Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 12

Samueli Atsanzika Anthu

12 Pambuyo pake Samueli anawuza Aisraeli onse kuti, “Ine ndamvera zonse zimene munandiwuza ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero. Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”

Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.”

Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.”

Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.”

Samueli anawawuzanso kuti, “Yehova ndiye amene anasankha Mose ndi Aaroni kuti atulutse makolo anu mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake tsopano imani pomwepa kuti ndikufotokozereni pamaso pa Yehova, za ntchito za chipulumutso zimene Yehova anachitira inu ndi makolo anu.

“Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano.

“Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu. 10 Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’ 11 Choncho Yehova anatumiza Yeru-Baala, Bedani, Yefita ndi Samueli ndipo anakulanditsani mʼmanja mwa adani anu amene anakuzungulirani, kotero munakhala mwamtendere.

12 “Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu. 13 Tsopano nayi mfumu imene mwayisankha, imene munayipempha. Onani, Yehova wakupatsani mfumu. 14 Ngati muziopa Yehova ndi kumamutumikira ndi kumamumvera, osamupandukira ndiponso ngati inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Yehova Mulungu wanu, ndiye zinthu zonse zidzakuyenderani bwino. 15 Koma mukapanda kumvera Yehova ndi kumupandukira, ndiye adzakulangani pamodzi ndi mfumu yanu yomwe.

16 “Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu! 17 Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.”

18 Choncho Samueli anapemphera, ndipo Yehova anatumiza mvula ya mabingu tsiku lomwelo. Apo anthu aja anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.

19 Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.”

20 Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse. 21 Ndipo musatsate mafano achabechabe amene alibe phindu ndipo sangakupulumutseni popeza ndi achabechabe. 22 Yehova adzakana anthu ake kuopa kuti dzina lake lamphamvu linganyozeke, pakuti chinamukondweretsa Yehova kuti akusandutseni inu kukhala anthu ake. 23 Ndiponso kunena za ine, zisachitike kuti ndichimwire Yehova pakulephera kukupemphererani. Ndipo ine ndidzakuphunzitsani njira yabwino ndi yolungama kuti muziyendamo. 24 Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani. 25 Komabe mukapitirira kuchita zoyipa, ndiye kuti inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzachotsedwa.”

Aroma 10

10 Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe. Popeza ndiwachitira umboni kuti ndi achangu pa zinthu za Mulungu koma osati mwachidziwitso. Pakuti sanadziwe chilungamo chochokera kwa Mulungu ndipo anafuna kukhazikitsa chawochawo. Iwo sanagonjere chilungamo cha Mulungu. Khristu ndiye mathero amalamulo kuti aliyense amene akhulupirira akhale olungama pamaso pa Mulungu.

Mose akulemba motere zachilungamo cha malamulo, “Munthu amene achita zinthu izi adzakhala ndi moyo pozichita.” Koma chilungamo cha chikhulupiriro chikuti, “Usanene mu mtima mwako kuti, ‘Kodi ndani amene akwere kumwamba?’ ” (ndiko, kukatsitsa Khristu) “kapena ‘Ndani adzatsikira ku dziko la anthu akufa?’ ” (ndiko, kukamutenga Khristu kwa akufa). Nanga akuti chiyani? “Mawu ali pafupi ndi inu. Ali mʼkamwa mwanu ndi mu mtima mwanu.” Ndiwo mawu achikhulupiriro amene ife tikuwalalikira, kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10 Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa. 11 Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.” 12 Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye 13 pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”

14 Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? 15 Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”

16 Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?” 17 Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu. 18 Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti,

“Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi.
    Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”

19 Ine ndifunsanso kuti, kodi Israeli sanazindikire? Poyamba Mose akuti,

“Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake.
    Ine ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.”

20 Ndipo Yesaya molimba mtima akuti,

“Anandipeza anthu amene sanali kundifunafuna.
    Ndinadzionetsera kwa amene sanafunse za Ine.”

21 Koma zokhudzana ndi Aisraeli akuti,

“Tsiku lonse ndinatambasulira manja anga
    kwa anthu osandimvera ndi okanika.”

Yeremiya 49

Uthenga Wonena za Aamoni

49 Yehova ananena izi:

Amoni,

“Kodi Israeli alibe ana aamuna?
    Kapena alibe mlowamʼmalo?
Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?
    Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
Koma nthawi ikubwera,”
    akutero Yehova,
“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo
    ku Raba, likulu la Amoni;
ndipo malo awo opembedzera milungu yawo
    adzatenthedwa ndi moto.
Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo
    kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”
            akutero Yehova.
“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!
    Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!
Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;
    thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,
chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,
    pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
Chifukwa chiyani mukunyadira
    chigwa chanu,
inu anthu osakhulupirika
    amene munadalira chuma chanu nʼkumati:
    ‘Ndani angandithire nkhondo?’
Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe
    zochokera kwa onse amene akuzungulira,”
            akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse.
“Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake.
    Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.

“Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,”
            akutero Yehova.

Uthenga Wonena za Edomu

Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu:

“Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani?
    Kodi anzeru analeka kupereka uphungu?
    Kodi nzeru zawo zinatheratu?
Inu anthu a ku Dedani, thawani,
    bwererani ndi kukabisala ku makwalala
chifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esau
    popeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.
Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu
    akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
Anthu akuba akanafika usiku
    akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
10 Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau.
    Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo,
    kotero kuti sadzathanso kubisala.
Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka.
    Palibe wonena kuti,
11 ‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza.
    Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”

12 Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho. 13 Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”

14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova:
    Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti,
“Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu!
    Konzekerani nkhondo!”

15 “Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina.
    Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.
16 Kuopseza kwako kwakunyenga;
    kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,
iwe amene umakhala mʼmapanga
    a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri.
Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga,
    ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”
            akutero Yehova.
17 “Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha.
    Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo
    chifukwa cha kuwonongeka kwake.
18 Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora,
    pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,”
            akutero Yehova,
“motero palibe munthu
    amene adzakhala mu Edomu.

19 “Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani
    kupita ku malo a msipu wobiriwira,
Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo.
    Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine.
Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani?
    Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
20 Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova
    ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani.
Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo
    ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
21 Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera;
    kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
22 Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka
    nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu
    idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.

Uthenga Wonena za Damasiko

23 Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa:

“Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha
    chifukwa amva nkhani yoyipa.
Mitima yawo yagwidwa ndi mantha
    ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
24 Anthu a ku Damasiko alefuka.
    Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa
    chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu.
Ali ndi nkhawa komanso mantha
    ngati za mayi pa nthawi yake yochira.
25 Mzinda wotchuka
    ndi wachikondwerero uja wasiyidwa!
26 Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa;
    ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,”
            akutero Yehova Wamphamvuzonse.
27 “Ndidzatentha malinga a Damasiko;
    moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”

Uthenga Wonena za Kedara ndi Hazori

28 Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa:

“Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara.
    Kawonongeni anthu a kummawako.
29 Landani matenti awo ndi nkhosa zawo,
    ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo.
    Mutengenso ngamira zawo.
Anthu adzafuwula kwa iwo kuti,
    ‘Kuli zoopsa mbali zonse!’

30 “Thawani mofulumira!
    Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,”
            akutero Yehova.
“Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu;
    wakonzekera zoti alimbane nanu.

31 “Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere,
    umene ukukhala mosatekeseka,”
            akutero Yehova,
“mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo;
    anthu ake amakhala pa okha.
32 Ngamira zawo zidzafunkhidwa,
    ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa.
Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali.
    Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,”
            akutero Yehova.
33 “Hazori adzasanduka bwinja,
    malo okhalamo nkhandwe
mpaka muyaya.
    Palibe munthu amene adzayendemo.”

Uthenga Wonena za Elamu

34 Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu:

35 Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu,
    umene uli chida chawo champhamvu.
36 Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamu
    kuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga;
ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi,
    ndipo sipadzakhala dziko
    limene anthu a ku Elamu sadzafikako.
37 A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo
    komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo.
Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga
    ndipo adzakhala pa mavuto,”
            akutero Yehova.
“Ndidzawapirikitsa ndi lupanga
    mpaka nditawatheratu.
38 Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamu
    ndipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,”
            akutero Yehova.

39 “Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezera
    anthu a ku Elamu dziko lawo,”
            akutero Yehova.

Masalimo 26-27

Salimo la Davide.

26 Weruzeni Inu Yehova
    pakuti ndakhala moyo wosalakwa.
Ndadalira Yehova
    popanda kugwedezeka.
Patseni mayeso, Inu Yehova ndipo ndiyeseni,
    santhulani mtima wanga ndi maganizo anga;
pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse,
    ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.
Ine sindikhala pansi pamodzi ndi anthu achinyengo,
    kapena kufunsa nzeru kwa achiphamaso.
Ndimanyansidwa ndi msonkhano wa anthu ochita zoyipa
    ndipo ndimakana kukhala pansi pamodzi ndi oyipa.
Ndimasamba mʼmanja mwanga kuonetsa kusalakwa kwanga
    ndi kupita kukatumikira pa guwa lanu la nsembe, Inu Yehova,
kulengeza mofuwula za matamando anu
    ndi kuwuza onse za ntchito zanu zodabwitsa.
Ndimakonda Nyumba imene Inu Yehova mumakhalamo,
    malo amene ulemerero wanu umapezekako.

Musachotse moyo wanga pamodzi ndi ochimwa,
    moyo wanga pamodzi ndi anthu akupha anzawo,
10 amene mʼmanja mwawo muli ndondomeko zoyipa,
    dzanja lawo lamanja ladzaza ndi ziphuphu.
11 Koma ine ndimakhala moyo wosalakwa;
    mu msonkhano wa anthu anu ndidzatamanda Yehova.

12 Ndayima pa malo wopanda zovuta
    ndipo ndidzatamanda Yehova mu msonkhano waukulu.

Salimo la Davide.

27 Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
    ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
    ndidzachita mantha ndi yani?
Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane
    kudzadya mnofu wanga,
pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo,
    iwo adzapunthwa ndi kugwa.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,
    mtima wanga sudzaopa.
Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane,
    ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.

Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,
    ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:
kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova
    masiku onse a moyo wanga,
ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,
    ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
Pakuti pa tsiku la msautso
    Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo;
adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake
    ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
Kotero mutu wanga udzakwezedwa
    kuposa adani anga amene andizungulira;
pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe;
    ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.

Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova
    mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!”
    Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
Musandibisire nkhope yanu,
    musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;
    mwakhala muli thandizo langa.
Musandikane kapena kunditaya,
    Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
10 Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya
    Yehova adzandisamala.
11 Phunzitseni njira yanu Inu Yehova,
    munditsogolere mʼnjira yowongoka
    chifukwa cha ondizunza.
12 Musandipereke ku zokhumba za adani anga,
    pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane
    ndipo zikundiopseza.

13 Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;
    ndidzaona ubwino wa Yehova
    mʼdziko la anthu amoyo.
14 Dikirani pa Yehova;
    khalani anyonga ndipo limbani mtima
    nimudikire Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.