Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 14

14 Tsiku lina Yonatani mwana wa Sauli anawuza mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka Afilisti tsidya ilo.” Koma iye sanawuze abambo ake.

Sauli ankakhala mʼmalire a Gibeya pa tsinde pa mtengo wamakangadza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600. Pakati pawo panalinso Ahiya amene ankavala efodi. Iye anali mwana wa Ahitubi, mʼbale wake wa Ikabodi mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo. Koma palibe amene anadziwa kuti Yonatani wachoka.

Pa mpata pamene Yonatani ankafuna kudutsa kukafika ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti kunali thanthwe lotsetsereka mbali ina ndi lina lotsetsereka mbali inayo. Thanthwe limodzi linkatchedwa Bozezi ndipo linalo linkatchedwa Seni. Thanthwe limodzi linali chakumpoto kuyangʼanana ndi Mikimasi, ndipo thanthwe linalo linali chakummwera kuyangʼanana ndi Geba.

Yonatani anawuza mnyamata wake womunyamulira zida uja kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka anthu osachita mdulidwewo. Mwina Yehova adzatigwirira ntchito. Palibe chomuletsa Yehova kutipulumutsa, ngakhale tikhale ambiri kapena ochepa.”

Mnyamata uja anati, “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukhumba. Ine ndili nanu pamodzi. Chimene mtima wanu ukhumba ndi chomwenso ine ndikhumba.”

Yonatani anati, “Tiye tsono tiwoloke kupita kumene kuli anthuwo ndi kukadzionetsa kwa iwo. Akatiwuza kuti, ‘Imani pomwepo mpaka tikupezeni,’ ife tikangoyima pomwepo osapita kumene kuli iwoko. 10 Koma akadzati, ‘Bwerani kuno,’ ndiye ife tikapitedi, chifukwa ichi chidzakhala chizindikiro chakuti Yehova wapereka mʼmanja mwathu.”

11 Choncho awiriwa anadzionetsa ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti. Tsono Afilistiwo anati, “Taonani! Aheberi akutuluka mʼmaenje mʼmene anabisala.” 12 Anthu a ku kaboma kaja anafuwula kwa Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Bwerani kuno ndipo tikuphunzitsani phunziro.”

Ndipo Yonatani anati kwa mnyamata wake. “Nditsate pakuti Yehova wapereka Afilistiwa mʼmanja mwa Aisraeli.”

13 Choncho Yonatani anakwera mokwawa, ndipo mnyamata wake uja ankamutsata. Tsono Yonatani anathira nkhondo Afilisti aja namawagwetsa, ndipo mnyamata wake uja ankawapha pambuyo pa iyeyo. 14 Nthawi yoyambayo Yonatani ndi mnyamata wake uja anapha anthu makumi awiri ndipo anawaphera pa malo ochepa okwanira ngati theka la ekala.

Aisraeli Agonjetsa Afilisti

15 Tsono gulu lonse la ankhondo, ndiye kuti iwo amene anali mʼmisasa ndi mʼminda ndiponso iwo amene anali ku kaboma ka ankhondo kaja, onse anagwidwa ndi mantha aakulu. Dzikonso linagwedezeka, choncho anthu anachita mantha koopsa.

16 Alonda a Sauli a ku Gibeya dziko la Benjamini atangomwaza maso anangoona chigulu cha asilikali chikumwazikana uku ndi uku. 17 Kenaka Sauli anawawuza anthu amene anali naye kuti, “Awerengeni asilikali kuti muona amene wachoka.” Atawawerenga anapeza kuti Yonatani ndi mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo palibe.

18 Tsono Sauli anawuza Ahiya kuti, “Bwera nalo Bokosi la Mulungulo.” (Nthawi imeneyo nʼkuti efodiyo ili ndi Ahiya pamaso pa Aisraeli). 19 Pamene Sauli amayankhula ndi wansembe, phokoso limanka likulirakulira mu msasa wa Afilisti, Kotero Sauli anati kwa wansembe, “Leka kuwombeza.”

20 Ndipo Sauli ndi asilikali onse amene anali naye anasonkhana kupita kukamenya nkhondo, ndipo anangoona chisokonezo chachikulu kwambiri. Afilisti akuphana okhaokha. 21 Aheberi ena amene kale anali ndi Afilisti mpaka kukakhala ku misasa yawo, iwonso anatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraeli amene ankatsata Sauli ndi Yonatani. 22 Ngakhale Aisraeli amene ankabisala ku dziko lamapiri la Efereimu atamva kuti Afilisti akuthawa, nawonso anawathamangitsa Afilistiwo nawathira nkhondo. 23 Nkhondo inapitirira mpaka kufika ku Beti-Aveni. Choncho Yehova anapulumutsa Aisraeli tsiku limenelo.

Yonatani Adya Uchi

24 Koma asilikali a Israeli anavutika tsiku limenelo, chifukwa Sauli anawalumbirira Aisraeli kuti, “Wotembereredwa munthu aliyense amene adzadya kusanade, ine ndisanalipsire adani anga!” Kotero palibe wankhondo aliyense amene analawa chakudya.

25 Gulu lonse la ankhondo linalowa mʼnkhalango mmene munali uchi. 26 Atalowa mʼnkhalango, anaona uchi ukukha, koma palibe amene anadya, pakuti ankaopa lumbiro lija. 27 Koma Yonatani sanamve kuti abambo ake anawalumbirira anthu aja choncho anatenga ndodo yake imene inali mʼdzanja lake ndipo anayipisa mu chisa cha njuchi. Choncho iye anadya uchiwo ndipo mʼmaso mwake munayera. 28 Kenaka mmodzi mwa Asilikali anamuwuza kuti, “Abambo ako alumbirira anthu nati, ‘Wotembereredwa munthu aliyense amene adye chakudya lero.’ Nʼchifukwa chake anthu alefuka.”

29 Yonatani anati, “Abambo anga achita chinthu choyipira dziko. Taonani mʼmaso mwanga mwayera chifukwa ndalawa uchiwu pangʼono. 30 Zikanakhala zabwino kwambiri anthuwa akanadya lero zofunkha za adani awo. Zikanatero tikanapha Afilisti ochuluka.”

31 Tsiku limenelo Aisraeli anapha Afilisti kuchokera ku Mikimasi mpaka ku Ayaloni. Koma Aisraeliwo analefuka kwambiri ndi njala. 32 Choncho iwo anathamangira pa zofunkha ndipo anatenga nkhosa, ngʼombe ndi ana angʼombe. Iwo anazipha zonsezi nazidya pamodzi ndi magazi omwe. 33 Koma anthu ena anawuza Sauli kuti, “Taona anthu akuchimwira Yehova pakudya nyama yomwe ili ndi magazi.”

Ndipo Sauli anati, “Mwaonetsa kusakhulupirika. Tsopano gubuduzirani mwala waukulu pano.” 34 Kenaka Sauli anati, “Mwazikanani pakati pa anthu ndi kukawawuza kuti aliyense abwere ndi ngʼombe yake kapena nkhosa yake, ndipo adzayiphe pomwe pano ndi kuyidya. Musachimwire Yehova pakudya nyama imene ili ndi magazi.”

Kotero aliyense anabwera ndi ngʼombe yake usiku womwewo ndi kuyipha pomwepo. 35 Ndipo Sauli anamangira Yehova guwa. Ili linali guwa loyamba limene Sauli anamangira Yehova.

36 Sauli anati, “Tiyeni titsatire Afilisti usikuwu ndi kulanda zinthu zawo mpaka mmawa. Tisasiyepo wamoyo ndi mmodzi yemwe.”

Ankhondowo anayankha kuti, “Chitani chilichonse chimene chikukomerani.”

Koma wansembe anati, “Tipemphe uphungu kwa Mulungu poyamba.”

37 Choncho Sauli anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndiwatsatire Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwathu?” Koma Mulungu sanamuyankhe tsiku limenelo.

38 Choncho Sauli anati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu, ndipo tiyeni tione kuti kodi tchimo limeneli lachitika bwanji lero? 39 Pali Yehova amene amapulumutsa Israeli, ngakhale tchimolo litapezeka ndi mwana wanga Yonatani, iye afe ndithu.” Koma palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthuwo amene anamuyankha.

40 Tsono Sauli anawuza Aisraeli onse kuti, “Inu mukhale mbali imodzi. Ine ndi mwana wanga Yonatani tikhala mbali inayo.”

“Chitani chilichonse chimene chikukomerani.”

41 Ndipo Sauli anapemphera kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, “Chifukwa chiyani simunandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati tchimoli lipezeka ndi ine kapena ndi Yonatani mwana wanga, Inu Mulungu wa Israeli, aoneke ndi Urimu. Koma ngati wochimwa ndi anthu anu, Aisraeli aoneke Tamimu.” Maere anagwera Sauli ndi Yonatani ndipo anthu anapezeka osalakwa. 42 Sauli anati, “Chitani maere pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga.” Ndipo maere anagwera Yonatani.

43 Kenaka Sauli anati kwa Yonatani, “Ndiwuze chimene wachita.”

Ndipo Yonatani anamuwuza kuti, “Ine ndinangolawa uchi pangʼono ndi ndodo yangayi. Ndiye ine ndili wokonzeka kufa.”

44 Sauli anati, “Mulungu andilange ngakhale kufa kumene, ngati sufa iwe Yonatani.”

45 Koma anthuwo anafunsa Saulo kuti, “Kodi Yonatani afe, iye amene wagwira ntchito iyi yayikulu yopulumutsa Aisraeli? Osatheka! Pali Yehova ngakhale tsitsi ndi limodzi lomwe lapamutu pake silidzathothoka, pakuti wachita zimenezi lero ndi thandizo la Mulungu.” Choncho anthuwo anamupulumutsa Yonatani, ndipo sanaphedwe.

46 Pambuyo pake Sauli analeka kulondola Afilisti, kenaka anabwerera ku dziko lawo.

47 Sauli ali mtsogoleri wa Israeli, anachita nkhondo ndi adani awa omuzungulira: Mowabu, Amoni, Edomu mafumu a ku Zoba ndi Afilisti. Kulikonse kumene ankapita ankawagonjetsa. 48 Anachita nkhondo mwamphamvu ndi kugonjetsa Aamaleki. Choncho anapulumutsa Aisraeli mʼmanja mwa anthu amene ankawalanda zinthu zawo.

Banja la Sauli

49 Ana aamuna a Sauli anali Yonatani, Isivi ndi Maliki-Suwa. Analinso ndi ana aakazi awiri, dzina la mwana wake wamkulu wamkazi linali Merabi ndipo la mwana wake wamngʼono wamkazi linali Mikala. 50 Dzina la mkazi wake linali Ahinoamu. Iyeyu anali mwana wa Ahimaazi. Dzina la mkulu wa ankhondo a Sauli linali Abineri mwana wa Neri, mʼbale wa abambo a Sauli. 51 Kisi abambo a Sauli ndi Neri abambo a Abineri anali ana a Abieli.

52 Pa moyo wake wonse, Sauli ankakhalira kuchita nkhondo pakati pa Israeli ndi Afilisti. Ndipo Sauli ankati akaona munthu aliyense wamphamvu kapena wolimba mtima ankamulemba ntchito mu gulu lake lankhondo.

Aroma 12

Nsembe za Moyo

12 Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu. Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani. Pakuti monga aliyense wa ife ali ndi thupi limodzi koma ziwalo zambiri, ziwalozi sizili ndi ntchito yofanana. Momwemonso mwa Khristu ife amene tili ambiri tipanga thupi limodzi ndipo chiwalo chilichonse ndi cholumikizika ku chinzake. Ife tili ndi mphatso zosiyana, molingana ndi chisomo chopatsidwa kwa ife. Ngati mphatso ya munthu ndi kunenera, musiyeni ayigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chake. Ngati ndi kutumikira, musiyeni atumikire. Ngati ndi kuphunzitsa, musiyeni aphunzitse. Ngati ndi kulimbikitsa, musiyeni alimbikitse. Ngati ndi kupereka kuthandiza osowa, musiyeni apereke mowolowamanja. Ngati ndi utsogoleri, musiyeni alamulire mosamala. Ngati ndi kuonetsa chifundo, musiyeni achite mosangalala.

Chikondi

Chikondi chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwiritsitsa chabwino. 10 Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni. 11 Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye. 12 Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero. 13 Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo.

14 Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere. 15 Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira. 16 Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse.

17 Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense. 18 Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere. 19 Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye. 20 Koma,

“Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya.
    Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa.
Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”

21 Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.

Yeremiya 51

51 Yehova akuti,

“Taonani, ndidzadzutsa mphepo yowononga
    kuti iwononge Babuloni pamodzi ndi anthu a ku Lebi Kamai.
Ndidzatuma alendo ku Babuloni
    kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu.
Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse
    pa tsiku la masautso ake.
Okoka uta musawalekerere
    kapena wonyadira chovala chawo chankhondo.
Musawasiye anyamata ake kuti akhale ndi moyo;
    koma muwononge ankhondo ake kotheratu.
Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babuloni
    lomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe.
Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiye
    ndi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse,
koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimo
    pamaso pa Woyerayo wa Israeli.

“Thawaniko ku Babuloni!
    Aliyense apulumutse moyo wake!
    Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake.
Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange;
    Yehova adzamulipsira.
Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova;
    kuti aledzeretse dziko lonse lapansi.
Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake;
    nʼchifukwa chake tsopano inachita misala.
Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka.
    Mulireni!
Mfunireni mankhwala opha ululu wake;
    mwina iye nʼkuchira.”

Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni,
    koma sanachire;
tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo,
    pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga,
    wafika mpaka kumwamba.’

10 “ ‘Yehova waonetsa poyera kuti ndife osalakwa;
    tiyeni tilengeze mu Ziyoni
    zimene Yehova Mulungu wathu wachita.’

11 “Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi,
    popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni.
Motero adzalipsira Ababuloni
    chifukwa chowononga Nyumba yake.
Ndiye Yehova akuti,
    ‘Nolani mivi, tengani zishango.’
12 Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni!
    Limbitsani oteteza,
ikani alonda pa malo awo,
    konzekerani kulalira.
Pakuti Yehova watsimikiza
    ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.
13 Inu muli ndi mitsinje yambiri
    ndi chuma chambiri.
Koma chimaliziro chanu chafika,
    moyo wanu watha.
14 Yehova Wamphamvuzonse analumbira pali Iye mwini kuti:
    Ndidzakutumizira adani ochuluka ngati dzombe,
    kuti adzakuthire nkhondo ndipo adzafuwula kuonetsa kuti apambana.

15 “Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;
    Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake
    ndipo anayala thambo mwaluso lake.
16 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba.
    Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula
    ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.

17 “Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;
    mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.
Mafano akewo ndi abodza;
    alibe moyo mʼkati mwawo.
18 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.
    Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.
19 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.
    Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse,
kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.
    Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

20 “Iwe Babuloni ndi ndodo yanga,
    chida changa chankhondo.
Ndi iwe ndimaphwanya mitundu ya anthu,
    ndi iwe ndimawononga maufumu,
21 ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo,
    ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake.
22 Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi,
    ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata,
    ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali.
23 Ndi iwe ndimaphwanya mʼbusa ndi ziweto,
    ndi iwe ndimaphwanya mlimi ndi ngʼombe,
    ndi iwe ndimaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri a ankhondo.

24 “Inu mukuona ndidzalanga Babuloni ndi onse amene amakhala mʼdziko la Babuloni chifukwa cha zolakwa zonse anachita ku Ziyoni,” akutero Yehova.

25 “Taonani, ndikukuzenga mlandu, iwe phiri lowononga,
    amene umawononga dziko lonse lapansi,”
            akutero Yehova.
“Ndidzatambalitsa dzanja langa pofuna kukulanga,
    kukugubuduzira pansi kuchokera pa matanthwe ako,
    ndi kukusandutsa kukhala phiri lopserera.
26 Palibe ngakhale ndi mwala wako umodzi umene anthu adzawutenga
    kuti awugwiritse ntchito kumangira nyumba,
    chifukwa iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,”
            akutero Yehova.

27 “Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko!
    Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu!
Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo;
    itanani maufumu awa:
    Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo.
Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye;
    tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.
28 Konzekeretsani mitundu ya anthu.
    Amenewa ndiwo mafumu a Amedi,
abwanamkubwa awo, atsogoleri a ankhondo,
    ndiponso ankhondo a mayiko amene amawalamulira, kuti idzathire nkhondo Babuloni.
29 Dziko likunjenjemera ndi kunthunthumira,
    chifukwa zidzachitikadi zimene Yehova wakonzera Babuloni;
kusakaza dziko la Babuloni
    kuti musapezeke wokhalamo.
30 Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo;
    iwo angokhala mʼmalinga awo.
Mphamvu zawo zatheratu;
    ndipo akhala ngati akazi.
Malo ake wokhala atenthedwa;
    mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.
31 Othamanga akungopezanapezana,
    amithenga akungotsatanatsatana
kudzawuza mfumu ya ku Babuloni
    kuti alande mzinda wake wonse.
32 Madooko onse alandidwa,
    malo onse obisalamo alonda atenthedwa ndi moto,
    ndipo ankhondo onse asokonezeka.”

33 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,

“Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigu
    pa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti,
    Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.”

34 A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga,
    watiphwanya,
    ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu.
Watimeza ngati ngʼona,
    wakhuta ndi zakudya zathu zokoma,
    kenaka nʼkutilavula.”
35 Anthu a ku Ziyoni anene kuti,
    “Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.”
Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti,
    “Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.”

36 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,

“Taona, ndidzakumenyera nkhondo
    ndi kukulipsirira;
ndidzawumitsa nyanja yake
    ndipo akasupe ake adzaphwa.
37 Motero Babuloni adzasanduka mulu wa nyumba zogumuka,
    malo okhala nkhandwe,
malo ochititsa mantha ndi onyozedwa,
    malo wopanda aliyense wokhalamo.
38 Anthu ake onse adzabangula ngati mkango,
    adzadzuma ngati ana amkango.
39 Ngati achita dyera
    ndiye ndidzawakonzera madyerero
    ndi kuwaledzeretsa,
kotero kuti adzasangalala,
    kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,”
            akutero Yehova.
40 “Ine ndidzawatenga
    kuti akaphedwe ngati ana ankhosa onenepa,
    ngati nkhosa zazimuna ndi mbuzi.

41 “Ndithu Babuloni walandidwa,
    mzinda umene dziko lonse lapansi limanyadira wagwidwa!
Taonani, mmene Babuloni wasandukira chinthu chochititsa mantha
    pakati pa mitundu ya anthu!
42 Nyanja yakwera ndi kumiza Babuloni;
    mafunde ake okokoma aphimba Babuloni.
43 Mizinda yake yasanduka bwinja,
    dziko lowuma ndi lachipululu,
dziko losakhalamo wina aliyense,
    dziko losayendamo munthu aliyense.
44 Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni,
    ndidzamusanzitsa zimene anameza.
Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye.
    Malinga a Babuloni agwa.

45 “Tulukani mʼBabuloni anthu anga!
    Pulumutsani miyoyo yanu!
    Thawani mkwiyo woopsa wa Yehova.
46 Musataye mtima kapena kuchita mantha
    pamene mphekesera zikumveka mʼdziko mwanu.
Chaka ndi chaka pamabuka mphekesera
    za ziwawa mʼdziko lapansi,
    ndiponso yakuti mfumu yakuti ikuthira nkhondo mfumu ina.
47 Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithu
    pamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni;
dziko lake lonse lidzachita manyazi
    ndi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.
48 Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo
    zidzayimba mokondwa chifukwa cha kugwa kwa Babuloni.
Anthu owononga ochokera kumpoto
    adzamuthira nkhondo,”
            akutero Yehova.

49 “Babuloni anapha anthu ambiri pa dziko lapansi.
    Tsono, nawo anthu a ku Babuloni ayenera kuphedwa
    chifukwa anapha anthu a ku Yerusalemu.
50 Inu amene munapulumuka ku nkhondo ya Babuloni,
    chokani pano ndipo musazengereze!
Kumbukirani Yehova ngakhale muli ku mayiko akutali,
    ganizirani za Yerusalemu.”

51 Inu mukuti, “Tikuchita manyazi,
    chifukwa tanyozedwa
    ndipo nkhope zathu zili ndi manyazi,
chifukwa anthu achilendo alowa
    malo opatulika a Nyumba ya Yehova.”

52 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,
    “Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake,
ndipo mʼdziko lake lonse
    anthu ovulala adzabuwula.
53 Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalenga
    ndi kulimbitsa nsanja zake,
    ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,”
            akutero Yehova.

54 “Imvani mfuwu wolira kuchokera ku Babuloni.
    Imvani phokoso lachiwonongeko chachikulu
    kuchokera mʼdziko la Babuloni.
55 Pakuti Yehova akuwononga Babuloni,
    ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu.
Mfuwu wa adani ukumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri.
    Phokoso lawo likunka likwererakwerera.
56 Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni,
    ankhondo ake agwidwa,
    ndipo mauta awo athyoka.
Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango;
    adzabwezera kwathunthu.
57 Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake,
    abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo;
adzagona kwamuyaya osadzukanso,”
    akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

58 Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwa
    ndipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa;
mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe.
    Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”

59 Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo. 60 Yeremiya anali atalemba mʼbuku za masautso onse amene adzafike pa Babuloni ndi zina zonse zokhudza Babuloni. 61 Yeremiya anawuza Seraya kuti, “Ukakafika ku Babuloni, ukaonetsetse kuti wawawerengera anthu onse mawu onsewa. 62 Ndipo ukanene kuti, ‘Inu Yehova, mwanena kuti mudzawononga malo ano, kotero kuti simudzatsala munthu kapena nyama mʼdziko muno; lidzakhala chipululu mpaka muyaya.’ 63 Ukakatha kuwerenga bukuli, ukalimangirire ku mwala ndipo ukaliponye pakati pa mtsinje wa Yufurate. 64 Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene adzamirire Babuloni ndipo sadzadzukanso chifukwa cha masautso amene adzamugwere.’ ”

Mawu a Yeremiya athera pamenepa.

Masalimo 30

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

30 Ndidzakukwezani Yehova,
    chifukwa mwanditulutsa kwakuya,
    ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo
    ndipo Inu munandichiritsa.
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,
    munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;
    tamandani dzina lake loyera.
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi
    koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;
utha kuchezera kulira usiku wonse,
    koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,
    “Sindidzagwedezekanso.”
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,
    munachititsa phiri langa kuyima chilili;
koma pamene munabisa nkhope yanu,
    ndinataya mtima.

Kwa Inu Yehova ndinayitana;
    kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga
    ngati nditsikira ku dzenje?
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?
    Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;
    Yehova mukhale thandizo langa.”

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;
    munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.
    Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.