Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 15

Yehova Akana Sauli Kukhala Mfumu

15 Samueli anawuza Sauli kuti, “Yehova anandituma ine kuti ndikudzozeni kukhala mfumu ya anthu ake, Aisraeli. Tsopano imvani zimene Yehova akunena. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzalanga Aamaleki chifukwa cha zimene anawachita Aisraeli. Paja iwo analimbana ndi Aisraeli pa njira pamene Aisraeliwo ankachoka ku Igupto. Tsopano pita kathire nkhondo Aamaleki ndi kuwononga kwathunthu zinthu zonse zimene ali nazo. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe. Mukaphe amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ngʼombe ndi nkhosa, ngamira ndi abulu.’ ”

Kotero Sauli anayitana ankhondo ake nawawerenga ku Telaimu. Ankhondo oyenda pansi analipo 200,000 ndipo mwa iwowa 10,000 anali a fuko la Yuda. Sauli anapita ku mzinda wa Aamaleki nawubisalira mʼkhwawa. Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki.

Tsono Sauli anakantha Aamaleki kuchokera ku Havila mpaka ku Suri, kummawa kwa Igupto. Sauli anatenga Agagi mfumu ya Aamaleki, koma anthu ake onse anawapha ndi lupanga. Koma Sauli ndi ankhondo ake sanaphe Agagi, sanaphenso nkhosa ndi ngʼombe zabwino ngakhalenso ana angʼombe ndi ana ankhosa onenepa. Chilichonse chimene chinali chabwino sanachiphe. Koma zonse zimene zinali zoyipa ndi zachabechabe anaziwononga.

10 Kenaka Yehova anawuza Samueli kuti, 11 “Ine ndikumva chisoni chifukwa ndinayika Sauli kukhala mfumu. Wabwerera mʼmbuyo, waleka kunditsata ndipo sanamvere malangizo anga.” Samueli anapsa mtima, ndipo analira kwa Yehova usiku wonse.

12 Samueli anadzuka mmamawa ndipo anapita kukakumana ndi Sauli. Koma anthu anamuwuza kuti, “Sauli anabwera ku Karimeli, ndipo kumeneko wadziyimikira mwala wachikumbutso cha iye mwini. Tsopano wachokako ndipo wapita ku Giligala.”

13 Samueli atamupeza Sauli, Sauliyo anati kwa Samueli, “Yehova akudalitseni! Ndachita zonse zimene Yehova analamula.”

14 Koma Samueli anati, “Nanga bwanji ndikumva kulira kwa nkhosa ndi ngʼombe?”

15 Sauli anayankha, “Zimenezi Asilikali azitenga kuchokera kwa Aamaleki. Iwo anasungako nkhosa ndi ngʼombe zabwino kuti akapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma zina zonse anaziwononga.”

16 Koma Samueli anati kwa Sauli, “Khala chete! Ima ndikuwuze zimene Yehova wandiwuza usiku wathawu.”

Sauli anayankha kuti, “Ndiwuzeni.”

17 Apo Samueli anati, “Munali wamngʼono pa maso pa anthu, koma tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko a Israeli. Yehova anakudzozani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraeli. 18 Ndipo Yehova anakutumani kuti, ‘Pitani mukawononge kwathunthu Aamaleki, anthu oyipa aja. Mukachite nawo nkhondo mpaka kuwatheratu.’ 19 Chifukwa chiyani simunamvere mawu a Yehova? Chifukwa chiyani munathamangira zofunkha ndi kuchita choyipira Yehova?”

20 Koma Saulo anawuza Samueli kuti, “Ine ndinamveradi mawu a Yehova. Ndinapita kukachita zimene Yehova anandituma. Ndinabwera naye Agagi, mfumu ya Amaleki, koma Aamaleki ena onse anaphedwa. 21 Koma pa zofunkhazo anthu anatengapo nkhosa, ngʼombe ndi zabwino zina zoyenera kuwonongedwa kuti akapereke ngati nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.”

22 Koma Samueli anayankha kuti,

“Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina
    kapena kumvera mawu a ake?
Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe,
    ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa.
23 Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza,
    ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano.
Chifukwa mwakana mawu a Yehova.
    Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.”

24 Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera. 25 Tsopano ndikukupemphani, khululukireni tchimo langa ndipo mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova.”

26 Koma Samueli anawuza Sauli kuti, “Ine sindibwerera nawe. Inu mwakana mawu a Yehova. Choncho Iyenso wakukanani kuti musakhale mfumu yolamulira Aisraeli.”

27 Samueli akutembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo unangʼambika. 28 Samueli anati kwa iye, “Yehova wangʼamba ufumu wanu kuchoka kwa inu, ndipo waupereka kwa mnzanu woposa inu. 29 Mulungu wa ulemerero wa Israeli sanama kapena kusintha maganizo ake; pakuti iye si munthu, kuti asinthe maganizo ake.”

30 Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.” 31 Pamenepo Samueli anabwerera ndi Sauli, ndipo Sauli anapembedza Yehova.

32 Kenaka Samueli anati, “Bwera nayeni kuno Agagi, mfumu ya Amaleki ija.”

Choncho Agagi anapita kwa Samueli mokondwa chifukwa ankaganiza kuti, “Ndithu zowawa za imfa zapita.”

33 Koma Samueli anati,

“Monga momwe lupanga lako linasandutsira amayi kukhala wopanda ana,
    momwemonso amayi ako adzakhala opanda mwana pakati pa amayi.”

Ndipo Samueli anapha Agagi pamaso pa Yehova ku Giligala.

34 Ndipo Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita ku mudzi kwawo ku Gibeya wa Sauli. 35 Samueli sanamuonenso Sauli mpaka imfa yake ngakhale kuti ankamulira Sauliyo. Yehova anamva chisoni kuti anasankha Sauli kuti akhale mfumu ya Israeli.

Aroma 13

Kumvera Aulamuliro

13 Aliyense ayenera kumvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sunachokere kwa Mulungu. Olamulira amene alipo anayikidwa ndi Mulungu. Kotero kuti, iwo amene awukira ulamuliro atsutsana ndi chimene Mulungu anakhazikitsa. Ndipo amene atero adzibweretsera okha chilango. Pakuti olamulira saopseza amene amachita zabwino koma amene amachita zoyipa. Kodi mukufuna kukhala osaopa olamulira? Tsono chitani zoyenera ndipo adzakuyamikirani. Pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokuchitirani zabwino. Koma ngati muchita zoyipa muchite mantha, pakuti iye ali ndi mphamvu zolangira. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wobweretsa mkwiyo ndi kulanga onse ochita zoyipa. Nʼchifukwa chake ndi koyenera kugonjera olamulira, osati chifukwa choopa kulangidwa kokha komanso chifukwa cha chikumbumtima. Ichi nʼchifukwa chakenso inu mumapereka msonkho. Pakuti olamulira ndi atumiki a Mulungu amene amapereka nthawi yawo yonse kulamulira. Mubwezereni aliyense amene munamukongola. Ngati inu muli ndi ngongole yamsonkho, perekani msonkho kwa oyenera kuwalipira. Ngati ndi kuopa perekeni kwa oyenera kuwaopa ndipo ngati ndi ulemu kwa oyenera ulemu.

Chikondi Chimakwaniritsa Malamulo

Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo. Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” 10 Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.

11 Ndipo chitani ichi pozindikira nthawi ino. Nthawi yafika yoti inu mudzuke kutulo, chifukwa chipulumutso chathu chili pafupi tsopano kuposa pamene tinayamba kukhulupirira. 12 Usiku watsala pafupifupi kutha. Kwatsala pangʼono kucha. Tiyeni tsono tichotse ntchito zamdima ndipo tivale chovala chakuwunika. 13 Tiyeni tikhale moyenera monga nthawi ya masana, osati mʼmagulu amadyerero, achiwerewere ndi kuledzera, mʼmadama ndi zonyansa komanso osati mʼmagawano ndi nsanje. 14 Koma valani Ambuye Yesu Khristu ndipo musaganizire za momwe mungakwaniritsire zokhumba zachikhalidwe cha uchimo.

Yeremiya 52

Kuwonongeka kwa Yerusalemu

52 Zedekiya anali wa zaka 21 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Yehoyakimu. Chifukwa cha zonse zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda Yehova anakwiyira anthu ake mpaka kuwachotsa pamaso pake.

Tsono Zedekiya anawukira mfumu ya ku Babuloni.

Choncho mʼchaka cha chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku la khumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo Yerusalemu. Anamanga misasa ndi mitumbira yankhondo kunja kuzungulira mzindawo. Mzindawo unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya.

Pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti munalibe chakudya choti anthu nʼkudya. Tsono linga la mzindawo linabowoledwa, ndipo ankhondo onse anathawa. Iwo anatuluka mu mzindamo usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri a pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Ndipo anathawira ku Araba, koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika.

Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati, kumene anagamula mlandu wake. 10 Ku Ribulako mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona; ndiponso inapha akuluakulu onse a ku Yuda. 11 Ndipo inamukolowola maso Zedekiya, ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni kumene inakamuyika mʼndende kuti akhalemo moyo wake wonse.

12 Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi, chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo a mfumu, amene amatumikira mfumu ya ku Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. 13 Ndipo anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse. 14 Tsono gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene linali ndi mtsogoleri wa ankhondo a mfumu uja linagwetsa malinga onse ozungulira Yerusalemu. 15 Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, anthu aluso pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babuloni kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 16 Komabe Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anasiya anthu ena onse osaukitsitsa a mʼdzikomo kuti azigwira ntchito mʼminda ya mpesa ndi minda ina.

17 Ababuloni anaphwanya nsanamira za mkuwa, maphaka ndi chimbiya chamkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova. Anatenga mkuwa wonsewo nʼkupita nazo ku Babuloni. 18 Ankhondowo anatenganso mbiya, zochotsera phulusa, zozimitsira nyale, mbale zofukizira lubani, zikho pamodzi ndi ziwiya zina zonse za mkuwa zimene ankagwiritsira ntchito mʼNyumba ya Yehova. 19 Nebuzaradani uja anatenganso mabeseni, ziwiya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoyikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho ndi zina zonse zagolide ndi siliva.

20 Nsanamira ziwiri zija, chimbiya, maphaka ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri za mkuwa zochirikizira chimbiyacho zimene mfumu Solomoni anapangira Nyumba ya Yehova kulemera kwake kunali kosawerengeka. 21 Nsanamira imodzi kutalika kwake kunali mamita asanu ndi atatu, akazunguliza chingwe inali mamita asanu ndi theka; mʼkati mwake munali bowo ndipo kuchindikala kwake kunali zala zinayi. 22 Pamwamba pa nsanamira iliyonse panali mutu wamkuwa umene kutalika kwake kunali mamita awiri. Pozungulira pake panali ukonde ndi makangadza, zonsezo za mkuwa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangadza ake ndipo inali yofanana ndi inzake ija. 23 Mʼmbali mwake munali makangadza 96; makangadza onse pamodzi analipo 100 kuzungulira ukonde onse.

24 Mtsogoleri wa ankhondo uja, anagwira Seraya mkulu wa ansembe ndi Zefaniya, wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apachipata. 25 Mu mzindamo anagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndi alangizi amfumu asanu ndi awiri. Anagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu mʼdzikomo, pamodzi ndi anthu ena 60 amene anali mu mzindamo. 26 Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondoyo anawatenga onse napita nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula. 27 Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloniyo inalamula kuti anthuwo aphedwe.

Motero anthu a ku Yuda anapita ku ukapolo, kutali ndi dziko lawo. 28 Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi:

Mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023;

29 mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,

anatenga anthu 832 kuchokera mu Yerusalemu;

30 mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,

Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo a mfumu anagwira Ayuda 745 kupita ku ukapolo.

Onse pamodzi analipo anthu 4,600.

Kumasulidwa kwa Yehoyakini

31 Mʼchaka chimene Evili-Merodaki analowa ufumu wa Babuloni, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, namutulutsa mʼndende. Izi zinachitika pa tsiku la 25 la mwezi wa khumi ndi chiwiri zitatha zaka 37 chitengedwere Yehoyakimu ku ukapolo. 32 Evili-Merodaki anakomera mtima Yehoyakini, namupatsa malo aulemu kuposa mafumu ena amene anali naye ku Babuloni. 33 Choncho Yehoyakini analoledwa kuvula zovala zake za ku ndende ndipo tsiku ndi tsiku ankadya ndi mfumu pa moyo wake wonse. 34 Tsiku ndi tsiku mfumu ya ku Babuloni inkamupatsa Yehoyakini phoso lake nthawi yonse ya moyo wake, mpaka pa nthawi ya imfa yake.

Masalimo 31

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

31 Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;
    musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;
    mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
Tcherani khutu lanu kwa ine,
    bwerani msanga kudzandilanditsa;
mukhale thanthwe langa lothawirapo,
    linga lolimba kundipulumutsa ine.
Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
    chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
Ndimasuleni mu msampha umene anditchera
    pakuti ndinu pothawirapo panga.
Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga;
    womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.

Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe;
    ine ndimadalira Yehova.
Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu
    popeza Inu munaona masautso anga
    ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.
Inu simunandipereke kwa mdani
    koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.

Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;
    maso anga akulefuka ndi chisoni,
    mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10 Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima
    ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;
mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,
    ndipo mafupa anga akulefuka.
11 Chifukwa cha adani anga onse,
    ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;
ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.
    Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12 Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;
    ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;
    zoopsa zandizungulira mbali zonse;
iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,
    kuti atenge moyo wanga.

14 Koma ndikudalira Inu Yehova;
    ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
    ndipulumutseni kwa adani anga
    ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
    pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.
17 Yehova musalole kuti ndichite manyazi,
    pakuti ndalirira kwa Inu;
koma oyipa achititsidwe manyazi
    ndipo agone chete mʼmanda.
18 Milomo yawo yabodzayo ikhale chete,
    pakuti chifukwa cha kunyada
    ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.

19 Ndi waukulu ubwino wanu
    umene mwawasungira amene amakuopani,
umene mumapereka anthu akuona
    kwa iwo amene amathawira kwa Inu.
20 Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa,
    kuwateteza ku ziwembu za anthu;
mʼmalo anu okhalamo mumawateteza
    kwa anthu owatsutsa.

21 Matamando akhale kwa Yehova,
    pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine
    pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.
22 Ndili mʼnkhawa zanga ndinati,
    “Ine ndachotsedwa pamaso panu!”
Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga
    pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.

23 Kondani Yehova oyera mtima ake onse!
    Yehova amasunga wokhulupirika
    koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.
24 Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,
    inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.