M’Cheyne Bible Reading Plan
10 Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi: 2 Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’ ”
3 “Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo. 4 Adzakupatsa moni ndi kukupatsa malofu awiri a buledi. Iwe udzalandire bulediyo.
5 “Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera. 6 Kenaka Mzimu wa Yehova udzabwera pa iwe ndi mphamvu, ndipo udzayamba kulosera nawo pamodzi. Ndipo udzasinthika kukhala munthu wina. 7 Zizindikiro izi zikakachitika, dzachite chilichonse manja ako angathe kuchita, pakuti Mulungu ali nawe.
8 “Tsono tsogola kupita ku Giligala. Ine ndidzabwera ndithu kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Koma ukandidikire masiku asanu ndi awiri mpaka ine nditabwera kuti ndidzakuwuze zomwe udzachite.”
Sauli Avekedwa Ufumu
9 Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo. 10 Atafika ku Gibeya, anakumana ndi gulu la aneneri. Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwamphamvu, nayamba kulosa nawo. 11 Pamene onse amene ankamudziwa kale anamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anafunsana wina ndi mnzake. “Kodi nʼchiyani chachitika ndi mwana wa Kisi? Kodi Sauli alinso mʼgulu la aneneri?”
12 Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?” 13 Sauli atasiya kuloserako, anapita ku kachisi ku phiri.
14 Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?”
Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.”
15 Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.”
16 Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza.
17 Samueli anayitana Aisraeli onse kuti asonkhane pamaso pa Yehova ku Mizipa. 18 Ndipo anawuza Aisraeli onse kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi kukupulumutsani mʼdzanja la Igupto ndi mʼdzanja la mafumu onse amene ankakuzunzani.’ 19 Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.”
20 Samueli atasonkhanitsa mafuko onse a Israeli, fuko la Benjamini linasankhidwa. 21 Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze. 22 Tsono anthu anafunsanso kwa Yehova kuti, “Kodi munthuyu wabwera kale kuno?”
Ndipo Yehova anayankha kuti, “Inde wabisala pakati pa katundu.”
23 Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa. 24 Samueli anafunsa anthu onse kuti, “Kodi mukumuona munthu amene Yehova wasankha? Palibe wofanana naye pakati pa anthu onse.”
Kenaka anthu onse anafuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
25 Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo.
26 Sauli anapitanso ku mudzi kwawo ku Gibeya, pamodzi ndi anthu amphamvu amene Mulungu anawafewetsa mitima. 27 Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko.
Moyo Watsopano mwa Khristu
8 Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa 2 chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa. 3 Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu, 4 ndi cholinga chakuti chilungamo chofunikira cha lamulo chikwaniritsidwe kwathunthu mwa ife amene sitikhala monga mwachikhalidwe chathu cha uchimo koma mwa Mzimu.
5 Pakuti anthu amene amakhala monga mwa makhalidwe oyipa a thupi amayika malingaliro awo pa zinthu zathupi. Koma amene amakhala monga mwa Mzimu amayika malingaliro awo pa zinthu za Mzimu. 6 Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere. 7 Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero. 8 Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.
9 Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu. 10 Ndipo ngati Khristu ali mwa inu, thupi lanu ndi lakufa chifukwa cha uchimo, koma mzimu wanu ndi wamoyo chifukwa cha chilungamo. 11 Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.
12 Kotero abale, ife tili ndi zoti tikwaniritse, koma osati za khalidwe lathu lauchimo, kumachita zofuna zake. 13 Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu. 15 Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.” 16 Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu. 17 Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Ulemerero wa Mʼtsogolo
18 Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife. 19 Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu. 20 Pakuti chilengedwe sichinasankhe kugonjera zopanda pake, koma mwachifuniro cha Iye amene analola kuti chigonjere. Koma chili ndi chiyembekezo 21 chakuti chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulandiranso ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.
22 Ife tikudziwa kuti chilengedwe chonse chakhala chikubuwula ndi ululu ngati ululu wa nthawi yobereka mwana mpaka tsopano lino. 23 Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu. 24 Pakuti ife tinapulumutsidwa mʼchiyembekezo ichi. Koma chiyembekezo chimene chimaoneka si chiyembekezo ayi. Kodi ndani amene amayembekezera chimene ali nacho kale? 25 Koma ngati ife tiyembekeza chimene tikanalibe, ndiye kuti tikuyembekeza modekha mtima.
26 Momwemonso, Mzimu amatithandiza ife mʼkufowoka kwathu. Ife sitidziwa momwe tiyenera kupempherera koma Mzimu mwini amatipempherera mobuwula ndi mawu osafotokozedwa. 27 Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.
Oposa Agonjetsi
28 Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake. 29 Pakuti amene Mulungu anawadziwiratu, anawasankhiratunso kuti akonzedwe mʼchifanizo cha Mwana wake, kuti Iye akhale Mwana woyamba kubadwa mwa abale ambiri. 30 Iwo amene anawasankhiratu, anawayitananso. Amene Iye anawayitana anawalungamitsanso ndipo amene anawalungamitsa anawapatsanso ulemerero.
31 Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani? 32 Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anamupereka chifukwa cha ife tonse. Iye adzalekeranjinso pamodzi naye kutipatsa ife zinthu zonse mwaulere? 33 Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha? Ndi Mulungu amene amalungamitsa. 34 Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera. 35 Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga? 36 Monga kwalembedwa:
“Chifukwa cha inu, ife tikuphedwa tsiku lonse:
ife tikutengedwa ngati nkhosa zoti zikaphedwe.”
37 Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda. 38 Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, 39 ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Uthenga Wonena za Afilisti
47 Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:
2 Yehova akuti,
“Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;
adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.
Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,
mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.
Anthu adzafuwula;
anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira
3 akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,
phokoso la magaleta ake
ndi kulira kwa mikombero yake.
Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;
manja awo adzangoti khoba.
4 Pakuti tsiku lafika
lowononga Afilisti onse
ndi kupha onse otsala,
onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.
Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,
otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.
5 Anthu a ku Gaza ameta mipala;
anthu a ku Asikeloni akhala chete.
Inu otsala a ku chigwa,
mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?
6 “Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,
kodi udzapumula liti?
Bwerera mʼmalo ako;
ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’
7 Koma lupangalo lidzapumula bwanji
pamene Yehova walilamulira
kuti lithire nkhondo
Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”
Salimo la Davide.
23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
3 amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
chifukwa cha dzina lake.
4 Ngakhale ndiyende
mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
zimanditonthoza.
5 Mumandikonzera chakudya
adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
chikho changa chimasefukira.
6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
kwamuyaya.
Salimo la Davide.
24 Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo,
dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
2 pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja
ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.
3 Ndani angakwere phiri la Yehova?
Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
4 Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,
amene sapereka moyo wake kwa fano
kapena kulumbira mwachinyengo.
5 Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova
ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
6 Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;
amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.
Sela
7 Tukulani mitu yanu inu zipata;
tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
8 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Yehova Wamphamvuzonse,
Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
9 Tukulani mitu yanu, inu zipata;
tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
10 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
Yehova Wamphamvuzonse,
Iye ndiye Mfumu yaulemerero.
Sela
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.