M’Cheyne Bible Reading Plan
Ukwati wa Samsoni
14 Samsoni anapita ku Timna ndipo kumeneko anaonako mtsikana wa Chifilisiti. 2 Atabwerera kwawo, anawuza abambo ndi amayi ake kuti, “Ine ndaona mtsikana wa Chifilisiti ku Timna, tsono mukanditengere ameneyo kuti akhale mkazi wanga.”
3 Koma abambo ndi amayi ake anayankha kuti, “Kodi palibe mkazi pakati pa abale akowa kapena pakati pa anthu a mtundu wako, kuti iwe upite kukapeza mkazi kwa Afilisti anthu osachita mdulidwe?”
Koma Samsoni anawuza abambo ake kuti, “Kanditengereni ameneyu basi, pakuti ndamukonda.” 4 (Abambo ndi amayi ake sankadziwa kuti zimenezi zinali zochokera kwa Yehova, pakuti Yehova amafuna powapezera chifukwa Afilistiwo. Nthawi imeneyo nʼkuti Afilisti akulamulira Aisraeli). 5 Choncho Samsoni pamodzi ndi abambo ake anapita ku Timna. Akuyandikira minda ya mpesa ya ku Timna, mwadzidzidzi anamva kubuma kwa mkango waungʼono ukubwera kumene kunali iye. 6 Tsono Mzimu wa Yehova unafika ndi mphamvu pa Samsoni ndipo ngakhale analibe chida mʼmanja mwake, iye anakadzula mkangowo ngati akukadzula mwana wambuzi. Koma sanawuze abambo kapena amayi ake zimene anachitazo. 7 Kenaka Samsoni anapita kukakambirana ndi mkaziyo, ndipo anamukonda mtsikanayo.
8 Patapita nthawi, Samsoni anabwerera kukatenga mtsikana uja. Panjira anapatuka kukaona mkango unawupha uja, ndipo anangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake. 9 Tsono anakomberako uchi uja mʼmanja mwake ndi kumapita akudya. Atabwereranso kwa abambo ndi amayi ake, anawapatsako uchiwo ndipo anadya. Koma sanawawuze kuti uchi umenewo anawufula mu mkango wakufa.
10 Tsopano Samsoni anapita ku nyumba kwa mtsikanayo. Ndipo kumeneko Samsoni anakonza phwando monga ankachitira anyamata. 11 Makolo a mkwatibwiyo atamuona, anasankha anyamata makumi atatu kuti akhale naye.
12 Samsoni anawawuza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi. Mukandiwuza tanthauzo lake asanathe masiku asanu ndi awiri aphwandowa, ndidzakupatsani zovala makumi atatu za bafuta ndi zina makumi atatu za tsiku la chikondwerero. 13 Koma ngati simutha kundiwuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa zovala makumi atatu zabafuta ndi zina za tsiku la chikondwerero.”
Iwo anamuyankha kuti, “Tiwuze mwambi wakowo tiwumve.”
14 Iye anati,
“Chakudya chinatuluka mu chinthu chodya chinzake;
ndipo chozuna chinatuluka mu chinthu champhamvu.”
Panapita masiku atatu anthuwo akulephera kumasulira mwambiwo.
15 Tsiku lachinayi anthuwo anawuza mkazi wa Samsoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako kuti akuwuze tanthauzo la mwambiwu. Ngati sutero tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya abambo ako. Kodi unatiyitana kuti mudzatilande zinthu zathu?”
16 Kenaka mkazi wa Samsoni anayamba kulira pamaso pake namuwuza kuti, “Inu mumandida ndipo simundikonda. Mwaphera anyamata a mtundu wathu mwambi, koma ine wosandiwuza tanthauzo lake.”
Samsoni anamuyankha kuti, “Taona sindinawuze abambo kapena amayi anga, ndiye ndiwuze iweyo?” 17 Mkaziyo anamulirira masiku onse asanu ndi awiri aphwandowo. Choncho pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuwuza tanthauzo lake popeza amamukakamiza. Ndipo mkaziyo anakawuza abale ake aja tanthauzo la mwambiwo.
18 Pambuyo pake anthu a mu mzinda aja anamuwuza Samsoni pa tsiku lachisanu ndi chiwiri dzuwa lisanalowe kuti,
“Chozuna nʼchiyani choposa uchi?
Champhamvu nʼchiyani choposa mkango?”
Samsoni anawawuza kuti,
“Mukanapanda kutipula ndi ngʼombe yanga yayingʼono,
simukanatha kumasulira mwambi wangawu.”
19 Ndipo Mzimu wa Yehova unafika pa iye mwamphamvu. Choncho anatsikira ku Asikeloni naphako anthu makumi atatu, natenga zovala zawo za tsiku la chikondwerero napereka kwa anthu amene anamasulira mwambi wake. Kenaka anabwerera ku nyumba ya abambo ake ndi mkwiyo waukulu. 20 Ndipo mkazi wa Samsoniyo anamukwatitsa kwa amene anali mnzake womuperekeza pa ukwati paja.
Ku Korinto
18 Zitatha izi, Paulo anachoka ku Atene ndipo anapita ku Korinto. 2 Kumeneko anakumana ndi Myuda wina dzina lake Akula, nzika ya ku Ponto amene anali atangofika kumene kuchokera ku Italiya pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudiyo analamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Paulo anapita kukawaona. 3 Popeza Paulo anali mʼmisiri wosoka matenti monga iwo, iye anakhala nawo namagwirira ntchito pamodzi. 4 Tsiku la Sabata lililonse Paulo amakambirana ndi anthu mʼsunagoge, kufuna kukopa Ayuda ndi Agriki.
5 Sila ndi Timoteyo atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo ankangogwira ntchito yolalikira yokha basi, kuchitira umboni Ayuda kuti Yesu ndiye Khristu. 6 Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, “Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina.”
7 Ndipo Paulo anatuluka mʼsunagoge napita ku nyumba yoyandikana ndi sunagoge ya Tito Yusto, munthu wopembedza Mulungu. 8 Krispo, mkulu wa sunagoge, pamodzi ndi a pa banja lake lonse anakhulupirira Ambuye; ndiponso Akorinto ambiri amene anamva Paulo akulalikira anakhulupiriranso nabatizidwa.
9 Usiku wina Ambuye anaonekera kwa Paulo mʼmasomphenya namuwuza kuti, “Usaope, pitiriza kuyankhula, usakhale chete. 10 Pakuti Ine ndili nawe, palibe aliyense amene adzakukhudza ndi kukuchitira choyipa, chifukwa mu mzinda muno ndili ndi anthu ambiri.” 11 Choncho Paulo anakhala kumeneko chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi akuphunzitsa Mawu a Mulungu.
12 Galiyo ali mkulu wa boma wa ku Akaya, Ayuda mogwirizana anamugwira Paulo napita naye ku bwalo la milandu. 13 Iwo anati, “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mwanjira zotsutsana ndi malamulo athu.”
14 Pamene Paulo ankati ayankhule, Galiyo anati kwa Ayuda, “Ukanakhala mlandu wochita choyipa kapena wolakwira mnzake, bwenzi nditakumverani bwinobwino. 15 Koma popeza ndi nkhani yokhudza mawu, mayina ndi malamulo anu, kambiranani nokhanokha. Ine sindidzaweruza zinthu zimenezi.” 16 Kotero iye anawapirikitsa mʼbwalo la milandu. 17 Kenaka iwo anagwira Sositene, mkulu wa sunagoge, ndipo anamumenya mʼbwalo la milandu momwemo. Koma Galiyo sanasamale zimenezi.
Prisila, Akula ndi Apolo
18 Paulo anakhalabe ku Korinto masiku ambiri. Kenaka anawasiya abale nakwera sitima ya pamadzi kupita ku Siriya, pamodzi ndi Prisila ndi Akula. Asanakakwere sitima ya pamadzi, anameta tsitsi lake ku Kenkreya chifukwa anali atalumbira. 19 Iwo anafika ku Efeso, kumene Paulo anasiyako Prisila ndi Akula. Iye yekha analowa mʼsunagoge nakambirana ndi Ayuda. 20 Iwo atapempha kuti akakhale nawo nthawi yayitali, iye anakana. 21 Koma pamene amachoka anawalonjeza kuti, “Ndidzabweranso Mulungu akalola.” Ndipo anakwera sitima ya pamadzi kuchoka ku Efeso. 22 Pamene Paulo anafika ku Kaisareya, anakwera kukapereka moni ku mpingo kenaka anatsikira ku Antiokeya.
23 Atakhala kwa kanthawi ku Antiokeya, Paulo anachokako nayendera madera onse a ku Galatiya ndi ku Frugiya kulimbikitsa ophunzira onse.
Za Apolo
24 Pa nthawi yomweyi Myuda wina dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Alekisandriya anafika ku Efeso. Anali munthu wophunzira ndi wodziwa bwino Malemba. 25 Apoloyu anaphunzitsidwa njira ya Ambuye, ndipo anayankhula ndi changu chachikulu naphunzitsa za Yesu molondola, ngakhale amadziwa ubatizo wa Yohane wokha. 26 Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.
27 Pamene Apolo anafuna kupita ku Akaya, abale anamulimbikitsa, nalemba kalata kwa ophunzira a kumeneko kuti amulandire. Atafika kumeneko, anathandiza kwambiri amene anakhulupirira mwachisomo. 28 Pakuti iye anatsutsa Ayuda mwamphamvu pamaso pa anthu, natsimikiza kuchokera mʼMalemba kuti Yesu ndiye Khristu.
Yuda Adzatumikira Nebukadinezara
27 Zedekiya mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kulamulira, Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2 “Tenga zingwe zomangira ndi mitengo ya goli ndipo uzimangirire mʼkhosi mwako. 3 Tsono utumize uthenga kwa mafumu a Edomu, Mowabu, Amoni, Turo ndi Sidoni kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya Yuda. 4 Uwapatse uthenga wokapereka kwa ambuye awo ndipo uwawuze kuti: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Mukawuze ambuye anu kuti: 5 Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna. 6 Tsopano ndidzapereka mayiko anu onse kwa mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Ndamupatsanso nyama zakuthengo zonse kuti zimutumikire. 7 Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.
8 “ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu. 9 Choncho musamvere aneneri anu, owombeza anu, otanthauza maloto anu, amawula anu kapena amatsenga anu akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni.’ 10 Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu. 11 Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ”
12 Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo. 13 Nanga inu ndi anthu anu, muferenji ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, zimene Yehova waopsezera mtundu wina uliwonse umene sudzatumikira mfumu ya ku Babuloni? 14 Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza. 15 Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.”
16 Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu. 17 Musawamvere. Tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo mudzakhala ndi moyo. Mzindawu usandukirenji bwinja? 18 Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni. 19 Pakuti Yehova akunena za zipilala, za mbiya ya madzi, maphaka ndi ziwiya zina zimene zatsala mu Yerusalemu. 20 Izi ndi zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni sanatenge pamene anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda kupita ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu, pamodzi ndi anthu olemekezeka a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 21 Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena za zinthu zimene zinatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi mu Yerusalemu kuti, 22 ‘Zidzatengedwa kupita ku Babuloni ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzawakumbukirenso,’ akutero Yehova. ‘Pamenepo ndidzazitenganso ndi kuzibwezanso ku malo ano.’ ”
Zizindikiro za Kutha kwa Masiku Yomaliza
13 Iye atachoka mʼNyumba ya Mulungu, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Aphunzitsi taonani! Miyala ikuluikulu! Nyumba zikongolerenji!”
2 Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuziona nyumba zikuluzikuluzi? Palibe mwala ndi umodzi pano umene udzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
3 Yesu atakhala pansi pa phiri la Olivi moyangʼanana ndi Nyumba ya Mulungu, Petro, Yakobo, Yohane ndi Andreya anamufunsa Iye pambali kuti, 4 “Tatiwuzani, izi zidzachitika liti? Nanga chizindikiro chakuti zatsala pangʼono kukwaniritsidwa chidzakhala chiyani?”
5 Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani kuti wina asakunyengeni. 6 Anthu ambiri adzabwera mʼdzina langa, nadzati, ‘Ine ndi Iyeyo,’ ndipo adzanamiza anthu ambiri. 7 Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi. 8 Mtundu udzawukira mtundu unzake, ndi ufumu kuwukira ufumu unzake. Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana, ndi njala. Izi ndi chiyambi chabe cha zowawa monga mayi pobereka.
9 “Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. 10 Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. 11 Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.
12 “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 13 Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
14 “Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri. 15 Aliyense amene ali pa denga la nyumba yake asatsike kapena kulowa mʼnyumba kukatenga kanthu kalikonse. 16 Aliyense amene ali ku munda asabwerere kukatenga mkanjo wake. 17 Kudzakhala koopsa mʼmasiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! 18 Pempherani kuti zimenezi zisadzachitike nthawi yozizira, 19 chifukwa masiku amenewo adzakhala owawitsa osafanana ndi ena kuyambira pachiyambi, pamene Mulungu analenga dziko, kufikira lero ndipo sadzafanananso ndi ena. 20 Ambuye akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwiratu, amene anawasankha, Iye anawafupikitsa. 21 Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire. 22 Pakuti akhristu onama ndi aneneri onama adzaonekera ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa kuti anyenge osankhidwiratu ngati kutakhala kotheka kutero. 23 Choncho khalani tcheru; ndakuwuzani zonse nthawi isanafike.
24 “Koma masiku amenewo, masautsowo atatha,
“ ‘dzuwa lidzada,
ndipo mwezi sudzawala;
25 nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo,
ndipo mayiko mumlengalenga adzagwedezeka!’
26 “Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero. 27 Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.
28 “Tsopano phunzirani phunziro ili kuchokera ku mtengo wamkuyu. Pamene msonga za nthambi zake zikhala za nthete ndipo masamba ake ayamba kuphukira, mumadziwa kuti dzinja layandikira. 29 Momwenso pamene muona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti wayandikira, ali pa khomo. 30 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. 31 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Tsiku ndi Ora Sizikudziwika
32 “Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha. 33 Khalani maso! Khalani tcheru! Simudziwa pamene nthawi imeneyo idzafike. 34 Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.
35 “Inunso muyenera kukhala maso chifukwa simukudziwa nthawi imene mwini nyumba adzabwere, kaya madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena tambala akulira, kapena mʼbandakucha. 36 Ngati atabwera mwadzidzidzi, asadzakupezeni inu muli mtulo. 37 Zimene ndikunena kwa inu, ndikunena kwa aliyense: ‘Khalani tcheru!’ ”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.