Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yoswa 8

Kuwonongedwa kwa Mzinda wa Ai

Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako. Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.”

Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku nawapatsa malamulo awa kuti, “Mvetsani bwino; mukabisale kuseri kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma nonsenu mukakhale okonzekera nkhondo. Ine ndi gulu langa lonse tikayamba kuwuputa mzindawu, ndipo akadzangotuluka kudzalimbana nafe, ife tidzawathawa monga tinachitira poyamba. Iwo adzatithamangitsa mpaka titawakokera kutali ndi mzindawo, pakuti iwo adzati, ‘Akutithawa monga anachitira poyamba.’ Pamene ife tizidzathawa, inu mudzatuluke pamene mwabisalapo ndi kulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mzindawo. Mukakawulanda mzindawo mudzawuyatse moto. Mukachite monga mwa mawu a Yehova. Amenewa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”

Yoswa atawatumiza, anapita ku malo wokabisalakowo ndipo anadikirira kumeneko. Malowa anali pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma Yoswa anagona usiku umenewu pakati pa gulu lake lankhondo.

10 Mmawa mwake, Yoswa anadzuka nayitana asilikali ake. Tsono iye pamodzi ndi akuluakulu a Aisraeli anatsogola kupita ku Ai. 11 Gulu lonse la nkhondo limene linali ndi iye linatsogolako ndi kukamanga zithando pafupi ndi mzindawo chakumpoto mopenyana nawo. Pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. 12 Yoswa anali atatenga asilikali 5,000 ndi kuwabisa pakati pa Ai ndi Beteli, kumadzulo kwa mzindawo. 13 Anakhazika anthuwo mokonzekera nkhondo. Gulu lalikulu la nkhondo linakamanga zithando zawo kumpoto kwa mzinda, ndipo gulu lina linakamanga zithando zawo kumadzulo kwa mzindawo. Usiku umenewo Yoswa anakagona ku chigwa.

14 Mfumu ya Ai itaona ankhondo a Yoswa, inachita zinthu mofulumira. Inadzuka mmamawa ndipo inapita pamodzi ndi anthu ake ku malo otsika oyangʼanana ndi Araba kuti akachite nkhondo ndi Aisraeli. Koma iyo sinadziwe kuti ayithira nkhondo kudzera kumbuyo kwa mzindawo. 15 Yoswa ndi Aisraeli onse anachita ngati agonja ndi kumathawira ku chipululu. 16 Anthu onse a ku Ai anawuzidwa kuti awapirikitse. Ndipo iwo anapirikitsadi Yoswa uja, ndi kupita kutali ndi mzinda wawo. 17 Palibe munthu wamwamuna wa mzinda wa Ai kapena wa Beteli amene sanatuluke kukapirikitsa Aisraeli. Iwo anasiya mzinda wosatseka ndi kumapirikitsa Aisraeli.

18 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Loza mkondo uli mʼdzanja lako ku Ai pakuti ine ndipereka mʼdzanja lanu mzindawo.” Kotero Yoswa analoza mkondowo ku Ai. 19 Atangotambalitsa dzanja lake, anthu amene anabisala aja ananyamuka msangamsanga pamalo pawo ndi kuthamangira kutsogolo. Iwo analowa mu mzindamo ndi kuwulanda ndipo anawutentha mofulumira.

20 Anthu a ku Ai aja atangochewukira mʼmbuyo anaona utsi uli tolotolo. Koma mpata woti athawireko panalibe pakuti Aisraeli amene amathawira ku chipululu anabwerera nayamba kuwathamangitsa. 21 Yoswa ndi Aisraeli onse ataona kuti obisalira aja alanda mzinda ndipo kuti utsi unali tolotolo, iwo anatembenuka ndi kuyamba kupha anthu a ku Ai. 22 Nawonso Aisraeli amene anali mu mzindamo anatuluka kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho iwo anazingidwa mbali zonse ndi Aisraeli ndipo onse anaphedwa. Palibe amene anatsala wamoyo kapena wothawa 23 kupatula mfumu ya ku Ai yokha imene anayigwira nabwera nayo kwa Yoswa.

24 Aisraeli aja atatha kupha anthu onse a ku Ai amene anali mʼthengo ndi mʼchipululu kumene anawapirikitsira, onse anabwerera ku Ai ndi kupha onse amene anali mu mzindamo. 25 Chiwerengero cha anthu onse a ku Ai, amuna ndi akazi, amene anaphedwa pa tsiku limeneli chinali 12,000. 26 Yoswa sanatsitse dzanja lake limene ananyamula mkondo mpaka ataona kuti onse amene amakhala mu mzinda wa Ai aphedwa. 27 Tsono Aisraeli anatenga zoweta ndi katundu yense wa anthu ophedwa aja, monga momwe Yehova analamulira Yoswa.

28 Pambuyo pake Yoswa anawutentha mzinda wa Ai ndi kuwusiya bwinja monga ulili leromu. 29 Iye anapachika pa mtengo mfumu ya Ai ndipo anayisiya mpaka madzulo. Pomwe dzuwa linalowa Yoswa analamula kuti akachotse mtembowo ndi kukawutaya ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo anawunjikapo mulu waukulu wa miyala. Muluwo ulipobe mpaka lero lino.

Kuchitanso Pangano pa Phiri la Ebala

30 Ndipo Yoswa anamanga guwa lansembe la Yehova Mulungu wa Israeli pa phiri la Ebala. 31 Analimanga motsata zimene Mose mtumiki wa Yehova analamulira Aisraeli, ndiponso potsata zomwe zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose kuti guwa lansembe likhale la miyala yosasemedwa ndi chitsulo. Pa guwalo anapereka kwa Yehova nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. 32 Kenaka anthu onse akupenya, Yoswa analemba pa miyala chitsanzo cha malamulo amene Mose analemba. 33 Aisraeli onse, akuluakulu awo, atsogoleri awo ndi oweruza awo, alendo pamodzi ndi mbadwa, anayimirira mbali zonse ziwiri za Bokosi la Chipangano la Yehova, ena uku ena uku moyangʼanana ndi ansembe a Chilevi. Theka la anthu linayima patsogolo pa phiri la Gerizimu ndipo theka lina patsogolo pa phiri la Ebala, monga momwe Mose mtumiki wa Yehova anawalamulira mʼmbuyomo pamene anawapatsa malangizo podalitsa Aisraeli.

34 Pambuyo pake Yoswa anawerenga mawu onse a malamulo, madalitso ndi matemberero monga momwe zinalembedwera mʼbuku la malamulo a Mose. 35 Yoswa anawerenga mawu onse amene Mose analamula, gulu lonse la Israeli limene linasonkhana likumva. Amayi, ana ndi alendo omwe okhala pakati pawo anali pomwepo.

Masalimo 139

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

139 Inu Yehova, mwandisanthula
    ndipo mukundidziwa.
Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;
    mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga;
    mumadziwa njira zanga zonse.
Mawu asanatuluke pa lilime langa
    mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.

Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe;
    mwasanjika dzanja lanu pa ine.
Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga,
    ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.

Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu?
    Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu?
Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko;
    ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko.
Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa,
    ngati ndikakhala ku malekezero a nyanja,
10 kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,
    dzanja lanu lamanja lidzandigwiriziza.

11 Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu
    ndipo kuwunika kukhale mdima mondizungulira,”
12 komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu;
    usiku udzawala ngati masana,
    pakuti mdima uli ngati kuwunika kwa Inu.

13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
    munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
    ntchito zanu ndi zodabwitsa,
    zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
    pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
    Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
    asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
    ndi zosawerengeka ndithu!
18 Ndikanaziwerenga,
    zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
    pamene ndadzuka, ndili nanube.

19 Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu!
    Chokereni inu anthu owononga anzanu!
20 Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa;
    adani anu amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.
21 Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova?
    Kodi sindinyansidwa nawo amene amakuwukirani?
22 Ndimadana nawo kwathunthu;
    ndi adani anga.

23 Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga;
    Yeseni ndipo mudziwe zolingalira zanga.
24 Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine,
    ndipo munditsogolere mʼnjira yanu yamuyaya.

Yeremiya 2

Aisraeli Asiya Mulungu

Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti,

“ ‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako,
    mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi,
mmene unkanditsata mʼchipululu muja;
    mʼdziko losadzalamo kanthu.
Israeli anali wopatulika wa Yehova,
    anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola;
onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa
    ndipo mavuto anawagwera,’ ”
            akutero Yehova.

Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo,
    inu mafuko onse a Israeli.

Yehova akuti,

“Kodi makolo anu anandipeza nʼcholakwa chanji,
    kuti andithawe?
Iwo anatsata milungu yachabechabe,
    nawonso nʼkusanduka achabechabe.
Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti,
    amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto
natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma
    ndi lokumbikakumbika,
mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima,
    dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’
Ndinakufikitsani ku dziko lachonde
    kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina.
Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langa
    ndi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa.
Ansembe nawonso sanafunse kuti,
    ‘Yehova ali kuti?’
Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe;
    atsogoleri anandiwukira.
Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala,
    ndi kutsatira mafano achabechabe.

“Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,”
            akutero Yehova.
    “Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.
10 Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone,
    tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino;
    ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe:
11 Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene unasinthapo milungu yake?
    (Ngakhale kuti si milungu nʼkomwe).
Koma anthu anga asinthitsa Mulungu wawo waulemerero
    ndi mafano achabechabe.
12 Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi,
    ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,”
            akutero Yehova.
13 “Popeza anthu anga achita machimo awiri:
Andisiya Ine
    kasupe wa madzi a moyo,
ndi kukadzikumbira zitsime zawo,
    zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.
14 Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi.
    Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere?
15 Adani ake abangulira
    ndi kumuopseza ngati mikango.
Dziko lake analisandutsa bwinja;
    mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.
16 Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesi
    akuphwanyani mitu.
17 Zimenezitu zakuchitikirani
    chifukwa munasiya Yehova Mulungu wanu
    pamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu?
18 Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto,
    kukamwa madzi a mu Sihori?
Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya,
    kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
19 Kuyipa kwanuko kudzakulangani;
    kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani.
Tsono ganizirani bwino,
    popeza ndi chinthu choyipa
kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu;
    ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu.
            Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.

20 “Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu
    ndi kudula msinga zanu;
    munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’
Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere.
    Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali
    ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
21 Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika;
    unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika.
Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesa
    wachabechabe wonga wa kutchire?
22 Ngakhale utasamba ndi soda
    kapena kusambira sopo wambiri,
    kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,”
            akutero Ambuye Yehova.
23 “Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse;
    sindinatsatire Abaala’?
Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja;
    zindikira bwino zomwe wachita.
Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro
    yomangothamanga uku ndi uku,
24 wakhala ngati mbidzi yozolowera mʼchipululu,
    yonka ninunkhiza pa nthawi yachisika.
    Ndani angayiretse chilakolako chakecho?
Mphongo iliyonse yoyikhumba sidzavutika.
    Pa nthawi yachisika chakecho mphongoyo idzayipeza.
25 Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi
    ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu.
Koma unati, ‘Zamkutu!
    Ine ndimakonda milungu yachilendo,
    ndipo ndidzayitsatira.’

26 “Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa,
    moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi;
Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo,
    ansembe ndi aneneri awo.
27 Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’
    ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’
Iwo andifulatira Ine,
    ndipo safuna kundiyangʼana;
Koma akakhala pa mavuto amati,
    ‘Bwerani mudzatipulumutse!’
28 Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha?
    Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani
    pamene muli pamavuto!
Inu anthu a ku Yuda,
    milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.

29 “Kodi mukundizengeranji mlandu?
    Nonse mwandiwukira,”
            akutero Yehova.
30 “Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu;
    iwo sanaphunzirepo kanthu.
Monga mkango wolusa,
    lupanga lanu lapha aneneri anu.

31 “Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova:

“Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israeli
    kapena ngati dziko la mdima wandiweyani?
Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda;
    sitidzabweranso kwa Inu’?
32 Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake,
    kapena kuyiwala zovala zake za ukwati?
Komatu anthu anga andiyiwala
    masiku osawerengeka.
33 Mumadziwa bwino njira zopezera zibwenzi!
    Choncho ngakhale akazi oyipa omwe mumawaphunzitsa njira zanu.
34 Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo
    magazi a anthu osauka osalakwa.
    Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba.
Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,
35     inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa,
    sadzatikwiyira.’
Ndidzakuyimbani mlandu
    chifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’
36 Chifukwa chiyani
    mukunkabe nimusinthasintha njira zanu?
Aigupto adzakukhumudwitsani
    monga momwe Asiriya anakuchititsani manyazi.
37 Mudzachokanso kumeneko
    manja ali kunkhongo.
Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira,
    choncho sadzakuthandizani konse.

Mateyu 16

Afarisi ndi Asaduki Afuna Chizindikiro

16 Afarisi ndi Asaduki anabwera kwa Yesu ndi kumuyesa pomufunsa kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.

Iye anayankha kuti, “Kunja kukamada, inu mumati, kudzakhala nyengo yabwino popeza thambo ndi lofiira. Ndipo mmawa mumati, ‘Lero kudzakhala mvula yamphepo popeza thambo ndi lofiira ndi mitambo ya mvula.’ Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a thambo koma simungathe kutanthauzira zizindikiro za nthawi. Mʼbado woyipa ndi wachigololo umafuna chizindikiro chodabwitsa koma palibe ngakhale chimodzi chidzapatsidwa kupatula chizindikiro cha Yona.” Pamenepo Yesu anawasiya nachoka.

Yisiti wa Afarisi ndi Asaduki

Koma atawoloka nyanja, ophunzira anayiwala kutenga buledi. Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani, khalani tcheru ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.”

Iwo anakambirana pakati pawo za izi ndipo anati, “Ichi nʼchifukwa chakuti sitinatenge buledi aliyense.”

Yesu atadziwa zokambirana zawo, anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukambirana zakuti, ‘mulibe buledi?’ Inu achikhulupiriro chochepa. Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza? 10 Kapena buledi musanu ndi muwiri amene anadya anthu 4,000, nanga ndi madengu angati amene munadzaza? 11 Zitheka bwanji kuti inu simukumvetsetsa kuti Ine sindinkayankhula nanu za buledi? Koma inu chenjerani ndi yisiti wa Afarisi ndi Asaduki.” 12 Kenaka iwo anazindikira kuti Iye samawawuza kuti achenjere ndi yisiti wa buledi koma ndi chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.

Petro Avomereza za Yesu

13 Yesu atafika ku chigawo cha Kaisareya Filipo, Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Kodi anthu amati Mwana wa Munthu ndi ndani?”

14 Iwo anayankha kuti, “Ena amati ndi Yohane Mʼbatizi; ena amati ndi Eliya; komanso ena amati Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.”

15 Iye anafunsa kuti, “Nanga inuyo mumati ndine yani?”

16 Simoni Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”

17 Yesu anati kwa iye, “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, popeza si munthu amene anakuwululira izi koma Atate anga akumwamba. 18 Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa. 19 Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.” 20 Pamenepo Iye anachenjeza ophunzira ake kuti asawuze wina aliyense kuti ndi Khristu.

Yesu Aneneratu za Imfa Yake

21 Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa.

22 Petro anamutengera Iye pambali nayamba kumudzudzula kuti, “Dzichitireni chifundo Ambuye, sizingachitike kwa Inu ayi.”

23 Yesu anatembenuka nati kwa Petro, “Choka pamaso panga Satana! Iwe ndi chokhumudwitsa kwa Ine; iwe suganizira zinthu za Mulungu koma zinthu za anthu.”

Za Kusenza Mtanda

24 Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine. 25 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. 26 Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? 27 Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.

28 “Ine ndikuwuzani inu choonadi, ena amene akuyimirira pano sadzalawa imfa asanaone Mwana wa Munthu akudza mu ufumu.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.