Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Oweruza 17

Mafuno a Mika

17 Munthu wina dzina lake Mika wochokera ku dziko la mapiri la Efereimu anawuza amayi ake kuti “Ndinamva inu mukutemberera munthu amene anaba ndalama zanu zasiliva 1,100. Ndalamazo zili ndi ine, ndinatenga ndine.”

Pamenepo amayi akewo anati, “Yehova akudalitse mwana wanga!”

Choncho Mika anabweza ndalama 1,100 za siliva kwa amayi ake, ndipo amayi akewo anati, “Ine ndapatulira Yehova ndalama za silivazi kuti mwana wanga aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Ndiye tsopano ndikubwezera ndalamazo.”

Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake.

Mikayu anali ndi kachisi, ndipo anapanga efodi ndi mafano otchedwa terafimu. Anapatula mwana wake mmodzi kuti akhale wansembe. Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense amachita zomwe zinamukomera.

Ku Betelehemu mʼdziko la Yuda kunali mnyamata wina amene anali wa fuko la Levi. Iyeyu anachoka mu mzinda wa Betelehemu uja ku Yuda kukafuna malo ena okhala. Akuyenda, anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ku nyumba ya Mika.

Tsono Mika anamufunsa kuti, “Mukuchokera kuti?”

Ndipo iye anayakha kuti, “Ndine Mlevi wochokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Ndikufunafuna malo okhala.”

10 Tsono Mika anati kwa iye, “Khalani ndi ine. Mukhale ngati mlangizi wanga ndi wansembe, ndipo ine ndizikupatsani ndalama za siliva khumi pa chaka komanso zovala ndi zakudya.” 11 Choncho Mleviyo anavomera kuti azikhala naye, ndipo mnyamatayo anakhala ngati mmodzi mwa ana ake aamuna. 12 Pambuyo pake Mika anapatula Mleviyo ndipo mnyamatayu anakhala wansembe. Tsono ankakhala mʼnyumba ya Mika. 13 Ndipo Mika anati, “Tsopano ndadziwa kuti Yehova adzandikomera mtima chifukwa Mleviyu ndiye wakhala wansembe wanga.”

Machitidwe a Atumwi 21

Paulo Apita ku Yerusalemu

21 Titalawirana nawo, tinachoka kumeneko mʼsitima ya pamadzi, ndipo tinayenda molunjika mpaka kufika ku Kosi. Mmawa mwake tinapita ku Rode, kuchokera kumeneko tinapita ku Patara. Kumeneko tinapeza sitima yapamadzi yopita ku Foinike. Choncho tinalowamo nʼkunyamuka. Tinaona chilumba cha Kupro ndipo tinadutsa kummwera kwake nʼkupita ku Siriya. Tinakayima ku Turo chifukwa sitima yathuyo imayenera kusiya katundu kumeneko. Tinafunafuna ophunzira kumeneko, ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku asanu ndi awiri. Iwowa, mwa Mzimu Woyera anakakamiza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. Koma nthawi yathu itatha, tinachokako ndi kupitiriza ulendo wathu. Ophunzira onse pamodzi ndi akazi awo ndi ana anatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Ndipo kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja ndi kupemphera. Titatsanzikana, tinalowa mʼsitima ija, iwowo anabwerera ku nyumba zawo.

Ife tinapitiriza ulendo wathu wochokera ku Turo mpaka tinafika ku Ptolemayi. Kumeneko tinalonjera abale ndi kukhala nawo tsiku limodzi. Tinachoka mmawa mwake, mpaka tinakafika ku Kaisareya. Tinapita kukakhala mʼnyumba ya mlaliki Filipo, amene anali mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi awiri aja. Iye anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa amene anali ndi mphatso ya uneneri.

10 Titakhala kumeneko masiku ambiri, kunabwera mneneri wina wochokera ku Yudeya dzina lake Agabu. 11 Atafika kwa ife, anatenga lamba wa Paulo, nadzimanga naye manja ake ndi mapazi ake ndipo anati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwini lambayu, Ayuda adzamumanga chomwechi ku Yerusalemu, ndipo adzamupereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina.’ ”

12 Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu kumeneko tinamudandaulira Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima? Ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha ayi, komanso kufa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” 14 Titalephera kumuletsa tinamuleka ndipo tinati, “Chifuniro cha Ambuye chichitike.”

15 Pambuyo pake, ife tinakonzeka ndi kunyamuka kumapita ku Yerusalemu. 16 Ena mwa ophunzira a ku Kaisareya anatiperekeza mpaka kukatifikitsa ku nyumba ya Mnasoni, kumene tinakonza kuti tizikhalako. Iye anali wa ku Kupro ndiponso mmodzi wa ophunzira oyambirira.

Paulo Afika ku Yerusalemu

17 Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandira mwachimwemwe. 18 Mmawa mwake Paulo pamodzi ndi ife tonse tinapita kwa Yakobo, ndipo akulu onse a mpingo anali komweko. 19 Paulo anawalonjera ndi kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.

20 Atamva zimenezi, iwo anayamika Mulungu. Kenaka anawuza Paulo kuti, “Mʼbale, ukuona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene anakhulupirira, ndipo ndi okhulupirika potsatira Malamulo a Mose. 21 Iwo anawuzidwa kuti iwe umaphunzitsa Ayuda onse amene akukhala pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Mose, kuti asamachite mdulidwe kapena kutsatira miyambo. 22 Nanga pamenepa ife titani? Iwo adzamva ndithu kuti iwe wabwera, 23 tsono iwe chita zimene ife tikuwuze. Tili nawo amuna anayi pano amene anachita lumbiro kwa Mulungu. 24 Muwatenge anthu amenewa, ndipo muchite nawo mwambo wowayeretsa ndipo muwalipirire zoti apereke kuti amete tsitsi lawo. Kotero aliyense adzadziwa kuti palibe choonadi pa zimene anamva za inu, koma kuti inu mwini mumakhala moyo womvera Malamulo. 25 Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.”

26 Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.

Agwira Paulo

27 Ali pafupi kutsiriza masiku asanu ndi awiriwo, Ayuda ena ochokera ku Asiya anaona Paulo mʼNyumba ya Mulungu. Iwo anawutsa gulu lonse la anthu ndipo anamugwira Paulo, 28 akufuwula kuti, “Inu Aisraeli, tithandizeni! Ndi uyu munthu uja amaphunzitsa anthu onse ponseponse kuti azinyoza mtundu wathu ndiponso Malamulo athu ndi malo ano. Kuwonjezera pamenepo, walowetsa Agriki mʼbwalo la Nyumba ino ndipo wadetsa malo opatulika.” 29 Iwo ananena izi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mu mzindamo ndipo iwo ankaganiza kuti Paulo anamulowetsa mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.

30 Mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anabwera akuthamanga kuchokera kumbali zonse. Anamugwira Paulo, namukokera kunja kwa Nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo anatseka zipata. 31 Pamene anthuwo ankafuna kupha Paulo, nkhaniyi inamveka kwa mkulu wa magulu a asilikali a Aroma kuti mzinda wonse wa Yerusalemu wasokonezeka. 32 Nthawi yomweyo iye anatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali ndi kuthamangira kumene kunali anthuwo. Anthuwo ataona mkuluyo ndi asilikali ake analeka kumenya Paulo.

33 Mkulu wa asilikaliyo anabwera nagwira Paulo, ndipo analamula kuti amangidwe ndi maunyolo awiri. Kenaka iye anafunsa kuti ndi ndani ndipo wachita chiyani. 34 Ena mʼgulumo anafuwula chinthu china ndi enanso chinanso. Tsono popeza mkulu wa asilikaliyo sanathe kudziwa choonadi chenicheni chifukwa cha phokoso, analamula kuti Paulo atengedwe kupita ku malo a asilikali. 35 Paulo atafika pa makwerero olowera ku malo a asilikaliwo, ananyamulidwa ndi asilikali chifukwa cha ukali wa anthuwo. 36 Gulu la anthu limene linamutsatira linapitiriza kufuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi!”

Paulo Ayankhula

37 Asilikali ali pafupi kulowa naye ku malo awo, iye anapempha mkulu wa asilikaliyo kuti, “Kodi mungandilole ndiyankhulepo?”

Mkulu wa asilikaliyo anafunsa kuti, “Kodi umayankhula Chigriki? 38 Kodi sindiwe Mwigupto uja amene masiku apitawo unayambitsa kuwukira ndi kutsogolera anthu 4,000 owukira aja nʼkupita nawo ku chipululu?”

39 Paulo anayankha kuti, “Ine ndine Myuda, wa ku Tarisisi ku Kilikiya. Sindine nzika ya mzinda wamba. Chonde loleni ndiyankhule nawo anthuwa.”

40 Ataloledwa ndi mkulu wa asilikaliyo, Paulo anayimirira pa makwereropo nakweza dzanja lake kwa gulu la anthuwo. Onse atakhala chete, iye anayankhula nawo mʼChihebri.

Yeremiya 30-31

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

30 Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndakuwuza. Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”

Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda: “Yehova akuti:

“Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa,
    ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.
Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti:
    Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana?
Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna
    atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira?
    Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri!
    Sipadzakhala lina lofanana nalo.
Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo,
    koma adzapulumuka ku masautsowo.”

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo,
    ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo
ndipo ndidzadula zingwe zowamanga;
    Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.
Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo
    ndiponso Davide mfumu yawo,
    amene ndidzawasankhira.

10 “ ‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo;
    usade nkhawa, iwe Israeli,’
            akutero Yehova.
‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali,
    zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo.
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere,
    ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha.
11 Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’
    akutero Yehova.
‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu
    kumene ndinakubalalitsirani,
    koma inu sindidzakuwonongani kotheratu.
Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa.
    Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ”

12 Yehova akuti,

“Chilonda chanu nʼchosachizika,
    bala lanu ndi lonyeka.
13 Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu,
    palibe chiyembekezo choti inu nʼkuchira,
    palibe mankhwala ochiritsa inu.
14 Abwenzi anu onse akuyiwalani;
    sasamalanso za inu.
Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira.
    Ndipo ndakulangani mwa nkhanza,
chifukwa machimo anu ndi ambiri,
    ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
15 Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu?
    Bala lanu silingapole ayi.
Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri
    ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.

16 “Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa;
    adani anu onse adzapita ku ukapolo.
Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso;
    onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.
17 Ndidzachiza matenda anu
    ndi kupoletsa zilonda zanu,
            akutero Yehova,
‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika.
    Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”

18 Yehova akuti,

“Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo
    ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo;
mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake,
    nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
19 Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova
    ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo.
Ndidzawachulukitsa,
    ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika;
ndidzawapatsa ulemerero,
    ndipo sadzanyozedwanso.
20 Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale,
    ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga;
    ndidzalanga onse owazunza.
21 Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo.
    Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo.
Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira.
    Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane
    popanda kuyitanidwa?”
            akutero Yehova.
22 “Choncho inu mudzakhala anthu anga,
    ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”

23 Taonani ukali wa Yehova wowomba
    ngati mphepo ya mkuntho.
Mphepo ya namondwe
    ikuwomba pa mitu ya anthu oyipa.
24 Mkwiyo woopsa wa Yehova sudzachoka
    mpaka atakwaniritsa zolinga
    za mu mtima mwake.
Mudzamvetsa zimenezi
    masiku akubwerawo.

31 “Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”

Yehova akuti,

“Anthu amene anapulumuka ku nkhondo
    ndinawakomera mtima mʼchipululu;
    pamene Aisraeli ankafuna kupumula.”

Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati,

“Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire.
    Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.
Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli;
    mudzasangalala poyimba tizitoliro tanu,
ndipo mudzapita kukavina nawo
    anthu ovina mwachimwemwe.
Mudzalimanso minda ya mpesa
    pa mapiri a Samariya;
alimi adzadzala mphesa
    ndipo adzadya zipatso zake.
Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwula
    pa mapiri a Efereimu nati,
‘Tiyeni tipite ku Ziyoni,
    kwa Yehova Mulungu wathu.’ ”

Yehova akuti,

“Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo,
    fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse.
Matamando anu amveke, ndipo munene kuti,
    ‘Yehova wapulumutsa anthu ake
    otsala a Israeli.’
Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto,
    ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezera
    ndi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi.
    Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno.
Adzabwera akulira;
    koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza.
Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzi
    mʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo.
Chifukwa ndine abambo ake a Israeli,
    ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba.

10 “Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;
    lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja;
‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsanso
    ndipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’
11 Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakobo
    anawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu.
12 Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;
    adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova.
Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta,
    ana ankhosa ndi ana angʼombe.
Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino,
    ndipo sadzamvanso chisoni.
13 Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.
    Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala.
Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo;
    ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.
14 Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino,
    ndipo anthu anga adzakhuta ndi zabwino zanga,”
            akutero Yehova.

15 Yehova akuti,

“Kulira kukumveka ku Rama,
    kulira kwakukulu,
Rakele akulirira ana ake.
    Sakutonthozeka
    chifukwa ana akewo palibe.”

16 Yehova akuti,

“Leka kulira
    ndi kukhetsa misozi
pakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,”
            akutero Yehova.
    “Iwo adzabwerako ku dziko la adani.
17 Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,”
            akutero Yehova.
    “Ana ako adzabwerera ku dziko lawo.

18 “Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti,
    ‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva.
    Koma inu mwatiphunzitsa kumvera.
Mutibweze kuti tithe kubwerera,
    chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.
19 Popeza tatembenuka mtima,
    ndiye tikumva chisoni;
popeza tazindikira
    ndiye tikudziguguda pachifukwa.
Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa
    chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’
20 Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,
    mwana amene Ine ndimakondwera naye?
Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula,
    ndimamukumbukirabe.
Kotero mtima wanga ukumufunabe;
    ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,”
            akutero Yehova.

21 “Muyike zizindikiro za mu msewu;
    muyimike zikwangwani.
Yangʼanitsitsani msewuwo,
    njira imene mukuyendamo.
Bwerera, iwe namwali wa Israeli,
    bwerera ku mizinda yako ija.
22 Udzakhala jenkha mpaka liti,
    iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika?
Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”

23 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’ 24 Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa. 25 Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.”

26 Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma.

27 “Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachulukitsa anthu pamodzi ndi ziweto mʼdziko la Israeli ndi la Yuda. 28 Monga momwe ndinasamalira powazula, powagwetsa, powagumula, powawononga ndi powachita zoyipa, momwemonso ndidzasamala powamanga ndi powadzala” akutero Yehova. 29 “Mʼmasiku amenewo anthu sadzanenanso kuti,

“Makolo adya mphesa zosapsa,
    koma mano a ana ndiye achita dziru.

30 Mʼmalo wake, munthu aliyense adzafa chifukwa cha tchimo lake. Iye amene adzadye mphesa zosapsazo ndiye amene mano ake adzachite dziru.”

31 “Masiku akubwera,” akutero Yehova,
    “pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
    ndiponso nyumba ya Yuda.
32 Silidzakhala ngati pangano
    limene ndinachita ndi makolo awo
pamene ndinawagwira padzanja
    nʼkuwatulutsa ku Igupto;
chifukwa anaphwanya pangano langa,
    ngakhale ndinali mwamuna wawo,”
            akutero Yehova.
33 “Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli
    atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo
    ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo
    ndipo iwo adzakhala anthu anga.
34 Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,
    kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’
chifukwa onse adzandidziwa Ine,
    kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”
            akutero Yehova.
“Ndidzawakhululukira zoyipa zawo
    ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

35 Yehova akuti,

Iye amene amakhazikitsa dzuwa
    kuti liziwala masana,
amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyezi
    ziziwala usiku,
amene amavundula nyanja
    kuti mafunde akokome,
    dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
36 Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga.

37 Yehova akuti,

“Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo.
    Ngati patapezeka munthu
amene angathe kupima zakuthambo
    nʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”

38 “Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya. 39 Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa. 40 Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”

Marko 16

Kuuka kwa Yesu

16 Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu. Mmamawa, tsiku loyamba la Sabata, dzuwa litangotuluka kumene, anali pa ulendo wopita ku manda ndipo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi akatikugudubuzira mwala pa khomo la manda ndani?”

Koma atakweza maso awo, anaona kuti mwala umene unali waukulu kwambiri wagubuduzidwa kale. Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha.

Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo. Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’ ”

Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha.

[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe vesi 9 mpaka 20.]

Yesu Aonekera kwa Mariya Magadalena

Yesu atauka kwa akufa mmawa pa tsiku loyamba la Sabata, anayamba kuonekera kwa Mariya Magadalena, amene anatulutsa mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri. 10 Iye anapita ndi kukawawuza amene anali ndi Yesu, amene ankakhuza maliro ndi kulira. 11 Atamva kuti Yesu ali moyo ndikuti amuona, iwo sanakhulupirire.

Yesu Aonekera kwa Ophunzira Awiri

12 Zitatha izi Yesu anaonekera mʼmaonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali ku dera la ku mudzi. 13 Iwo anabwerera ndi kudzawawuza enawo; koma iwo sanakhulupirirebe.

Yesu Ayankhula kwa Ophunzira Khumi ndi Mmodzi

14 Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.

15 Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse. 16 Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa. 17 Tsono zizindikiro izi zidzawatsata amene adzakhulupirira: Mʼdzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula malilime atsopano; 18 adzanyamula njoka ndi manja awo; ndipo pamene adzamwa mankhwala akupha, sadzawapweteka nʼpangʼonongʼono pomwe; adzasanjika manja awo pa anthu odwala ndipo odwalawo adzachira.”

Yesu Apita Kumwamba

19 Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu. 20 Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.