Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 5-6

Bokosi la Chipangano Pakati pa Afilisti

Afilisti atalanda Bokosi la Mulungu lija, analitenga kuchoka ku Ebenezeri kupita ku Asidodi. Kenaka anatenga Bokosi la Chipanganolo nabwera nalo ku nyumba ya Dagoni ndi kuliyika pambali pa Dagoni. Anthu a ku Asidodi atadzuka mmawa mwake, anangoona Dagoni atagwa pansi chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova! Iwo anatenga Dagoni ndi kumuyimika pamalo pake. Koma mmawa mwakenso atadzuka, anaona Dagoni atagwa chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova. Mutu wake ndi manja ake zinali zitaduka ndi kugwera pa khonde polowera, thunthu lake lokha ndilo linatsala. Nʼchifukwa chake mpaka lero ansembe a Dagoni kapena wina aliyense amene amalowa mʼkachisi wa Dagoni ku Asidodi saponda pa khonde.

Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira. Anthu a ku Asidodi ataona zimene zimachitika anati, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lisakhale kuno chifukwa akutizunza ife pamodzi ndi mulungu wathu Dagoni.” Choncho anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anawafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu wa Israeli tichite nalo chiyani?”

Iwo anayankha kuti, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lipite ku Gati.” Kotero analichotsa Bokosi la Mulungu wa Israelilo.

Koma atafika nalo ku Gati, Yehova analanga mzindawo, ndipo anthu anachita mantha aakulu. Iye anazunza anthu a mu mzindawo, ana ndi akulu omwe, ndi zithupsa. 10 Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni.

Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.” 11 Kotero iwo anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anati, “Chotsani Bokosi la Mulungu wa Israeli, libwerere ku malo ake. Tikapanda kutero lidzatipha ife ndi anthu athu.” Pakuti mu mzinda monse munali mantha aakulu kwambiri ndipo Mulungu ankawalanga kwambiri anthu a kumeneko. 12 Anthu amene sanafe anavutika ndi zithupsa, ndipo kulira kwa anthu a mu mzindamo kunamveka kumwamba.

Bokosi la Chipangano Libwerera ku Israeli

Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri. Tsono Afilisti anayitana ansembe ndi amawula ndipo anati, “Tichite nalo chiyani Bokosi la Yehova? Tiwuzeni momwe tidzalitumizira ku malo ake.”

Iwo anayankha kuti, “Ngati mufuna kubweza Bokosi la Mulungu wa Israeli, musalitumize wopanda kanthu, koma muyesetse kulitumiza pamodzi ndi nsembe yopepesera machimo. Mukatero mudzachiritsidwa, ndipo mudzadziwa chifukwa chiyani chilango cha Yehova sichikukuchokani.”

Afilisti anafunsanso kuti “Kodi ife tipereke nsembe yanji yopepesera machimo?”

Iwo anayankha kuti, “Mupereke zifanizo zagolide za zithupsa zisanu ndi zamakoswe asanu malingana ndi chiwerengero cha akalonga a Afilisti popeza mliri womwewo wagwera inu ndi akalonga anu. Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu. Nʼchifukwa chiyani mukuwumitsa mitima monga anachita Aigupto ndi Farao? Mulungu atawalanga anthu a ku Igupto aja kodi suja anawalola Aisraeli kuti azipita ndipo anapitadi?

“Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu. Mutenge Bokosi la Yehova ndi kuliyika pa galetapo ndipo pambali pake pakhale Bokosi, mʼmene muyikemonso zinthu zagolide zomwe mukutumiza kwa Iye monga nsembe yopepesera machimo. Kenaka, mulisiye lizipita. Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.”

10 Anthu aja anachitadi zimenezi. Anatenga ngʼombe zamkaka ziwiri nazimanga ku galeta lija. Koma ana awo anawatsekera mʼkhola. 11 Tsono anayika Bokosi la Yehova pa galeta pamodzi ndi bokosi limene munali makoswe agolide ndi zifanizo zawo za zithupsa. 12 Ngʼombe zija zinapita molunjika kutsata msewu wopita ku Beti Semesi zikulira njira yonse. Sizinakhotere kumanja kapena kumanzere. Akalonga a Afilisti anazitsatira mpaka mʼmalire a Beti-Semesi.

13 Nthawi imeneyi anthu a ku Beti-Semesi amakolola tirigu mʼchigwa ndipo pamene anayangʼana ndi kuona Bokosi la Chipangano likubwera anakondwa. 14 Galeta lija linafika ku munda wa Yoswa ku Beti-Semesi ndipo linayima. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu anawaza nkhuni galetalo, ndipo anapha ngʼombe zija ndi kuzipereka ngati nsembe zopsereza kwa Yehova. 15 Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova. 16 Atsogoleri asanu a Afilisti ataona izi anabwerera ku Ekroni tsiku lomwelo.

17 Zifanizo zagolide za zithupsa zimene Afilisti anatumiza ngati nsembe zopepesera machimo kwa Yehova zinkayimirira mizinda isanu iyi motere: chimodzi cha ku Asidodi, china cha ku Gaza ndi zina za ku Asikeloni, Gati ndi Ekroni. 18 Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero.

19 Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri. 20 Tsono anthu a ku Beti-Semesi anafunsa, “Ndani angathe kuyima pamaso pa Yehova Mulungu Woyera? Bokosi la Chipanganoli lipita kuti likachoka pano?”

21 Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.”

Aroma 5

Mtendere ndi Chimwemwe

Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene anatsekulira njira mwachikhulupiriro yolowera mʼchisomo mʼmene takhazikikamo. Ndipo tikukondwerera chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo. Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake.

Pakuti pa nthawi yake, tikanali ochimwa, Khristu anatifera anthu osapembedzafe. Sizichitika kawirikawiri kuti munthu wina afere munthu wolungama, ngakhale kuti chifukwa cha munthu wabwino wina atha kulimba mtima kumufera. Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.

Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu. 10 Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye? 11 Sikuti izi zili chomwechi chabe, koma timakondweranso mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Kudzera mwa Iye, ife tsopano tayanjanitsidwa ndi Mulungu.

Imfa Kudzera mwa Adamu, Moyo Kudzera mwa Yesu

12 Choncho monga momwe tchimo linalowa mʼdziko lapansi kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mu tchimo, mʼnjirayi imfa inafika kwa anthu onse pakuti onse anachimwa. 13 Pakuti Malamulo asanaperekedwe, tchimo linali mʼdziko lapansi. Koma pamene palibe Malamulo, tchimo silitengedwa kukhala tchimo. 14 Komabe, imfa inalamulira kuyambira nthawi ya Adamu mpaka nthawi ya Mose. Inalamulira ngakhalenso pa iwo amene sanachimwe posamvera Malamulo monga anachitira Adamu. Adamuyo amene anali chifaniziro cha wina amene ankabwera.

15 Koma sitingafananitse mphatso yaulereyo ndi kuchimwa kwa anthu. Pakuti ngati anthu ambiri anafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga chisomo cha Mulungu ndi mphatso zomwe zinabwera ndi chisomo cha munthu mmodzi, Yesu Khristu, ndi kusefukira kwa ambiri! 16 Ndiponso, mphatso ya Mulungu sifanana ndi zotsatira za kuchimwa kwa munthu mmodzi. Chiweruzo chinatsatira tchimo la munthu mmodzi ndi kubweretsa kutsutsidwa koma mphatso inatsatira zolakwa zambiri ndi kubweretsa kulungamitsidwa. 17 Pakuti ngati, chifukwa cha kulakwa kwa munthu mmodziyo, imfa inalamulira kudzera mwa munthu mmodziyo, kuli koposa bwanji nanga kwa iwo amene adzalandira chisomo chochuluka ndi mphatso yachilungamo, adzalamulira mʼmoyo kudzera mwa munthu mmodzi, Yesu Khristu.

18 Choncho monga tchimo limodzi linabweretsa kutsutsika pa anthu onse, chimodzimodzinso ntchito imodzi yolungama inabweretsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuwapatsa moyo. 19 Pakuti kusamvera kwa munthu mmodzi kunasandutsa anthu ambiri kukhala ochimwa, chimodzimodzinso anthu ambiri adzasanduka olungama kudzera mwa munthu mmodzinso.

20 Malamulo a Mulungu anaperekedwa ndi cholinga chakuti anthu onse azindikire kuchuluka kwa machimo awo. Koma pamene machimo anachuluka, chisomo chinachuluka koposa. 21 Choncho monga momwe tchimo linkalamulira anthu ndi kubweretsa imfa pa iwo, chomwecho kunali koyenera kuti chisomo chilamulire pobweretsa chilungamo kwa anthu, ndi kuwafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

Yeremiya 43

43 Yeremiya atatsiriza kuwawuza anthuwo mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova anamutuma kuti akawawuze, Azariya mwana wa Hosayia ndi Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi anthu onse odzikuza anawuza Yeremiya kuti, “Ukunama iwe! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti unene kuti, ‘Musapite ku Igupto kukakhala kumeneko.’ Koma ndi Baruki mwana wa Neriya amene akukulimbikitsa kuti utiletse zopita ku Igupto ndi kuti mʼmalo mwake tidzipereke mʼmanja mwa Ababuloni, kuti iwo atiphe kapena kutitenga ukapolo ku Babuloni.”

Motero Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi anthu onse sanamvere lamulo la Yehova loti akhale mʼdziko la Yuda. Mʼmalo mwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo anatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene anabwera kudzakhala mʼdziko la Yuda kuchokera ku mayiko onse kumene anabalakirako. Mʼgulu la anthu otengedwalo munali amuna onse, akazi ndi ana, ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anawasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani pamodzinso ndi mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya. Kotero anthuwo analowa mʼdziko la Igupto chifukwa anakana kumvera Yehova, nakafika ku Tapanesi.

Ndipo Yehova anayankhula ndi Yeremiya ku Tapanesi kuti, “Tenga miyala inayi yayikulu ndipo uyikwirire mʼdothi pa chiwundo cha polowera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Uchite zimenezi Ayuda onse akuona. 10 Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayitana mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzakhazika mpando wake waufumu pa miyala imene ndayikwirira apayi. Iye adzafunyulula tenti yake yaufumu pa miyala imeneyi. 11 Iye adzabwera kudzathira nkhondo Igupto. Iwo oyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri, iwo oyenera kutengedwa ukapolo adzatengedwa ukapolo, ndipo iwo oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga. 12 Adzayatsa moto mʼnyumba zopembedzera milungu ya Igupto. Adzayeretsa dziko la Igupto monga momwe mʼbusa amayeretsera chovala chake pochotsamo nsabwe. Pambuyo pake adzachoka mʼdziko la Igupto mwa mtendere. 13 Ku Iguptoko adzagwetsa zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzera mulungu wa dzuwa. Adzatentha ndi moto nyumba za milungu ya ku Igupto.’ ”

Masalimo 19

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
    thambo limalalikira ntchito za manja ake.
Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
    usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
    liwu lawo silimveka.
Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
    mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
    Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
    ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
    ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
    palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.

Lamulo la Yehova ndi langwiro,
    kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
    amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
Malangizo a Yehova ndi olungama,
    amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
    amapereka kuwala.
Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
    chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
    ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
    kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
    kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
    powasunga pali mphotho yayikulu.

12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
    Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
    iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
    wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.

14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
    zikhale zokondweretsa pamaso panu,
    Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.