakana, ine ndinakakamizidwa kupempha kuti ndikaonekere pamaso pa Kaisara, sikuti ndinali ndi kanthu konenezera mtundu wanga. 20 Pa chifukwa ichi ndapempha kuti ndionane nanu ndi kuyankhula nanu. Pakuti nʼchifukwa cha chiyembekezo cha Israeli ndamangidwa unyolo uwu.”
21 Iwo anayankha kuti, “Ife sitinalandire kalata iliyonse yochokera ku Yudeya yonena za iwe, ndipo palibe mmodzi wa abale amene anachokera kumeneko anafotokoza kapena kunena kalikonse koyipa ka iwe. 22 Koma ife tikufuna kumva maganizo ako ndi otani, pakuti tikudziwa kuti ponseponse anthu akuyankhula zotsutsana ndi mpatuko umenewu.”
23 Iwo anakonza tsiku lina loti akumane ndi Paulo, ndipo anabwera anthu ambiri ku nyumba kumene amakhala. Kuyambira mmawa mpaka madzulo, Paulo anawafotokozera ndi kuwawuza za ufumu wa Mulungu ndipo anayesa kuwakopa kuti akhulupirire Yesu kuchokera mʼMalamulo a Mose ndiponso mʼmabuku a Aneneri. 24 Ena anakopeka ndi zimene Paulo ananena, koma enanso sanakhulupirire. 25 Ndipo anayamba kuchoka popeza sanagwirizane pakati pawo Paulo atanena mawu awa omaliza akuti, “Mzimu Woyera anayankhula zoona za makolo anu pamene Iye ananena kudzera mwa Mneneri Yesaya kuti,
26 “Pita kwa anthu awa ndi kuwawuza kuti,
‘Kumva mudzamva, koma osamvetsetsa;
kupenya mudzapenya, koma osaona kanthu.’
27 Pakuti mtima wa anthu ndi wokanika;
mʼmakutu mwawo ndi mogontha,
ndipo atsinzina kuti asaone kanthu.
Mwina angapenye ndi maso awo,
angamve ndi makutu awo,
angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,
Ineyo nʼkuwachiritsa.
28 “Chifukwa chake ine ndikufuna mudziwe kuti chipulumutso cha Mulungu chatumizidwa kwa anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzamvera.” 29 Paulo atanena mawu amenewa, Ayuda aja anachoka akutsutsana kwambiri.
30 Paulo anakhala kumeneko zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yobwereka yomwe amalipira ndipo ankalandira aliyense amene amabwera kudzamuona. 31 Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.
Yeremiya Aponyedwa Mʼchitsime cha Matope
38 Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasi-Huri, Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasi-Huri mwana wa Malikiya anamva zimene Yeremiya ankawuza anthu onse kuti, 2 “Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo. 3 Mzinda uno udzaperekedwa ndithu kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulande.’ ”
4 Tsono akuluakuluwo anawuza mfumu kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa. Iye akutayitsa mtima asilikali pamodzi ndi anthu onse amene atsala mu mzinda muno, chifukwa cha zimene akuwawuza. Munthu ameneyu sakufunira zabwino anthuwa koma chiwonongeko chawo.”
5 Mfumu Zedekiya anayankha kuti, “Munthuyu ali mʼmanja mwanu. Ine sindingakuletseni chimene mukufuna kumuchitira.”
6 Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo.
7 Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini. 8 Ebedi-Meleki anatuluka ku nyumba ya mfumu kukayiwuza kuti, 9 “Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.”
10 Tsono mfumu inalamula Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, “Tenga anthu makumi atatu, ndipo mukamutulutse mʼchitsimemo mneneri Yeremiya asanafe.”
11 Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya. 12 Ebedi-Meleki, Mkusi, anawuza Yeremiya kuti, “Ika sanzazo mkwapa mwako kuti zingwe zingakupweteke.” Yeremiya anachitadi zimenezi, 13 ndipo anamukoka ndi zingwe ndi kumutulutsa mʼchitsimecho. Ndipo Yeremiya anakhalabe ku bwalo la alonda.
Zedekiya Afunsanso Yeremiya
14 Tsiku lina Mfumu Zedekiya anayitana mneneri Yeremiya ndipo anabwera naye ku chipata chachitatu cha Nyumba ya Yehova. Mfumu inawuza Yeremiya kuti, “Ndikufuna kukufunsa kanthu kena, ndipo usandibisire chilichonse.”
15 Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Ndikakuyankhani, kodi simundipha? Ngakhaletu ine nditakulangizani, inu simudzandimvera.”
16 Koma Mfumu Zedekiya mwachinsinsi inalumbira kwa Yeremiya kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene amatipatsa moyo, sindidzakupha ngakhalenso kukupereka kwa amene akufuna kukuphawa.”
17 Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo. 18 Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’ ”
19 Mfumu Zedekiya inati kwa Yeremiya, “Ine ndikuopa Ayuda amene anathawira kale kwa Ababuloni, pakuti mwina Ababuloniwo adzandipereka kwa Ayudawo ndipo iwowo adzandizunza.”
20 Yeremiya anayankha kuti, “Ngati mumvera Yehova ndi kuchita zimene ndakuwuzani, ndiye kuti zinthu zidzakuyenderani bwino. Inu simudzaphedwa. 21 Koma mukakana kudzipereka, chimene Yehova wandiwululira ndi ichi: 22 Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti,
“ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa,
ndipo anakugonjetsa.
Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope;
abwenzi ako aja akusiya.’
23 “Akazi pamodzi ndi ana anu adzaperekedwa kwa Ababuloni. Inuyo simudzapulumuka mʼmanja mwawo koma mfumu ya ku Babuloni idzakugwirani; mzinda uno adzawutentha.”
24 Pamenepo Zedekiya anati kwa Yeremiya, “Usawuze munthu wina aliyense zimene takambiranazi, ukatero udzaphedwa. 25 Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’ 26 udzawawuze kuti, ‘Ine ndimapempha mfumu kuti isandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani kuti ndikafere kumeneko.’ ”
27 Akuluakulu onse anabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye anawayankha monga momwe mfumu inamulamula. Choncho palibe amene ananenanso kanthu, pakuti palibe amene anamva zomwe anakambirana ndi mfumu.
28 Ndipo Yeremiya anakhalabe mʼbwalo la alonda mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu unalandidwa.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
11 Mwa Yehova ine ndimathawiramo.
Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti,
“Thawira ku phiri lako ngati mbalame.
2 Pakuti taona oyipa akunga mauta awo;
ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta,
pobisala pawo kuti alase
olungama mtima.
3 Tsono ngati maziko awonongeka,
olungama angachite chiyani?”
4 Yehova ali mʼNyumba yake yoyera;
Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba.
Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu;
maso ake amawayesa.
5 Yehova amayesa olungama,
koma moyo wake umadana ndi oyipa,
amene amakonda zachiwawa.
6 Iye adzakhuthulira pa oyipa
makala amoto ndi sulufule woyaka;
mphepo yotentha idzakhala yowayenera.
7 Pakuti Yehova ndi wolungama,
Iye amakonda chilungamo;
ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide.
12 Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;
okhulupirika akusowa pakati pa anthu.
2 Aliyense amanamiza mʼbale wake;
ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.
3 Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo
ndi pakamwa paliponse podzikuza.
4 Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;
pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”
5 “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu
ndi kubuwula kwa anthu osowa,
Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,
“Ndidzawateteza kwa owazunza.”
6 Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro
monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,
oyengedwa kasanu nʼkawiri.
7 Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo
mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.
8 Oyipa amangoyendayenda ponseponse
anthu akamayamikira zochita zawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.