Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 24

Davide Amusiya Sauli Wosamupha

24 Sauli atabwera kuchokera kumene amathamangitsa Afilisti anamva kuti, “Davide ali mʼchipululu cha Eni Gedi.” Tsono Sauli anatenga asilikali 3,000 odziwa kumenya bwino nkhondo kuchokera pakati pa Aisraeli onse ndipo anapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale.

Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo. Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’ ” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli.

Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli. Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.” Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka.

Kenaka Davide anatuluka mʼphanga muja ndipo anayitana Sauli, “Mbuye wanga!” Sauli atayangʼana mʼmbuyo, Davide anawerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi. Anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumamvera mawu a anthu kuti, ‘Davide wakukonzerani chiwembu?’ 10 Lero lino inu mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphanga muja. Ena anandiwuza kuti ndikupheni, koma ndakusiyani. Ndinati, ‘Sindidzapha mbuye wanga pakuti ndiye wodzozedwa wa Yehova.’ 11 Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe. 12 Yehova aweruze pakati pa inu ndi ine, akulangeni chifukwa cha zoyipa zimene mukundichitazi, koma dzanja langa silidzakukhudzani. 13 Paja anthu akale anati, ‘Munthu woyipa, ntchito zakenso ndi zoyipa.’ Kotero dzanja langa silidzakukhudzani.

14 “Kodi mfumu ya Israeli yadzalondola yani. Inu mukuthamangitsa yani? Galu wakufa kodi? Nsabwe kodi? 15 Nʼchifukwa chake Yehova agamule, inde aweruze pakati pa inu ndi ine ndi kupeza wolakwa. Yehova anditeteze ndi kundipulumutsa mʼdzanja lanu.”

16 Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza. 17 Anawuza Davide kuti, “Ndiwe wolungama kuposa ine. Iwe wandikomera mtima pamene ine ndakuchitira zoyipa. 18 Iweyo lero lino wandifotokozera zabwino zimene wandichitira. Yehova anandipereka mʼdzanja lako koma iwe sunandiphe. 19 Kodi munthu atapeza mdani wake angamulole kuti apite wosamuvulaza? Motero Yehova akuchitire iwe zabwino chifukwa cha zimene wandichitira lerozi. 20 Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako. 21 Tsopano undilonjeze molumbira lero mʼdzina la Yehova kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira kapena kufuta dzina langa pa banja la makolo anga.”

22 Choncho Davide analumbira pamaso pa Sauli. Pambuyo pake Sauli anabwerera kwawo, koma Davide ndi anthu ake anapitanso ku phanga kuja.

1 Akorinto 5

Wachigololo Achotsedwe mu Mpingo

Mbiri yamveka kuti pakati panu pakuchitika chigololo. Ndipo chigololo cha mtunduwu ngakhale pakati pa akunja sichingapezeke; munthu akumagonana ndi mkazi wa abambo ake. Ndipo inu mukudzitukumulabe. Kodi simukanayenera kudzazidwa ndi chisoni ndipo mukanamuchotsa pa chiyanjano chanu munthu wochita zimenezi? Ngakhale sindili nanu mʼthupi, ndili nanu mu mzimu. Ndipo ineyo ndapereka kale chiweruzo pa munthu amene amachita zotere, ngati kuti ndili komweko. Mukasonkhana mu dzina la Ambuye athu Yesu, ine ndili nanu mu mzimu, ndipo mphamvu ya Ambuye athu Yesu ili pomwepo, mumupereke munthuyu kwa Satana, kuti chikhalidwe chake cha uchimo chiwonongedwe ndikuti mzimu wake udzapulumuke pa tsiku la Ambuye.

Kudziwa kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti yisiti wochepa amafufumitsa mphumphu yaufa wonse wa tirigu? Chotsani yisiti wakale kuti mukhale ndi mphumphu yopanda yisiti, monga inu muli. Pakuti Khristu, Mwana Wankhosa wa Paska wathu, anaperekedwa nsembe. Choncho, tiyeni tisunge chikondwererochi, osati ndi yisiti wakale, wowononga ndi woyipa, koma ndi buledi wopanda yisiti, buledi woona mtima ndi choonadi.

Ndakulemberani mʼkalata yanga kuti musayanjane nawo anthu achigololo. 10 Pamenepatu sindikutanthauzatu anthu a dziko lapansi lino amene ndi achigololo, kapena aumbombo, kapena opeza ndalama mwachinyengo, kapena opembedza mafano. Kukanatero mukanangochoka mʼdziko lapansi lino. 11 Koma tsopano ndikukulemberani kuti musayanjane ndi aliyense amene adzitcha mʼbale koma ndi wachigololo, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, kapena wonamizira anzake, woledzera kapena wopeza ndalama mwachinyengo. Munthu wotere ngakhale kudya, osadya naye pamodzi.

12 Kodi ndipindulanji kuti ndiweruze anthu amene si a mu mpingo? Kodi simuyenera kuweruza iwo amene ali mu mpingo? 13 Mulungu adzaweruza akunja. “Chotsani woyipayo pakati panu.”

Ezekieli 3

Tsono Mulungu anandiwuza kuti, “Mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya kenaka upite ukayankhule ndi Aisraeli.” Choncho ndinayasama ndipo anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.

Kenaka Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsa kuti ukhute.” Choncho ndinadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi mʼkamwa mwanga.

Pamenepo Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita tsopano kwa Aisraeli ndipo ukawawuze mawu anga. Sindikukutuma kwa anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, koma kwa Aisraeli. Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, amene mawu ake sungawamvetse. Ndithu ndikanakutuma kwa iwowa, bwenzi iwo atakumvera. Koma Aisraeli sadzakumvera chifukwa iwo sakufuna kumvera Ine. Paja Aisraeli onse ndi okanika ndiponso a mtima wowuma. Tsono ine ndakhwimitsa nkhope yako mofanana ndi nkhope zawo. Ndalimbitsanso mutu wako mofanana ndi mitu yawo. Ine ndidzakusandutsa wolimba ngati mwala wa dayimondi umene uposa thanthwe lina lililonse kulimba kwake. Usachite nawo mantha kapena kuopsedwa nawo. Paja anthuwa ndi awupandu.”

10 Anatinso, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetse bwino zimene ndikukuwuzazi ndipo mawu angawa uwasunge bwino mu mtima mwako. 11 Tsopano upite kwa Aisraeli anzako amene ali ku ukapolo ndipo ukayankhule nawo. ‘Kaya akamvera kaya sakamvera,’ koma uzikawawuza kuti, Ambuye Wamphamvuzonse akuti zakutizakuti.”

12 Pamenepo Mzimu unandinyamula ndipo kumbuyo kwanga ndinamva liwu lamphamvu ngati chivomerezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Yehova kumene Iye amakhala!” 13 Phokoso ndinkalimvalo linali la kugundana kwa mapiko a zamoyo ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, limene linkamveka ngati chivomerezi chachikulu. 14 Mzimu wa Yehova unandikweza ndi kundinyamula ndipo ndinachokapo ndili wowawidwa ndi wonyuka mu mtima. Ndipo dzanja la Yehova linali pa ine mwa mphamvu. 15 Choncho ndinafika kwa amene anali mu ukapolo ku Telabibu pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndinakhala pansi pakati pawo masiku asanu ndi awiri, ndili wothedwa nzeru kwambiri.

Chenjezo kwa Israeli

16 Atatha masiku asanu ndi awiriwo, Yehova anandiwuza kuti, 17 “Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza. 18 Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 19 Koma ukamuchenjeza munthu woyipa koma iye osatembenuka mtima kuleka zoyipa zake kapena kusiya njira zake zoyipa, munthuyo adzafa chifukwa cha uchimo wake koma iwe udzapulumutsa moyo wako.

20 “Ngati munthu wolungama asiya chilungamo chake ndi kuchita uchimo ndipo Ine nʼkumuyika mʼzoopsa, munthuyo adzafa ndithu. Popeza iwe sunamuchenjeze, adzafadi chifukwa cha tchimo ndipo chilungamo chake sichidzakumbukiridwa, koma ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. 21 Koma ngati umuchenjeza munthu wolungama kuti asachimwe ndipo iye nʼkuleka kuchimwa adzakhala ndi moyo ndithu chifukwa anamvera chenjezo, ndipo iwe udzapulumutsa moyo wako.”

22 Nthawi ina dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandiwuza kuti, “Nyamuka upite ku chigwa, kumeneko ndikayankhula nawe.” 23 Choncho ndinanyamuka kupita ku chigwa. Ndipo ndinaona ulemerero wa Yehova kumeneko, ngati ulemerero umene ndinaona mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara ndipo ndinagwa pansi chafufumimba.

24 Koma Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa. Tsono Yehova anandiyankhula nati: “Pita, kadzitsekere mʼnyumba mwako. 25 Ndipo iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe motero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu. 26 Ndidzamatirira lilime lako kukhosi, kotero kuti udzakhala chete wosatha kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu aupandu. 27 Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.’ Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka.”

Masalimo 39

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kwa Yedutuni. Salimo la Davide.

39 Ndinati, “Ndidzasamalira njira zanga
    ndipo ndidzasunga lilime langa kuti ndisachimwe;
ndidzatseka pakamwa panga ndi chitsekerero
    nthawi yonse imene woyipa ali pamaso panga.”
Koma pamene ndinali chete
    osanena ngakhale kanthu kalikonse kabwino
    mavuto anga anachulukirabe.
Mtima wanga unatentha mʼkati mwanga,
    ndipo pamene ndinkalingalira, moto unayaka;
    kenaka ndinayankhula ndi lilime langa:

“Yehova ndionetseni mathero a moyo wanga
    ndi chiwerengero cha masiku anga;
    mundidziwitse kuti moyo wanga ndi wosakhalitsa motani.
Inu mwachititsa kuti masiku anga akhale ochepa kwambiri,
    kutalika kwa zaka zanga ndi kopanda phindu pamaso panu;
    moyo wa munthu aliyense ndi waufupi.
            Sela
Munthu ali ngati chithunzithunzi chake pamene akuyenda uku ndi uku:
    Iye amangovutika koma popanda phindu;
    amadzikundikira chuma, osadziwa kuti chidzakhala chayani.

“Koma tsopano Ambuye kodi ndifunanso chiyani?
    Chiyembekezo changa chili mwa Inu.
Pulumutseni ku zolakwa zanga zonse;
    musandisandutse chonyozeka kwa opusa.
Ine ndinali chete; sindinatsekule pakamwa panga
    pakuti Inu ndinu amene mwachita zimenezi.
10 Chotsani mkwapulo wanu pa ine;
    ndagonjetsedwa ndi nkhonya ya dzanja lanu.
11 Inu mumadzudzula ndi kulanga anthu chifukwa cha tchimo lawo;
    mumawononga chuma chawo monga njenjete;
    munthu aliyense ali ngati mpweya.
            Sela

12 “Imvani pemphero langa Inu Yehova,
    mverani kulira kwanga kopempha thandizo;
    musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu,
popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa;
    monga anachitira makolo anga onse.
13 Musandiyangʼane mwaukali, choncho ndidzatha kusangalala
    ndisanafe ndi kuyiwalika.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.