Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 3

Yehova Ayitana Samueli

Samueli ankatumikira Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Masiku amenewo mawu a Yehova sankamveka pafupipafupi. Kuona zinthu mʼmasomphenya sikunkachitikanso kawirikawiri.

Tsiku lina Eli, amene maso anali ofowoka ndi kuti sankatha kuona bwino, anagona pa malo ake. Nthawiyi nʼkuti nyale ya Mulungu isanazimitsidwe. Samueli anali gone mu Nyumba ya Yehova, kumene kunali Bokosi la Chipangano cha Mulungu. Yehova anayitana Samueli.

Iye anayankha kuti, “Wawa.” Ndipo iyeyo anathamangira kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera ndamva kuyitana.”

Koma Eli anati, “Ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” Ndipo iye anapita kukagona.

Yehova anayitananso, “Samueli!” Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, “Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana.”

Eli nati, “Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone.”

Nthawiyi nʼkuti Samueli asanadziwe Yehova ndipo Mawu a Yehova nʼkuti asanawululidwe kwa iye.

Yehova anayitananso Samueli kachitatu ndipo Samueli anadzuka ndikupita kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera popeza mwandiyitana ndithu.”

Apo Eli anazindikira kuti Yehova ndiye ankayitana mnyamatayo. Tsono Eli anamuwuza Samueli kuti, “Pita ukagone ndipo akakuyitananso ukanene kuti, ‘Yankhulani Yehova, pakuti mtumiki wanu ndikumvetsera.’ ” Choncho Samueli anapita ndi kukagona pamalo pake.

10 Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!”

Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.”

11 Ndipo Yehova anati kwa Samueli, “Taona, patsala pangʼono kuti ndichite chinthu china mu Israeli chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzamve. 12 Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndinayankhula zokhudza banja la Eli kuyambira poyamba mpaka pomaliza. 13 Pakuti ndinamudziwitsa kuti Ine ndikhoza kulanga banja lake kwamuyaya chifukwa cha zoyipa zimene ana ake ankadziyipitsa nazo. Iye ankadziwa zimenezi koma osawaletsa. 14 Nʼchifukwa chake ndinalumbira kuti, ‘Zoyipa zimene banja la Eli linandichita sizidzafafanizidwa mpaka muyaya ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.’ ”

15 Samueli anagona mpaka mmawa. Atadzuka anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova. Iye anachita mantha kumuwuza Eli za masomphenya ake. 16 Koma Eli anamuyitana nati, “Samueli mwana wanga.”

Samueli anayankha kuti, “Wawa.”

17 Tsono Eli anafunsa kuti, “Yehova wakuwuza chiyani? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu ngati undibisira chilichonse cha zimene wakuwuza.” 18 Choncho Samueli anamuwuza zonse, sanamubisire kalikonse. Ndipo Eli anati, “Iye ndi Yehova, mulekeni achite chimene chamukomera.”

19 Yehova anali ndi Samueli pamene amakula, ndipo zonse zimene ankayankhula zinkachitikadi. 20 Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dera la Dani mpaka ku Beeriseba anazindikira kuti Yehova analozadi chala pa Samueli kuti akhale mneneri wake. 21 Yehova anapitiriza kuoneka ku Silo, ndipo kumeneko anadziwulula yekha kwa Samueli mwa mawu ake.

Aroma 3

Kukhulupirika kwa Mulungu

Nanga kodi pali ubwino wotani pokhala Myuda, kapena muli ubwino wanjinso mu mdulidwe? Ubwino wake ndi wambiri mʼnjira zonse! Choyambirira iwo anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti awasunge.

Nanga zili bwanji ngati ena analibe chikhulupiriro? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawo kukanalepheretsa kukhulupirika kwa Mulungu? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti,

“Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula
    ndi kupambana pamene muweruza.”

Koma ngati kuyipa mtima kwathu kuonetsa poyera kuti Mulungu ndi wolungama, ife tinganene chiyani? Kodi tinganene kuti Mulungu ndi wosalungama pamene aonetsa mkwiyo wake pa ife? (Ine ndikuyankhula monga mmene anthu ena amayankhulira). Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ngati zikanakhala zotero, kodi Mulungu akanaweruza bwanji dziko lapansi? Wina atanena kuti, “Ngati kunama kwanga kukuonetsa koposa kuti Mulungu ndi woona, ndi kuwonjezera pa ulemerero wake, nanga nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa kuti ndine wochimwa?” Nʼchifukwa chiyani osanena kuti, monga ena amanena mosasamala kuti, “Tiyeni tichite zoyipa kuti zabwino zionekere?” Anthu onena zoterewa kulangidwa kwawo ndi koyenera.

Palibe Munthu Wolungama

Kodi timalize bwanji? Kodi Ayuda ndife oposa anthu ena? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Ife tinanena kale kuti Ayuda ndi a mitundu ina omwe ndi ochimwa. 10 Monga kwalembedwa kuti,

“Palibe munthu wolungama, inde palibe ndi mmodzi yemwe.
11     Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira,
    palibe amene amafunafuna Mulungu.
12 Onse apatukira kumbali,
    onse pamodzi asanduka opandapake.
Palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita zabwino,
    palibe ngakhale mmodzi.”
13 “Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;
    ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.”
“Ululu wa mamba uli pa milomo yawo.”
14     “Mʼkamwa mwawo ndi modzaza ndi zotemberera ndi mawu owawa.”
15 “Mapazi awo afulumira kukakhetsa magazi.
16     Kusakaza ndi chisoni kumaonekera mʼnjira zawo,
17 ndipo njira ya mtendere sayidziwa.”
18     “Saopa Mulungu ndi pangʼono pomwe.”

19 Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu. 20 Chifukwa chake palibe mmodzi amene adzayesedwa wolungama pamaso pake chifukwa chosunga Malamulo, kuti ife timazindikira tchimo kupyolera mu Malamulo.

Kulungama Mwachikhulupiriro

21 Koma tsopano chilungamo chochokera kwa Mulungu, osati chochokera ku Malamulo, chaonetsedwa. Ichi ndi chimene Malamulo ndi Aneneri amachitira umboni. 22 Timakhala olungama pamaso pa Mulungu pamene takhulupirira Yesu Khristu. Mulungu amachitira zimenezi anthu onse amene akhulupirira Khristu. Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, 23 pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Mulungu 24 ndipo onse alungamitsidwa mwaulere mwa chisomo chake chifukwa cha Khristu Yesu amene anawawombola. 25 Mulungu anamupereka Iyeyu kuti pokhetsa magazi ake, akhale nsembe yokhululukira machimo. Mulungu anachita zimenezi kufuna kuonetsa chilungamo chake. Chifukwa cha kuleza mtima kwake, sanalange anthu chifukwa cha machimo amene anachita kale. 26 Iye anachita izi kuti aonetse chilungamo chake lero lino. Anthu azindikire kuti Iye ndi wolungama ndipo amalungamitsa aliyense amene akhulupirira Yesu.

27 Nanga tsono pamenepa munthu anganyadenso? Kunyadatu kwachotsedwa. Chifukwa cha Malamulo? Kodi Malamulo samafuna ntchito za munthu? Ayi, koma mwachikhulupiriro. 28 Ife tikunenabe kuti munthu amalungamitsidwa mwachikhulupiriro osati mwakusunga Malamulo. 29 Kodi Mulungu ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si Mulungu wa a mitundu inanso? Inde wa a mitundu inanso, 30 popeza ndi Mulungu mmodzi yemweyo amene adzalungamitsa mwachikhulupiriro ochita mdulidwe ndi osachita mdulidwe kudzera mʼchikhulupiriro chomwecho. 31 Kodi tsono ife, tikutaya Malamulo pamene tikunena kuti pafunika chikhulupiriro? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Komatu ife tikukwaniritsadi Malamulo.

Yeremiya 41

41 Pa mwezi wachisanu ndi chiwiri Ismaeli mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama amene anali wa banja laufumu ndiponso mmodzi wa atsogoleri a ankhondo a mfumu, anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ndi anthu khumi. Pamene ankadya naye kumeneko, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu khumi aja anayimirira ndi kupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Choncho anapha munthu amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kukhala bwanamkubwa wa dzikolo. Ismaeli anaphanso Ayuda onse amene anali pamodzi ndi Gedaliya ku Mizipa, kuphatikizanso asilikali a Ababuloni amene anali ku Mizipako.

Mmawa mwake, anthu asanadziwe kuti Gedaliya waphedwa, kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova. Ismaeli mwana wa Netaniya anachoka ku Mizipa akulira kupita kukakumana nawo. Atakumana nawo, iye anati, “Bwerani mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.” Atafika pakati pa mzinda, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu amene anali naye anawapha anthuwo ndi kuwaponya mʼchitsime. Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja. Tsono chitsime chimene anaponyamo mitembo ya anthu amene anawaphawo pamodzi ndi mtembo wa Gedaliya chinali chimene mfumu Asa anachikumba poopsedwa ndi Baasa mfumu ya Israeli. Ismaeli mwana wa Netaliya anachidzaza ndi mitembo.

10 Pambuyo pake Ismaeli anatenga ukapolo anthu ena onse amene anali ku Mizipa: ana aakazi a mfumu pamodzi ndi ena onse amene anatsalira kumeneko, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wawo. Ismaeli mwana wa Netaliya anatenga ukapolo anthuwa ndi kuwoloka nawo kumapita ku dziko la Aamoni.

11 Pamene Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye pamodzi anamva zoyipa zonse zimene Ismaeli mwana wa Netaniya anachita, 12 anatenga ankhondo awo onse kupita kukamenyana ndi Ismaeli mwana wa Netaniya. Anakamupeza kufupi ndi chidziwe chachikulu cha ku Gibiyoni. 13 Pamene anthu onse amene Ismaeli anawagwira anaona Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali naye, anasangalala. 14 Anthu onse amene Ismaeli anawagwira ukapolo ku Mizipa anabwerera ndi kupita kwa Yohanani mwana wa Kareya. 15 Koma Ismaeli pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, anathawa Yohanani ndi kuthawira kwa Aamoni.

Kuthawira ku Igupto

16 Kenaka Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye anatsogolera anthu onse otsala a ku Mizipa amene anawapulumutsa kwa Ismaeli mwana wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Anthu amenewa anali: asilikali, akazi, ana ndi amuna ofulidwa otumikira mfumu amene anawatenga ku Gibiyoni. 17 Ndipo ananyamuka nayima ku Geruti Kimuhamu pafupi ndi Betelehemu pa ulendo wawo wopita ku Igupto 18 kuthawa Ababuloni. Iwo anaopa Ababuloniwo chifukwa Ismaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babuloni inamuyika kukhala bwanamkubwa wa dzikolo.

Masalimo 17

Pemphero la Davide.

17 Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo;
    mverani kulira kwanga.
Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa
    popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.
Kusalakwa kwanga kuchokera kwa inu;
    maso anu aone chimene ndi cholungama.

Ngakhale Inu mutafufuza mtima wanga ndi kundisanthula usiku,
    ngakhale mutandiyesa, simudzapeza kanthu;
    Ine ndatsimikiza kuti pakamwa panga sipadzachimwa.
Kunena za ntchito za anthu,
    monga mwa mawu a pakamwa panu,
Ine ndadzisunga ndekha
    posatsata njira zachiwawa.
Mayendedwe anga akhazikika pa njira zanu;
    mapazi anga sanaterereke.

Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha;
    tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.
Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu,
    Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja
    iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.
Mundisunge ine ngati mwanadiso;
    mundibise mu mthunzi wa mapiko anu,
kuchoka kwa oyipa amene amandizinga ine,
    kuchoka kwa anthu amene ndi adani anga, amene andizungulira ine.

10 Iwo amatseka mitima yawo yopanda chifundo,
    ndi pakamwa pawo amayankhula modzitamandira.
11 Andisaka, tsopano andizungulira
    ndi maso awo atcheru, kuti andigwetse pansi.
12 Iwo ali ngati mkango wofuna nyama;
    ngati mkango waukulu wokhala mobisala.

13 Dzukani Yehova, mulimbane nawo ndipo muwagwetse pansi;
    landitseni kuchoka kwa oyipa ndi lupanga lanu.
14 Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere,
    kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno.

Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu;
    ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri,
    ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
15 Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu;
    pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.